Nyanja: Bible for Genesis

Formatted for Translators

©2022 Wycliffe Associates
Released under a Creative Commons Attribution-ShareAlike 4.0 International License.
Bible Text: The English Unlocked Literal Bible (ULB)
©2017 Wycliffe Associates
Available at https://bibleineverylanguage.org/translations
The English Unlocked Literal Bible is based on the unfoldingWord® Literal Text, CC BY-SA 4.0. The original work of the unfoldingWord® Literal Text is available at https://unfoldingword.bible/ult/.
The ULB is licensed under the Creative Commons Attribution-ShareAlike 4.0 International License.
Notes: English ULB Translation Notes
©2017 Wycliffe Associates
Available at https://bibleineverylanguage.org/translations
The English ULB Translation Notes is based on the unfoldingWord translationNotes, under CC BY-SA 4.0. The original unfoldingWord work is available at https://unfoldingword.bible/utn.
The ULB Notes is licensed under the Creative Commons Attribution-ShareAlike 4.0 International License.
To view a copy of the CC BY-SA 4.0 license visit http://creativecommons.org/licenses/by-sa/4.0/
Below is a human-readable summary of (and not a substitute for) the license.
You are free to:
The licensor cannot revoke these freedoms as long as you follow the license terms.
Under the following conditions:
Notices:
You do not have to comply with the license for elements of the material in the public domain or where your use is permitted by an applicable exception or limitation.
No warranties are given. The license may not give you all of the permissions necessary for your intended use. For example, other rights such as publicity, privacy, or moral rights may limit how you use the material.

Genesis

1

1Po yamba, Mulungu anapanga ku mwamba na ziko ya pansi. 2Ziko inalibe maonekedwe yabwino ndipo yenzelibe vinthu vilivonse. Mudima unali pamwamba pa nyanja. Muzimu wa Mulungu unali kuyenda pamwamba pa manzi.3Mulungu nakamba, "lekani kuwale," ndipo kunawala. 4Mulungu anaona kuti kuwala kunali bwino. Anapatula kuwala kucoka ku mudima. 5Mulungu anapasa zina ya kuwala "muzuba," na mudima "usiku." Kwenze kumazulo na kuseni, siku yoyamba.6Mulungu anakamba, "Lekhani pa nkhale kupatuka kwa manzi, ndipo lekani manzi ya patukane ku chokela ku manzi. 7Mulungu anapanga mulenga lenga no patula manzi yanali pansi pa mulenga lenga na pa mwamba pa mulenga lenga. china nkhala mwamena. 8Mulungu ana itana mulenga lenga " Mu mwamba." Iyi mumazulo na kuseni, siku ya chiwili.9Mulungu anakamba, "Lekhani manzi pansi yakhale pa malo yomozi, lekhani malo yo yuma ya aneke," Chi na nkhale mwamene. 10Mulungu ana itena malo yo yuma "ziko." na yonse manzi anaitana "nyanja." anaona ati inali yabwino.11Mulingu anakamba, "lekani ziko ichose vomela: mitenfgo yo bala mbue ndi cipaso mutengo obala cipaso camene mbeu ili mukati, ili yonse yopalana na mutundu wake." chi nkhala mwamene. 12Ziko ina chosa vomela, vomela vochosa mbeu yolingana na mutundu wake. mitengo yo bala cipaso yolingana na mutundu wake. Mulungfu anaona kuti zinali bwino. 13Apa kunli kuma zolu na kuseni. siku yoyamba.14Mulungu anakamba," lekani munkale vo sanika mwamba kuti ku patule usiku na muzuba ndipo vinkale vo uneselako, nyengo, masiku na zaka. 15Lekani vo sanika vili mu mwanba vipase ku wala ziko. Chinali mwamene.16Mulungu anapanga zo sanikila vili vikulu, Ikulu imozi ku lamulila muzuba, ndi ing,ono ku lamulila usiku. Anapanga anso nenyezi. 17Mulyngu anaviyika mu mwamba kuti vizi pasa ku wala pa ziko, 18ku lamulia muzuba ndi usiku, ndi ku patula ku wala kuli mudima. Mulungu anaona ati inli ya bwino. 19Ndiye ku nali ku mazulo ndipo kuseni. siku ya nambala fo20Muliungu anakamba,"lejani manzi ya zule na zo lengewa za moyo za mbili, ndi nyoni zo mbululuka pa mwamba pa pa ziko mu mulenga lenga". 21Mulungu ana lenga vo lengewa vikulu vamu nyanja, na vonse vili na moyo mwatundu wake, lengewe vamene vima yenda ndi zo zulisa manzi konse, ndi zi nyoni zonse zama papiko mwamutundu wake. Mulungu anaona arti inLI BWINO.22Mulungu ana zidalisa, ku kamba kuti nkalani "balanani ndipo mupake," ndipo ku zulisa manzi yamu nyanja. Lekani nyoni zi pake pa ziko. 23Kunali ku mazulo ndipo kuseni.Siku ya faive24Mulungu anakamba,"Lekani ziko iyi chose zo lengewa za moyo, ili yonse ku lingana na mutundu wake, zobeta, vinthu vokwaba, ndipo ni nyama vapa ziko ya pansi, ili yonse ku lingana na mutundu wake". Chinali mwamene. 25Mulungu anapanga vi nyama vonse ku lingN na mutndu wake ndipo vonsew vonse vokwaba pa ntaka na mutundu wake. Anaona ati chili bwino.26Mulungu anakamba,"Lekani ti pange munthu muchi fanizo chatu, muma onekedwe yatu. Lekani ankale na ulamulili pali nsomba zamu nyanja, na pali nyoni zamu mwamba, na zobeta, na zonse zapa ziko ya pansi na vonse vokwaba pa ziko ya pansi. (malembedwe yena ya kalke yali ndi "pa mwamba pa zobeta, pa mwamba pa nyama zapa ziko ya pansi ndipo vonse vo kwaba pa ziko ya pansi") 27Mulungu anakenga munthu mu chi fanizo chake. Mu chi fanizo cjake anamu lenga iye. Mwamuba na Mukazi anaba lenga iye.28Mulungu anaba dalisa ndiku pba uza "Balanani, mupakaise. zulisani ziko ya pansi ndiku gonjesa. Nkalani na ulamulilo pali nsomba zamu nyanja, pali nyoni za mulenga lenga, ndipo vonse vinthu va moyo vamene viyencda pa ziko ya pansi". 29Mulungu anakamba," Ona, naku pasa vomela vopasa mbeu ili pa ziko, na mutengo ulina chipaso chili na mbeu mukati mwake. viza nankala vo kudya vako.30Ku chinyama chili chonse pa ziko ya pansi, nyoni za ku mwamba, na vonse vo lengewe vili na mpepo ya moyo. Napasa vomela vonse kuti vinkale vokudya". Chi na nkala mwamene. 31Mulungu anaona vonse vamene anapanga. Onani, chi nali bwino maningi. Ndiye kunali kumazulo na kuseni, siku ya nambala sikisi

2

1Ndipo kumwamba na ziko yapasi zinalengedwa, na onse vintu vamoyo, vamene vinazulamo. 2Pa siku ya seveni mulungu anasiliza nchito zamene enzeli kuchita, ndiponso ana pumula pa siku ya seveni ku nchito yake yonse. 3Mulungu anandalisa siku ya seveni na kuyi patula chifukwa musiku yakaena anapumula kuchoka ku nchito zake zonse zamene anachita mukulenga kwake.4Izi ndizochitika zokhudza kumwamba ndi dziko lapansi pamene zinalengedwa, pa tsiku limene Yehova Mulungu anapanga dziko lapansi ndi zakumwamba. 5Panalibe chitsamba chamtchire padziko lapansi, ngakhale chomera chamthengo sichinamera, pakuti Yehova Mulungu anali asanavumbitsire mvula padziko lapansi, ndipo panalibe munthu wolima nthaka. 6Koma kunkakwera nkhungu yotuluka pansi nathirira dziko lonse lapansi.7Yehova Mulungu anapanga munthu kuchokela ku doti yapansi, ndipo anamupemela mumpuno mpepo ya umoyo ndiponso munthu anankala wamoyo. 8Yehova Mulungu anashanga munda ku maba mu Eden ndipo mwamene muja anaikamo munthu wamene anapanga.9Kuchokela kudoti yapansi yehova Mulungu analengasa mutengo uli onse ku kula zo oneka ku menso ndipo za bwino kudya. kufakilamo na mutengo na mutenga wa kuziwa chabwino na choipa. 10Mumana unachikela mu Eden kutila munda. Kuchikela apo unamabikana ndipo unankala mimana zili 4.11Zina ya mumana oyamba ni Pishoni, ndiye yamene iyenda ku malo yonse ya Havilah, kwamene kuli golide. 12Golide ya pa malo paja niya bwino. Pamalo paliko na bdellium na mwala wa onikisi.13Zina ya mumana wa chibili ni Gihoni. Weve uyenda mu malo yonse ya kushi. 14Zina ya mumana wa chitatu ni Tigirisi, ndipo uyenda ku maba kwa Asuri mumana wa namba 4 ni Euferetesi.15Yehovah Mulungu unatenga mwamuna naku muika mu munda wa Edeni kuti azisebenzamo naku sungamo. 16Yehova Mu analamulila mwamuna, kuti, " Ndiwe omasuka kudya kuli mutengo uli onse wa m'munda. 17Koma kuchokela mu mutengo oziba vabwino na voipa osadya, chifukwa siku yamene uzakadyako, zoona zoona uzaka mwalila."18Ndipo Yehova Mulungu anakamba, "sichabwino kuti mwamuna ankale eka. Nizamupangila omutundiza omu wamila." 19Kuchokela ku ooti, Yehova Mulungu anapanga nyama zonse zamuziko na nyoni zonse za mumwamba. Ndipo anavibwelesa kuli munthukuona vamene azaviyitana. chili chonse chamene munthu annaitana chilengedwe chai moyo chili chonse, yamene iyo yenze zina. 20Munthu anapasa mazina ku vobeta vonse, ku nyoni zinse za mumwamba, ndipo naku nyama zonse zamu sanga. Koma kuli mwamuna eve kanalibe anapezeka omutandiza umilinga.21yehova Mulungu analengesa munthu kuti agone tulo tukulu ndipo mwamuna anagona. Yehova Mulungu anatenga mbambo imozi ya mwamuna naku valapo pa malo ya tupi pamene abatenga mbambo. 22Na mbambo yamene Yehova Mulungu anatenga kuli mwamuna anapanga mukazi na kumubwelesa kuli mwamuna. 23Mwamuna anakamba, "Manje apa, iyi ni bonzo yama bonzo yanga, na tupi ya tupi yanga. Azaitaniwwa mukazi chifukwa anachokela kuli mwamuna."24Chifukwa cha icho mwamuna aza choka panyumba ya batate bake naba mai bake no kubwela pamozi na mukazi wake ndipo babili aba baza panga tupi imozi. 25Bonse babili mwamuna na mukazi wake banali chitako koma sibenzeli kunvela nsoni.

3

1Lomba njoka yenze yocenjera maningi kucila vinyama vonse vamsanga vamene yawe Mulungu anapanga. Anakamba kuli muzimai, " Nanga Mulungu anakamba kuti, ' Musadye kumutengo uliwonse mu munda?" 2Muzimai anauza njoka kuti, " Tingadye cipaso chamu mitenga ya munda, 3koma pali mutengo wamene uli pakati pa munda, mulungu anakamba kuti, ' simungadye, kapena kucigwira, olo muzamwalira.'"4Njoka inakamba ku muzimai," Simuzamwalila. 5Pakuti mulungu aziwa kuti tsiku muzakadya mesnso yako ya zakasenguka, ndiposo uzaka nkhala monga mulungu, kuziba voipa na vabwino. 6" Pamene muzimai anaona kuti mtengo niwabwino kudya, ndipo nio kondweresa menso, ndipo mtengo wenze wopasa cilako lako copusa munthu nzelu, mukazi anatengapo cipaso anadya anadya ndipo anapasako mwamuna wake wamene enze na eve, ndipo anadya.7Menso yao wonse babili ya nasenguka, ndipo bana ziba kuti binali cinthuko. Anatenga matepo ya mutengo anampanga vovala vao. 8Bana mvera mudidi ua Yehova Mulngu ayenda mu munda mumazulo, ndipo mwamuna na mukazi wake anazibisa beka kutoka ku menso ya Yehova mulungu mu mitengo zamu munda.9Yahova Mulungu anaitana mwamuna nakumufunsa kuti, " Uli kuti?" 10Mwamuna anayankha kuti, " Nakumverari mu munda, nenze na mantha, ndaba nenze cinthako. Nenze nabisama." 11Mulungu anakamba, " Nindani akuuza kuti wenze cinthako? Kodi wadya mumtengo nina kulesa kuti osadyamo?"12Mwamuna anakamba kuti, " Muzimai wamene munanipasa kunkhala naye, ananipasa cipaso camumtengo, ndipo ndinadya." 13Yehova mulungu anakamba kuli mudzimai, " nivichani vamene wacita?" Muzimai anakamba kuti, " Njoka inani nama, ndipo ndinadya."14Yheva Mulungu anakamba na njoka, " Cifukwa wacita ici, iwe weka ndiwe wotembelereka pakati kavinyama vamsanga. uzayamba kuyenda na mala yako, ndipo ndi dothi uzadya masiku yonse ya moyo wako. 15Ndizaipo kuzondana pali iwe na muzimai, na pakati ka mbeu yako na yake. Azamiyula mutu wako, ndipo iwe uza myula kadenene kake."16Kuli muzimai anakaba kuti, " Nizaika maningi kubabo mukubala bana kwako; ni muvobaba uzabala bana bako. Kufuna kwako kuzakuala kwamwamuna wako koma azakulamulila."17Kuli Adamu anakamba kuti, "Cifukwa wa mwera mau ya mkazi wako, wadya kucokela mumtengo, wamene ninaku uza kuti osadyemo,' yotembelereka ni nthaka cifukwa cha iwe; masik yonse uzadya kupitila munchito zobaba. 18Izakulelela minga nazolasa ndipo uzadya vomera mumunda. 19Na cibe capamenso yako uzadya mkate, pakana ubwerere ku dothi, ndaba ndiye kwamene unacoka. Iwe ndiwe dothi, na kudothi uzakabwerela."20Mwamuna anaitana mkazi wake Eva cifukwa enze mai wa vamoyo vonse. 21Yehova Mulungu anapangira Adamu na mkazi wake vovala vavikumba nakubavalika.22Yehova Mulungu anakamba, Manje munthu ankhala monga ise kuziba voipa na vabwino. Manje safunika kuvomekezewa kufika kufupi, ndi kutenga mu mtengo wamoyo, nakudya, na kunkhala namoyo inthawi zonse." 23Ndipo Jehova Mulungu ana mucosamo mu munda, wa Edeni kuti akalime mu nthaka mwamene ana coka. 24Ndipo Mulungu anacosamo mwamuna mu munda, ndipo anaikapo kelebimu ku mawa kwa munda wa Edeni, na lupanga yoyaka yamene yenze kupidamuka kulikonse, cifukwa cosonga njira yoyenda ku mtengo wamoyo.

4

1Mwamuna anaziba Eva mjukazi wake ndipo anankala na pakati naku bala Kaini. Eva anakamba, "Nabala mwana mwamuna na tandizo ya Yehova." 2Ndipo ana bala mubale wake Abelo. Manji Abelo anankala mu busa koma Kaini ulima mu munda.3Vinachitika mukayenda kwa nthawi Kaini analete vipaso vamu munda mongo vopeleka kwa Yehova. 4Koma abelo, analeteko nyama zoyambila kubadwa pali nyama zake na mafuta. Yehova anavomela Abelo na vopalike vake. 5Koma Kaini no vopeleka vake sina vomele. Ndipo Kaini ana kalipa maningi, naku khumundwa.6Yoheva aba uza Kaini, "Nichifukwa chani wakalipa naku khumundwa? 7Ngati wa chita cha bwino siuza vomelewa? koma ngati siuna chite chabwino uchimo ugogoda pa chiseko ufuna kuku lamulila, koma ufunika ku ugonjesa."8Kaini ana kamba na Abelo mu bale wake. Zinachika kuti pamene banali mu minda Kaini anaukila mubale wake naku mupaya. 9Ndipo Yehova anafunsa Kaini, "Alikuti Abelo nubale wako?" Anakamba, "Sinniziba. Nanga ndine malonda wake?"10Yehova akamba, "Nicani chame wachita?" magadzi ya mubale wake yanililila kuchoka pansi. 11Manje wa tembelelewa ku xhokela pansi, pamene pasegula kwamwa kakekulandila muhadzi ya mubale wako kuchoka ku kwanja yako. 12Uka lima munda, kucho manje apa siuzakupasa kuchola mumpavu yake uzankhala othaba mulandu na oyendayenda.13Kaini anakamba kuli Yehova, "Chilango changa chakulisa pitilila vamene ningakwanise. 14Zoona, mwanipitikitsa pa siku ya lelo mu munda uno, ndipo niza bisiwa pa menso panu. Niza nkhala utaba mulandu na oyendayenda mu chalo, na aliyense azanipeza ozani paya ine." 15Yehova anamuuza, "Ngati aliyense aza paya kaini; azabweseewa kasano ndi kabili." Ndipo Yehova anayika chizindikilo pali Kaini kuti ngati aliyense amupedza, uyo muthu si azamu menya.16Ndipo Kaini anchoka pa manso ya Yehova naku nkhala kumalo ya Nodi; ku mawa kwa Edeni. 17Kaini ana ziba mukazi wake nakunkhala na pakati. Anabala Enoki. Anamanga muzi nakuii pasa zina ya mwna wake Enoki mwamuna.18Kuli Enoki kuna badwa Iradi. Iradi anankhala tate wa Mehujeli. Mehujeli anakhala tate wa Methusheli. Methusheli anankhala tate wa Lamekhi. 19Lamekhi ana kwatila ba kadzi babili. zina yamukadzi umodzi inali Ada, na zina yamukadzi wina inali Zilla.20Aada ana bala Jabala. Anali tate wa wonse banali kunkhala muma hema bamene banali na Zobeta. 21Zina yamu bale inali Jubala. Anali tate wa bonse bame amalidza zilimba. 22Koma Zila ana bala Tubala-kaini, opanga Zisulo za munyala ya blonze no nsimbi. Mulongosi wa Tubala-Kaini anali Nama.23Lamekhi ana uza bakadzi wake, "Ada na Zila nvelani mau yanga; imwe akadzi ba lamekhi, nelani vamene nikambe. Chifukwa napaya munthu ndaba anipanga chilonda ine, munyamata pakuti myula ine. 24Ngati Kaini banamubwezela kasano nathibili, ndipo lamekhi azabwezelawa kokwanila sevente seveni.25Adamu ana Ziba mukadzi wake nafuti, ndipo mukadzi wake abala mwana wina mwamuna. Anamu pasa zina yakuti Seti nakukamba kuti, "Mulungu anipasa mwana mwamuna winangu pamalo ya Abelo, chifukwa Kaini anamu paya." 26Mwana mwamuna anabadwa kuli Seti amanupasa dzina yakuti Enosi. Panthawi iyo banthu banayamba kuyitana pa dzina ya Yehova.

5

1Iyi ndiye mbili ya bobadwa kwa Adamu pasiku lamene Mulungu anapanga mutundu wa anabapanga bolingana naye. 2Mwamuna na mukazi anabapanga. Anabadalisa nakuba pasa zina kuti bantu pamene anabapanga.3Pamene Adamu anankhala zaka 130, anankhala tate wamwana mwamuna olingana naye, namaonekedwe yake, anamupasa zina Seti. 4Pamene Adamu anankhala tate wa Seti, anankhala zaka 800. Anankhala tate wa bana bambili bamuna na bakazi. 5Adamu anankhala zaka 930 nakumwalila.6Pamene Seti anankhala zaka 105, anankhala tate wa Enoshi. 7Pambuyo pake anankhala tate wa Enoshi, anankhala zaka 807 na kunkhala tate wa bana bambili bamuna na bakazi. 8Seti anankhala zaka 912, ndipo anamwalila.9Pamene Enoshi anankhala zaka 90, anankhala tate wa Kenani. 10Pambuyo pake anankhala tate wa Kenani, Enoshi anankhala zaka 815. Anankhala tate wa bana bambili bamuna na bakazi. 11Enoshi anankhala zaka 905, ndipo anamwalila.12Pamene Kenani anankhala zaka 70, anankhala tate wa Mahalaleli. 13Pambuyo pake anankhala tate wa Mahalaleli, Kenani anankhala zaka 840. Anankhala tate wa bana bambili bamuna na bakazi. 14Kenani anankhala zaka 910, ndipo anamwalila.15Pamene Mahalaleli anankhala zaka 65, anankhala tate wa Jaredi. 16Pambuyo pake anankhala tate wa Jaredi, Mahalaleli anankhala zaka 830. Anankhala tate wa bana bambili bamuna na bakazi. 17Mahalaleli anankhala 895, ndipo anamwalila.18Pamene Jaredi anankhala zaka 162, anankhala tate wa Enoke. 19Pambuyo pake anankhala tate wa Enoke, pamene anankhala tatea Enoke, Jaredi anankala zaka 800. Anankhala tate wa bana bambili bamuna na bakazi. 20Jaredi anankhala zaka 962, ndipo anamwalila.21Pamene Enocki anankhala zaka 65, anankhala tate wa Methuselah. 22Enoki anayenda na mulungu zaka 300, pambuyo pake anankhala tate wa Methuselah. Anankhala tate wa bana bambili bamuna na bakazi. 23Enoki anankhala zaka 365. 24Enoki anayenda na mulungu, ndiponso anasoba, chifukwa mulungu anamutenga.25Pamene Methuselah anankhala zaka 187, anankhala tate wa Lameki. 26Pambuyo pake anankhala tate wa lameki, Methusela anankhala zaka 782. Anankhala tate wa bana bambili bamuna na bakazi. 27Methuselah anankhala zaka 969. Ndipo anamwalila.28Pamene Lameki anankhala zaka 182, anankhala tate wa mwana mwamuna. 29Anamupasa zina Noah, nokamba kuti " Uyu azatipasa kupumula kunchito zantu na kubaba kwa nchito za manja, zamene tifunika kuchita chifukwa cha ntaka wamene yehova anatembelela."30Lameki anankhala zaka 595 pamene anankhala tate wa Noah. Anankhala tate wa bana bambili bamuna na bakazi. 31Lameki anankhala zaka 777. Ndiponso anamwalila.32Pambuyo pake Noah anankhala zaka 500, anankhala tate wa Shem, Ham, ndi Japheth.

6

1Zinacitika izi pamene anthu anayamba kupaka pa ziko lonse na bana banakazi anabadwa kwa iwo. 2Bana amuna a mulungu anaona bana banakazi ba anthu kuwama. Ndipo anabakwatira kunkhala akaazi awo aliyense anasankhapo wake. 3Yahova anati, " Mzimu wanga suzapitiliza kulimbana na munthu nthawi yonse, cifukwa iye ali munthu. Moyo wake azakala zaka izo."4Vimbinga vinali pa calo pa masiku yaja, ndi pambuyo pake. Izi zinacitika pamene bana ba muna ba mulungu anakwatila bana ba kazi ba anthu ndipo bana balilana bana. Amena anali vimbinga panthawi ija ya kale ndi zomveka.5Yawe anaona kuti kuyipa mtima kwa munthhu kuli kukula pa ziko, ndipo maganizo yao ya mitima yao yanali yoipilathu nthawi zonse. 6Yahova cinamubaba kuti anapanga munthu pa ziko, ndipo anamvela kuipa mumutima wake.7Ndipo Yehova ananena, " Nizacosapo mtundu wa anthu wamene ndina mpanga ine pa calo ca pansi - mtundu wa anthu ndi nyama, ndi zokalaba zonse ndi tunyoni twamwamba, cifukwa nimvela kuipa kuti ninampanga izi." 8Koma Nowah anapeza mwayi pamaso pa Yehova.9Izi ndiye zamena zinacitika kwa Nowah. Nowah analiye munthu wolungama, ndipo pakati pa anthu analibe ili yonse pa nthuwi yake. 10Nowa annayenda na Mulungu. Nowa anakhalatate wa bana bamuna batatu: Shemu, Hamu ndi Jafeti.11Ziko linaipa pa meso ya Mulungu ndipo inali yozula na ciwawa. 12Mulungu danaona ziko; Onani, Inali yoipa kwamnbili cifukwa muntu aliyense woipa mujila yonse ya ziko.13Mulungu anakamba na Nowa, " Naona kuti yakwana nthuwi, kuti nicosepo munthu wonnse cifukwa calo cazola na ciwawa vicitika mwa iye, Zoonadi, Nizabaononga pamozi ndi ziko. 14Koma kuli iwe upange chombo kucokela kuci mtengo ca kipulesi. Upange zipinda mu chombo ndi kuyanzikapo coletsa manzi kungena mkati na kunja. 15Umu ndiye mwamena uzapangila: Kutalimpa kwa chombo ikale mikonoila 300, kufupika kwake mikono ili 50, ndikutalimpa mikono 30.16Upange mtenge wa chombo ndi usilize ndi mkono umodzi kuyambila pa mwamba pa cipuna. Uyikipo ciseko kumbali kwa chombo ndipo upange capansi, cacibili ndi cacitatiu cogonapo. 17Nvela nili pafupi nakubwelesa cigumula ca manzi yambili pa ziko, kuonanga vintu vonse vamoyo va pa ziko. vonse pa ziko vizamwalila.18Koma nizanga chipangano na iwe uzabwela mu chombo, iwe na bana bako bamuna, na mukazi wako, na bakazi ba bana bako bamuna. 19Ndi zolengendwa zonse zamoyo zibili zibili uzibwelese mu chombo, zimuna na zikazi, zinkale na umoyo na iwe.20Vinyoni kulingana na mtundu wake, pa nyama kulingana ndi mtundu wake, pa zokalaba za pa dothi kulingana ndi mtundu wake, zibili zosi yana zizabwela kuli iwe kuzisunga namoyo. 21ika pamozi vakudya vosiyala ndipo usunge kuti vikhale vakudya na vao." 22Ndipo Nowa anacita izi. Kulingana na vonse vamena Mulungu anamulamulila, ndipo anacita.

7

1Yehova ana kamba kuli Nowa, "Bwela, iwe mzonse zamunyumba mwako, mu combo, diponso naoka kutindiwe ulungama pamanso panga mu mbado uwu. 2Pa nyama zonse zo tela utele zi muna zili seveni ndi zikazi zili seveni pa nyama zosa yela, pali izo ulete zibili imunz ndi ikazi yake. 3Ndi nyoninso zamulengalenga ulete zimuna zili seveni kazi zili seveni kuti mutundu wake usasite oa ziko lonse.4Muma siku yali seveni niza lezalengesa nvula ikaloke na ziko kwa ma siku fote ndi usiku fote nizaonanga zonse zamoyo zamane nina panga.'' 5Nowa ana cita vonse vemene Yehova ana mula mulila.6Nowa anali na zaka zobadwa sikisi handredi pamene nvula ina loka paziko ya pansi. 7Nowa, bana bake bamuna, mukazi wake, na bakazi ba bana bake bana nge mu combo chifukwa ca nvula.8Nyama zo yela na zo sa yela, nyoni na vonse vo kwaba pa ntaka. 9Zibili zibili, imuna naikazi, zina bwela kuli Nowa nongena muchombo, mwamene Mulungu analamulila Nowa. 10Ku coka muma siku wali seveni manzi ya mbili yana bwela pa ziko ya pansi.11Mu caka chamene Nowa anali na zaka sikisi handredi mu mwezi wa cibili pa siku ya seventini, pa siku yamene iyi, tusime tonse twa manzi tuna seguka, ndi mazunila aku mwamba yana seguka. 12Nvula ina yamba ku loka ndi kugwa oa ziko ya pansi masiku yali fote zunba ndi usiku.13Pasiku yamene iya Nowa bana bake mbamuna, Shemu, Hamu ndi Jafeti namukazi wa Nowa ndi bakazi ba bana ba Nowa banangena mu Chomba. 14Bana ngena pamozi ndi nyama zamu sanga kulingana ndi mutundu wake, ndi zonse zo beta, kulinga na ndi mutundu wake, ndi zokwaba kulinga ndi mutundu wake, ndi nyoni zonse kulingana ndi mutundu wake ndi zina zolengedwa na mapipippo.15Vibili vibili vitengedwe vonse va mpweya moyovina kuli Nowa naku ngena mu Chombo. 16Nyama zamene zina ngena zanali zimuna nazikazi zotengdwa zonse; zina ngena moonga Mulungu ana mu lamulila. Ndipo yehova anaba valila ci seko.17Ndipo manzi yambili yana bwela pa ziko ya pansi masiku fote, ndipo manzi yana paka naku nyamula chomba cina nyamuka pa mwamba pa ziko. 18Manzi yana zula pamalo yonse ya pa ziko ya pansi naku nyamula chomba pamwamba pa manzi.19Manzi yana nyamula maningi pa ziko ya pansi ndipo malupili yonse yanali pansi palenga lenga yana vininkiliwa. 20Manzi yana nyamuka mikono fifitini pamwamba pamapili.21Vose vamoyo vinali kuyenda pa ziko ya pansi viana mwalila nyoni, zibeto, nyama zamu sanga, na vonse vo lengedwa va moyo vinali vambili pa ziko ko yonse, ndipo na bantu bonse. 22Vonse vamoyo bolengedwa vamoyo vinali kunkala pansi venzo pema mpweya yamoyo kupitila mu mpuno zaba, zina pa.23Ndiponso zonse zamoyo zenze pa ziko zina cosewapo, banthu ndi nyama ndi zokwa ndi nyoni zamlengalenga. Zonse zina onengedwa kucoka pa ziko ya pansi Nowa cabe na banja benze naeve mu chomba bana siyiwa. 24Manzi yanankala pa ziko masiku 150.

8

1Mulungu anaganizila pali nowa, vonse vinyama vamu sanga, na vonse vinyama vo beta pa nyumba ve anali navo mu chombo. Mulungu anapanga mpempo kufuzikila pa chalo, na manzi yana yamba kuyamba kungena pansi. 2Tumigodi twa manzi yapatali namazenela yaku mwamba yana valika na mvula inaleka kuloka. 3Manzi yachigumula yana yamba ku ngena pansi pan'gono pan'gono kuchoka pa chalo, ndipo pambuyo pa masiku iso. Manzi yana ngena pansi.4Chombo chinankazikika papili la Arareti, mu mwenzi wa seveni siku la seveni. 5Manzi yanapitiliza kungena pansi kufikila mu mwenzi wateni pa siku yo yamba ya mwenzi,myamba ya mulupi inayamba kuonekala.6Pamene panapita masiku foti Nowa anasegula zenela yaku chomba chamene anapanga. 7Nakutuma chikwalala chamene chenze mbululuka kuyenda nakubwela futi mpaka kufikila pamene manzi yanayumila pa chalo.8Nowa futi anatuma ka nkunda kuti ka kaone ngati manzi yasilila pachalo, 9koma ka nkunda kana soba po ika mendo yake, naku bwelela kuli eve mu chombo. Nowa anachosa kwanja yake, nakuka tenga, nakuka ngenesa mu chombo.10Anayembekezako masiku seveni yenangu nakutuma futi ka nkunda ku choka mu chombo. 11Ka nkunda kana bwelela kuli eve mu mazulo. Ona! kukamwa kwake kunali tepo yosayuma ya mpesa yotuolewa manse manse. Mwaicho Nowa anaziba kuti manzi pa ziko ya pansi yana ngena pansi. 12Anayembekezako masiku seveni nakutuma futi ka nkunda, koma sikana bwelele kuli eve futi.13Zinali zinachitika mu chaka cha six dundred na chaka cho yamba, mu mwenzi oyamba, pasiku yo yamba yo mu mwenzi, pamene manzi yana yuma mu ziko yapansi. Nowa anasegula cho valila chapa chombo, naku yangana panja, anaona kuti, onani pamwamba pa pansi panze po yuma. 14Mumwezi wachibili, pasiku ya 27 ya mwenzi, ziko yapansi inali yo yuma.15Mulungu anati kuli Nowa,, 16"Choka muchombo, ie, mukazi wako, bana bako bamuna, na bakazi bana bako bamene uli nabo. 17Choka na vonse vamoyo vamene uli navo, vinyoni, vinyama, na vonse vamene vimakalaba pa ziko ya pansi kuti vipake maningi pa ziko yanpasi vika balane naku paka pa ziko yapansi."18Ndipo Nowa anachoka muchombo na bana bake bamuna, mukazi wake, na bakazi ba bana bake. 19Na vilengedwe vonse vamoyo, vonse vokalaba pansi, na vinyoni, vonse vo yenda pa ziko yapansi kulingana na mabanja yao, yina choka muchombo.20Nowa anapanga guwa po pempelela Yehova. anatenga vinyama voyela, na vinyoni voyela naku vipeleka monga nsembe pa guwa yo pempele lapo Yehova. 21Mulungu ana nunsha kafungo ka bwino naku kamba mu mutima wake, "Siniza ka tembelela ntaka futi chifukwa cha bantu, nangu maganizo yamitima yao niyo impa kuyambila ku umwana. Olo kuononga vonse va moyo, monga mwamene na chitila. 22Pamene ziko yapansi ikaliko, ntau yambeu naku kolola kuzizila na kupya, ntau yakupya na ntawi yaku zilila, muzuba na usiku silvzakasiya.

9

1Ndipo Mulungu anadalisa Nowa na bana bake bamuna nakubauza " Mubalane, mupake, na kuzyuzya chalo chapasi. 2Kukuyopa na mantha kuzankala panyama zonse zamoyo pa ziko yapansi, pali nyoni, pali vonse vamene viyanda pansi, na pali nsomba zonse zamu manzi. Vapasiwa mumanja yako.3Vonse voyenda vamoyo vizankhala vakudya kuli iwe. Monga mwamene nina kupusila vomela vobilibila manje nikupasa vonse. 4Koma nyama yamoyo osadya nama gazi yke mukati. koma osadye nyama namoyo wake nama gazi yake-mukati.5Koma mazi yako, moyo ulimu magazi yako, ni zafuna malipilo. Kuchoka ku kwanga ya nyama yonse niza ifuna. Kuchokela kukwanja yamuntu alionse, ndiye kuti, kuchokela kukwanja ya wamene apaya mubale wake, nizafusa iwe pazaumoyo wake. 6Aliyense wamene akhesa magazi yamuntu, nayeve magazi yake yaza kesedwa namuntu, chifukwa muntu analengedwa muchifaniza chake. 7Koma kuli imwe, balanani na kupaka mumwazi zikone pa chalo na kupaka."8Mulungu anakamba na Nowa nabana bake bamene analinabo, kukamba, 9" Kuli ine, velani! Nizasimikiza chipangano changa nayiwe nabonse bana bake bazambadwa mumbuyo mwako, 10chonse chitu chamoyo chamene ulinacho na nyoni na vibeto navonse vilegedwe vapaziko yapasi vilinayiwe pavonse vamene vinachoka muchombo, vili vonse vamoyo vilegedwe vapaziko yapasi.11Ine nizasimikiza zachipangano changa nayiwe sivizakachitikapo futi kuti vamoyo vonse vikaonogeke namazi ya chi gumulu sikuzaka kalapo manzi yachigumula yo ononga ziko yapasi." 12Mulungu anakamba, "Ici diye cho onesa chipangano chamene nipanga pakati payine na ine na vonse vamoto vilegdwe vamene vili nayiwe, kwa bonse bombadwa kusongolo: 13Nafaka utawalenza wanga mumakumbi kuti chikale cho onelako chipagano pakati paine na zinko yapansi.14Izafika tau pamene nizaleta makumbi pazinko yapansi nautawalenza uzaoneka mumakumbi, 15nizaka kumbuka chipangano, chilipali ine na ewe navonse vamoyo, vilengedwe, manzi siyaza kakalapo ya chigumulu yo ononga vonse vilegedwe.16Utawalenza uzakala mumakumbi koma ndipo niza wo ona kuti nikumbukile chipangano chamuyaya chilipakati pamulungu nachose chamoyo chilegedwe chili paziko yapansi." 17Ndipo mulungu kuli Nowa, "Ichi diye chozibisa chipangano chamene ninavomekeza pali ine na vonse vilegedwe va pazinko yapansi."18Bana bamuna ba Nowa bamene bana choka muchibwato banali Semu, Hamu, Yafeti. Hamu anali tate wake Kenani. 19Aba batatu banali bana bamuna ba Nowa, ndipo kuchokela kulibeve zinko yapansi yinazula.20Nowa nayamba kukala mulimi, ndipo anashanga munda wa mpansa. 21Anamwako vinyu na kolewa. Anagona osa vinokila mu hema yake.22Ndipo Hamu, tate wa Kenani, anona chintako cha atate bake an kuuza a bale bake babili panja. 23Mwaicho semu na Yafeti bana tenga chinyula nakuika pa mapewa yao na yamba kuyanda chambuyo naku vini nkila chitako cha a tate bao. Vinso vou vinalangana ku mbali kuti basaune chitako cha atate bao.24Pamene Nowa ana uka anakololoka, azimba vamene mwana wake mwamuna mung'ono anachita kuli eve. 25Ndipo anakamba, " Azankhala otembelelelwa kaini. Azankala kapola wanchito waba bale bake."26Anakamba futi, " Yehova, mulungu wa Semu, adalisike, na Kenani ankale wa nchito wake. 27Mulungu akulise malo ya Yafeti, nakuleka kuti apange nyumba yake mu hama ya Semu. ;lekani Kenani ankhale wachinto wake."28Pamene manzi yachigumulu yanapita nowa anankala zaka fili handiledi na fifite. 29Vonse pamozi masiku ya Nowa yanali naini handiledi anafa.

10

1Aba ndiye bana banabadwa kubana bamuna ba Nowa aba ni, Shami, Hami, na Jafati. Bana bamuna banabadwa kuli beve pamene manzi ya chigumula ina sila.2Bana bamuna ba Jafati banali Goma, Magogi, Medai, Javeni, Tubai, Meshaki na Tilas. 3Bana bamuna ba Goma banali Ashkenazi, Riphati na Togama. 4Bana bamuna ba Javani banali Elisha, Tashishi, Kitimina na Dodanimi. 5Ndiye kwamene bantu benze kunkala kumbali kwa manzi bana patuluka n yenda mumulo yao. Ali ensa na mu kambidwa wao, kulingana na mu koka, na mutundu wao.6Bana bamuna ba Hamu banali Kushi, Mizlaim, Puti, na Kenani. 7Bana bamuna ba Kushi banali Sebai, Havila, Sabtai, Roma na Sabatoka. Bana bamuna ba Rama banali sheba na Dedani.8Kushi anankala Tate wa Nimilodi wamena anali oyamba kuogojetsa pa chalo. 9Anali opaya nyama wa mpamvu pa mansa ya Yehova. Ndiye chifukwa ukambiwa kuti, " Monga nimolodi opaya nyama wa mpamvu pamanso Yehova." 10Malo oyamba ya ufumu yanali Babiloni, Uliki, Aaaaaaaaaaaaaaaakadi, na Kaine, mudela ya Shina.11Ku choka pa malo aya anayenda ku Assilia naku manga Niniva, Rihoboti Iri, Kala, 12Na Reseni, inali ku winiya na Kala. 13Mazlim annkhala Tate wa a Ludite waa Anamitesi, waa Lehabitesi, waa Nafituhitesi. 14Waa Patlusitesi, waakasluhitesi ( kwa mane ar Filisiti ana choka) Na ba Kaftolitesi.15KAnani ana nkala Tate wa Sidoni mwana wake oyamba, nawa Hefi, 16ndeponso wa Jabusites na Amonitesi waa Girgashites, 17waa Hitites, waa Arkitesi, waa Sinitesi, 18waa Aivaditesi, waa Zemalitesi nawa a Hamatitesi. Kuchoka apo mikoka yaa Kanani ina yamba kupaka.19Malite yaa Kanani ana chokela ku Sidoni kuyangana ku GErari, mpaka ku Gaza, monga uyenda ku Sondoma na Gomola, Adima, na Zeboimi, mpaka ku lasa. 20Aba ndiya banali bana bamuna ba hHamu, mwa banja, mwamene ba kambila, kuao ku malo, na kumaziko yao.21Bana bamuna banabadwa kuli Shemu, mukulu wa Jafeti, Shemu na eva ni makolo ya bonse banthu ba a Eba. 22Bana bamuna ba Shamu banali Elamu, Ashul, Alfasadi, Lud na Alamu. 23Bana bamuna ba Alam banali uzi, Hul. Geta, na Misheki.24Alfasadi ana nkala Tate wa Shelah, na Shelah anankala Tate wa Eba. 25Eba anankala na bana babili. Zina ya umozi anali Pelegi, pakuti mumasiku yake chalo china gabanikiwa. Mubale wake zina yake anali Joktani.26Jokatani anankala tate wa Alimodadi, Shelefi, Hazamaveti, Jela. 27Hadolam, Uzal, Dikla, 28Obali, Abimaeli, Sheba. 29Opfili, Havila, na Jobabi. Bonse aba banali bana bamuna ba Joktani30MAlo yao yana chokela ku mesa, konse kufika kou Sfal, na mapili ya ku maba. 31Aba banali bana bamuna ba Shemi, kulingana nami koka yao, na makamibidwe yao na mu malo yao. Kulingana na maiko yao.32Aya yanali mikoka ya bana bamuna ba Nowah, kulingana namibado yao, kulingana namaiko yao. Kuchokela kuli aya maiko yana gabanikana na kuyenda pa chalo panse, pamene manzi ya chigumula yana sila.

11

1Ndipo ndziko lonse lapansi ina sebanzesa chilankulindwe chimozi ndipo banali namau yamozi. 2Pamane benzeli kuyenda yenda ku mawa, bana peza malo ku shina ndipo banankala kwamene.3Banakambisana, "Bwelani, tapange naku shoka bwino mchelwa." Banali na nchelwa mu malo mwa myala na manenekela ngati ndaka. 4Bana kamba, Bwelani tiyeni tizipangile teka muzinda na nsanja yamene izafika kumwamba, ndipo tizipangile zina ife teka. Naati sitizachita, tizapasulidwa mudziko lonse lapansi.5ndipo Yehova anaseluka pansi kuti aone muzinda na nsanja vamene bana ba adamu banamanga. 6Yehova anakamba, ''onani, nibanthu bamodzi nachikambidwe chimodzi ndipo bayamba kuchita ivi! manji manji kulibe chizankala chovuta kuchita pali vamene baganiza kuchota. 7Bwelani tiyende pansi nakusokoneza chilankulidwe chao, kuti basanvelane,"8Ndipo Yehova anaba mwandza- mwandwa kuchoka kuja mu ziko lonse yapansi ndipo banaleka mumanga muzinda. 9Cifukwa chaichi, ziko yaka inali Babelo ku chofukwa kuja Yehova anasokoneza chilankulidwe cha ziko yonse lapansi ndipo kuchokela kuja Yehova anaba mwazamwaza pa ziko lonse.10Aba banali bana ba Shemu. Shemu anali nazaka handredi, ndipo anankala tate wa Arphaxad zaka zibili pamene ciina pita chigumula. 11Shemu anankala zaka 500 Pamene anankala tate wa Arphaxad. Anankala futi tate wabana bamuna nabana bakazi benangu.12Pamene Arphaxadi anali zaka 35 anankala tate wa Shela. 13Arphaxadi ananakala zaka 403 pamene anankala tate wa shela. Anankala futi tate wa bana bamuna na bakazi benangu.14Pamene shela anali na zaka 30 anankala tate wa Eberi. 15Shela anankala zaka 403 pamene anankala tate wa Eberi. Anankala futi tate wabana bena bamuna na bakazi.16Pamene Eberi anali na zaka 34, anankala tate wa Pelegi. 17Eberi anali na zaka 430 pamene anankala tate wa Pelegi. Anankala futi tate wabana bamuna na bakazi benangu.18Pamene Pelegi anali na zaka 30 anankala tate wa Reu. 19Pelegi anankala zaka 209 pamene anankala tate wa Reu. Anankla futi tate wabana bamuna na bakazi.20Pamene Reu anali na zaka 32 anankala tate wa Serugi. 21Reu anankala zaka 207 pamene anankla tate wa Serugi. Anankala futi tate wabana bamuna na bakazi benangu.22Pamene Serugi anali na zaka 30 anannkala tate wa Naholi. 23Serugi anakala zaka 100 pamene anankala tate wa Nahori. Anankala futi tate wabana bamuna na bakazi benangu.24Pamene Nahori anali na zaka 39 anankala tate wa Tera. 25Nahori anankala zaka 119 pamene anankala tate wa Tera. Anankala futi Tate wa ban bamuna n a bakazi benangu. 26Pamene Tera anali na zaka 70, anankala tate wa Abrahamu, Nahori na Harani.27Ndipo aba banli bana ba Tela. Tela anankala tate wa Abrahamu, Nahori, na Harani ndipo Horani anankala tate wa Loti. 28Harani anafela pa pamenso ya Tela tate wake muziko yamene anabadwilamo ku Uri mu Kalidea.29Abrahamu na Nahoro bana tenga bakazi. Zina yamukazi wa Nahoro inali Milika, mwana wa Harani, wamene enzeli tate wa Milika na Isaki. 30Ndipo Sarai anali mkazi wamene senzekubala; anali mwana.31Tela ana tenga Abramu mwamuna wa mwana wake mwamuna Harani, na Sarai mupongozi wake, mukazi wamwana wake mwamuna abranu, ndipo pamozi bana choka mu Uri waku Kalidea, kuyenda ku Harani ya Kenani. Koma bana bwela ku Harani ndipo banankala kwamene. 32Tela anankala zaka 205 ndipo anafela mu Harani.

12

1Ndipo Yehova ana muuza Abrahamu, " Choka muziko yako, nakuli babululu bako, nakuli nyumba yaba tate bako, kumalo yamene ine niza ku langiza iwe. 2Niza mpanga kuchoka kuli iwe, ziko ikulu, nakukudalisa, naku panga zina lako ikulu, uza nkhala daliso. 3Niza dalisa abo bamene bakudalisa, koma amene akuetmbela naine niza batembelela. Kupitila muli iwe mabanja yonse yapa chalo baza dalisika."4gNdipo Abrahamu anayenda, monga mwamene Yehova ana muuzila, na Loti, anayenda na eve. Abramu analina zaka sevente fiive pamene ana choka mu Haran 5Abramu anatenga Sarai, mukazi wake, Loti, mwana wa mubale wake, vintu vawo vonse vamene bana peza, pamodzi na bantu bamene banatenga ku Haran. Bana choka nakuyenda ku malo ya Kanani nakufika mu malo ya Kanani.6Abramu anapitamo mu malo paka kufika ku Shechem, ku mtengo wa Thundu mu Moreh. Pa nthawi ija Akanani anali nkhunkhala mu malo. 7Yehova anaonekela kuli Abramu, naku kamba, " Ku bana bobadwa kuli iwe niza pasa malo aya." Ndipo pamene paja Abramu ana manga guwa kuli Yehova wamene anaonekele kuli eve.8Kuchokela kuja ana vendela ku phiri yaku ziko yaku mawa mu Betele, kwamene anayika hema yake, na Betele kumazulo na Ai ku mawa. Kuja ana manga guwa ya Yehova nakuyitana pa zina la Yehova. 9Ndipo Abramu anapitiliza ulendo, kuyenda moyagana ku Negev.10Kunali njaa mu dziko, ndipo Abramu anayenda ku Egypito ku nkhala, cifukwa njala ina liyi nkhulu kwambili mu dziko. 11Pamene anali kugena mu Egypito, ana kamba naye Sarai mukazi wake, " Ona kuno, ni ziba kuti ndiwe muzimai wokongola. 12Pamene Ai Egypito bakakuona iwe, baza kamba kuti, ' Uyu ndiye mukazi wake,' na kunipaya ine, koma bazakusunga wa moyo. 13Ukambe kuti ndiwe mulongosi wanga, pakuti vinkhale va bwino pali ine cifukwa ca iwe, na umoyo wanga uzapulumusiwa cifukwa ca iwe."14Cina citika kuti pamene Abramu anagena mu Eygpito, AiEygpito anaona kuti Sarai anali wokongola maningi. 15Pamene bana bamuna ba Farao bana muona, naku mutamanda kuli Farao, naku mupeleka muzimai mu nyumba ya Farao. 16Cifukwa ca eve, Falao anamucitila va bwino Abramu, ndipo Abramu analandila mbelele na ngombe, abulu amuna, anchito amuna, anchito akazi, abulu akazi na ngamila.17Ndipo Yehova ana muvutisa Fsrao na nyumba yake na matenda yakulu cifukwa ca Sarai, mukazi wa Abramu. 18Farao ana muyitana Abramu, nakukamba, " Nichani camene wacita kuli ine? Cifukwa ni cani sunani uze ine kuti anali mukazi wako? 19Nicani camene unakambila, 'Nimulongesi wanga,' kuti ni mutenge nkhukhala mukazi wanga? Manje apa, uyu mukazi wako, mutenge, ndipo muyende." 20Ndipo Farao analamulila kuli banyamata bake za eve, nakumupisha, pamodzi na mukazi wake na vonse vamene enze navo.

13

1Ndipo Abramu anayenda ku Negevu kuchokela ku Egipito, yeve, mkazi wake, na zonse zake. Lote naye anayenda nawo. 2Apa Abramu anali wolemela maningi mu viweto, mu siliva, na golide.3Anapitiliza pa ulendo wake kuchokela ku Negevu mpaka kubete, pamalo pamene panali tenti yake kale, pakati pa Betele na Ayi. 4Anayenda kumalo kwamene kunali guwa yamene anamanga poyambila.5Naye Lote, wamene anali paulendo na Abramu, anali naviweto, namatenti. 6Malo anawachepela kuti onse awili ankhale pamozi pafupi na muyake, kamba ka inchi sanakwanise kunkhalila pamozi chifukwa katundu wawo unapakisa. 7Panalinso, kuvutana pakati pa osunga vinyama va Abramu na lote. Pali iyi nthawi muli aya malo mwenze kunkhala ma Kanani na ma Pelizayiti chifukw chake.8Abramu anakambisana na Lote, "pasankhala kuvutana pakati paiwe na ine, ndipo pakati pa sunga vinyama wako na wanga; ndawa, nipachibale apa. 9Malo yonse siyowonekela kuli iwe pitiliza ndipo uzi choseko weka kuli ine. Ngati uzayenda kulefuti ine nizayenda kunangu. Kapena ngati uzayendala kukwanja kodyela, ine nizayenda kulefuti."10Ndipo Lote anayangana yangana nakuona kuti malo onse amanzi a Yolodani yanali yonyolowa bwino paliponse mpaka ku zowa, monga munda wa yawe, monga dothi ya ku Egypito. Apa nishi mulungu akalibe kuononga Sondomu na Gomola. 11Apa Lote anazisankhila payeka malo akufupi namanzi yonse ku mumana wa Yolondono ndipo anyyenda chakumawa, ndipo abalewa anatayikana.12Ablamu anakuda mmalo akukamaru, ndipo Lote anankhala pakati pa tawuni ya kufupi na manzi. Anakonza matenti yake kutali ku sondomu. 13Koma wanthu waku Sondomu na Gomola anali amakhalidwe oyipa, ochimwila Mulungu.14Yawe anakamba na Abramu atatayi koma na Lote. " Yangana kuchokela pamalo pamene wayi milila, kumpoto kumwela, kumawa na kuwesti. 15Aya malo yonse yamene uwona, nizakupasa iwe na mbadiwe zako kwamuyaya.16Niza pakisa amibadwo yako molinga na michenga ya ziko yapansi. kwakuti kapena munthu anga kwanishe kwelenga michanga yapaziko yapasi, ndiye kuti amibadwo woko angawele ngewe. 17Nyamuka uyendeyende muutali na ufupi wa malo aya, pakuti nizayapasa kwa iwe. 18Kamba ka ichi Ablamu ananyamula tenti yake nakubwela kunkhala pa mitenso ya ku mamile, yamene yapezeka ku Hebloni ndipo apo anamanga guwa ya Yehova.

14

1Inofika nthawi ya masikhu ya Amlafelo, mfumu ya ku shima, alioki, mfumu ya elasa, kedalama mfumu ya elamu na fidolo, mfumu yaku Goimu, 2Mpaka ba namenya nkondo yo kangana na Bela, mfumu yaku Sodomu. Besha, mfumu ya Gomola. Shimabu, mfumu ya Adimo, Shemeba, mfumu ya Zeboyimu, na Bela, mfumu, ( wamene baitana kuti Zoa).3Aba bakusogolo mafumu yo kwanla faivi ana gwilizana pa modzi mu malo ya marizi yaku Sidimu, (yamene baitana kuti kite nyanja ya sauti). 4Zaka zokwanila twobvu bamali ku Sebejela kedalaoma, khoma mu chaka cha sateni bana mu ukila. 5Ndiponso mu chaka cafotini, kedalama na mfumu zinali na eve zina bwela ku menya lefaimu mu Ashifaloti Kamoimu ma zuzitesi mu Hamu, ba Emitesi baku shave Kiliataimu. 6Na ba Holitesi mu mapili yaku mapili m'calo caku Sega, polingama ku talipa monga elo palari, yamene ili pafupi na dezeti.7Ndiposo ba nabwelela ndi kufika ku Eri mushipati, ( yamene baitana futi kuti Kadeshi), naku gonjesa calo conse ca ku Amolekaitesi, ndi ba Amolaiti benza nkala ku Hazezoni Tamah. 8Ndiponso mfumu yaku Sodomu, mfumu yaku Gomola, mfumu ya Adama, mfumu ya zeboyimu, na mfumu yamu Bela (yamene boitana futi kuti Zoa) anayenda panja na ku konzelekela nkondo yaku malo ya manzi yaba Sidimu. 9Mokangana na Kedalaoma, mfumu mfumu yaku Elamu. Tido, mfumu yaku Goimu. Amulafelo, mfumu yaku shina Nioki, mfumu elasa, mfumu zili folo zina kangana na zili faivi.10Apa manje m'chigwa ca Sidimu m'nali mo zula ndi migodi ya manenekela, ndipo mfumu zaku sodomu naku Gomola pamene zinali kutaba, zinagwelamo. Ba mene banasala banataba ku ma pili. 11Apa mafumu yamatenga katundu yonse yaku Sodomu na Gomola mangonse zofumkila kuli beve ndipo bana bwelela kwamene bana chokela. 12Pamene bana enda bana tenga na Loti, mwana anabadwa kuba m'bale wa Abramu, wamene anali ku nkala ku Sodom, pamozi nazeke zonse.13Ndipo umozi anapulumuka anam'bweza kuyenda ku udza Abramu mu Hebeli. Wamene anali kunkala pakati pa mitengo yaku mamule, mu Amolite, anali m'bale wa Eshukolo na ana, bonse pamodzi banali kumbali ya Abramu. 14Apo pamene Abramu anavela kuti bodani bagwila mbululu wake, anasongolela amuna bopuzisiwa bo nkondo bobodwila mu banja yake bokwana 318, ndipo anapisha bodani m'paka ku Dani.15Iye ana gabanisa bantu bake bamuna usiku nakuyamba ku menyana nawo, naku bapisha m'paka ku Hoba, yamene ili ku m'polo kwa Damasikasi. 16Ndipo anabwela na zafunikila zonse, na m'bululu wake Loti nazake gonse, na bazimayi na banthu benangu.17Pamene Abramu anabwelela kugonjesa Kedalaona na ma mfumu yanali kumbali yake, mfumu yaku Sodomu ina yenda kukumona naye ku maloya chigwa ku shave ( yamene ba itana kuti malo ya chigwa ca mfumu). 18Melekizedeki, mfu yaku Salemu inabwela na mukate na vinyu. Anali wanaembe wa Mulungu wamukulu.19Ana mudalisa eve pokambakuti, " Adalisike Abramu na Mulungu wake wamu mwamba, wamene analenga ku mwamba na ziko lapansi. 20Adalisike Mulungu waku mwamba mwamba, wamene anakupasa badam bako m'kwanja mwako." Kuchoka apo Abramu ana mupasa chakumi pa zonse zake.21Mfumu yaku Sondomu inakamba kuti Abramu ati, " Nipase bantu, koma tenga katundu yonse niyako." 22Abramu anakamba kwa mfumu yaku Sodomu ati, " Nanyamula manja ku mwamba kuti yawe, Mulungu waku mwamba mwamba, wolenga ziko yaku mwamba napansi. 23Kuti sinizatengapo kantambo, olo kamagila nsapato, kapena chili chonse cako, kuti usakakambepo, 'Ati ninamulemelesa Abramu.' 24Sinizalenga chili chonse kuchosako chabe vamene anyamata ba ny'ono bany'ono banadiya ndiponso mbuli ya nyamata amene ananipelekeza. Lekani Aneli, Esikolo na mamile dengepo mbali yawo.

15

1kuchoka apa mau ya Yehova yanabwela kuli Abulam mumasomphenya, kukamba kuti, "Usa yope, Abramu! ndine wokuchingilila ndipo ndine mphoto yako yaikulu." 2Abramu anakamba kuti, "Ambuye Yehova, muzanipasa chani, pakuti nilibe mwana, ndipo oloba nyumba yanga ni Elyeza waku Damasicus?" 3Abramu anakamba kuti, "Pakuti simunanipase mwana, onani, umozi obadwa munyumba yanga azankhala oni loba!"4Ndipo, onani, mau ya mulungu yana bwela kuli eve, kukamba, "Uyo munthu saza nkhala oloba waku; koma wamene azachokela kuthupi yako ndiye wamene azankhala oloba wako." 5Ndipo anamubwelelsa panja, na kukamba, "Yangana kumwamba, na kupenda nyenyezi, ngati unga kwanise kuzipenda." Ndipo namuuza kuti, "Ndiye mwamene obadwa mwaiwe bazankhalila."6Anakhulupilila Yehova, ndipo chinapendeka kuli eve monga chilungamo. 7Anamuuza iye kute, "Ndine Yehova, wamene anakuchosa mu Uri wa Achaudini, kukupasa malo aya kuti ulobe." 8Anakamba, "Ambuye Yehova, nizaziba bwanji kuti chizankhala choloba changa?"9Ndipo anamuuza kuti, "Niletele ng'ombe ikazi yazaka zitatu, mbuzi ikazi yazaka zitatu, nambelele yazaka zitatu, nkhunda, nanjiba. 10anamulete zonse, ndiku yang'amba pa bili, ndiku vifaka vi langanana, coma sana patulisane nyoni. 11pamene vi nyoni vinabwela pansi pama tupi ya nyama yokufa. Abramu ana vi pisha.12Ndipo pamene zuba inali kuyenda pansi, Abramu anagona tulo ndipo, onani, vonse vi nali pafupi naye vinakhala mudima ndiku yofya. 13Ndipo Yehova anati kwa Abramu,"ziba kuti bobadwa pa mboyo pako bazankhala alendo pa malo yamene si ili yabo, ndipo banhkala mukapolo ndi ovutisiwa.14Nizaweluza calo chija camene bazasebenzela, ndipo kuchoka apo baza choka na vinthu vambili. 15coma muzayenda ku malo yaba tate banu mu mutendere, ndipo muzashikiwa zaka za bwino zaunkhalamba. 16mubadwo wa nambala fo baza bwela futi, po peza machimo yama Amoni yakalibe kufika pama lile,".17Pamene zuba inangena ndipo kwenze mudima, onani, poto yenze na chusi ndi nyali yo yaka pakati kama duswa. 18Pasiku ija Yaweh anapanaga chipangano na Abramu, kukamba kuti, "Kuli bonse bamubadwe bako naba pasa malo aya, ku chokela kumumana wa Iguputo kufikila kumumana yampamvu, Yufurate- 19ma Kenetes, ma Kenezete, ma Kadomonetes, 20ma Hittetes, ma Perizzites, ma Refates, 21ma Amorites, Canaanites, ma Girgashites, na ma jebutes."

16

1Manje Sara, mukazi wa AAAAbrahamu, sana mu barile mwana eye, koma anali na wacito mukazi. Munthu waku Ejipito, wamene zina yake Aga. 2Ndipo Sara ana kamba na Abulahamu. ' Ona, Yehova anigwila ene kusakhala na bana. Enda uka gone na wacito. Ciga nkale kuti nizankhala na bana mwa eye." Abulahamu anavela ku mahu ya Sara, 3pamene Abrahamu anankhala zake 10 mukanani pemozi na Sara, mukazi wa Abulamu, ana pasa aga, wacito wake waku Ejipito, mwa muna wake ku nkhala mu kazi wake. 4Sopano anli chibwezi na Aga, ndipo anankhala namimba. Pamene ana ona kuti ana kuti ankhala namimba. Ana nkhala na chifukwa na omulemba wachito wake.5Ndipo Sara anakamba na Abrahamu, " Uku kulakwa kwanga chifukwa cha ewe. Ni nakupasa wachito wanga mukazi kuti ukale naye, pame anaona kuti ankhala namimba omulemba chito wake. Sinina muko dwelese mu maso yake. Leka Yehova a weluze pakati paine na ewe. 6Koma Abulamu anakamba kuli Sara, " Ona pano, wachito wako muzimai ali mu manja yako. Chita na eve chimane uganiza uza ku wamiza. " Sopano Sara ana chita mwankhaza na eve, ndipo anataba kuchoka kwa eve.7Mu ngelo wa Yehova ana mupeza mu bali ya manzi muchipululu, mu bali ya mumanzi pajila Suri 8Ana kamba, " Aga, wachito wa Sara, uchikelekuti ndipo uyenda kuti? " Ndipo ana yanka kuti, " Nili kutaba kuli unilemba chito wanga."9Mu ngelo wa Yehova ana kamba nae. " Bwelela kuli okulemba chito wako. Zipeleke na kuzi chepesa ku ulomulilo wake." 10Ndipo mu ngelo wa Yehova ana kamba nae, " ni zaku chulukisa kwabili obabadwa kwaiwe. Kuti ba ka khale bubili ochuka osabelengeka."11Mu ngelo wa Yehova anakambaso naye. " Onani, wankala na mimba uzakara na mwana mwamuna. Ndipo uza mu etana Zina Ishemaeli. Chifukwa Yehova a vera kuvutisika kwako. 12Aza nkhala munthu. Ngati bulu wamu sanga, azakhala osa velana na munthu aliyese, ndipo aza siyana naba bale wake."13Ndipo anapase zina iyi kuli Yehova wamene kamba naeye, "Ndiwe Mulungu wamene uniona ine," ndaba ana kamba, " Kodi ne pitiliza ku ona, ngankhale pa buyo poni ona ene? " 14Kwaichoo chi ceme china itanidwa Beaya Roi, Onani, chili pakhati Kadesh ndi Beredi.15Aga ana bara mwana mwamuna kwa Abramu, ndi Abramu anamupa zina mwana wake mwamuna wamene Aga anamu barila, Ishmaeli. 16Abrahamu anali ndi zaka Eite sikisi pamene Aga ana bara Ishmaeli kwa Abramu.

17

1Pamene Abramu anali ndi zaka naite naine, Yehohova anaonekela kuli Abramu ndipo anakamba, " Ndine Mulungu wamphavu zonse. Yenda pamanso panga, ndipo nshala ulibe chifukwa. 2Ndipo ndizasimikiza mapangano yanga ndi ine, ndipo muzapaka nakupitilila."3Abramu anagwada moika wake pansi ndipo mulungu anakamba naye, nati, 4" Kwaine, ona, chipangano changa chili naiwe. Unkhala tate wamaiko ambili. 5Zina yako sizankhala Abramu, koma izakahala Abrahamu ndipo nakusankha unkhala tate wamaiko yambili. 6Ndizakubalisa iwe zaona , ndipo nizapanga mitundu yambili kuchoka mwaiwe, ndipo mafumu azabadwa kuchokela kuli iwe.7Nizapanga chipangano pakati pa iwe na ine na obadiwe pambuyo iwe mumibado yao yonse kwa chipangano chamuyayaya, kukhala mulungu wako na obadwa kwa iwe pa mbuyo pako. 8Nizakupasa iwe, na obadwa kwa iwe pa mbuyo pako, malo amene mukhalamo, malo yonse yamu canaan, malo yamene muzakhala nayo kwamuyayaya ndipo nizankhala mulungu wabo."9Ndipo Mulungu anati kuli Abrahamu, " Iwe, ufunika kusunga chipangano, iwe na obadwa kwaiwe pa mbuyo pako mumibado yao yonse. 10Ichi ni chipangano changa, chamene iwe ufunika kusunga, pali ine na iwe na obadwa kwa iwe pa mbuyo pako: Amina bonse bafunika kudulidwa. 11Bafunika kudulidwa khanda yakusogolo, na ichi chizankala chitsazo chachipangano changa pali ine na iwe.12Bana bonse bamuna bali namatsiku eyiti afunika kudulidwa, mumibado zabantu bako bonse. Kuikilapo na onse obadwa munyumba mwako na iwo amene aguliwa na ndulama kuli alendo amene si obadwa kwa iwe pa mbuyo pako. 13Mwamuna amene abadwa munyumba mwako na wamene waguliwa na ndalama afunika kudulidwa. Mwaicho chipangano changa chizankhala mu nkhanda yanu mu chipangano chosasila. 14Mwamuna aliyense wamene sanadulidwe na mu dulidwe wakanda yakusogolo afunika kuchotsedwa pakati pa bantu bake. Apwanya chipangano chonga."15Mulungu anakamba kuli Abrahamu kuti, " Mukazi wako Sara, osamuitana futi Sarai. Koma Sarah. 16Nizamudalitsa, ndipo nizakupasa mwana mwamuna muli yeve. Nizamudalitsa, ndipo azankhala mai wamaiko ambiri. Mamfumu abantu azachokela kwa yeve."17Abrahamu anagwada nakuika mutu wake pansi, nakuseka ndipo anakamba mumtima wake, " Kodi mwana angabadwe kuli mwamuna alinazaka handiedi? Nizontheka bwanji Sarah, alinazaka naite, kubala mwana mwamuna?" 18Abrahamu anakamba kuli Mulungu kuti, " Ishmaheli azankhalila pamaso panu!"19Mulungu anati, "Iyayi, koma mukazi wako Sarah azakubalira mwana wamwamuna, ndipo uzaka mupasa zina ya Isaki. Nizakhazikisa chipangano changa ndi iye chifukwa chipangano ndi chamuyayaya na obadwa pa mduyo pake. 20Pali Ishmayeli, nakubvela. Ona, namu dalitsa iye ndipo nizamupanga kuchuluka kwambili. Azakhala tate wabana twove achimu amfumu ndipo azakhala dziko yaikulu. 21Koma chipangano changa niza khazikisa ndi Isaki, wamene Sarah azakubalira iwe pa nthawi ino chaka chitubwera."22Pamene anasiliza kukamba nayo, Mulungu anachokapo pali Abrahamu. 23Abrahamu anatenga Ishmayeli mwan wake mwamuna, na bamene bonse banabadwila mumfumba mwake, na bamene bonse banali munyumba mwa Abrahamu, ana dulidwa khanda yao ya kutsogolo pa tsiku yamene ija, monga mwamane mulungu anakambila naye.24Abrahamu anali ndi naite naine zaka zaku badwa pamene anadulidwa khada yaka yakutsongolo. 25Ishmayeli mwana wake anali ndi zaka satini pamene anadulidwa khanda yake yakutsogolo. 26Patsiku imene ija Abrahamu na Ishmayeli mwana wake mwamuna anadulidwa. 27Amuna onse amumumba mwake anadulidwa naye, pamozi nabonse bana badwila munyumba na bonse bamene banagulidwa na ndalama tuchokele ku maiko yene.

18

1Yehova anaonekela kwa Abraham pa mtengo wa Mamre, pamene anankhala pa ciseko pa kazuba ka siku. 2Anayanga kumwamba ndipo, onani anaona bamuna batatu baimilila pasogolo pake. Pamene anabaona, anathamanga kukumana noa kucoka pongenela pa nyumba na kugwanda kuika mu wake pansi.3Anati, "Ambuye banga, ngati napeza mwai mumenso mwanu, napapata musapitilire wanchito wanu." 4Lekani manzi yang'ono yabwekesewe, sambani kumendo, pumulani pansi pa mtengo. 5Lekani nibwelese cakudya cing'ono, kuti muzipumulise imwe mweka. Kucoka apo mungayende, pakuti mwabwelela kwa wanchito wanu. " Bananyankha." Cita monga mwamene wakambila.6Ndipo Abrahamu Anayenda kuli Sara mofulumila, naku muuza kuti, "Endesa, tenga mapimo yatatu ya fulaulo, panga fulawa, upange buledi." 7Pamene apo Abrahamu anatamanga kuyenda ku ng'ombe, nakutenga kang'ombe kamwana kamene kanali kabwino, nakumupasa wanchito, wamene anaenda kukakonza chakudya. 8Eve anatenga mafuta yonunkira na mukaka, na kamwana kang'ombe kamene kanali kanakonzewa, nakuyika chakudya pasogolo pabo, ndipo anayimirira pafupi nawo pansi pa mtengo pomene beve banali kudya.9Ana mufunsa kuti, "Nanga Sara mukaziwako alikuti?" Anayanka kuti, "Ali muja, muhema." 10Ndipo anakamba kuti, Nizabwera kuli iwe nthawi yamasika, ndipo onani, Sara mukazi wako azakankala na mwana mwamuna. Sara apo anali kumvelera pakomo ya hema yamene inali kumbuyo kwake.11Manje Abulahamu na Sara banali banakalamba ndipo banali na zaka zobadwa zambili, na Sara anali atapitirira msinkhu wobala bana. 12Ndipo Sara anaseka m'mtima mwake, nakukamba mumtima mwake kuti, Pamene nankala nkalamba ine nika pezemo kusangalala?"13Yehova anakamba kuli Abrahamu kuti, Nanga nichifukwa chani Sara aseka nakukamba kuti, Nanga nizankala na mwana pamene nakalamba? 14Nanga kuli chamene akangiwa Yehova? Ntawi ngati yamene ino chaka chamene chibwela Sara azankala na mwana mwamuna." 15Koma Sara anakana, kukamba kuti, Sininasekeko ine, chifukwa anayopa. Eve anamuyanka kuti, "Iyi, iwe wenze waseka."16Pamene apo bamuna baja bananyamuka kuti bayende moyang’ana Sodomu. Abrahamu adaenda nabo kukabapelekeza munjira. 17Koma Yehova anakamba kuti, "Kansi nimubise Abrahamu chamene nifuna kuchita, 18po ona kuti Abrahamu azankala mtundu ukulu wamphamvu, ndipo mitundu yonse zapa ziko yapansi zizadalisika muli eve? 19Pakuti ninamusanka kuti alangize bana bake, na banja yake ya kumbuyo kwake, kuti basunge njila ya Yehova, kuchita chilungamo na chiweruzo, kuti Yehova afikilize kwa Abrahamu vamene anakamba na eve.20Pamene apo Yehova anakamba kuti, "Chifukwa chakuti kulira kwa Sodomu na Gomora nikukulu, ndipo chifukwa chimo yawo niyayi kulu maningi, 21nizaselukila kwamene kuja, kuti nikazionele kulila koshushana nayeve kwamene kwabwela kuli ine, ngati nimwamene mwachitikila. Ngati simwamene, nizaziba. "22Pamene apo bamuna baja banapindamuka kucokela kwamene kuja, nakuyenda ku Sodomu, koma 23Abulahamu anasala ali imilile pamanso pa Yehova. Abrahamu ana fendela pafupi nakukamba kuti, "Manje muzawononga bolungama pamodzi na bantu boipa?24Kapena balimo bolungama makumi yasanu mukati mwa mzinda wamene uyu. Nanga muzai ononga yonse, mosayasiya malo aya chifukwa cha bolungama bali makumi yasanu bamene bali mwamene muja? 25Chinkale kutalitali naimwe kuti muchite chamene ichi, kupaya bolungama pamozi na boipa, kuti bolungama nabeve bachiwe munjila imozi. Chinkale kutalitali na imwe! Nanga muweruzi wa ziko yonse yapansi sazachita cholungama?" 26Yehova anakamba kuti," Nikapezamo m'Sodomu bolungama makumi yasanu mukati mwa munzi, nizayasunga malo aya chifukwa chao. "27Abrahamu anayankha nakukamba kuti, "Onani, nachitenga pali ine kukamba naba Ambuye banga, ngakale kuti ndine doti na milota. 28Manje ngati kuzakala chabe bolungama bosakwanila makumi yasanu? Nanga muzawononga muzinda wonse chifukwa cha kupelebela bantu basanu?" Anamuyanka kukamba kuti, "Sininga yese kuwu wononga nikapezako makumi yanayi na yasanu."29Ndipo anakamba nafuti kuli eve kuti, Nanga bakapezekamo chabe makumi yanayi mwamene muja? Eve anamuyanka kuti, "Sinizachita chifukwa cha makumi yanayi yamene ayo." 30Ndipo anakamba kuti, Musakalipe, Ambuye, kuti ine nikambe. Nanga mukapezeka chabe kuti muli bali makumi yatatu mwamene muja." Eve anamuyanka kuti, "Sinizachichita, nikapeza makumi yatatu mwamene muja." 31Ndipo anakamba kuti, Onani, nakamba ba ba Mbuye banga! Manje kapena mwapezeka makumi yabiri mwamene muja. Eve anayanka kuti, "Sinizawononga chifukwa cha makumi yabili ayo."32Anakamba kuti, "Nipempa kuti, musakalipe, Ambuye, ndipo ndipo nizakamba kosiliza. Mwina kapena ni kumi chabe bamene bazapezekamo mwamene muja." Pamene apo anamba kuti, "Sinizawononga chifukwa cha kumi." 33Ndipo Yehova anaenda njila yake pamene anasiliza kukamba na Abrahamu, na Abrahamu anabwerera kuyenda kunyumba kwake.

19

1Ba ngelo banabwela ku Sodom kumazulo, pamene Loti enzenkale pongenela mu muzinda wa Sodom. Pamene Loti anabawona, ananya mukka kuyenda kubatumanya , anangwada no paka mutu wake pansi. 2Anakamba kuti, " Napapata bakulu banchito yanga, niku pempani kuti mubwele kuny' umba kwa wa chitowanu, munkale usiku, musambe naku meendo. Munganya muke kuseeni noyenda njila yanu." Bana yaanta, " Iyayi, tizagona pano pangila." 3Anapapata cho koselela, banayenda na yeve nongena munyumba. Anakoza zokudya nopanga mukate ulibbe vopakisa, ndipo banadya.4pe bakalibe kogona, bamuna ba mumuzida, bamuna bamu Sodomu, bana zinguluka nyumba bana nabakulu bamuna boonse bamumizinda yonse. 5Bana yitana Loti, banati kuli yeve, " balikuti bamuna bamene babwela kuli iwe usiku uno? balete kuli ise, tibazibe."6Ndipo Loti ananyenda panja pachiseko no vala chiseko kumbuyo kwake. 7Akamba, " Namimpempani abbale banga, musachite zo chimwa. 8wayonani, nilina bana bakazi babili bekakalibe kuziba mwamuna. nivomeleseni, niku papatani, kuti nibalete kuli imwe, ndipo muzachita zo kondwelesa aba, chifukwa bamu chinvili chamutenge wanga."9Banati, "bwelela mumbuyo! "Bana kamba nafuti, "uyu anabwela kunkala wachilendo, manje afina kunkala woweluza wata! Manje tizamuchita zoyipa kuchila beve." Banalimbana naye mwa muna, banalimbana na Loti, ndipo bana bwela pafupi kufuna kupwanya chiseko.10Ndipo bamuna banachosa kwanja no donsele Loti munyumba kuli beeve no vala chiseko. 11Balendo ba Loti bna vela menso ya bamuna benze panja pa chiseko cha myumba, bana na ba kulu, ndipo banalema pe benzo josa kusakila chiseko.12Bamuna banakamba kuli Loti. "uliko nawuliwonse pano? Mupongozi mwamuna, mwna mwamuna, mukazi na uliwonse wako mumuzinda, bachose pano. 13Tifuna kuwononga malo ano, chifukwa kulila kwawo kwavenka mamingi kuli yehova ndipo atituma kuti tiwononge malo ano."14Loti anayenda kukamba na azipongizi bake bamuna, bamuna bana lonjeza kukwala bana bake, anati, musanga, chokani pamalo aya, chifukwa Yehova afuna kuwononga muzinda."Kubapongozi bake bamuna chinawoneka monga a seka. 15Pamene kunacha, angelo anawuza Loti, kuti, "yambani kuyenda, tenga mukazi wako na bana bako bakazi bali pano, musanyekele pamozi na chilango chamuzinda."16Anawayawaya. Ndipo bamuna bangwila kwanya kwake, kwanga kwamukazi wake, namanja yabana bake bakazi kuchoka mumuzinda. 17Pebanabachoza panja, mwamuna umonzi anati, "Tamangilani umoyo wani! musayangene kumbuyo, usankale mumalo yalibe kantu kalikonse. Tamangila kulupili kuti musa nyeke."18Loti anati kuli Beeve, "iyaye, napapata, bakulu banchito yanga! 19Wanchito wanu apeza chisomo pamenso yanu, anso mwanilangisa chifundo chopitilila mukupulumusa umoyo wanga. Ndipo siningtamangile kulupili, chifukwa chiwonongeko chachikulu chinganipeze, ndipo nizafa. 20Wona, uja muzinda alipafupi maningi kutabilako, anso nikang'ono napapata, lekani niyenda (sikangono?), Ndipo umoyo wanga uzapulumuka.21Anamuwuzu iye, "Chabwino, Nivomekeza pempo iyo, siniza wononga muzinda ye wakamba. 22Yendesa! tanamanga kja, sinizachita chilichose paka ufikeko." Ndipo uyu muzinda unali zowa.23Pamene zuba inekwele pa ziko Loti anali anafika ku Zowa. 24Yehova analokesa nvula ya Saufa mu mulilo kuchokela kumwamba mu sodom na Gomora. 25Ana wononga mizinda zija, an malo yalibe kantu kalikoonse , nazonse zamoyo zinanili mumuzinda, nazonse zomela pansi.26Ndipo mukazi wa Loti, anali kumbuyo kwake, anayangana kumbuyo, ana sanduka cuulu cha saulti. 27Abrahamu ananyamuka kuseni, no yenda pa malo pamene enze anayimilila ana Yehova. 28Anayanga pansi ku Sodoma na Gomora nowona, chusi chinyamuka kuchioka pansi monga chusi chamu fanasi.29Pomwe Mulungu ana wonnga muzinda wa maloyalibe chilichonse, Abrahamu anabwela mumaganizo ya Mulungu. Anatuma Loti kuchoka pakati pa chiwonengeko pamene anaeononga muzinda wamene Loti analikunkalamo.30Koma Loti anachoka mu Zowa kuyenda kunkala kupili nabana bake babili bakazi, chifukwa anali na manta kunkala mu Zowa. Anankhala mu cimubo ca mulipili. Eve na bana bake bakazi.31Mwana woyamba anawuza mufana wake, "batate bakakota, kulibe bamuna konse kulibe mwamuna azagona naise monga mweba machitila pa ziko la pansi. 32Bwele, tiye timwese batate moba, ndipo tizagona nabo, kuti tusunge mbewu ya batate batu." 33Uja usiku banapasa batate bawo moba. Ndiponso woyambila anayenda nongona nabatate bake; batate bake sibanazibe pe anagona, na pe anawuka.34Siku yokonkapo woyambila anawuka mung'ono, "nvela, nonangona nabatate usiku wapita, Tiye tibamwese moba lelo usiku nafuti, ndipo uzayenda kugona nabo, kuti tisunge mbwe yabatate batu." 35Uja usiku nawo banapasa batate bawo moba, ndipo mung'ono anayenda kugona nabatate bawo. Batate bake sibanazibe pe anagona na pe anawuka.36Bana bonse babili ba Loti banankala na mimba yabatate bawo. 37Woyambbila anabala mwamuna, ndipo anamupasa zina Mohabu. Anankala kolo wana Mobaiti balelo. 38Ndipo mupana wake, anabala mwana mwamuna, no mupasa zina la Ben-ammi-nchipo anankala kolo wa mantu ba Ammoni ba lelo.

20

1Abrahamu anacokako kuja kupita ku malo ya Nagev, ndipo anankhala pakati padesi na suri. Enze mulendo wonkhala mu Gerari. 2Abrahamu anakamba pali Sara mkazi wake, " Uyu ninabadwa naye." Abimeleki mfumu ya Gerari anaitana Sara na kumtenga. 3Koma Mulungu anabwela kwa Abimeleki mu maloto usiku, na kuti kwa eve, " Ona, ndiwe munthu wokufa cifukwa ca mkazi wamene watenga, pakuti ni mkazi wa munthu."4Manje Abimeleki sanabwele pafupi na eve ndipo anakamba kuti, "Ambuye, munga paye ziko yalungama? 5Sanakambe eve eka kwa ine, ' ninabadwa naye, 'Nacita ici mwa ulemu wa mtima wangu na kupanda cifukwa kwa manja banga."6Ndipo Mulungu anakamba kuti kwa eve m'maloto, " Ee, niziba naine kuti mu ulemu wa mtima wako wacita ici, ndipo naine ninakulesa kunicimwila. Mwaici sininakuvomeleze iwe kuti umugwire. 7Mwaici, bweza makazi wa munthu, pakuti ni mneneri. Azakupemphelera, ndipo uzankhala moyo. Koma ngati sumubwezela, ziba kuti iwe na ose amene uli nao zoona muzafa."8Abimeleki ananyamuka kuseni seni na kuziitanila banhito. Anabauza ivi vinthu vonse kwa beve, na banthu banacit mantha. 9Ndipo Abimeleki anaitana Abrahamu na kukamba kuti, " Nicani camene wacita kwa ise? Nakucimwila bwanji, kuti wanibwelesela ine ufumu wanga cimo ikulu? Wanicitila camene siwenzofunika kucita."10Abimeleki anakamba kuti kwa Abrahamu, " Unaona cani kuti ucite ici cinthu?" 11Abrahamu anakamba kuti, " Cifukwa ninaganiza, ' zoona mulibe kuyopa mulungu mu malo muno ndipo bazanipaya cifukwa ca mkazi wanga.' 12Pakuti, zoona ninabadwa naye, ni mwana mkazi wa batate banga, koma osati mwana mkazi wa amai banga; ndipo anankhala mkazi wanga.13Pamene Mulungu ananilengesa kucoka pa nyumba ya batate banga na kuyenda kucoka ku malo aba kupita pa malo pena. Ninakamba kuti kwa eve, ' ufanika unilangize kukhulupilika kwako monga mkazi wanga: Pamalo paliponse pamene tizayenda, ukambe za ine, " Ninabadwa naye." 14Ndipo Ambimeleki anatenga mbelele na ng'ombe, na akapolo bamuna na bakazi, na kubapeleka kwa Abrahamu. Ndipo anambwezela Sara, mkazi wa Abrahamu, kwa eve.15Abimeleki anakamba kuti, " Ona, malo bangaali m'manja mwako. Nkhala paliponse pamene pazakukondwelesa." 16Kwa Sara anakamba kuti, " Ona, napasa wobadwa naye wako ma sauzande ya silive. Ici nikuvinikila zolakwa pali iwe mu menso mwa onse bali na iwe, na pamenso pa aliyense, wapangiwa wonkhalilatu wolungama."17Ndipo Abrahamu anapemphela kwa Mulungu, ndipo Mulungu anapolesa Abimeleki, mkazi wake, na bakapolo bake bakazi kuti bakwanise kunkhale na bana. 18Pakuti Yehova analengesa onse bakazi ba mnyumba mwa Abimeleki bankhaliletu osabala, cifukwa ca Sara, mkazi wa Abrahamu.

21

1Yahova anaikako nzelu kuli Sara monga mwamene ana kambila, na Yahova anachitila Sara vamene ana kamba. 2Sara ana nkhala na mimba nakubala mwana mwamuna wa Abrahamu mu ukhalamba wake pa nthuwi yamene Mulungu ana kamba. 3Abrahamu anamu pasa zina mwana wamene kuli eve, wamene Sara anamu balila, Isaki. 4Abrahamu anamu duka mwana wake Isaki pamene ana kwanisa masiku eiti, monga mwamene Mulungu ana lamulila kuli eve.5Abrahamu anali ana zaka handiladi pamene mwana wake Isaki anabandwa. 6Sara anati, " Mulungu ani lengesa ku seka; bonse banza nvela baza seka naine." Ni ndani ana ganizila kuti. 7Ndiposo Sara anati, " Ni ndani ana ganizila kuti Sara anga nkale na bana koma namu balila mwana mwamuna mubu nkalamba wake.8Mwana ana kula nakuleka ku nyonkha ndipo Abrahmu ana panda chikondwelelo chacikulu pamene ana siya ku nyoka Isaki. 9Sara ana ona mwana wa Haga waku Egipito, wamene ana balila Abrahamu amuseka.10Tsopano anati kuli Abrahamu, " Mu choseni pano kapolo na mwana wake, chifukwa mwana wa kapolo saza nkala oloba pamodzi na mwana wanga Isaki." 11Ichi chinamu nkalila chomu vitisa abrahamu chifukwa cha mwna wake.12Ndipo Mulungu anati kuli Abrahamu, " Osa nkala ovutisiwa chifukwa cha mwana, na kapolo wako. Nvele mau yake yonse yamene akamba pali iyi nkani, chigukwa ni muli Isaki mwamene bonse bodwa bakupaza pasiwa zina. 13Ndipo niza pangaso mwana wa kapolo mukazi ziko, chifukwa nobo badwa wako.14Ndipo Abrahamu anacita kuseni, naku tenga mukate na chikumba cho tengelamo manzi, naku pasa Haga no ika mwana pamusana pake. Ana yenda ku chipululu ku Bereseba. 15Pamene manzi yanasila muchi kumba cho tengamo manzi, anasiya mwna munsi mwa mtengo. 16Ana yenda, ankala patali na mwana, mutunda wa Muvi, anazi kambisa eka, nisaoneko kufa kwa mwana wanga, "' Ndipo ana nkalapo oneka naye, ana bwela ayamba kulilamo kuwa.17Mulungu anamvela kulila kwa mwana, ndipo mungeli wa Mulungu anaitana kuli Haga ku chokela ku mwamba, naku kamba kuli eve, "Ni chani chaku vuta, Haga? Osa yopa chifukwa Mulungu anamvela kulila kwa mwana kwamene alili. 18Nyamuka imika mwana nakumulibisa: chifukwa Nizampanga eve kunkhala ziko ikulu.19Ndipo Mulungu anamu segula menso, nakuona chisime cha manzi. Ana yenda nakuika manzi muchi tumba cha manzi, no pasa mwana kumwa. 20Ndipo Mulungu anali mwana uja, ndipo ana kula. Ana nkala mu chipululu Nunkhala wopaya nyama. 21Ana nkala mu chipululu cha Parana, ndipo amai bako anamu tengela mukazi waku malo ya Egipito.22Ina fika ntawi pamene Abimeleki na Fikolakulu ankonda ana kamba kuli Abrahamu kuti, "Mulungu ali na iwe mu vonse vamene uchita. 23Tsopano vomele na ine pa Mulungu kuti suza chita boza na ine, olo bana banga nangu bonse bo badwa kuli ine. Ni langize malo yemene unali ku nkalamo monga wachilendo mubu bwino chimozi mozi. 24Abrahamu anati, "Na vomela."25Abrahamu ana dandaula pali chisime chamene anamupoka kuli anchito ba Abimeleki. 26Abimeleki anati, " Siniziba wamene ana chita ivo. Koma futi sunai uzepo; panka apa manje." 27Ndipo Abrahamu ana tenga mbelele na ng'ombe naku pasa Abimeleki, na amuna abili naku panga chi pangano.28Tsopano Abrahamu ana tenga bana ba mbelele seveni zikazi naku zi ika [a zeka. 29Abimeleki anati kuli Abrahmu, " Tantauzo ya izi nyama zamene wa ika pa zeka ni chiyani? 30Ana yankha tenga mu manja mwanga zizani nkalila umboni, kuli nina kumba chisime."31Ndipo malo aya anaya ita beresheba, chifukwa bonse babili bana panga lonjezo. 32Ana panga ma panyano pa Beresheba, na Abimeleki na Fikol, mukulu wa nkonda, ana bwelela ku malo ya filisiti.33Abrahamu ana shanga chi mtengo cha tamariski ku Beresheba. Napamene apo ana pempeza Yahova, wamuyayaya Mulungu. 34Abrahamu ana nkala wachi lendo mu malo ya Filisiti masiku yambili.

22

1Pamene ivi vinapita Mulungu anayesa Abrahamu. Anamu uza kuti, "Abrahamu!" Abrahamu anayanka kuti, "Ine nili pano." 2Mulungu anakamba kuti, "Mutenge mwana wako, mwana mwamuna wako eka, wamene ukonda, Isaki, uyende ku malo ya Molaya. Umupase ankale nsembe yoshoka pa pili imozi yakuja, yamene nizaku uza." 3Mwa ichi Abrahamu anaima kuseni-seni, anakwela bulu yake, anatenga banyamata babili bang'ono pamozi na eve, na Isaki mwana wake. Anatyola mitengo zopelekelapo nsembe, nanyamuka ulendo kuyenda kumalo kwamene Mulungu anamu uza.4Pa siku yachitatu Abrahamu anaimya menso nakuyaona malo pataliko. 5Abrahamu anauza banyamata bake kuti, "Lindilani pamene pano na bulu, ine na munyamata tiyenda apo. Tizapembeza naku bwela futi kuli imwe." 6Abrahamu anakonza nkuni za nsembe naku ikapo mwana wake Isaki. Ananyamula kumanja mulilo na lupanga; ndipo bana enda pamozi.7Isaki anauza Abrahamu tate wake kuti, "Batate banga," ndipo banamuyanka kuti, "Ine pano, mwana wanga." Anakamba kuti, "Onani, uyu apa mulilo na nkuni, manje nanga kamwana ka nkosa kopeleka nsembe kali kuti?" 8Abrahamu anayanka kuti, "Mulungu azapeleka eka mwana wankosa wa nsembe yo ocha, mwana wanga." Mwamene umo banaenda, bonse babili pamozi.9Pamene banafika pamalo yamene Mulungu anamuwuzapo eve, Abrahamu anamanga guwa yansembe pamene apo na kuyikapo nkuni zija. Pamene apo anamangilila Isaki mwana wake, nakumugoneka paguwa yansembe, pamwamba pa nkuni. 10Abrahamu anatambasula kwanja kwake nakutenga mupeni kuti apaye mwana wake.11Ndipo mungelo wa Yehova anamuitana eve kuchokera kumwamba kukamba kuti, "Abrahamu, Abrahamu!" ndipo anati, Ine pano. 12Eve anakamba kuti, "Usaike kwanja yako pali munyamata uyo, kapena kumuchita chilichonse choipa, chifukwa manje naziba kuti iwe uyopa Mulungu, popeza kuti sunanikanile ine mwana wako, mwamuna wobadwamo eka."13Abulahamu anaimya menso yake ndipo, onani, kumbuyo kwake kunali nkosa yamphongo yamene inagwiliwa na nsengo zake. Abulahamu anaenda kukaitenga nkhosa yamene ija na kuipeleka monga nsembe yopsereza mumalo mwa mwana wake. 14Ndipo Abrahamu anaitana malo yamene yaja kuti ni "Yehova azapeleka", kufikila na lelo, "Pamwamba pa lupili ya Yehova vizapasiwa.15Mungelo wa Yehova anaitananso Abrahamu kachibili kuchokera kumwamba, 16naku kamba kuti- “Yehova akamba kuti, Ine nalapa pa ine kuti chifukwa wachita chintu chamene ichi, kosanikanila mwana wako mwamuna umozi eka, 17nizakudalisa Nizachulukisa mbewu zako monga nyenyezi za kumwamba, na monga muchenga wa mumbali mwa nyanja; ndipo mbewu zako zizatenga chipata cha adani awo.18Kupitila mwa mbewu yako, mitundu zonse zapa ziko yapansi zizadalisika, chifukwa wamvera mawu yanga.” 19Ndipo Abrahamu anabwelela kuli banyamata bake, ndipo anachoka nakuyenda bonse pamozi ku Biyasheba, ndipo eve anankala ku Biyasheba.20Chinachitika kuti pamene ivi vinapita banamuuza Abrahamu kuti, Milika nayeve anabala bana kuli mubale wako Naholi. 21Aba banali mwana wake woyamba Uzi, mubale wake Buzi, Kemuweli anabala Alamu, 22Kesedi, Hazo, Piludashi, Yidilafu na Betuele.23Betuele anabala Rabeka. Aba ndiye bana basanu na batatu bamene Milka anamubalira Naholi mubale wa Abrahamu. 24Mukazi wake wamung'ono, dzina yake Reuma, anaba nafuti Teba, Gahamu, Tahasi na Maaka.

23

1Sarai anankhala zaka 127. Izi ndiye zaka zawumoyo wa Sarai. 2Sarai anafela mu Kiriti Arba, ndiye kuti, Hebroni, muziko ya Kenani. Abrahamu ana dandaula na kulila Sara.3Pamene apo Abrahamu anayamuka na ku cokako kwa mukazi wake wokufa, na kunena ku bana ba A'Heti, kuti, 4" Ndine mulendo pakati panu. Nipasenikoni malo ya manda pakati pa imwe, kuti ni ike wanga okufa.5Wana wa Heti bana muyankha Abrahamu, kuti, 6" Tiveleni ife, bwana wanga. Ndimwe mwana wa mfumu wa Mulungu pakati katu. Ikani wokufa wanu mumanda yathu ya bwino. Kulibe amene azakulesa manda yake, kuti uyikemo wa kufa wako."7Abrahamu ananyamuka naku gwanda kubantu amudziko, kuli bana A'Heti. 8Iye anakamba nabo, kuti ngati imwe mwavomela kuti n ike bokufa wanga, manje ninveleni na kunimpepelako kuli Efulon mwana wa Zohari, kuli ine. 9Muni funsileko kuti aningulise kavu ya Machipela, yamene alinayo, yamene ili kumapeto yakumunda wake. Pa mutengo wake wonse, anigulise powonekela ngati malo yoyikapo ba kufa."10Isapano Efroni anali anankhala pakati pa bana ba Heti, ndipo Efroni Mhiti anayanka Abrahamu mu manso ya bana ba Heti, na bonse bamene bana bwela mu geti yamu zinda wake, kuti, 11iyayi, bwana wanga, niveleni ine, naku pasani munda, na kavu yamene ili mukati. Nakupasa iwe pa manso ya bana ba banga. Nakupasa iwe kuti uyike okufa wako."12Pamene apo Abrahamu anagwanda pa manso pa bantu a mudziko. 13Anakamba na Efron mukuvelela kwa bantu bamu dziko, kuti, koma ngati mufuna, napapata niveleni. Nizalipila zamunda. Tengani ndalama kuchokela kuli ine, ndipo niza ika wokufa wanga kuja."14Efron anayankha Abrahamu, kuti 15" Chonde, bwana wanga, niveleni ine. Ka malo ka nthaka ko kwanila muyeso wafolo handredi ma shekeli ya siliva, ni cani ici camene cili pakati pali ine na iwe? Ika wakufa wako." 16Abrahamu anavelela kuli Efulon ndipo Abrahamu ana pimila Efulo muyeso wa siliva wamene ana tomola pokamba milandu nabana bamuna ba Heti, Folo handiledi ma shekelo ya siliva, kulinga na kapimidwe ka bwino kama londa.17Munda wa Efulon, wamene unali mu Machifela, wamene unali pa fupi na mamre, uyo ndiye yonse yamene inali mu munda na konse muma lile, vina pasiwa 18Bana vingulisa kuli Abrahamu pa manso ya bana bamuna ba Heti, pali bonse bamene benze bana bwela mu geti ya mu zinda wake.19Pasongolo pake, Abrahamu ana yika thupi ya Sara mukazi wake mu kavu ya mu munda wa machipela, wamene uli pafupi na Mamre, uyu ndiye Hebloni, muziko ya Kanani. 20Ndipo munda na kavu vinalimo vina pasiwa kwa Abrahamu kuti vinkhale katundu wake woyikilamo malilo, kucokela ku bana ba muna ba Heti.

24

1Manje Abrahamu anali anakula maningi ndipo Yehova anamudalisa Abrahamu muvinthu vonse. 2Abrahamu anati kwa wanchito wake, wamene anali mukulu pa nyumba yake ndiponso wamene anali kulamulila zonse anali nazo, "faka kwanja kwako pansi pa chibelo changa. 3Ndipo nizakulapisa iwe pa Yehova, Mulungu wakumwamba, ndi Mulungu wapansi, kuti usakamutengele mukazi mwana wanga mwamuna kuchokela kwa Akenaniwo, mwamene napanga nyumba yanga. 4Koma uzayenda ku Ziko yanga, kuli ba bale banga nakumutengela mukazi mwana wanga Isaki.5Wanchito anakamba naye kuti, nanga ngati mukazi sazafuna kunikonkha kuziko lino? Nizakamutenga mwana wanu ku Ziko kwamene munachokela imwe? 6Abrahamu anamuuza kuti, "uone kuti usakamutenge mwana wanga kwamene uko. 7Yehova Mulungu wakumwamba, wamene ananitenga ine kuchoka kunyumba ya batate banga na ku Ziko laba bale banga wamene anakamba na ine na kulumbila kwa ine kuti, ku mbeu zako nizakupasa iyi Ziko,''wamene azatuma mungelo kuyenda pasogolo pako kuti akusogolele kutenga mukazi wa mwana wanga kwamene uko.8Koma ngati mukazi sazafuna kukukonkha iwe, uzankhala omasuka pakulapila kwanga. koma siufunika kutenga mwana wanga kwamene uko. 9Ndipo wanchito anaika kwanja kwake pansi pa chibelo cha Abrahamu bwana wake, ndipo analapila kwa iye pa chintu chamene icho.10Wanchito anatenga kuchokela kwa bwana wake ngamira zili teni ndipo anayambapo. Anatenganso mpaso zosiyana siyana kuchokela kuli ba bwana bake. Ananyamuka na kuyenda ku gawo la Aramu Naharaimu, ku muzinda wa Nahori. 11Anagwadisa ngamira kunja kwa muzinda kuchisime cha manzi. Iyi inali ntawi yakumazulo pamene bakazi banachoka kuyenda mukutapa manzi.12Ndipo anati, "Yehova, mulungu wa ba bwana banga ba Abrahamu, nipaseni kupambana ine lelo ndi kukulupilika kwanu muchipangano ndi Bwana wanga Abrahamu. 13Onani, Ine naimilila pa chisime cha manzi, ndipo nana bakazi ba mu muzinda babwela mu kutapa manzi. 14Lekani chichitike motele, nikauza musikana, "napapata bweza pansi mugomo wako kuti nimweko manzi, ndipo azakamba kuti, Imwa, ndipo nizamwesanso na ngamira; wamene uyo ankhale mukazi osankila kapolo wanu Isaki. Pali ichi nizaziba kuti mwalangiza kukulupilika kwa chipangano kwa bwana wanga.15Chinachitika kuti pamene akalibe kusiliza kukamba, Onani, Rebeka anachoka ndi mugomo wake pa pewa. Rebeka anabadwa kwa Batuele mwana wa mwamuna wa Milika, mukazi wa Nahori, mubale wa Abrahamu. 16Uyu mukazi anali wabwino ndiponso anali namwali. Sanazibepo mwamuna. Anaselukila ku chisime, ndipo anazulisa mugomo wake nakukwela pamwamba.17Ndipo wanchito anatamanga kuti akumane naye nakukamba kuti, napapata nipaseko yang'ono manzi mu mugomo wako. 18Änati, Imwa, bwana wanga,"ndipo anayendesa nakubweza pansi mugomo wake mu manja mwake nakumupasa cha kumwa.19Pamene anasiliza kumupasa chakumwa, anati, "Nizatapa manzi ya ngamira zako, mpaka zimwe zonse." 20Ndipo anayendesa na kuchosa mu mugomo nakufaka muchomwelamo, nakutamangila kuchisime mukutapa manzi ya ngamira zonse."21Mwamuna anamulangana iye osakamba kanthu kuona kuti kapena Yehova anamuyendesa bwino mu ulendo wake kapena iai. 22Pamene ngamira zinasiliza kumwa , mwamuna anachosa mpete yapampuno ya golide kulemela kwake sikelo lateka, na vibili va golide vibango vaku manja kwake volemela teni lateka. 23Ndipo anafunsa, "Ndiwe mwana wa bandani? Niuze napapata, kodi kuliko malo kuli ba tate bako kunyumba tigoneko usiku?24Anayankha kuti, Ine ndine mwana wa Betuele mwana wa wamwamuna wa Milika, wamene anabala kwa Nahori." 25Anamuuza futi nati, tili na wambili uzu na vakudya ndiponso na malo yogonamo usiku.26Mwamuna anagwada na kuyamika Yehova. 27Anati, adalisike Yehova Mulungu wa bwana wanga Abrahamu, wamene sanakane ku kulupilika kwa chipangano ndi chifundo chake mwa bwana wanga. Koma monga ine , Yehova anisogolela munjila ya kunyumba ya ba bale ba bwana wanga.28Ndipo mukazi wachichepele anatamanga nakuuza baku nyumba ya ba Mai bake vonse vintu. 29Manje Rebeka anali na mulongsi wake zina lake Labani. Labani anatamangila mwamuna wamene anali kunja kumuseu waku chisime. 30Pamene anaona mpete ya pampuno ndi vibango vakumanja kuli kalongosi wake, na pamene ananvela mau ya Rebeka mulongosi wake, ivi ndiye vamene mwamuna aniuza, anayenda kuli mwamuna, ndipo onani, anaimilila na ngamira pa chisime.31Ndipo Labani anati, "bwela, Iwe wodalisika wa Yehova. Ni chani uimilila panja? Nakonza nyumba na malo ya ngamira." 32Ndipo mwamuna anabwela kunyumba nakumasula ngamira. Ngamira zinapasidwa mauzu na vakudya, na manzi yanapasidwa kuti asambe kumendo na mendo yaba muna bonse banali naye.33Banamukonzela vakudya, kuti adye, koma anati, sinizadya nikalibe kukamba vamene nifuna kukamba. "Koma Labani anamuuza kuti, "Kamba." 34Anamuuza kuti, ndine wa nchito wa Abrahamu." 35Yehova anamudalisa bwana wanga kwambili ndiponso niolemela. Anamupasa iye nkosa na ng'ombe, siliva na golide, ba nchito bamuna na bakazi, ndi ngamira naba bulu.36Sara, mukazi wa bwana wanga, anabala mwana mwamuna kwa bwana wanga pamene bwana wanga anakota, ndiponso anamupasa vonse vinali vake. 37Bwana wanga ananilumbilisa ine kuti, usamutengele mwana wanga mukazi waku Kanani, mu malo mwamene ine ninkhala. 38Koma, uyende ku banja ya batate banga, nakuli ba bale banga, nakutenga mukazi wa mwana wanga.39Nizamuuza bwana wanga, "nanga ngati mukazi sazanikonkha." 40Koma ananiuza kuti, "Yehova wamene niyenda naye, azatuma mungelo na iwe nakukudalisa munjila yako, kuti umutengele mwana wanga kuchokela kuli ba bale banga na kuli ba banja ba batate. 41Koma uzankhala omasuka ku chipangano changa ukabwela kuli ba bale banga iye kuli iwe. Ndipo uzankala omasuka ku chipangano changa.42Ndipo nafika lelo ku chisime cha manzi, nakukamba, Yehova, Mulungu wa bwana wanga Abrahamu, napapata, ngati muzaniyendesa bwino munjila yanga- 43Nilipo pano, naimilila pa chisime cha manzi---lekani mukazi azabwela kutapa manzi, mukazi wamene nizauza, napapata nipaseko manzi yang'ono mu mugomo wako kuti nimwe." 44Mukazi azaniuza ine, "Imwa, ndiponso nizapasa manzi na ngamira zako."lekani ankhale mukazi inu, Yehova, mwamusankha wa mwana wa bwana wanga!45Nikalibe kusiliza kukamba mumutima mwanga, Onani, Rebeka anachoka ndi mugomo wake pa pewa yake, na kuselukila ku chisime na kutapa manzi. Ndipo ninamuuza, napapata nipaseko manzi yakumwa. 46Mwamusanga anatula mugomo wake pachipewa nati, "Imwa, ndiponso nizapasa ngamira zako manzi. Ndipo ninamwa, ndipo anamwesanso na ngamira.47Ninamufunsa nati, ndiwe mwana wa bandani? anati, ndine mwana wa Betuele, mwana wa mwamuna wa Nahori, wamene Milika anabala kwa Iye. Ndipo ninafaka mpete pampuno yake na vibango kumanja yake. 48Ndipo ninagwesa nkope yanga na kulambila Yehova, na kutokoza yehova, nakudalisa Yehova, Mulungu wa bwana wanga Abrahamu, wamene ananisogolela ine munjila, kuti nikamupezele mwana mukazi wake wa banja ya bwana wanga wa mwana wake mwamuna.49Sopano, ngati muli okonzeka kulangiza chikondi cha zoona na chikulupililo kwa bwana wanga, niuzeni. Ngati iai, niuzeni, kuti nipatukile ku kwanja kwaku manja kapena kukwanja ya manzele.50Ndipo Labani ndi Batuele anayankha kuti, Ichi chintu chachokela kwa Yehova: Sitingakambe kwa iwe choipa kapena chabwino. 51Onani, Rebeka ali pamenso pako, mutenge ndipo uyende, kuti ankhale mukazi wa mwana mwana wa bwana wako , mwamene Yehova akambila."52Pamene wanchito wa Abrahamu ananva mau yawo, anagwesa nkope pansi pamenso ya Yehova. 53Wancito uyu anatulusa zabwino za siliva na zabwino za golide, na vovala nakumupasa Rebeka. anapasanso mpaso zabwino kwa mubale wake nakuli ba Mai bake.54Ndipo iye na bamuna anali nawo ba nadya na kumwa. Banankhala kuja usiku bonse, ndipo pamene banauka kuseni, anati, nitumeni kwa bwana wanga. 55Mubale wake na ba Mai bake banati, lekani mukazi mun'gono ankhale naife masiku yang'ono masiku yali teni.56Koma anabauza kuti, "musanichingilize, chifukwa Yehova ananidalisa munjila yanga. Nitumeni kuti ningayende kuli bwana wanga. 57Banati, "tizamuitana mukazi wamung'ono nakumufunsa." 58Ndipo banamuitana Rebeka nakumufunsa, "uzayenda nauyu mwamuna?"Iye anayankha, "Nizayenda."59Ndipo banamutuma kalongosi wawo Rebeka, pamozi naba nchito bake bakazi, muulendo wake pamozi ndi wanchito wa Abrahamu na banthu bake. 60Banamudalisa Rebeka nati, "mulongosi watu, leka unkhale make wa bana wanu sauzandi ndi teni sauzandi, ndipo leka bana bako batenge makomo ya bonse bamene babazonda.61Ndipo Rebeka ananyamuka, iye naba nchito bake bakazi nomanga pa ngamira, nakumukonkha mwamuna. Wanchito uja anamutenga Rebeka nakuyenda naye. 62Isaki anali kunkhala ku Negev, ndipo anachokela ku Beer Lahai Roi.63Isaki anachoka kuyenda mukuganiza mu munda kumazuloNdipo analangana kusogolo nakuona, Onani, kunali ngamira zinali kubwela." Rebeka analangana, pamene anaona Isaki, anaseluka pa ngamira. 64Anauza wanchito wake, "Nindani uja mwamuna wamene ayenda mumunda kubwela kuti akumane naife? 65Wanchito anati, "Ni bwana wanga."Ndipo iye anachosa chovinikila kumenso, nakuzivinikila.66Wanchito anamuuza Isaki vonse vamene anachita. 67Ndipo Isaki anamubwelesa iye kunyumba kwa Sara amai bake, nakumutenga Rebeka, nakunkhala mukazi wake, ndipo anamukonda. Ndipo Isaki anatontozedwa pambuyo pa infa ya ba Mai bake.

25

1Abrahamu a natenga mkazi wina, zina yake enze Keturah. 2Ndipo anambalira iye Zimirani, Yokisani, Medeni, Midiyani, Isibaki ndi Suwa. 3Ndipo Yokisani anakhala taet wa Sheba na Dedani, bana ba Dedani banali ba Assyriarl, ndi Letosu, ndi Leum. 4Bana ba Midian bamuna benze Ephari, Epheri, Harlok, Abida, na Eldaah, bonse aba benze bana ba Ketura.5Abrahamu anapasa Isaki vinthu vake vonse. 6Koma pene enze namoyo, anapasa mphaso bana bamuna ba bakazi bake bang'ono naku batuma kuziko la kumawa, kubacosa kuli Isaki, mwana wake.7Aya ndiye yannali masiku yazaka zimene Abrahamu anakhala namoyo, zake 175. 8Abrahamu anapema kosiliza ana walila nazaka zabwino zokolamba, munthu nkhote namoyo okwana, anatengewa kuli banthu bake.9Isaki na Ishumaele bana bake, bana muika mumphanga isa makipela mu munda wa Ephrori mwana wa zohari mu hitati, yamene iri pafupi na mamure. 10Munda wamene Abrahamu enze anangula kuli bana ba Heti. Ndiye Abrahamu na mkazi wake Sara banai kiwa. 11Pambuyo paimfa ya Abrahamu, mulungu anadalisa mwana wake Isaki, ndipo Isaki enze kunkhala pafupi na Beeri Lahai Roi.12Ndipo aba ndiye benze bana ba Ishumaele, mwana wa Abrahamu yamene Hagara mu Egipito, kapolo wa Sara, anabalira Abrahamu.13Aya ndiye ynze mazina ya bana ba bamuna ba Ishumaele kulingana namwamene banabadwira: Nabioti woyamba wa Ishumaeli, Kedar, Adbeel, Mibsam, 14Mishma, Duma, na MAsa, 15na Hadad, Tema, Jetur, Naphish, na Kedemah. 16Aba ndiye benze bana ba Ishumaele, ndipo ndiye yenze mazina yao, kulingana na mizi yao na misasa zao; akalonga 12 kulingana na mitundu yao.17Izi ndiye zaka zamoyo wa Ishumaele, zaka 137, ndipo iye anamwalira, ndipo anatengawa kuli bathu bake. 18Ndipo banakhala, kuyambira ku Havilah na kufika ku Ashhuri, yamene ili pafupi na Egipito, monga iyenda ku Assirila. bankhala boyambana bekha bekha.19Ivi ndiye venze vocitika va Isaki, mwana wa Abrahamu, Abahamu ana bala Isaki. 20Isaki enzeli na zaka 40 pamene kwatira mkazi wake Rabeka, mwana wa Betuero mu Aramearl wa ku Paddors Arars, Mlongo wake wa Labari mu Aramearl.21Isaki anapemphelera mkazi wake kwa Tehova cifukwa senze kubala, ndipo Yehova anayankha pemphero yake,ndipo mkazi wake Rabekah anakhala navumo. 22Bana banavutana muvumo mwake , ndipo anakamba kuti, " Cifukwa ni chani ivi vicitika kuli ine?" Ndipo anayenda kufusa Yehova pali ivi.23Yehova anakamba nayeve, " Maziko yabili yali mu vumo mwako, Mangulu yabili ya banthu ya zachoka muli iwe, gulu izakhala ya mphavu kucila inzake, ndipo mkulu azakhala kapolo wa mufana."24Pamene nthawi yobala inakwana, Taonani, mwenze ba mpundu mu vumo. 25Mwana woyamba anacoka wofiila monse monga chovala camasaku, ndipo ana mupasa zina yake Esau. 26Pambuyo pake mubale wake anacoka, kwanja kwake kunagwira kadenene ka Esau. Anapasiwa zina ya Yakoba. Isaki enze nazaka 60 pamene mkazi wake anabala.27Ndipo banyamata banakula, ndipo Esau anakhala oziba kusakira nyama, munthu wa msanga. Koma Yakobo enze munthu wa zii, wamene enze kukhala mumatenthi. 28Ndipo Isaki anakonda Esau cifukwa anadya nyama zamene anasakira, koma Rabekah anakonda Yakobo.29Ndipo yakobo anaphika supu, Esau anabwera kucoka kusanga, analema nanjala. 30Esau anakamba na Yakobo ati, " Nipaseko supu yofilla napapata nalema!" Ndiye cifukwa zina yake enze Edomu.31Yakobo anakamba kuti, " Coyamba unigulise ukulu wako," 32Esau anati ona nili pafupi nokufa, ukulu uli nanchito bwanji kuli ine? 33Yakobo anakamba kuti, " Yambira kulumbirira kuli ine" Ndipo Esau analumbila njazi ndipo mnjira iyo anagulisa ukulu waka ku Yakobo. 34Yakobo anapasa Esau mkate na supu yo phika, ndipo anadya na kumwa, ndipo ananyamuka noyenda. Esau anapepusa ukulu wake munjira iyi.

26

1Ndipo kunali mu ziko, kumbali kwanjala yoyamba yamene ina chitikka muma siku ya Abrahamu. Isaki anayenda kuli Abimeleki, mfumu yaba Aphistini ku Gela.2Manje Yehova anaonekela kuli eve naku muuza kuti, "usayende ku Egypito; nkala mu ziko yamene nakuuza kunkala. 3Nkala mwamene muno mu zika. Ndipo niza nkala naiwe naku kudalisa iwe; kuli iwe naku bobadwa muli iwe, nizakupasa ma ano chamene ninalapila kuli Abrahamu tate wako.4Nizapakisa bobadwa mwa iwe monga nyenyezi za kumwamba, ndipo nizapasa kuli bobabdwa mwa iwe maziko yonse ayakupitila muli iwe maziko yonse ytapansi yazadalisika. 5Nizachita ichi chifukwa Abrahamu ananvelele mau yanga nakusunga malangizo yanga, lamulo langa, malemba yanga, na malamulo yanga."6Ndipo Isaki anankala ku Gerari. 7Pamene bazimuna bana funsa pali mukazi wake, anakamba. "Nimulongo wanga." ananvela mantha kukamba, "Nimu kazi wanga," chifukwa enzekuganiza, bazimuna bakuno ku malo bazani paya kuti batenge Rabeka, chifukwa niwabwino." 8Pamene Isaki anakalako maningi kuja Abimelelki mfumu wabo ba Philistini ana sonjela pa (Zenela). Anayanga onani, Isaki anali ku gwila Rabeka, mukazi wake.9Abimeleki ana muitana Isaki kuli eve ana muza, "Ona, Zoona nimukazi wako chifukwa nichani unakamba kuti nimu longo wako?" Isaki ana muza eve, "chifukwa nenze kuona monga wina angani paye kuti amu tenge." 10Abimeleki anakamba, " Nichani ichi chamena wachita kuli ise? Cinali nichapafupi kuti umozo wabantu agone namukazi wako, ndipo sembe watiletela kuchimwa pali ise." 11Ndipo Abimeleki anaba Chenjeza bonse bantu naku bauza, "Aliyense wamene azangwila uyu mwamuna olo mukazi wake zoona azapaiwa."12Isaki anashanga mbeu mu ziko muja naku kolola muchaka chamene kali handredi cifukwa Yehova anamudalisa. 13Anankala mwamuna wolemela, ndipo anankala wolemela ndi kulemela paka anankala wolemela maningi. 14Anali na mbelele na ng'ombe zambili nabanja ukulu. Ba Philistini bana mukumbwila.15Manji visime vonse namene banchito batate bake banakumba mumasiku ya Abrahamu tate wake, Ma Philistini bana vilekesa mwaku vifwikala na doti. 16Abimelelki anamuza Isaki, "Yenda coka kuli ise, pakuti ndiwe wampavu maningi kuchila ise." 17Ndipo Isaki anachokako kuja nakunkala muchifwa ua Gerari, nakunkala mwamene kuja.18Koma futi Isaki anafukulula visime vamanzi, vamene vinakumbiwa mu masiku ya Abrahamu tate wake. Ba Philistini benze bana vifwikila kuchokela pa infa ya Abrahamu. Isaki anavipasa visime ma zina yamene batate bake banali kuvitana. 19Pamene banchito ba Isaki banakumba chigwa bana peza kuja cisime chamanzi yoyenda. 20Bamuna bobeta baku Gerari bana yambana na muna bobeta ba Isaki, ndipo banakamba, "aya nimanzi yatu." ndipo Isaki anaitana cisime "Eseki," cifukwa abayambana nayeve.21Ndipo bana kumba cisime cinangu, ndipo bana yambana pali icho, futi, ndipo anachitana anachipasa zina "Sitina." 22Anachoka kuja ndipo anakumba futi cinangu cisime, koma sibana yambana pali ici. ndipo anachitana Tehoboti, nakukamba kuti. "Manje Yehova ati pangila malo ise, ndipo tiza tukuka mu ziko.23Kuchoka apo Isaki anachokako naku yenda ku Beereseba. 24Yehova anamuokela usiku wamene uja nakukamba, "ndine Mulungu wa Abrahamu tate wako usayope, pakuti nili naiwe ndipo niza kudalisa iwe naku chulukisa bobadwa muli iwe chifukwa cha Abrahamu wa nchito wanga. 25Isaki anamanga guwa kuja na kuitana pa ziko ya Yehova. Kuja ana kokomela hema, ndipo banchito bake bana kumba cisime.26Ndipo Abimeleki anayenda kuli eve kuchokela ku Gerari, na Ahuzzati, na mu zake, na Phico, mukulu wa ba silikali. 27Isaki anabauza, nichani mwabwelela kuli ine pakuti muni zonda ndipo muna nipisha kuchoka kuli imwe?"28Banamuyanka kuti zoona taona kuti Yehova alina iwe. Ndipo taganiza kuti pankale kulapila pakati patu pakati patu na iwe. Manje tiyeni tipange chipangano naiwe, 29kuti silizatichita ise choipa, monga mwamene ise sitinaku chite voipa, monga mwamene tinakusungila bwino nakulaila mwa mutendele. Zoona, ndipo odalisika na Yehova."30Ndipo Isaki anabapangila pwando, ndipo bana dya naku mwa. 31Bana uka kuseni maningi naku lumbila kuli wina namu zake. Ndipo Isaki anaba laila, bana musiya mu mtendele. Siku yamene chisime shiba, ndipo zina ya muzinda uja ni Beershiba paka siku yalelo.32Siku yamene ija wanchito wa Isaki anabwela naku muuza pali chisime chaene bana kumba. Bana kamba "Tapeza manzi." 33Anachitana chisime shiba, ndipo zina ya muzinda uja ni Beershiba paka siku yallelo.34Pamene Esau enze na zaka fote, anatenga mukazi, Judi mwana wa Beeri waku Hittiti, naye basimati mukazi wa Eloni waku Hitti. 35Banaleta misozi kuli Isaki na Rabeka.

27

1Pamene Isaki anakula na menso yake yanaleka kuonesesa kuti analeka nakuona, anaitana Esau, mwana wake mwamuna mukulu naku mu uza, "Mwana wanga." Esau anati kuli eve "Nili Pano," 2ndipo Isaki anakamba, "Ona kuna nakota siniziba siku yamene nizafa.3Chifukwa chaicho tenga zida zako, chola chako cha mivwi, na uta wako, na kuyenda mu sanga nakunigwilila nyama. 4Nipangile chakudya cha bwino, chamene nikonda, ndipo ulete kuli ine kuti nichidye na kuku dalisa iwe nikalibe kufa."5Ndipo Rabeka anamvela pamene Iski anali ku kamba na Esau mwana wake. Esu anayenda mu sanga kuti agwile nyama nakuleta. 6Rabeka ana uza Yakobo mwana wake mwamuna kuti, "Yangana kuno, namvela atate bako bakamba na mubale waiko Esau. Bakamba kuti, 7'Niletele nyama yamusanga ndipo unipangile chakudya chabwino, kuti nichidye naku kudatisa iwe pamenso ya Yehova nikalibe kufa.'8Ndipo chifukwa chaicho, mwana wanga, mvela mau yanga yamene niku lamula iwe. 9Yenda kuvibeto nakuniletela tubana tw mbuzi tubili twa bwino; ndipo nizatupanga chakudya chabwino cha atate bako, monga mwamene bachikondela. 10Uzapeleka kuli atate bako, kuti bachidye nakukudalisa bakalibe kufa."11Yakobo anauza Rabeka amai bake, " Onani, Esau mubale wanga ali na upipi, koma ine ndine mwamuna osalala, 12kapena batate banga baza ni gwila ine, ndipo nizaoneka kuli beve ngati onama. Nizaziletela tembelelo neka osati daliso."13Amai bake bana mu uza eve, "Mwana wanga, leka tembelelo ibwele pali ine. Mvelela mau yanga, ndipo yenda, ulete kuli ine." 14Ndipo Yakobo anaenda nakutenga tu bana twa mbuzi tubili naku tuleta kuli bamai bake, ndipo bamai bake bana panga chakudya chabwino, monga atate bake banali ku kondela.15Rabeka anatenga vovala va bwino va Esau, mwana wake mukulu mwamuna, wamene anali navo munyumba, naku valika Yakobo, mwana wake mungono mwamuna. 16Ana muvalika chikumba cha ka mbuzi kangono ku manja yake na ku mbali yaku mukosi wake osalala. 17Anaika chakudya cha bwino na mukate wamene anapanga mu manja mwa mwana wake mwamuna Yakobo.18Yakobo anaenda kuli ba tate bake naku kamba, "Batate banga." Batate bake bana kamba "Nili pano; ndiwe ndani mwana wanga?" 19Yakobo ana bauza batate bake, "ndine Esau mwana wanu oyamba. Nachita monga mwenze mwani uzila. Manje ukani nakudyako nyama yanga yamusanga, kutimunidalisa ine."20Isaki ana mu uza mwana wake mwamuna, "Nanga wanga?" anati, "Chifukwa Yehova Mulungu wanu aileta kuli ine." 21Isaki anati kuli Yakobo, "Bwela pafupi, pali ine kuti nikugwile iwe, mwana waga mwamuna, kuti nizibe gati zo ona ndiwe mwana wanga Esau olo kapena sindiwe."22Yakobo anayenda kuli Isaki tate wake, ndipo Isaki anamugwila naku kamba, "Mau ni mau ya Yakobo koma manja ni manja ya Esau. 23Isaki sana muzibe, chifukwa manja yake yenze na upipi, monga ya mubale wake Esau, ndipo Isaki ana mudalisa.24Anakamba "Nanga ndiwe zo ona mwana wanga mwamuna Esau?" Anayanka, "Ndiwe" 25Isaki anti "Leta chakudya kuli ine ndipo nizadya nyama yako yamu sanga, kuti nikudalisa." Yakobo ana muletela chakudya: Isaki anadya, Yakoba anamuletela vinyu, ndipo anamwa.26Ndipo atate bake ba isaki bana mu uza. "Manje bwela pafupi nakuni pyopyona mwan wanga mwamuna." 27yakobo anabwela pafupi naku mupyopyona, ndipo ananusha kafungo ka vovala vake na kumudalisa anakamba "Ona, kafungo kam mwana wanga kali monga kamusanga mwamene Yehova ana dalisa.28Mulungu akapase mbali ya mame yako mwamba, mbali yakuina kwa ziko yapansi, na mbeu zambili na vinyu vanyowani.29Lekabantu baku sebenzele na maziko yakugwadile unkale bwana kuli ba bale bako, ndipo leka bana bamai bako bamuna baka gwadile iwe uyo wamene azaku tembelela atembelelewe: Wamene azakudalisa adalisiwe."30Pamene panja Isaki anasiliza kudalisa yakobo, na yakobo anachoka namata pamenso pa Isaki tate wake Esau mubale wake anabwela kuchokela mukugwila nyama. 31Na eve anapanga chakudya chabwino nakuleta kuli batate bakee. Ana bauza batate bake, " Atate, ukani ndipo mudyeko nyama yamasanga ya mwana wanu,kuti mini dalise."32Isaki tate wake anakamba kuli eve, "ndiwe ndani?" anati, "Ndine mwana wanu mwamuna oyamba , Esau." 33Isaki ananjenjema maningi nakukamba ati, "Nanga ni ndani wamene enze apaya nyama yamusanga nakuniletela? Ninali nadya yonse ukalibe kubwela, ndipo namudalisa uyo. Zo ona, uyu azankala odalisika."34Pamene Esau anamvela mau ya atate bake, analila maningi, mokalipa naku kamba kuti kuli batate bake, " Nidaliseni ine, naine batate banga." 35Isaki anakamba, "Mubale wako enze abwela kuno monamiza, nakutenga madaliso yako."36Esau anakamba, "Uyu zoona zina yake si yakobo chifukwa aninama ine kabili anaipoka choyenela chaku badwa kwanga, ndipo, onani, manje atenga madaliso yanga. Ndipo anakamba, "Simunanisugileko daliso?" 37Isaki anayaka naku kamba kuli Esau, "Ona, namupanga bwana wako, nakumupasa babale bake bonse monga ba nchito, ndipo na mupasa mbeu na vinyu ya sopano. Nanga nichani chamene ningakuchitila, mwana wanga mwamuna?"38Esau anakamba kuli batate bake, "Mulibe olo daliso imozi yanga, atate banga? Ni daliseni, naine, atate banga." Esau analila mo punda.39Isaki atate bake banayanka nakukamba kuli eve, "Ona, malo kwamene uzayenda kunkala yaza nkala ku tali na chuma cha ziko yapansi kutali na mame yakumwamba. 40Kupitila mulupanga yako uzankala, naku sebenzela mubale wako. Koma ngati wamu ukila, uzachosa goli yake mu mukosi wako."41Esau anamuzonda yakobo chifukwa cha madaliso yamene bana mupasa batate bake. Esau anakamba mumutima wake, "Masiku yolila batate banga yali pafupi; yakapita nizamupaya mubale wanga Yakobo." 42Mau ya Esu mwana mwamuna yana uziwa kuli Labeka. Ndipo anaitana Yakobo mwana wake mwamuna mungono naku kamba kuli eve, "Ona Esau azitontoza eka pali iwe pakuganiza ku kupaya iwe.43Manje, mwana wanga mwamuna, nimvelele ine nakutabila kuli Labani, mubale wanga, mu Halani, 44Kankaleko na eve pangono, mpaka ukali wa mubale wako uchepeko, 45mpaka ukali wamubale wako uchokeko kuli iwe, nakuibala vamene una chita kuli eve. Ndipo nizatuma nakuku bweza kuno. Nichifukwa cha chani niza kutayani bonse babili pa siku imozi?46Rabeka anakamba kuli Isaki, "Nalema nao umoyo chifukwa cha bana bakazi baku Heti ngati yakobo akwatila bana bakazi bena bana bakazi bakuno kumalo, umoyo wanga uzankala bwino bwnji?"

28

1Isaki anaitana Yakobo, anamu dalisa, nakumulamulila, "usaka tenge mukazi ochokela kuli bazikazi baku Kenani. 2Nyamuka, yenda ku Padani Aramu, ku nyumba ya Bethueli ba mai ba batate bako naku tenga mukazi kuchoka kuja, umozi mwana mukazi wa Labani, mubale wa bamai bako.3Leka Mulungu wampamvu zonse aku dalise, aku pange obala ndipo akuchuluse kuti munkale bantu bambili. 4Leka akupase daliso ya Abrahamu, kuli iwe, naku bana bobadwa pambuyo pako kuti ungene muziko yamene unali kunkalamo, yamene Mulungu anapasa Abrahamu."5Pamene apo Isaki anatuma Yakobo. Yakobo anayenda ku Padani Aramu, kuli Laban mwana mwamuna wa Betulo waku Aramea mubale wa Rebekah, ba mai ba Yakobo na Esau.6Manje Esau anaona kuti Isaki anadalisa Yakobo na kumutuma kuyenda ku Padani Aramu, kuti akatenge mukazi wa kuja. Anaona futi, kuti Isaaki anamudalisa na kumulamulila kuti, "usaka tenge mukazi pa bakazi baku Kenani." 7Esau anaona futi Yakobo anamvelela batate bake naba mai bake, nakuyenda ku Padani Aramu.8Esau anaona kuti bakazi baku Kenani sibana kondwelese batate bake. 9Pamene apo anayenda ku Ishmaeli, nakutenga, kumbali kwa bakazi bake, Mahalati mwana mukazi wa Ishmaeli, mwana mwamuna wa Abrahamu mulongosi wa Nebaioti, ankale mukazi wake.10Yakobo anachoka ku Beersheba naku yenda caku Harani. 11Anabwela pa malo yena naku nkala kuja usiku onse, chifukwa zuba yenze inangena. Anatenga mwala umozi mu malo muja, naku ika pansi pa mutu wake, naku gona pa malo paja.12Analota naku ona makwelelo yana ima kuchoa pa ziko yapansi. Pamwamba pake panafika kumwamba ndipo bangelo ba Mulungu benzeli ku kwelapo naku selukapo. 13Onani, Yehova anaimilila pamwamba pake naku kamba, "Ndine Yehova, MUlungu wa Isaki. Pa malo yamene ya gona nizapasa iwe na bana bobadwa muli iwe.14Bana bobadwa muli iwe bazankala monga doit yapansi, ndip muza zulana mutali wa kumazulo, kumawa, kumpoto, ndipo na kumwela,kupitlila muli iwe namuli bobadwila muli, mabanja yonse yapa ziko yaza dalisika. 15Onani, Nili na iwe ndipo nizaku sunga kuli konse kwamene uzaka yenda. Nizakuleta iwe mu malo aya nafuti: chifukwa sisnizaka kusiya niza chita vonse vamene nina lonjeza kuli iwe."16Yakobo ana uka mutulo mwake, ndpo anakmba, "zo'ona Yehova ali pano pamalo, koma sininazibe. 17Anali na manta naku kamba, "Niyo yoyofya bwanji aya malo! aya siyena koma nyummba ya Mulungu. Apa nipolobeka kumwamba."18Yakobo anauka kuseni maningi naku tenga mwala wamene anabwela afaka pasni pa mutu wake. Anachipanga nga chipilala naku tilapo mafuta pamwamba pake. 19Anaitana zina malo yaja Betheli, koma zina ya muzinda uja inali Luzi.20Yakobo analapa chilapilo, kuti, "Ngati Mulungu azankala naine na kuni chigiliza pa njila iyi pamene niyenda, na kunipasa mukate okudya, na vovala vovala, 21chakuti ine nibwelele mwamu tendele ku nyumba ya batate banga, pamene Yehova azankala Mulungu wanga. 22Pamene mwala yuy wamene na imilika ngati pilala uzankala opatulika kuchokela pali vonse vamene wani pasa nizabwelesa chakumi kuli iwe."

29

1Pamene apo Yakobo anayenda paulendo wake na kufika ku malo ya bantu ba ku maba. 2Pamene anayangana, anaona chisime mumunda, na, onani, magulu yatatu ya mbelele yanali gone mumbali. chifukwa cikuchoka mu chicime ichi banali kumwesalamo mbelele, na mwala unali pakamwa pachisime unali ukulu. 3Pamene yonse magulu mbelele yanakumana paja, na bachibeta banali kuchosa mwala pakamwa pachisime na kupasa mbelele manzi, naku bwezapo chimwala futi pakamw pachisime, nakuchibweza mumalo yake.4Yakobo anakamba kuli benve kuti, "ba bale banga, mwachokela kuti?' bana yanka, "Tachokela ku Haran." Anakamba kuli benve, 5"Mumuziba Labani mwana mwamuna wa Naha? "Nabenve banakamba kuti, "Timuziba. " 6anakamba kuli benve kuti, "mwati alibwino?" Benve banakamba kuti, " alichabe bwino, na, yangananei kuja, Recho mwana wake mukazi abwela na mbelele."7Yakobo anakamba, "Onani, ni pakati pa siku. sintawi yama guli ya mbelele kukumana pamozi. mufunika kupasa mbelele manzi na kuyenda na kuzileka zidye." 8Banakamba kuti, "sitinga zipase manzi mpaka zonse mbelele zikumane pamozi. Na bamuna baza chosa chimwala pachisime kuchoka apo tizazipasa manzi mbelele."9Pamene Yakobo anali kukamba na benve, Recho ana bwela na mbelele zaba tate bake, chifukwa niwamene anali kuzibetela. 10Pamene Yakobo anaona recho, mwana mukazi wa Labani, mubale wa bamai bake, na mbelele za Labani, mubale wa bamai bake, Yakobo ana bwela pamene paja, naku vendesa mwala kuchoka pakamwa pachisimenakupasa manzi gulu ya mbelele za Labani, mubale wa bamai bake.11Yakobo ana pyopyonta Recho nakulila mo kuwa. Yakobo anauza Recho, kuti enve anali bululu wa batate bake, anali mwana wa Rabeka. 12Pamene apo enve anatmnaga na kuyenda ku'uza batate bake.13Pamene Labani ananvela iyi nkani ya Yakobo mwana mwamuna wamulonosi wake, anatamanga kuti bakumane na enve, na kumukumbatila, na kumu pyopyonta, na kumu bwelesa ku nyumba yake. Yakobo anauza Labani vonse ivi vintu. 14Labani ana kamba kuli enve, "iwe zo'ona ndiwe fupa yanga na munofu wanga." ndiye pamene Yakobo ana nkala na paka ntawi ya mwezi umozi.15Ndiye pamene Labani anakamba kuli Yakobo kuti unga ni sebenzele mahala chifukwa ndiwe bululu wanga? Niuze, malipilo yako yazankala bwanji?" 16Manje Labani enzeli na bana bakazi bali. Na zina ya mukulu yenze Leya, na zina ya mungono yenze Recho. 17Menso ya Leya yanali yofewa, koma Recho anali okongola, mukapangidwa nama onekedwe. 18Yakobo anakonda Recho, ndiye chamene anakambila, "nizaku sebenzelani zaka seveni ya Recho, mwana wanu mun'gono mukazi.19Labani anakamba kuti, "nicha bwino kuti ine nipupase enve kuli iwe, osati ine nipase enve kuli mwamuna wina. nkala na ine." 20Na Yacobo anasebenza zaka seveni ya Recho; koma yanamuonekela kwati nimasiku yangono, chifukwa cha mwanen ana mukondela.21Pamene apo Yakobo anakamba kuli Labani, "nipase ine mukazi wanga, chifukwa masiku yanga yakwanila kuti nimukwatile!" 22Manje Labani anaitana pamozi bantu bonse ba pamalo nokupanga pwando.232425Mumazulo, Labani anatenga Leya mwana wake mukazi nakumubwelesa enve kuli Yakobo, wamene anangena muli enve. Labani anapasa wanchinto mukzai Zilpankuli mwana wake mukazi Leya, kunkala wanchonto ake. Kuseni, onani, enze Leya! Yakobo anakamba kuli Labani, "nanga ndiye vichani vamene wa chita kuli ine? nanga ine sinina sebenzele Recho? Nichifukwa cha chani mwani nama ine?"26Labani anakamba, simwambo watu kupasa mwana mukazi mungono tikalibe kupasa mwana mukulu. 27Silizisa mulingu wa uy mwana mukazi, koma tizakupsa na winangu monga malipilo pakuni sebenzela zaka seveni zinangu."28Yakobo anachita sochabe, naku siliza mulingu wa Leya. Ndiye pamene Labani anamupasa Recho mwana wake mukazi kunkala mukazi wake an enve. 29Labani ana pasa Bilhah kuli mwana wake mukazi Recho, kunkala wanchito wake. 30Na Yakobo anangena muli Recho, na enve, koma ana konda Recho kupambana na Leya. Na Yakobo anamusebenzela Labani zaka zinangu zili seveni.3132Yehova anaona kuti Leya sanali okondewa, anasegula mala yake, koma Rcho analibe mwana. Leya anankala namimba nakubala mwana mwamuna, nakumu itana ina Rubeni. chifukwa anakamba kuti, "Chifukwa Yehova ayangana paku vutika kwanga; zo'ona apa maje bamuna banga bazani konda ine.33Ndiipo anakahala namimba futi na kubala mwana mwamuna. Ana kamba, "Chifukwa Yehova anvela kuti sindine okndewa, anipasa futi mwana mwamuna."Ana mupasa zina Simioni. 34Anankhala futi namimba nakubala mwana mwamusa. Anakamba, "apa manje bamuna banga bazangwilikana kuli naine, chifukwa naba balila bana bamuna batatu."Chaicho anaitaniwa zina ya Levi.35Ankhala na mimba futi nakubala mwana mwamuna anakamba, "ino ntawi nizamutamanda Yehova. Ndiye pamene apo ana mu itana zina yake Yuda; ndipo analaka kunkala na bana.

30

1Pamene Recho anaona kuti sana mubalile bana Yakobo, Recho anakumbwila mulongosi wake. Anakamba kuli Yakobo kuti, "Nipase bana, olo inzafa." 2Yakobo anakalipa chifukwa cha Recho. Anakmba kuti, "Ushe Ndine mulungu, anakulesa kuti unkale nabana?"3Anakamba kuti, "Ona, Pali wanchito wanga Bila. Gona naye, chakuti ati balile bana bolela pa mendo panga, ndipo ine nizankala na bana kupitila muli enve." 4Chakuti anamupasa Bila wanchito wake kuti ankale mukazi wake, ndipo Yakobo aanagona naye.5Bila anankala na mimba nakubala mwana mwamuna wa Yakobo. 6Pamene apo Recho anakamba kuti, "Mulungu anikambilako, ndipo anvela na mau yanga nakunipasa mwana mwamuna." Chifukwa chaichi anamuitana zina yake yake Dani.7Bila, wanchito wa Recho, anankala namimba futi naku balalila Yakobo mwana mwamuna wachibili. 8Recho anakamba kuti, "Namenyana na mulongosi wanga mwampavu ndipo napambana." Anamuitana zina yake Nafutali.9Pamene Leya anaona kuti aleka kubala bana, anatenga Zelipa wanchito wake nakumupasa kuli Yakobo kuti ankale mukazi wake. 10Zelipa, wanchito wa Leya, anabalila Yakobo mwana mwamuna. 11Leya anakamba kuti, "Uyu ndiye mwayi!" chakuti anamuitana zina yake Gadi.12Pamene Zelipa, wanchito wa Leya, anabalila Yakobo mwana mwamuna wachibili. 13Leya anakamba kuti, "Nakondwela! Chifukwa bana bakazi bazani itana ine kuti okondwela." Chakuti anamu itana zina yake Asha.14Rubeni anayenda mu munda pa masiku yochosa witi nakupeza maudeleki mu munda. Anayabwelesa kuli mayi wake Leya. Pamene Recho anakamba kuli Leya, "Unipaseko maudeleki yenangu ya mwana wako mwamuna." 15Leya anakamba kuli enve, "Iyi ninkani ing'ono kuli iwe? kuti unanipoka mwamuna wanga? Manje ufuna kunitengela na mandeleki ya mwana mwanga mwamuna?" Recho anakamba kuti ndiye pamene azagona naiwe usiku walelo, chifukwa cha mandeleki yamwana wako yamene uzani pasako mochinjanisha."16Yakobo anabwela kuchokela kumunda mumazulo. Leya anayenda kukumana naye nakukamba kuti, "Ufunika kugona na ine, chifukwa nakugula na mandeleki." Chakuti Yakobo anagona na Leya usiku. 17Mulungu anamunvelela Leya, anankala na mimba nakubalila Yakobo mwana mwamuna wa nambala faivi. 18Leya anakamba kuti, "Mulungu anipasa ine malipilo yanga, chifukwa namupasa muzimai wanchito wanga kuli bamuna banga." Anamupasa zina yake Isaka.19Leya anankala namimba nakubala mwana mwamuna wa nambala sikisi wa Yakobo. 20Leya anakamba kuti, "Mulungu anipasa ine mpaso yabwino. Apa manje mwamuna wanga azani lemekeza ine, ndaba namubalila bana bamuna bali sikisi." 21Pasogolo pake anabala mwana mukazi nakumupasa zina yake Dinna.22Mulungu anakamba na Recho mumaganizo naku munvelela. 23Anamulengesa kuti ankale na mimba. Anankala na mimba nakunkala na mwana mwamuna. Anakamba kuti "Mulungu anichosa nsoni zanga." 24Anamuitana zina yake Yosefe, kukamba, kuti, "Yawe alundilapo kuli ine mwana mwamuna winangu."25Pasogolo pake Recho anabala Yosefe, "Yakobo anakamba kulli Labani "Munimasule, pakuti niyenfe kumunzi kwatu nako ziko yanga. 26Munipase bakazi banga na bana banga bamene ninalipilila malipilo yokugwililani nchito, futi munileke niyende, kainge muziwa bwino nchito yamene nakugwili lani."27Labani anamu uza kuti, "Ngati apa uzani chitila chifundo mwamene uvionela vintu, uyembekeze, chifukwa nina ziba mumatesnga kuti Yawe anidalisa ine chifukwa cha iwe." 28Pamene apo anakamba kuti, "kamba mutengo wako weka, ndipo ine nizabalipila."29Yakobo anakamba kuli enve, "Uziba mwamene ninatumikila kuli iwe, na mwamene vinyama vako vachitila twino kuli ine. 30Pakuti mwenze natungo'no pamene ine nikalibe kubwela manje vapakilapo maningi. Yawe anakudalisani imwe paliponse peninali kusebenzela. Nanga niliti pamene nizapasako wamunyumba mwanga naine?"31Labani anafunsa kuti, "Nizakulipila chani?" Yakobo anakamba kuti "Simuzanilipila chilichonse. Ngati munga nichitele ichi chintu kuli ine, nizakavidyesa futi vinyama vanu nakusamala. 32Lekani ine nipitemo pakati pa vinyama vanu lelo nakuchosapo ka shipi kalikonse kamene kali nama iwanga natuma dontho, ndipo kabulaki pa mbelele, ndipo katuma dontho namizele pagulu ya mbuzi. Aaya ndiye yazankala malipilo yanga.33Kukulupilika kwanga kuzakanikambilako pasogolo panga, mukayende kuona malipilo yanga. iliyonse yamene siyizankala na mizele na madoti pakati pa mbuzi, nayo kuda pakati pa mbelele, ngati iliyonse izakapezeka naine, izakaganizilidwa kuti niyakuba," 34Laban anakamba kuti, "Anavomela. Leka mwamene wakambila mau yako."35Yamene ija siku Labani anachosapo mbuzi zimuna zamene zenzeli na mizele na madoti, na mbuzi zikazi zonse zamene zenze naka wayiti pa tupi, na zonse zokuda pakati pa mbelele, nakuzipasa mumanja mwa bana bake bamuna. 36Labani anayikapo ulendo wamasiku yatatu pakati payenve mwine na Yakobo. Chakuti Yakobo anapititliza kusebenza kusunga vinyama va Labani vamene vina salapo.37Yakobo anatenga misambo yafuleshi yojubiwa yawisi ya mtengo wapopula, na mutengo wa alamondi, na mutengo wapuleni, naku fundulamo tumilayeni twa waiti mpaka va wayiti vamukati mwa chimutengo vinaonekela ku tumi tengo. 38Pamene apo anayika tumitengo twamene anafundula pasogolo pa vinyama, pasogolo pama kontena yomweselamo manzi vinyama, pamene vinali kubwela kumwa manzi vinyama vinankala nama mimba pamene vinabwela kumwa manzi.39Vinyama vinali kugonana pafupi na tumitengo; ndipo vinyama vinabala bana bamizele, bamawanga na madoti. 40Yakobo anapatulapo mutundu yuy wa tubana twa mbelele, koma analeka kuti zonse zinangu ziyangane ksayidi kwe kunali vinayama vamizela vo kuda pavinyama va Labani. Pasogolo pake anazichoselapo vinyama vake mwine yeka ndipo sanali kusankaniza pamozi na vinyama va Labani.41Paliponse nkosa zolimba muvinyana zikayamba kugonana. ninshi Yakobo analikugoneka tumitengo mumakontena yomwelesamo manzi vinyama, apo vinyama vilangana patumitengo. 42Koma pamene vinyama vo foka maningi vinabwela, sanayike tumitengo pafupi navo. Chakuti vinyama vofoka vinankala va Labani, ndipo volimba vinankala va Yakobo.43Mwamuna yuy anankala olemela maningi. Anali na vinyama vambili, wanchito bakazi na bamuna, makameleo nama donke.

31

1Ndipo Yakobo anamva mau ya bana ba Labani, yamene banakamba, "Yakobo atenga vonse va batate bathu, apeza chuma conse ici kuckela mu vinthu va batate. 2Yacobo anaona kayang'anidwe pa menso pa Laban. Anaona kayang'anidwe kake kanacinja. 3Ndipo anatuma ndi kuitana Rakele ndi bwelala kuziko ya batate bako na ba bale bako ndipo nizankhala naiwe.4Yacobo anatuma ndi kuitana Rakele ndi Leya kui abwele kumunda kuli zobeta zake. 5Ndipo anakamba na beve, "Naona kayanganidwe kaba tate banu pali ine kacinja, koma Mulungu wa tate ali naine. 6Muziba kuti na mpavu zanga zonse nankhala nisebenzela batate banu.7Batate banu baninama na kucinja malipilo yanga kali 10, koma Mulungu sana muvomeka kucita coipa. 8Ngati anakamba kuti, nyama za manthongo ndiye malipiro yako, 'ndipo zonse nyama zinabala zamanthongo, ngati akamba kuti, zamizela zizakhala malipiro yako, ' ndipo nyama zonse zinabala zamizera. 9Cifukwa cake Mulungu anatenga nyama za batate banu na ni pasa.10ndipo pa nthawi yobala, ninaona muciloto mbuzi zimuna zinali kukwela nyama. Mbuzi zimuna zinali namizela, na mamphongo na mitundu yosiyana-siyana. 11Mungelo wa Mulungu anakamba na ine mu ciloto, 'Yakobo' ninakamba, 'nili pano.'12Anakamba kuti, nyamula menso yako ndipo uone mbuzi zonse zimuna zikwelana na nyama. Zinamizela mamphongo, na mitundu yosina-siyana, cifukwa naona vonse vamene Labani acita kuli iwe. Ndine 13Mulungu wa Betele, kwamene unathila mafuta pamwala, kwamene unalumbila kuli ine. Manje nyamuka ucoke m'malo yano na kubwelela kumalo kwamene unabdwila."14Rakele na Leya anayankha na kukamba na eve, nanga kulibe mbali na vosalila vathu munyumba ya batate? 15Sitisungiwa na eve monga ni balendo?cifukwa atigulisa nakuonongeltu nadalama zathu. 16Pa cuma ciliconse camene bacosako kuli batate bathu cankhala cathu na bana bathu. Manje, vilivonse vamene Mulungu akamba, cita."17Ndipo Yakobo ananyamuka noika bana bake bamuna na bazikazi bake pa ma bulu. 18Anaika zobeta zake pa songolo pake, pamozi nakatundu wake bonse, kuikilapo nanyama za mene anakhala nazo mu paddani Aramu. Ndipo anakonzekera kuyenda kuli Isaki tate wake mumalo yao ya Kanaani.19Pamene Labani anayenda kukasenga nkhosa zake, Rakele anaba tumilungu twa munyuma ya batate bake. 20Yakobo ana namanso Labani wa ku Aramean, po samu uza ati ayenda. 21Ndipo anathaba na vonse enze navo na kudusa pa mumana, ndipo anayendela ku phili yaziko ku Giliyadi.22Pasiku ya citatu Labani ana uziwa kuti Yakobo anathaba. 23Ndipo anatenga abale ake ndi kumupisha kwa ulendo wamasiku seveni. Anamupeza pa phiri ya ziko ya ku Giliyadi.24Ndipo Mulungu anabwera kwa Labala mu Aramean muciloto naku mu uza kuti, "Nkhala ocenjera kuti osakambe voipa olo vabwino kuli Yakobo. 25"Labani anapitilila Yakobo. Ndipo Yakobo anamanga hema yake mupili yaziko. Labani naye anakhala paja mba bale bake mupili ya Giliyadi.26Ndipo Labani anakamba kuli Yakobo, wacita cani, kuti unani nama nakunyamula bana banga bakazi monga ba kaida ba nkhondo? 27Cifukwa nicani unathaba mwacisinsi na kuninama ndiponso sunani uze ine? Asembe nina kupelekeza nakusangalala na nyimbo, ndi lingaka ndi coliza. 28Sunandi vomekeze ine ku mpsompsona bana banga bakazi na bamuna, manje wacita vopusa.29Vili mu mphavu zanga kukucita voipa, koma Mulungu waba tate bako anakamba usiku wasila ndipo anati, 'Khala wocenjela, kuti osakambe kuli Yakobo voipa na vabwino.' 30Manje wayenda cifukwa wenze kufuna maningi kubwelela kunyumba ya batate bako. Nanga nichani camene unabela milungu yanga?"31Yakobo anayankha nanena kwa Labani, "Chifukwa ninayopa nakuganiza kuti muzapoka bana banu bakazi mwampavu ndaba sinilaile. 32Alionse wamene aba milungu yanu saza pitiliza kukhala na moyo. Pamenso ya ba bale bathu, ona cili conse cili naise ngati nichanu mucitenge. "Cifukwa Yakobo sanazibe kuti Rakele ndiye anaba.33Labani anangena muhema ya Yakobo, na muhema ya Leya, ndiponso muhema ya banchito babili, koma sanaba peza. Anocoka muhema ya Leya na ku ngena muhema ya Rakele.34Ndipo Rakele anali anatenga milungu zamunyumba, anaviika pa conkhalila caca ngamila, ndi kunkhalapo. Labani anasakila muhema yonse, koma sana vipeza. 35Anakamba kuli atate bake, "Osakalipa, mbuye wanga, kuti siningamilile pamenso pano, cifukwwwa nili panthawi ya kumwezi. "Ndipo anasakila koma sana peza milungu za munyumaba mwake.36Yakobo anakalipa naku kangana na Labani. Anakamba kwa iye, "Kodi mulandu wanga ndiwa bwanji?Cimo yanga niya bwanji, kuti muzingo kuni konka konka? 37Popeza mwa sukila ponge pali katundu yanga. Nichani came mwapeza pavinthu vonse va munyumba yanu? Vileteni apa pali abale athu, kuti ba weruzu pakati ka ife.38Kwazakatwenti na nkhala naimwe. Nkhosa zanu nambuzi zikazi sizina kangangepo kubala, olo kapena kudyapo pa vo beta vako. 39Vina vina ng,ambiwa na vilombo sinina vilete kuli iwe, koma, ndine ninalipila pava mene vinasowa. Nthawi zonse mumanindi pilisa pali nyama yadoba, loko yabewa usiku olo muzuba. 40Ndipo nenzeko, musiku zuba inani shoka, mame ya usiku ndipo sinina gone usiku.41Izi zake twenti nankhala munyumba yako, nina kusebenzela iwe zaka fotini cifukwa ca bana bako babili bakazi, nazaka sikisi vobeta vako. Mwacinja malipilo kali teni. 42Pokhapo Mulungu wa batate banga, Mulungu wa Abrahamu ndi iye wamene kaki ayopa, anali na ine, zo ona mwenze kuti niyende popanda vilivonse mu manja mwanga. Mulungu ayangana kuvutika kwanga na mwamene nenze kusebenzera maningi, ndipo anaku kalipila busiku wayenda."43Labani anayankha na ku kamba kuli Yakobo, "Akazi aba ndiye bana banga bakazi, bazukulu niba zukulu bangaa, navobeta ni vobeta vanga. vonse vamene uona nivanga. Koma nichani lelo ninga cite kuli aba banga bakazi kapene bana bao bamene bana bala? 44Manje apa, tiye tipange cipangano, iwe naine,ndipo ndiye ciza nkhala kamboni pakati ka iwe na ine."45Ndipo Yakobo anatenga mwala nakuika pamwamba pa pila. 46Yakobo anakamba kuli babale bake, "Ikani miyala pamozi," ndipo banatenga miyala nakuzi bunjika. Ndipo banadyela pamwamba. 47Labani ana itanapo Jegara saha Duthu, koma Yakobo anaitanapo Gilayadi.48Labani anakamba, izi miyala ni kamboni pakati kaiwe naine, lelo "Cifukwa cake zina yake baitanapo Giliyadi. 49Paitaniwanso mizipa cifukwa Labani anakamba, Leka Yehova ayangane pakati kaiwe na ine, pamene tisiyana wina na muzake. 50Ngati suzasunga bana banga bakazi bwino, olo uzatenga bakazi bena pambali ya bana banga bakazi, loko palibe wina ali naise, ona, Mulungu ni kamboni pakati kaiwe na ine."51Labani anakamba kuli Yakobo, " Yangana pamwamba, ndipo ona pa pila, yamene naika pakati kaiwe naine. 52Iyi nthutu ndiye kamboni, na pila ni kamboni kuti sinaza jumpa iyi nthutu kubwera kuli iwe, ndipo na iwe suza jumpa iyi nthutu ku bwela kuli ine, kucita voipa. 53Leka Mulungu wa Abrahamu, na Mulungu wa Nahor, na milungu za ba tate bao, ziweruza pakati kathu." Ndipo Yakobo analapa pakuyopa batate bake Isaki.54Yakobo ana peleka nsembe pa phiri nakuitana abale bake kuti bazadye cakudya. Ba nadya na kunkhala busiku bonse pamwamba pa lupili. 55mumawa, Labani anauka, naku myompyona bazulu bake na bana bake bakazi na kubadalisa. Pamene Labani anacokapo nakubwelera kunyumba.

32

1Naye Yakobo anayenda njila yake naba ngelo ba Mulungu bana mukumanya iye. 2Pamene Yakobo ana one, "anakamba iyi i hema ya Mulungu." ana itana zina yayaja malo mahanayimu.3Yakobo ana tuma atumikila kusogolo kwake kuli mubale wake Esau mumalo yaseya, mu malo ya Edomu. 4Anabalamulila kukamba, Izi ndiye zamene uzakamba kuli mbuye wanga Esau. Ichi ndiye chamena akamba Yakobo kapolo kwanga kufika lelo. 5Nili ng' ombe na abuvu. na vaweta naba nchito bamuna na bakazi. Natuma aya mau kuli abwna banga kuti apeze mwai mu menso yako.6A mithenga banabwela kwa Yakobo ndipo anati, "Tina yenda kuona mubale wako Esau. Abwela kuzakumana naiwe, nabamuna bali fihandredi bali nayeve. 7Ndipo Yakobo anayopa na kukwiya. Ndipo anagaba banthu bamene enze mumagulu yabili, na vobetaa, ng' ombe, ndi mabulu. 8Anakamba kuti, "Ngati Esau abwela kugulu imozi ndi kuimenya, ndipo gulu yamene izasala izathaba.9yakobo anati, "Mulungu wa atate banga Abrahamu, ndi Mulungu wa batate banga Isaki, Yehova anakamba kwa ine, Bwelela ku ziko lako ndi kwa abale ako ndiponizakupeleka pasongolo. 10Sindine oyenela pali vonse vocita vacipangano co kholulupilila ndi zabwino11Napapata ni pulumuseni ku kwanja yu mu bale wanga, ku kwanja kwa Esau, chifukwa nili na mantha kuti azabwele ndi kundimenya ndi bazimai nabana. 12Koma wakamba kuti, "Nizakupanga kuti utukuke nizapanga bana bako monga dohti ya munyanja, yamene singabelengeke mu ma nambala.13Yakobo anakhamba uja usiku uja. Anatenga vina enze navo monga mphaso kuli Esau, mubale wake. 14Mbuzi zikazi zili thu handiledi ndi mbuzi zimuna zili twenti, nkhosa zikazi zili thuhandiledi, ndi nkhosa zimuna twenti. 15Ngamila zamkaka zili feti na tu bana twao. Ng'ombe zikazi zili fote, na ng'ombe zimuna zili teni, mabulu yakazi yali twenti ndi ma bulu yamuna yali tenni. 16Ivi anapasa mumanja nwa ba nchito bake, gulu payekha yeke, anakamba kuli ba nchito, "Pitani kusogolo kwanga ndipo muike mupata pakati panagulu.17Aba uza wa nchito woyamba kuti, pamene Esau mubale wanga akumana naiwe na kukufunsa, kukamba, ili kumbali yandani? Upita kuti? ni nyama zandani izi zili kusogolo kwako? 18Ndipo uza kamba kuti, 'ndiwa nchito wako Yokobo ndi mphaso yatumi ziwa kuli bwana wanga Esau. Ona, naye alikubwela mumbuyo mwathu.19Yakobo anapasanso malamulo gulu lacibili, lacitatu, ndi amuna onse ana konka, ng' ombe. Anakamba, muzakamba vinthu vimozi mu kakumana ndu Esau. 20Mufunika kukamba wa nchito wako Yakobo abwela pambuyo, "Cifukwa anaganiza," nizamu kondwelesa iye na mphaso zamene nituma kusogolo kwanga pambuyo pake, nikamu ona paena azandi landila ine. 21Mphaso zina yendelatu ku sogolo kwake.Iye usiku uja anakhala mu hema.22Yakobo anauka usiku ndipo anatenga bakazi bake babili, banchito bake babili bazimai, nabana bake bamuna levini, anabatuma kutauka pa abokola Yabboki. 23Munjila iye anabatuma kutauka mumana na cuma cao conse.24Taboko anasijiwa yeka, ndipo analimbana na munthu pakana kunaca. 25Pamene uja munthu anaona kuti sinizamkwanisa, anaonga nchafuyake, nchafu ya Yakobo inasinthani pamene banali kulimbana. 26Munthu uja anakamba, nisiye, apeza kwayamba kucha, "Yakobo anakamba, "Sinizakuleka pakana unidalise.27Munthu anakamba kuli yeve, "Zina yako ndiwe ndani? Yakobo anati, "Yakobo." 28Munthu anakamba, zina yako sizkhlnso Yakobo koma Israeli. Chifukwa walimbana ndi Mulungu ndi banthu koma wa pambana.29yakobo anafunsa, "Napapata niuze zina yako? Anati, "Ufunsila chani zina yanga? ndipo anamusalisa paja. 30Yakobo anaitana pamalo paja kuti peniwenlo popeza anti, naona Mulungu menso na menso ndipo moyo wanga wapulumuka.31Zuba inacoka pamena Yakobo anadusa peniwelo anali ku golontha chifukwa ca achafu yake. 32Ndiye chifukwa cake kufika nalelo banthu ba ku israeli si kudya nyama zamene zipezeka pafupi nanchafu cifukwa munthu ana onanga zibalo pa ku siyanisa nchafu Yakobo.

33

1Yakobo onayangana kumwamba, onani, Esau akubwela, pamodzi naive anali amuna ake 400. Yakobo anabagawa bana bake pakati pa ba leya, ba rakele ndi anchito akazi abili. 2Ndipo anaika anchito na bana bawo kiutsogolo, kukonkapo anali leya na bana bake na kukonkapo anali Rakele na Yosefe kumbuyo kwa bonse. 3Iye mwine anayenda patsogolo pa bonse. Iye anagwanda pansi ka 7, kufikila anafika pafupi na mbale wake.4Esau anamutamangila iye, na kumukumatila, na kumulandila ndi kumufyofyonta. Ndipo iwo analila. 5pamene Esau anayangana ku sogolo, anaona azimai ndi bana. Iye anakamba, " Nindani awa banthu amene bali na iwe? " Yakobo anakamba, " Aba ni bana amene Mulungu mwacisomo cake anapasiwa na wancito wanu."6Ndipo banchito akazi banafika pamodzi ndi bana bawo ndipo banagwanda pansi. 7Wokonkhapo anali Leya ndi bana bake anafika ndi kukwanda pasi. Posilizila Yosefe na Rakele ana bwela na kugwanda. 8Esau anakamba, " Utanthauza ciani pa banthu wonse aba bambili nakumana nao?" Yakobo anakamba, " Kuti nipeze mwayi pameso pa bwana wanga."9Esau anakamba, " Nili nazo zokwanila, mbale wanga. Zisungele zonse zamene ulinazo." 10Yakobo anakamba, " Yai, napapata, Ngati napeza mwayi pa menso panu, nipempa kuti mulandile mpaso iyi yofumila m'manja yanga. 200 nadi naona pa maso pano, cili nga nikuona pa maso pa Mulungu, ndipo mwani landila ine. 11Napapata landilani mpaso yanga yamene nakubweleselani ine, cifukwa Mulungu wacita naine mwa cisomo, ndipo ndili nazo zokwanila," Pamene Yakobo anamupapatila, Esau analandila mpaso ija.12Ndipo Esau anakamba, "Tiyeni tiyambepo kuyenda, ine nizakhala pa songolo panu." 13Yakobo anamu uza iye, " Mbuye wanga zibani ici kuti bana nibang'ono, ndi mbelele ndi ng'ombe zinyonsha tubana. Ngati tizayenda mwa mpavu cukanga siku imodzi cabe zibeto zizafa. 14Napapata lekani bwana ayende patsongolo pa kapolo wanu. Nizayenda pangono pang'ono, ngani mwazibeto zamene zili ku songolo, ndi monga bana, kufikila tifike kwa bwana wanga ku Seiri."15Esau anakamba, " Lekani nikusiyileni amuna banga amene bali na ine" Koma Yakobo anayankha, " Ciani mzacitila izo? Lekani nipeze mwayi pamanso ya bwana wanga." 16Ndipo Esau pa siku ija anayambapo ulendo wake kupita ku Seiri. 17Yakobo anayenda ku sokoti, kukazimangila iye mwine nyumba na makolo ya zibeto zake. Ndipo zina la malo ndi Sokoti.18Pamene Yakobo anacoka kufumila ku padamu Aramu, anafika bwino ku mzinda wa Shekemu, malo yopezeka mu Kenani anaphumulila pafupi ndi mzinda. 19Ndipo anagula malo pamene anamangila Hema kucokela ku mwana wa Hamo, tate wa Shekemu, ndi mutengo wa Hundriredi ziduswa za siliva. 20Kuja anamanga guwa ndikuipatsa zina kuti Eli Elone Isilayeli.

34

1Manje Dina mwana wa Leya wamene ana bala kuli Yakobo anayenda kukumana akazi aci cepele bamu malo. 2shekemu mwana wa hamori mu Hiviti, mwana mwamuna obadwa ku mfumu wamu malo, ana muona. Ana mutenga ndi kugona naye ndi kumu citisa manyazi. 3Ana tenga mutima na Dina, mwana wa Yakobo. Ana mukonda mukazi waci cepele ndi kukamba naye mo ndenka.4Shekemu ana kamba na atate bake Hamori kuka kamba kuti, " Tengani mukazi mungono uyu ankale mukazi wanga." 5Manje Yakobo ana nvela kuti, ana muonga Dina mwana wake. Bana bake ba muna banali na zibeto zake mu sanga, ndipo Yakobo analigwila mutendele panka bana bwela.6Hamori tate wa Shekemu ana yenda kuli Yakobo ku kamba naye. 7Bana bamuna ba Yakobo bana bwela ku coka kusanga pamene bana nvela za ici. Bamuna bana kwiyisida bana kalipa maningi cifukwa Israeli ananvesewa manyazi posona na mwana wa Yakoba mukazi, chintu moonga ici sicinali kufunika kuchitika.8Hamori ana kamba na beve, kuti, " Mwana wanga Shekemu akonda mwana wamunu mukazi napapata mupaseni ankale mukazi wake." 9Tikwatilane, tipaseni bana banu bakazi, ndipo tengani bana bathu bakazi kwa imwe. 10Muzankala naise ndi pamalo pazankala po seguka kuli imwe kunkala ndi ku gulisa ndi ku gula ka tundu."11Shekemu ana kamba kuli batate bake ndi abale bake. " Lekani ni peze mwai pa menso panu ndi vamene vili vonse muza kamba niza kupasani. 12Nifunseni pali vintu vikulu monga lobola na mphaso mwamene munga funile, ndipo niza kupasani vilivonse vamene muza ni uza, koma nipaseni mukazi wa ci cepele ankale mukazi wanga." 13Bana bamuna ba Yakobo bana yanka shekemu na Hamori tate wake mo nama, chifukwa Shekemu anaonga Dina mulongo wabo.14Bana kamba kuli beve, " Sitinga cite ici, ku pasa mulongo watu kuli aliyense osa dulidwa, ndipo ice cingankale ca ci soni kuli ise. 15Pali ici cabe ndiye pamene tizanvelana na imwe: Ngati uzankala odulidwa moonga ise, ngati mwanuna onse paimwe nadulidwa. 16Ndiposo tiza pasa bana batu bakazi kuliimwe, ndiponso tiza teza tenga bana banu bakazi kwa ise, ndipo tizankala pamozi nakunkala bantu ba mozi. 17Koma ngati simuti nvela ndi kudulidwa, ndiponso tiza tenga mu mulongo watu ndi kuyenda."18Mau yabo yana muko ndwelesa Hamori ndi mwana wake Shekemu. 19Uyu munyamata sana cedwe kucita vamene bana kamba, cifukwa anali okodwela mu mwana mukazi wa Yakobo, na chifukwa chakuti enzeli munthu wo lemekezeka maningi munyumba yatate bake yonse.20Hamori na Shekemu mwana wake mwamuna bana yenda pongenela mu mzinda wabo naku kamba naba banthu bamzinda, kuti, 21"Aba bantu bana mtendele naise, balekeni bankwe mu malo na kugulisilamo, zoonadi, aya malo niya kulu yobkwanila. Lekani titenge bana babo ba kazi bankale bakazi bathu, naku ba pase bana batu bakazi.22Pali ici cabe banthu aba ndiye pamene aba banthu baza vomela ku nkala naise na kunkala banthu ba mozi, ngati bamuna bonse pakati paise nebo dulidwa, mwamene balili odulidwa. 23Kansi vobeta vabo na katundu yabo nyama zao zonse sivizankala vatu? Ndipo tivomelezane, nabo na kunkala pakati patu."24Banthu bonse bamuzinda bana nvelela Hamori na Shekemu, mwana wake mwa muna. Bamuna bonse bana dulidwa. 25Pasiku ya ci tatu, pamene banali kunvela ku baba, pabana babili ba Yakobo (Simeon ndi Levi abale ba Dina), aliyense anatenga lupanga naku menya mzinda wamene unali ukutila nacititezo cake, naku paya bamuna bonse. 26Bana paya Hamori na mwana wake mwamuna Shekemu kusebenzesa lupanga. Bana tenga Dina ku coka ku nyumba kwa Shekemu nakuyenda.27Bana ba Yakobo bamuna benangu bana bwela kuma tupi yao kufa naku bela mzinda, chifukwa aba banthu bana ononga mulongosi wabo. 28Bana tenga vobeta vabo, ngombe zabo, aburu na vonse vamu mzinda na va minda yoba zunguluka. 29Cuma cabo conse. Bana bao bonse na ba kazi babo bana guliwa. Bana tengela pamozi na vonse vamu manyumba.30Yakobo ana kamba kuli Simeon na Levi "Musalete so vuta pali ine, kuni lengesa ku nunka kuli bonkala mu malo yano, akenani na Aperiziti ndine ocepe muku penda. Ngati ba zakumana bonse pamozi naku nicita cipongwe, ndipo nizaonengeka ine naba munyumba yanga." 31Koma Simeon na Levi ana kamba, " Kodi Shekemu Enzekufuna mulongosi wanthu moonga ni hule?"

35

1Mulungu ana uza Yakobo, "nyamuka, yenda mpaka kufikila ku Bethe, Ndipo ankale kwamene kuja. Manga guwa kwamene kusa ya mulungu, wamene ana oneka kuli iwe pamene anataba kuli Esau mubali wako. 2Ndipo Yakobo anauza ba munyumba yake na bonse bamene anali nabo, "ikani kutali tu milungu twa kunja twamene tuli naimwe, ziyeleseni mweka, ndipo chinjani vovala vanu. 3Ndipo tiyeni tiyambeko na kuyenda mpaka kufikila ku Bethel niza manga guwa kuja ya Mulungu, wamene ananiyanka mu musiku yo tangwanika, na ku nkala naine kuli konse kwamene nayenda."4Mwaicho banamupasa Yakobo tonse mulungu twa boza twamene tunali mu manja mwao, na masikiyo ya mene yanali ku matu yao. Yakobo anayafwikila mangansi mwa mutengo wathundu unali pafupi na she chem. 5Pamene banali kuyanda, Mulungu anapanga manta kugwela pa mizi zamene zanali kuba Sibaha bakonke bana ba Yakobo.6Mwaicho Yakobo anafaka ku Luz (amene inali Bethel), yamene inali kumalo yaku Kanaani, eye na bonse bantu bamene banali naye. 7Anamanga guwa kuja na kupasa Mulungu anazi onesa kuli eve pamene anali kutaba ku chokela kuli mu bale wake. 8Deborah, wachinto wa Rabekal, anafa. Anashikiiwa ku Bethel pansi pa mutengo wathundu, mwaicho bana itana malo yaja Allon Bakuthi.9Pamene Yakobo anabwela kuchoka ku Paddan Aran, Mulungu anaonekela kuli eve naku mudalisa. 10Mulungu anakamba kuli eve, "Zina yako si Iza itaniwa Yakobo. zina yako izanikala Iseali." waicho Mulungu anamuitana zina yake Isreali.11Mulungu anakamba kuli eve, "ndiwe Mulungu wampamvu zonse. Kaba laneni na kupaka. Ziko na magulu ya maiko yazachoka kuli imwe, pa bana banu. 12Malo yamene nina pasa iwe ku bana bo badwa mumbuyo mwako. niza bapasa malo." 13Mulungu anachokako ku malo kwamene nanakamba na naye.14Yakobo anaika mwala ukulu pamalo pamene Mulungu anali ku kamba naye. Pila ya mwala. Anafilapo chakumwa kunkala ngati nsembe na mafuta. 15Yakobo anaitana malo yamene Mulungu analikukamba naye, bethel.16Banali pa ulendo kuchokela ku Bethel, Rakel vumo inauka. 17Pamene vumo inauka mo vuta, omubalisa anamu uva, "osayopa, apa manja uzankala na mwana mwamuna winangu. 18Pamene anali kufa, anaku pema ko silizila anapasa zina mwana wake Ben-oni, koma atate bake banamuitana Benjamin. 19Rakel anafa ndipo banamu shika munjila yo yenda ku efrata (ndiye Bethlehem). 20Yakobo anaikapo mwala pa manda pake ni chozibilako pa manda pa Rakel mpaka lelo.21Isreali anayenda na kufika hema yake pasogolo pa yanganila vibeto vake. 22Akali kunkala kumalo kuja, Reubeni anagona na Bilhah nukazi wa atate bake waku mbali, na Isreali ananvela pali iyi nkani.23manji Yakobo anali na bana bamuna 12. Bana bake kuli Leya banali Reubeni, mwana wkae oyamba, ana Simeoni, Levi, Yudah, Isacha, na Zebulani. 24Bana bake kuli Rakel banali Yosefe na Banjamin. 25Bana bake kuli Bilhah wa nchito wachikazi banali Dani na Naphatali.26Bana ba Zelipa, wachoto wa Leya mukazi, banali Gad, na Asher. Bonse aba banali bana ba Yakobo bamene anabala ku Paddan Aram. 27Yakobo anayenda kuli Isaki atate bake, ku Mamre mu Kinah Arba ( chimozimozi Hebron) kwamene Abrahamu na Isaki banali ku nkala.28Isaki anankala zaka 108. 29Isaki abapema ka kosilizila nakufa, ndipo anatengewa ku makolo yake, nkalamba ya masiku yambili. Esau na Yakobo, mwana wake mwamuna, banamushika.

36

1Aba ndiye ba nali mibadwo ba Esau (ozibika futi ati Edomu). 2Esau anatenga bakazi bake ku chokela kuma kanani. Aba ndiye bakazi bake: Adahi mwana mukazi wa Eloni waku Hittite; Oholibamah mwana mukazi wa Ana, muzukulu zw Zibioni waku Hivitte; 3na Basemathi, mwana mukazi wa Ishmaeli, mulongosi wa Nebaioth.4Ada anabala Elifazi kuli Esau, na Basemati anabala Ruweli. 5Oholibama anabala Jeushi, Jalami, na Kora. Aba ndiye banali bana bamuna ba Esau banabadwa kuli eve mu malo ya Kenani.6Adahi ana bala Eliphaz kuli Esau, kuchoka apo Basemathi ana bala Reueli. oholibamah ana bala Jeushi, Jalam, na Korah. Aba ndiye ba nali bana bamuna ba Esau bana badwila ku malo ya Kanani. Esau anatenga bakazi bake, bana bake bamuna, bana bake bakazi na bonse bapa nyumba yake, na vobeta vake - navi nyama vake vonse, na vintu vake vonse, vamene anafaka pamozi ku malo ya kanani, naku chokako ku malo kuli mubale wake Yakobo. 7Ana chita chifukwa vinthu vabo vina paka kuti sibanga nkale pamozi. malo yamene bana nkhalapo siyi nakwanile kuba thandizila chifukwa chavobeta. 8Kuchoka apo Esau, Esau ozibakanso Edomu. ana nkhala ku ziko ya seir.9Aba ndiye ba nali midadwo ba Esau, makolo bama Edomite ku ziko ya seir. 10Aya ndiye yanali mazina ya bana ba muna ba Esau: Eliphazi mwana mwamuna wa Adahi, mukazi wa Esau; Reueli mwana mwamuna wa Basemathi, mukazi wa Esau. 11Bana bamuna ba Eliphazi benze Temani. Oma, Zifo, Gatami, na Kenazi. 12Timna, mpali ya Eliphazi, mwana mwamuna wa Esau, anabala Amaleki. Aba ndiye banali ba Zukulu ba Ada mukazi wa Esau.13Aba ndiye banali bana bamuna ba Reueli: Nahati, Zera, Shama, Mizza. Aba ndiye banali bazukulu Basemathi, mukazi wa Esau. 14Aba ndiye banali bana bamuna ba Oholibama, mukazi wa Esau, enzeli mwana mukazi wa Ana na muzukulu mukazi za ZibiyoniAnamu balila Esau Jeushi, Jalami, na Kora.15Uyu ndiye mutundu pali mibawo wa Esau: mibadwo wa Eliphazi, mwana oyamba wa Esau: Temani, Oma, Zifo, Kenazi, 16Kora, Gatami, na Amaleki. Ndiye yenzeli mutundu yamu mibabdwo ya Eliphaz ya Edom, Banali bazukulu ba Ada.17Uyu ndiye unali mutundu wa Reueli, mwana mwamuna wa Esau: Nahati, Zera, Shama, Mizza, Uyu ndiye unali mutundu obadwila klui Reueli ku malo ya Edomu. ndiye banali bazukulu ba Basemati, mukazi wa Esau. 18Uyu ndiye unali mutundu wa Oholibama: mukazi wa Esau: Jeush, Jalam, Kora. Uyu ndiye mutundu wa mibabdwo wa mukazi wa Esau Oholibama, mwana mukazi wa Ana. 19Aba ndiye banali bana bamuna ba Esau (ndiye futi Edomu), aba ndiye banali ma mfumu20Aba ndiye banali bana Seya waku Horiti, bonkhala pa malo: Lotani, Shobali, Zibiyoni, Ana, 21Dishoni, Eze, na Dishani. Uyu ndiye mutundu wama Horiti. bamene ba nkhala ku Eya pa malo ya Edomu. 22Bana Lotani benzeHori na Hemani, na Timna mulongosi wa Lotani.23Bana bamuna ba Shobali: Alvan, Manahati, Ebali, Shefo, na Onamu. 24Aba ndiye banali bana bamuna ba Zibiyon: Aiah na Ana. Uyu ndiye Ana anapeza kamugodi ka manzi youkupya muchululu pamene enze kudyesa ma donke ya Zibiyoni tate wake.25Aba ndiye banali bamu ba Ana: Dishoni na Oholibama, mwana mukazi wa Ana. 26Aba ndiye banali bana bamuna ba Dishoni: Hemdani, Eshabani, Ithran na Kerani. 27Aba ndiye banali bana bamuna ba Eze: Bilhan, ZAavani, na Akani. 28Aba ndiye banali bana bamuna ba Disheni: Uz na Arani.29Uyu ndiye unali mitundu wama Horites: Lotani, SHobali, Zibiyoni, na Ana, 30Dishoni, Ezeri, Dihani: izi ndiye zinali mitundu zama Horites, kulingana na mitundu wapa malo ya Seya.31Izi ndiye mfumu zinal ku lamulila pa malo ya Edomu pamene ili yonse ikalibe ku lamulilapa pali bana bamuna ba Isireli: 32Belai mwana mwamuna wa Bowa, ana lamula Edom, na zina ya muzinda yenzeli Dinhabah. 33Pamene Belai anafa, ndiye Jobabi mwana mwamuna wa Zera waku Bozrah, ana lamulila pa malo pake.34Pamene Jobabi anafa, Hushami enze waku malo kwa ma temanites, ana lamulila pa malo pake. 35Pamene Hushami anafa, Hadadi mwana mwamuna wa Bedadi wamene ana konjesa ma midiantes mu malo ya Moabi, ana lamulila pa malo yake . zina yamu muzunda inali Aviti. 36Pamene Hadadi anafa, ndiye pamene Samlahi waku Masrekah ana lamulila pa malo yake.37Pamene Samlahi anafa, ndiye Shauli waku Rehoboth ku kamumana ana lamulila pa malo yake. 38pamene Samlahi anafa,ndiye pamene Baal-Hanani mwana mwamuna wa Akbor, ndiye ana lamulila pa malo yake. 39pamene Baal-Hanani mwana mwamuna wa Akbor, anafa, ndiye pamene Hadar ana lamulila pa malo yake. ZIna ya muzinda yake yenzeli Pau. Zina yamu kazi wake inali Mehetabeli mwana mukazi wa Me Zahab.40Aya ndiye yanali mazina yaba sogoleli ku chokela kuli mibabdwo ya ESau, kulingana na mitundu na chigau chao. am Zina yabo: Timna, Alvah. Jethehi, 41Oholibama, Elahi, Pinon, 42Kenaz, Temani, Mibzar, 43Magdiel, na Irami. Aba ndiye banali ba sogoleli ba Edomu lulingana nama nkalidwe mu malo yamene bana tenga. ndiye enze Esau, tate wama Edomites.

37

1Yakobo anankala mu malo ya Kanani, mwamene anankalamo batate bake. 2Ivi ndiye vinachitika pa umoyo wa Yakobo, Yosefe, wamene anali munyamata mufana wa zaka seventini, anali kulonda vinyama nazibale bake. Anali na bana ba Bila na bana ba Zelipa, bakazi ba batate bake. Yosefe anali kubaletela lipoti yoyipa kuli tate wawo.3Koma manje Isilayeli anakonda Yosefe manigni kupambana na bana bake bamuna bonse chifukwa ndiye mwana anabadwa Yakobo atakalamba pa bana bamuna bonse. Anamupangila chovala chabwino maningi. 4Babale bake banaona kuti batate babo amukonda maningi kuchila na pa bana bonse. Anamuzonda andipo sanalikukamba naye bwino mwa chifundo.5Yosefe analota maloto, naku uza babale bake viloto vamene ivi. Banamuzondelako maningi. 6Anakamba kuli benve kuti, Napapata nvelani maloto yanga yamene na lota.7Onani, tinali kumanga mitolo ya vamumunda ndipo onani, mutlolwanga unayamuka nakuyimilila kuyanga kumwamba, ndipo onani, mitolo yanu inabwela mumbali zonse nakubelamila mutolo yanga." 8Babululu bake banakamba kuli enve kuti, "Zo'ona uzatilamulila ise? uzatisogolela zo'ona ise? Banamuzondelako enve chifukwa chamaloto yake na mau.9Analota maloto yenangu naku uzako babale bake. Anakamba kuti, "Onani, nenze nalota loto inangu: Zuba na mwezi na nyenyezi zili leveni zinali kugwadila ine." 10Anayenda kukamba maloto kuli batate bake chimozi mozi mwamene anauzila babale bake, ndipo batate bake anamukalipila. Anakamba kuli enve kuti, " namaloto yamu tundu bwanji aya yamene walota? ushe vizakachitika zo'ona kuti bamai bako naine naba bale bako tizabwela naku kugwadila pansi kuli iwe? 11Abale bake banamuchitlila jelasi, koma batate bake banasungila iyi nkani mumutima mwao.12Ba bale bake banayenda kukadyesela vinyama va batate babo ku Shekemu. 13Isilayeli anakamba kuli Yosefe kuti, "kodi azibale bako sibanyende kudyesa vinyama ku Shekemu? Bwela ndipo nizakutuma kuli benve." Yosefe anakamba kuli batate bake, "Ndine okonzeka." 14Anakamba kuli enve kuti, "Yenda manje, ukaone ngati vibayendela bwino benve navi nyama, ndipo uniletele mau." Ndipo Yakobo anamutuma kuchokela ku vale ya Hebroni ndipo Yosefe anayenda ku Shekemu.15Muntu winangu anamupeza Yosefe ali kuyenda musanga. Mwamuna uja anamufunsa "Usakila chani?" 16Yosefe anayanka kuti nisakila azibale anga, niuzeni, nisakila zaiblae anga, miuzeni napapata, kwamene balikudyesela vinyama. 17Mwamuna uja anati, "Banachokako kuno, ndaba na banvela bakamba kuti, tiyeni ku Dotani." Yosefe anaba konkamo ba bale bake bapeza ku Dotani.18Banaona bakali kutali, ndipo bakalibe kufika pafupi nabenve, bana pangana mwachiwembu kuti amupaye. 19Ba bale bake banakambisana kuti, "Onani, Uyu wamaloto wabwera pafupi. 20Bwelani manje apa, chifukwa chake, tiyeni timupaye timuponye mu umozi mu mugodi ilikuno. Tizakamba kuti, 'Chinyama chamusanga chinamudya. ' Tizaona vamene maloto yake yazasanduka."21Rubeni anamvela iyi nkani nakumupulumusa mumanja mwao. Anakmba kuti, Tisamu paye." 22Rubeni anakamba kuli benve kuti, "Osakesa magazi muponyeni mumu godi uyu uli kuno kusanga, koma asamu kumyako kwanja, "pofuna kuti angamupulumuse kumuchosa mumanja mwao nakuyenda kumupeleka kumubweza kuli batate bake.23Chinachitika kuti pamene Yosefe anafika pali bazibale bake, banamu vula chovala chake chokongola. 24Banamutenga nakumuponya mumugodi munalibe chintu, ndipo munalibe manzi mukati.25Bana nkala pansi kuti badye buledi. Bananyamula menso yabo nakuona, ndipo, onani, kunali kalavani yama Ishamealiti inali kubwela kuchokela ku Giliyadi, nama kamelo yabo yonyamula masipayisi na balami na mure. Banali paulendo bopeleka iyi katundu ku Iguputo. 26Yuda anakamba kuti kuli ba bale bake, "Pali pindu yabwanji ngati tizamupaya mubale watu nakubisa magazi yake?27Bwelani, ndipo tiyeni timugulise kuli ma Ishiamyeliti ndipo tisakumyepo manja yatu pali enve. Pakuti nimubale watu, magazi yatu, " Ba bale bake banamunvelela iyi. 28Mamechanti baku Midiyani banapitila pafupi. Ba bale bake banamudonsa Yosefe nakumunyamula kumuchosa mumugodi. Banamugulisa Yosefe kuli ma Ishimayeleti pa mutengo wa twenti ndalama za siliva. ndipo ma Ishimayeliti anamunyamula Yosefe kuyenda naye ku Iguputo.29Rubeni anabwelelapo pamugodi, ndipo onani, Yosefe analimo mumugoidi. 30Iye anang'amba vovala vake. Anabwelela kuli bazibale bake nakukamba kuti munyamata salimo! ndipo ine nizayenda kuti?"31Banapaya mbuzi naku tenga malaya ya Yosefe nakuya sunsika mu magazi. 32Pamene banaleta chija chovala kuli batate babo nakukamba kuti," Tapeza ichi. Tapapata chiyanganeni ngati ni chovala chamwana wanu kapena olo sichamene." 33Yakobo anachiziba nakukamba kuti, "Nichoavala cha mwana wanga mwamuna. Chinyama chamusanga chamudya. Yosefe akazuliwa zo'ona mumapisi na chinyama."34Yakobo anang'amba vovala vake naku vala 36chovala chamsaka mumusana. Analila mwana wake mwamuna masiku yambili. 35Bonse bana bake bamuna na bakazi bananyamuka kumu tandiza kulila momupepesa, koma anakana kumuchita kamfoti. Anakamba kuti, "Zo'ona nizayenda ku Shilo nikalikulila mwana wanga." Batate nake banalila mokuwa kamba ka enve. Ma Midiyanaiti yanamugulisa mu Iguputo kuli Potifa mu ofisala wa Farao, mukulu wama bodigadi.

38

1Inabwela ntawi pomwe Yuda anasiya abale bake nonkhala kuli omwe anali na zina la Hira. 2Anapeza kuja mwana mukazi wa mwamuna waku Kenaani anali na zina la Shuwa. Anamutenga ndipo anamungela.3Anankhala na mimba na bala mwana mwamuna. Anamupasa zina la Eri. 4Anankhala na mimba nafuti nomabala mwana mwamuna. Anamupasa zina la Onani. 5Anankhala na mwana mwamuna nafuti nomupasa zina Sela. Kunali ku Kezib kwe anamubalila.6Yuda anapezela Eri mwana wake woyambilila, mukazi wo kwatila zina lake anali Tama. Eri, mwana wa 7Yuda wo yamba, analiuchita zo chimwa pa menso ya Yehova. Yehova anamupaya.8Yuda anati kuli Onani, "ngenela mukazi wa Abbale bako. Chita nchito yamulamu mwamuna kuli eve, kuti ukulise mwana wamu abale bako. 9Onani anaziba kuti bana zibaza nkhala bake. Lyonse akangena kumukazi wamu bale wake, anatila pansi mpavu vachimuna kuti anankhale na mwana wa abale ake. 10Ve anachita venze vochimwisa pa menso ya Yehova, Yehova anamupaya na eve.11yuda anati kuli Tama, muoungozi wake, "Upitise kunkhala wofesdwa munyumba yabatate bako kafika sela, mwana wanga, akakule."chifukwa anayopa, " Kuti angafe nayeve, monga abale bake." Tama ayenda kunkhala munyumba yabatate bake.12Patapita ntawi itali, mwana mukazi wa Shua, mukazi wa Yuda, anafa. Yuda bana mutontoza ndipo anayenda kuli bo embela mbelele zake ku Tina , eve namukaze Hira waku Adulamayiti. 13Tama bana muwuza, "wona, ba pongozi bako bamuna bayenda ku Tina kuyembela mbelele zake." 14Anachosa zovala zamukazi wafedwa ndipo anazivwinikila na nyula nozimanga. anakhala pongenela mumalo ya Enami , inali pambali pa njila yaku Tina. chifukwa anawona kuti Sela akula koma sibanamukwatilise kuli eve.15Pamene Yuda anamuwona anaganiza monga nimukazi wachiwele wele chifukwa enze anabisa nkope yake. 16Anyenda kuli eve ndipo anti, "Bwela, leka naiwe chifukwa sana zibe kuti nimupongozi wake mukazi ndipo mukazi anakamba kuti, "Uzani pasa chani ukagona naine?"17Mwamuna anakamba kuti, "Niza kutumila kambuzi kang'ono kuchoka kuzobeta." mukazi anakamba kuti, "uzampasa lowezo kufikila ukatume?" 18Mwamuna anakamba kuti, "Nilonjezo bwanji yeningakupase? mukazi anayanka, "chidindo na ntambo yako na ndondo ili mumanja yako."Anamupasa no yenda kuli eve, ndipo anankhala na mimba yake.19Mukazi anayima noyenda njila yake. Anachosa nyula yake no vala zovala za wofedwa. 20Yuda anatumiza ka mbuzi kang'ono kupitiula mumunzake waku Adulamiyiti kuyi angetenge lonjezo lake kuchokela mumanja yamukazi, kuno sanamupeze.21Waku adulamayiti anafunsa ba muna ba pa malo, "alikuti mukazi wachiwelwwele enze pa mbali pa njila ya Enami?" Banakamba kuti."kunalibe mukazi wachiwelwbwele pano." 22Anabwele kuli Yuda anakamba kuti, "Sinamupeze. Nabamuna ba pamalo banakamba kuti, 'kuliba mukazi wechiwelewele pano." 23Yuda anakamba kuti, mutekeni usunge vintu, kuti tisaletelewe nsoni, chifukwa, nonatuma ka mbuzi kang'ono koma sunamupeze."24Pekunapita myezi itatu uda banamuza kuti. "Tama mupongozi wako mukazi achita zawewelele, ndipo anankhala mimba. "Yuda anakamba kuti, "Muleteni kuno timushoke." 25Pabanamuleta panja, anatuma utenga kuli bapongozi bake, "Nilinamimba ya mwamuna alina vintu ivi." Mukazi anakamba kuti, "Sakilani mwine wa ivi, chofundo na ntambo na ndondo." 26Yuda anaviziba no kamba kuti, "Niwolungama kuchila ine. chifukwa sinina mukwatolise ku mwna wanga, Sela."27Pamene inafika ntawi yonkala na mwana, Onani, bampundu banli mumala. 28Inafika pamene eze ku bala umozi anachosa kwanja panja, ndipo wabalisa anatenga ka ntambo ka redo no kamanga pa kwanja nokamba kuti, "Uyu ayambilila kuchoka."29Koma pamene ana bweza kwanja, ndipo, Onani, bale wake anayambilila kuchoka. Wobalisa anakamba kuti, "Mwewachokela!" Ndipo bana mwitana kuti Perezi. 30Bale wake anachika, anali naka ntambo ka redi pa kwanja, ndipo bana mwitana kuti Zera.

39

1Yosefe ana letewa ku Egipito. Potifa, mu sogoleli wa Farao wamene anali muklu wama malonde waku Egipito, anamu gula kuli ma Ishmaelites, wamene anamaleta kuja. 2Yehova anali na Yosefa ndipo ana nkala olemela kwambili. Ana nkala mu njumba ya bwana wake waku Egipito.3Abwana bake bana ona kuti Yehova anali na Yosefe na zonse zamene anali kuchita yehova ana chulukisa. 4Yosefe anapeza mwai. Anamu sebezela Potifa. Potifa anapanga Yosefe bwana wapa nyumba yake, navonse vintu vake, anavi ika mu manja mwake.5Zina chitika kuti choka pamene ana nkhala musogoleli wapa nyumba na vonse vintu, Yehova anadalisa nyumaba yawaku Egipito chifukwa cha yosefa. Daliso ya Yehova inali na vonse vintu va Potifa vamu nyumba namu munda. 6Potifa ana ika vonse vintu vake mumanja ya Yosefa. Sanali kufunika ku ganiza pali chili chonse koma chabe chokunya chamene eze kudya. Ndipo Yosefa anali wa bwino nakuoneka bwino.7Zina chitika ku choka apa kuti mukazi wa bwana wake anamu kumbwila Yosefe no kamba, " Gona na ine." 8Koma anakana ku gona naba kazi ba abwana bake, " Ona, bwan wanga sama ikako nzelu ku vonse nichita mu nyumba yabo, anani ika ku langanila vonse vintu vabo. 9Kulibe mwamukulu mu nyumba muna pali ine sana bisa kantu kuli ine koma iwe, chifukwa ndiwe mukazi wake. Ninga chite bwanji zo ipa izi naku chimwila Mulungu?"10Anakamba na Yosefa siku na siku, koma anakana ku ngona nabo olo ku nkala naye. 11Zina chitika kuti siku imozi anayenda ku sebenza ku nyumba. Amuna bonse sibana liko mu nyumba. 12Anamu gwila pa chovela naku kamba, " Gona na ine." Anasiya chovala mu manje yake, kutaba, kuyenda panja.13Ina bwela kuti, pamene anaona kuti psaya chovala mu manja naku tabila panja, 14ana itana amuna ku nyumba naku bauza kuti, " Ona, Potifa ati letela muntu wachi Hebeli kuti sobelesa. Ezeli abwela kuti agone na ine ndipo napunda. 15Zinaditika pamene napunda, ataba kusiya chovala naine, nakuyenda panja."16Ana ika chovala chake pafupi na eve mpaka ba bwana bake ba bwela ku nyumba. 17Anamu londolela izi, " Mu Hebeli wa nchito wamene unaleta kuli ise, eze abwela kuni sobelesa. 18Zabwela za chitika kuti pamene napunda, ataba kusiya chovala chake naine, atabila panja."19China chitika, pamene abwana ana vela ku londolola kwaba kazi abo, " Ichi ndiye chamene wa nchito wako achita kuli ine," Ana kalipa kwambili. 20Abwana ba Yosefa banamutenga naku ika mu ndende, mu malo mwamene akaidi ba mfumu banali. Ezeli mu ndende.21Koma Yehova anali na Yosefa nakumu onese ku kulupilika kwachi pangano. Anamu pasa mwai mu menso yao olonda ndende. 22Olonda ndende ana pasa mu manja mwa Yosefe bonse akaidi banali u ndende. Vilivonse vamene bana chita kuja, Yosefe anali oyanganila. 23Olonda ndende sanade nkawa pali chili chonse chinali mu manja yake, chifukwa Yehova anali na eve. Zili zonse zamene ana chita, Yehova ana chulukusa.

40

1Zinabwela pambuyo patapita ivi vintu, wopelekela chakumwa kwa mfumu ya ku Igupto ndi wopanga buledi anakalipisa bwana wawo, mfumu ya ku Igupto. 2Farao anakalipila banchito bake bakulu bakulu babili, mukulu opeleka chakumwa na mukulu bopanga buledi. 3Anabaika mu jele mu nyumba ya malonda mukulu, mu jele mwamene Yosefe analili.4Mukulu wa bamalonda anabapeleka mumanja uya Yosefe, ndipo iye anabasamalila. Bana nkhala mu jele kwa kantawi. 5Bonse babili bana lota chiloto, wopasa chakumwa na opanga bulendi ya mfumu ya ku Igupto pamene banali mu jele. Aliyense anali na chiloto usiku umozi, ndipo chiloto chili chonse chinali ndi chivumbuluso.6Yosefe anabwela kuseni mukubaona. Onani banali osakodwela. 7Anafunsa bakulu bakulu ba Farso bamene banali naye mu jele mu nyumba ya bwana wawo, nati nanga nichani muoneka osakondwela lelo? 8Iwo bana muyanka, bonse talota chiloto ndipo kulibe aliyense angamasulile. " Yosefe anabauza, " Kodi kumasulila sikwa Mulungu niuzeni, napapapta."9Mukulu opeleka chakumwa anamu uza chiloto chake Yosefe. Anamu uza kuti, onani, mutengo unali pasongolo panga. 10Mumutengo munali ntambi zitatu. Pamene unapulika, maluba anachoka ndipo unabala mpesa zakupya. 11Chiko cha Farao chinali mumanja mwanga. Ninatenga mpesa nakuzi fyantila mu chiko cha Farao, ndipo ninaika chiko mumanja mwa Farao."12Yosefe anati kwa iye, iyi ndiye tantauzo lake. Ntambi zitatu ni masiku atatu. 13Mu masiku yatatu Farao azakuchosa mu jele nakukubweza pa chito yako uzaika chiko mumanja mwa Farao, monga mwamene unalili opeleka chakumwa.14Koma ukaniganizileko zikayenda bwino naiwe. Ukamu uze Farao pali ine kuti akani choseko muno mu jele. 15Popeza ine ninali monga ogwiliwa kuchokela ku ziko la Ahebri, ngankhale kuno, sininalakwe kali konse kuti ni pezeke mu jele muno."16Pamene mukulu opanga bulendi anaona kuti kuvumbulusa kunali bwino, anati kwa Yosefe, " Naine nenze na chiloto ndipo, onani mabasiketi yatatu ya buledi yanali pa mutu panga. 17Mu basiketi ya pamwamba munali zosiyana siyana za kudya za Farao, koma tunyomi tunadya mu basiketi inali pa mutu panga."18Yosefe ana yanka nati, " Iyi ndiyo tantauzo. Mabasiketi yatatu ni masiku atatu. 19Mu masiku yatatu Farao azakuchosa mu jele ndipo azakupachika pa mutengo. Ndipo tunyoni tuzadya tupi yako.20Kunabwela kuti pasiku la chitatu, linali siku lakukumbukila kubadwa kwa Farao. Anapanga madyelelo yabanchito bake bonse. Kumwa na mukulu wopanga buledi, kuli ba nchito bake. 21Ana mubweza panchito yake mukulu wopeleka chakumwa ndipo anaikanso chiko mumanja mwa Farao. 22Koma anapachika mukulu wa opanga buledi, monga mwamene Yosefe anavumbulusila kwa iwo. 23Koma mukulu wa opeleka chakumwa uja sanamukumbukile Yosefe, ndipo anamuibala.

41

1Pamene panapita zaka zokwananila zibili zatuntulu, Farao analota. 2Onani, anaimilira mumbali mwa Nailo. Ndipo, onani, ng'ombe zisanu na zibili zinachoka mumumana wa Nailo, zabwino ndipo zoina futi, ndipo zinali kudya muma bango. 3Onani, ng'ombe zina zokwanila zisanu na zibili zinabwela kukonkapo kuchoka mu Nailo, zoyonda zosaoneka bwino. Beve banaimilila pafupi na ng'ombe zina mumpepete mwa mumana uja.4Ndipo ng'ombe zosaoneka bwino zija zoyonda zinadya ng'ombe zisanu ndi ziwiri zija zabwino zoina. Pamene apo Farao anauka. 5Anagona futi ndipo analota nafuti kachibili. Onani, ngala zisanu na zibili za tirigu zinamera pa phesi imodzi, zabwino na zabwino. 6Ndipo onani, ngala zisanu na zibili, zofota zo ochewa na mpepo ya kum'mawa, zinamela pambuyo pawo.7Mitu yofota inamela ngala zisanu ndi ziwili zija zabwino koma futi zozula. Pamene Farao anauka, onani, yanali chabe maloto. 8Ndipo kuseniseni muzimu wake unavutika maningi. Anatumiza kukaitana bamasenga pamozi na banzelu bonse ba ku Aigupto. Farao anabawuza beve maloto yake, koma panalibe wamene anakwanisa kumumangusulila Falao.9Pamene apo mukulu wa bopelekela chiko anakamba kuli Farao kuti, "Lelo niganizila oa volakwa vanga. 10Farao anakalipa na banchito bake, ndipo anani ponya mundende munyumba ya mukulu wa bolonda, ine na mukulu wa bopika buledi. 11Usiku wamene uja, eve na ine tinalota ali onse kulingana na tantauzo ya maloto yake.12Kwamene kuja tinali pamozi na munyamata wina wachi Heberi, wanchito wa mukulu wa basilikali bolondela mfumu. Tina muuza ndipo anati masulira maloto yatu. Anamasulira ali onse wa pali ise maloto yake. 13Vinachitika monga mwamene anatimangusulira, ndipo vinachiti. Farao ananibweza panchito yanga, koma winangu uja anapachikiwa. "14Pamene apo Farao anatumiza nakumuitana Yosefe. Beve banachita mwa mwachangu naku muchosa mu'ndende muja. Ndipo anagela sisi, nakuchinja vovala, nakungena mwa Farao. 15Farao anakamba na Yosefe kuti, Ine ninalota, koma palibe wamene angani mangusulire maloto yanga; koma namvela va iwe, kuti ukamvela chiloto, ukwanisa kumangusula. 16Yosefe anamuyanka Farao, kuti, "Sichilii mwa mwa ine. Mulungu azayanka Farao mwadaliso."17Farao ankamba na Yosefe kuti, "Mukulota kwanga ine, onani, ninaimilila mumbali mwa mumana wa Nailo. 18Onani, ng'ombe zisanu na zibili zinachoka mumumana wa Nailo, zoina zooneka bwino, ndipo zinadya pakati pa mabango.19Onani, ng'ombe zinangu zinabwela zokonkapo, zofoka, zosaoneka bwino, zoyonda. Ine sininaonepo muziko yonse ya Aigupto zosaoneka bwino monga zija. 20Ng'ombe zoyonda zosaoneka bwino zija zinadya ng'ombe zisanu ndi ziwiri zoyambilila zoina. 21Pamene zinazidya zija, sizinazibike kuti zinadya, chifukwa zinali zosaoneka bwino monga poyamba. Pamene apo ninauka.22Ninayang'ana chiloto changa, onani, ngala zisanu na ziwiri zinamela pa pesi imozi, zozula koma futi zabwino. 23Ndipo ona, ngala zina zisanu na zibili, zofota, zoyonda, zoochewa na na mpepo ya kum'mawa, zinamera pambuyo pabo. 24Ngala zoyonda zija zinamela ngala zisanu ndi ziwiri zabwino zija. Ninauza bamasenga baja, koma panalibe wamene anakwanilisa kunimangusulila ine."25Yosefe anakamba kluli Farao kuti, "Maloto ya Farao ni yolingana. Chamene Mulungu afuna kuchita achilangiza kuli Farao. 26Ng'ombe zisanu na zibili zabwino zija ni zaka zisanu na zibiri, ndipo mitu isanu na ibili yabwino ni zaka zisanu na zibiri. Maloto ayo ni yolingana.27Ng'ombe zikazi zisanu na zibili zoyonda zosakondewa zamene zinamela pambuyo pawo ndiye zaka zisanu ndi zibili, ndipo ngala zisanu na zibiri zoyonda zoochewa na mphepo ya kum'maŵa zizakala zaka zisanu na zibili za njala. 28Ichi ndiye chintu chamene ninakamba kuli Farao. Vamene Mulungu afuna kuchita amu langiza Farao. 29Onani, zaka zisanu na zibili zo chulukila zizabwela mudziko yonse ya Aigupto.30Zaka zisanu na zibili za njala zizafika pambuyo pako, ndipo zochuluka zonse zizaka ibalika m'dziko ya Aigupto, ndipo njala izaononga ziko. 31Vochulukila iva sivzazakumbukiliwa muziko chifukwa cha njala yamene izakonkapo, chifukwa izakankala yoyofya kwambili. 32Chamene chiloto ichi chabwezelewapo kuli Farao nichifukwa chakuti nkani yamene yi yankazikisiwa na Mulungu, ndipo Mulungu azachichita posachedwa.33Manje lekani Farao afunefune muntu wozindikila koma futi wanzeru, amunkazikise eve kunkala olanganila dziko ya Aigupto. 34Lekani Farao aike boyanganila ziko, ndipo atenge imodzi pa magawo yasanu ya zokolola za mu Aigupto muzaka zisanu ndi zibili zokolola vochulukila.35Basonkanise vakudya vonse va zaka vabwino vamene vizabwela ndipo basunge tirigu mumanja ya Farao, inkale yakudya mumi zinda. Bayenera kusunga. 36Chakudya chamene ichi chizankala chakudya chamu ziko mokwanila zaka 7 za njala yamene izankale muziko ya Iguputo. Munjila yamene iyi ziko si izawonongewa na njala."37Magangizo yamene aya yanali yabwino kuli Farao na kuli banthito bake bonse. 38Farao anakamba kuli banchito bake kuti, "Nanga tingapeze muntu wamene ali monga uyu, wamene muli Mzimu wa Mulungu?"39Ndipo Farao anakamba kuli Yosefe kuti, "Popeza kuti Mulungu akuwonesa iwe ivi vonse, palibe winangu wamene niwozindikila nafuti wanzelu monga iwe. 40Iwe uzankala woyanganila nyumba yanga, ndipo monga mwa mawu yako banthu banga bonse bazalamuliwa. Nizankala mkulu kuchila iwe pamupando chabe." 41Farao anakamba kuli Yosefe kuti, "Ona, nakunkazika iwe woyanganira ziko yonse ya Igupto."42Farao anavula mphete yake yozindikizila kumanja kwake nakuivalika pa kwanja ya Yosefe. Anamuvalika futi vovala va nyula yabwino maningi, ndipo anamumanga na cheni ya golide mumukosi mwake. 43Anamuyendesela mu galeta yachibili yamene anali nayo. Amuna banamu pundila pasogolo pake, "Gwadani pansi." Farao anamuika kunkala woyanganila ziko yonse ya Igupto.44Farao anakamba kuli Yosefe kuti, "Ine ndine Farao, ndipo kuchoselako iwe, palibe muntu wamene azatambasula kwanja yake kapena kwendo yake yake mu ziko yonse ya Igupto." 45Farao anaitana Yosefe zina yakuti "Zapenati-Paniya." Anamupasa Asenati, mwana wamukazi wa Potifera wansembe waku Oni, kuti ankale mukazi wake. Yosefe anayenda-yenda mu ziko ya Igupto.46Yosefe anali wa zaka makumi yatatu pamene anaimirira pamaso pa Farao, mfumu ya Igupto. Ndipo Yosefe anachoka pamenso pa Farao, naku yenda yenda mu ziko yonse ya Igupto. 47Muzaka zisanu na zibili mwa vochulukila va mu ziko ija vinapakisa mochilapo.48Anasonkanisa vakudya vonse va zaka zisanu na zibili vamene vinali muziko ya Igupto nakusungila vakudya vamene ivi mumizinda. Eve anaika vakudya mumizinda zamene zinali pafupi naminda zamene zinali mumbali mwake. 49Yosefe anasunga tirigu monga muchenga wa kumanzi, kufikila mpaka anasiya kupendela, chifukwa vinali vinapakisa kwambili mosakwanisika kupendewa.50Yosefe anali na bana bamuna zaka zibili za njala ikalibe kufika, wamene Asenati mwana wamukazi wa Potifera wansembe waku Oni anamubelekela eve. 51Yosefe anapasa zina mwana wake woyamba Manase, chifukwa anakamba kuti, "Mulungu andi ibalisa mavuto yanga yonse na banja yanga yonse ya batate banga." 52Anapasa zina ya mwana wake wachibili Efulemu, chifukwa anakamba kuti, "Mulungu anibalisa mu ziko ya vovutisa vanga."53Zaka zisanu na zibili za vakudya vambili vamene vinali mu ziko ya Igupto inasila. 54Zaka zisanu na zibili za njala zinayamba, monga mwamene anakambila Yosefe. Kunali njala muma ziko yonse, koma muziko yonse ya Igupto munali vakudya.55Pamene ziko yonse ya Igupto inali na njala, banthu banaitana kuli kuli Farao kuti abapase vakudya. Ndipo Farao anakamba kuli ba Igupto bonse kuti, Endani kuli Yosefe mukachite vamene eve akamba. 56Njala inali paliponse paziko yapansi. Yosefe anasegula nkokwe zonse nakugulisa kuli bantu baku Igupto. Njala inakula maningi muziko ya Iguputo. 57Dziko yonse inali kubwela ku Iguputo kugula tirigu kuli Yosefe, chifukwa njala ija inali inafika poipa kwambili paziko yonse yapansi.

42

1Ndipo Yakobo anaona kuti munali vakudya mu Egipito. Anakamba kuli bana bake bamuna. Cifukwa nichani muyang'ana yang'ana? 2Anakamba, onani apa, namvera kuti kuli vakudya mu Egipito, Yendakoni kuti mukati gulile kuti tinkhale namoyo tisamwalile. 3Abale bake ba Yosefe bali banayenda kugula vakudya ku Egipito. 4Koma Yakobo sana tume benjamini, mubale wake wa yosefe, pamozi na bale bale popeza anakamba kuti, "Niyopa kuti voipa vingacitike pali yeve.5Bana ba Israyeli banabwera kugura pakati kabaja banabwera, cifuka njala inali mu ziko ya Kanani. 6Ndipo Yosefe anali bolamulila ziko. Ndipo anali kugulisa kubanthu bonse ba muziko. Abale bake ba Yosefe banafika nakubelama pansi na nkhope zao pansi.7Yosefe anaona babele bake nakubaziba ana zibisi kuli beve naku kamba nabo mo limba anakamba nao, mwacokela kuti? Banakamba kuli tacokela ku Kanani kubwela kugula vo kudya. 8Yosefe anabaziba ba bale bake, koma beve sibana muzibe.9Ndipo Yosefe anakumbuka viloto vamene analota pali beve, anakamba nabeve kuti, ndimeneo oipa mwabwela kuona mbali zamene zilibe citezo mu ziko. 10" Anakamba kuli yeve kuti, awe mbuye wanga. Ba kapolo bako babwla kugula vakudya. 11Ndise bana bamunthu umozi tonse, ndife banthu bazoona, bakapolo bako si banthu oipa.12Anakamaba nao kuti, "Awe, mwabwela kuona malo mulibe citeyezo mu ziko 13Bana kamba kuti, "Ife akapolo bako tili abale tyovu, bana bamunthu umozi muziko ya kenani. Ona, mufuna maningi lelo ali nabatate bathu na mubale wathu umozi salimoyo."14Yosefe anababuza kuti, "Ndiye vamene naku uzani. ndimwe oipa. 15Pali ici muza yesewa na moyo wa falabo, simuzacoka pario, koma cabe ngati mubale wanu mung'onu abwere kuno. 16Tmani umozi mumusiye akatenge mubale wanu. Muzasala mundende, kuti mau yanu yayesewe. Kuona ngati muli cazo ona muli imwe. Ngati siivo, pa moyo wa Falao ndimwe oipa zo ona. 17Anaika bonse mundende musiku yatatu.18Yosefe anakamba nabeve pasiku yacitatu, " Citani ici kuti mukhale namoyo, Popeza niyopa Mulungu. 19Ngati ndimwe bamuna bazo ona, lekani umozi wa abale wanu akhale mundende iyi, koma imwe mu yende, nyamulani vokodya vanjala ya manyumba yanu. 20Bwelesani mufana wanu kuti mau yanu ya simikiziwe ndipo simuza mwalila." Ndio banacita zimezo21Banakambisana wina na muzake, " tinachimwila mubale wathu pakuti tina ona ,kutika kwa moyo wake pamene ana papata kuli ife pamene. anati pempha ndipo sitinamvela, cifukwa caici mavuto yatifikila. cifukwa caici mvuto yatikila. 22Rubene anabayankha, "KOdi sina kuuzane, Osamucimwila munyamata! Koma sina mvele? Manje onani, magazi yake ya funika kwa ife."23Sabanazibe kuti Yosefe anabamwesesa, cifukwa panali omasulila pakati kao. 24Anacoka pali beve ndipo analila. Ana bwelela kuli beve nokamba nao. Anatenga simiyoni nakumu manga menso yao. 25Yosefe ana lamulila ba nchito bake kuti ba zuze machola na vakudya, ndikuika ndalama za munthu alibonse mucola cake, ndi ku bapasa vose vofunika paulendo. zinacitika.26Abale anasenzesa Abulu ao vakudyandi kuyambapo. 27Pamene umozi anasegula saka kuti apase bulu zakudya mu malo yopumulila, ana ona ndalama zake. Taonani zinali muku segula kwa thumba yake. 28Anakamba kuli abale ake, " Ndalama zanga za bwezewamo, zioneni, zili mutumba yanga, "Mitima yanamila anapindamuka monjemela kuyanganana wina na mzake, kukamba kuti, "Nicani ici camene Mulungu acita kuli ise?"29Anayenda kwa Yakobo, tate wo muziko ya Kanani ndi kumu uza vonse vinaba citikila. Banakamba kuti. 30Munthu, mbuye waziko, an anakamba, naise moka lipo nakuti ona monga ndise oipa muziko. 31Takamba kuli yeve, ndife bamuna bazona, sindife boipa. 32Tili abale tyovu, bana ba atate bathu, umozi salimoyo, ndipo ndipo mung'ona lelo ati na batate muziko ya Kenani.33Munthoyo, mwine ziko, anakamba naise, kupitila muli ici nizaziba kuti ndimwe amuna bazo ona. Siyani mubale wanu umozi naine,, tengani vakudya ya njala ku manyumba yanu, ndipo yambaponi. 34Bwelesani mufana wanu maningi kuli ine. Ndipo nizaziba kuti sindimwe oipa, koma kuti ndimwe bamuna bazoona, Pamenepo ndizatulusa mubale wanu, ndipo muzagulisa muziko."35Vinacita pamene anasegula matumba yao kuti, taonani, thumba yalionse munali siliva. Pamene beve naba tate bao banaona mutumba ya siliva, banayopa. 36Yakobo tate wao anakamba kuli beve, "Mwanitengela bana banga, Yosefe salimoyo, Simioni naye ayenda, ndipo mufuna kutenga Benjamini. Vonse ivi vinthu vaninyamukila ine."37Rubene anakamba naba tate bake, kuti, mungapaye bana banga babili ngati siniza bwelesa Benjamini kuli imwe, muakeni mumanja yanga, ndipo ndizaleta kuli imwe futi." 38Yakobo anati, "Mwana wanga mwamuna sazayenda naiwe, popeza mubale wake anafa ndipo anasala yeka. Ngati voipa vizabwela pali yeve munjira yamene muyendamo, ndipo muzaleta imvi zanga ndicisoni kumanda.

43

1Njala inapitila mu malo. 2zinacitika pamene bana diya chakudya zamene bana bwelesa ku Igipito, ba tate babo bana kamba ku libeve, "Endani futi, tigulani vakudya."3Yudu ana bauza eo. " Munthu monenesa anaticejeza ife. 'Simuza ona nkhope yanga kufikila mubale wanu ngati ali naimwe.' 4Ndati muza tituma namubale wathu, tiza enda pasi ndi ku gulalila imwe vakudia. 5Ngati simumutuma eve, citi zaenda pansi, daba uyu munthu anakamba kwaise, simuza ona nkhope yanga pokapo mubale wanu ngatiali naimwe.'"6Israeli anakamba, " Chifukwa chani mwani chitila choipa pa kuniuza nyu munthu kuti mulina mubale wanu wina?" 7Bana kamba, " Uyu munthu anati fusa mopitilila zaise ndi banja lathu, ana kamba,' batate banu balimoyo? Kodi muli na mubale wanu wina?' Tina mu yankha eve kulingana ndi mafuso yake. Sembe tina ziba bwanji zamene aza kamba, 'muletani mubale wanu pasi?'"8Yuda anakamba kwa Israeli, tate wake. " Mutumeni mwana na ife, tiza yamuka ndi ku yenda kuti ti nkhale moyo ndi kuti ti safe, bose ife, naimwe, ndi oso bana bathu. 9Niza khala chosimikizilako kwa eve. Muza Muzanipasa muladu ine. Ngati siniza bwaza kwainu kumuonsa pamaso panu, ndipo lekani niyamule dadaulo muyaya. 10Angati sitina chedwe, choonadi ziko tawi asembe ti baleko kuno kaci bili."11Atate babo Israeli ana kamba kwabeve, ngati cinkhala chocho, maje chitani ici. Tangani zabwino mulomuno mumasaka. Pelekani pasi kwa munthu uyu paso zina baimu ndi uchi. Zonukilisa ndi maya, pistachio nati ndi almondi. 12Tengani dalama mupatikizapo mu manja yanu. Dalama ina bwe zalewa pamene muna segula masaka yanu. Zinyamuleni futi mumaja yanu. Kapena ana sokoneza.13Tenganiso mubale wanu. Nyamuka ndi ku yendaso kwa munthu uyu. 14Lekani mulungu wamphamvu zonse akupaseni imwe chifundo pamaso ya munthu uyu, kwakuti akamulekeleko mubale wanu ndi Benjamani gati nafielewa mwana, na feleawa. 15Anthu anatenga paso izi. Ndi mu manja yao antenhga zopatikiza muyeso wa dalama, pamozi ndi Benjamini. Ana nysmuka ndi kuyenda pasi ku Igipito ndi ana imilila kwa Yosefe.16Pamene Yosefe anaona Benjamini pamozi ano, a na kamba kuli osungila nyumba yake." Ba lete banthu munyumba, paya nyama ndi mpika daba banthu bazadya na ine muzuba. 17Osunga zamunyumba ya Yosefe ana chita monga Yosefe akambila. Anabaleta kunyumba ya Yosefe.18Aba banthu ba nacita manta chifukwa bana pelekewa kunyumba ya yosefe. ba na kamba, " Ni chifukwa cha dalama yamene ina bwezelewa muma saka tawi yoyamba tina ikiliwa mukati. Kuti ati sakile mupata motisuza ife. Kuti ati mage ise ndi kutitenga akapolo ndi a bulu. 19Ana mufikila osunga nyumba ya Yosefe ndi ku kamba naye po lobela munyumba, 20anati bwana, koyamba ku gula vakudia.21Zinazinachika, pamene tina fika pamalo tina pumulila tina segula masaka yanthu, ndipo, onani, aliyese pamene tina segula masaka tathu dalama zake zina mumasaka yenze yo kwanila mupimo. tazi bwelesa mumaja yathu. 22Dalama zina ndiposo tabwelesa mumaja yathu kugula vakudya. Citiziba wamene anti ikila mumasaka yathu." 23Osungu anakamba. " Mutendele ukhale na inu. Musa yope. Mulungu wanu ndi Mulungu watate wanu anakufakila moni dalama zanu musaka yanu. Nina ladila dalama yanu." Osunga ana muleta simiyoni kwa beve.24Osunga anaba peleka amuna kunyumba ya Yosefe. Anaba pasa manzi, nidipo bana suka medo yabo. Ana pasa zakudya mabulu yao. 25Bana kozekela paso za Yosefe kubwela kwake kwamu zuba, daba bana vela kuti zadiyela kuja.26Pamene Yosefe ata bwela kunyumba, ba naleta paso yamene yanali mumanja munyumba ndi kugwanda pansi. 27Anaba fusa zaumoyo wao ndi ku kamba. " Ushe batate banu bali cabe bwino, ba chikulile ba mene muna kambapo? Kondi ali moyo?"28Bana kamba, " Wachito wanu atate batu bali bwino akali namoyo." Ndipo anamu gwadila kumu chitila ulemu. 29Pamene ana nyamula menso yake ana ona Benjamini mu bale wake, mwana waba mao make mwamuna. Ndipo ana kamba, " Uyu dye mungono wake wamene una kambapo kuline?" Ndipo ana kamba. " Leka Mulungu aku chitile chisomo kwa iwe mwana wangu mwamuna."30Yosefe ana tamanga kuchoka muchibinda, daba china mukwila mutima kwabili kamba kabale wake ana sakila malo kwina kolilila ana enda ku chibinda chake ndi kulila. 31Ana samba kumenso kwake ndi ku cho. Ana zi lesa eve, ku kamba kuti, " Ikani va kuya."32Wachito ana konza chakudya cha Yosefe kwa eyeka ndipo abale bake pa beka aku Igoipito ano anadya pabeba chifukwa aku Igipito sanali dyele mukate pamozi nama Hebeli. Kwa ici ni chonyesa ku banthu ba ku Igipito. 33Abale bake ana nkhala pamaso pake Oyamba kubadwa kukonka mwamene bana badwila. Ndipo wa cicepele kuligana na uyamata wake anthu ana dabwisiwa chapamozi. 34Yosefe anatuma mupimo wazakudia pa songolo pake. Koma Benjamini mupimo unali usanu kupabana a bale ake. Anamwa ndipo bana kondwela na eve.

44

1Yosefe analamulila wanchito wa munyumba yake, ku kamba kuti, "Zulisa vakudya m'masaka ya bamjuna, kulingana na vamene bangakwanise kunyamula, ndipo ayike ndalama zake aliyense posengula saka yake. 2Uyike kapu yanga, ija ya siliva, pakamwa posegulila saka ya ija mungono paonse, na ndamala yake ya cakudya."Wanchito wa Yosefe anachita monga mwamene ana mu uzila.3Kuseni seni, ndipo bamuna aba banabauza bayende banatenga na ba buru bao. 4Pamene banacoka m'mzinda koma Sbana fike patali maningi. Yosefe anakamba ku wa nchito wake, "Nyamuka, konka ba muna, ndipo ukubapitilila, ubauze kuti, 'Nchifukwa chani mwa bwezela choipa pa cha bwino? 5Kodi iyi si kapu yamene abwana banga bama mmwela, na kapu yamene ba ma ombezelako? Ichi chintu chamene mwa chita, mwa chita choipa."6Wanchito anavapitilila na ku bauza mau Mau. 7Bamu uza, "Nichani ba bwana banga bakamba mau monga aya? Ichi chintu chisankale na banchito ku chita cha mutundu uyu.8Ona ndalama tinapeaza mosegulila masaka yatu, "yamene tinabweesa futi kuli kuchokeku Canani. Manke tingabe bwanji mu nyumba ya ba bwana bako siliva na golide? 9Ngati aliwonse pali ba nchito bako apezeka nayo, mutekeni amwalile, na ife tizankala ba kapolo ba mfumu wanga." 10Wanchito anakamba, Apa manje lekani chinkale monga mau yanu. Wamene azapezeka na kapu azankala kapolo wanga, koma imwe benangu m'mzakala mube mulandu."11Kuchoka apo munthu onse anayendesa nakubwelesa nakusitizila saka yake pansi, ndipo aliyense anasegula saka yake. 12Wanchito ana sakila. Anayambila mukulu pali onse nakusilizila na mung'ono pa bonse, ndipo kapu inapezeka musaka ya Benjamini. 13Apo bana ng'amba vovala vao. Munthu aliyense anaika katundu yake pali buru nakubwelela ku muzinda.14Yudah na abale nawo, "Nichani chamene mwachita ici? Simuziba kuti munthu monga ine nimachita zo-ombeza?" 15Yosefe anakamba, "Tingakambe chani kwa bwana wanga? Tizakamba chani? Kodi tizazilungamitse bwanji? Mulungu aipeza chimo ya mbadwa mubanchito banu. Onani, ndife bakapolo ba bwana wanga, ise namwane kapu yapezeka mumanja mwake."16Yudah anakamba, "Tingakambe chani kwa bwana wanga? Tizakamba chani? Kodi tingazilungamitse bwanji? Muungu aipeza chimo ya mbadwa mubanchito banu. Ona, ndife bakapolo ba bwana wanga, Ise nawamene kapu yopezeka mumanja mwake. 17Yosefe anakamba, "Chinkale patali naine cha mutundu uyu kuti ninga chichite, Munthu wamene enze apezeka na kape m'kwanja mwake, uyu munthu anzankala kapolo wanga, koma kwa imwe benangu mutende mwa mtendele kwa atate anu."18Kuchoka apo Yudah ababwela pafupi naye nakukamba, "'Mfumu yanga, anapapata lekani wanchito wanu akambeko ku munthu yanu, ndipo mu saleke ukali wanu kuti uyonekele pali kapolo wanu. Chifukwa imwe ni chimodzi modzi na Falao. 19Bwana wanga inafunsa banchito bake, kakamba," uli na atate alo m'bale.20Tinakamba kwa mfumu, "Tilinayo atate, ba chikulile na mwana wamu ukote wayo muny'ono. Koma mbale wake anafa, ndipo eve aka ndiye anasalapo ya ba mayi bake, na batate bake bomukonda. 21Ndipo munakamba kuli ba chinto banu,, mu bweleseni kiuli ine ni muone! 22Kuchoka apo tinakamba kuli ba bwana banga, 'Munyamata sangasiye ba tate bake. Ngati abasiya batate bake bazamwalila.23Ndipo munakamba kuli banchito banu, koma chabe mu bwele na m'bela wanu wamung'ono simuzakaona pa menso panga futi. 24Ndipo chanabwela kuti pamene tinaenda kuli banchito banu atate, tinoba ma ya abwana banga. 25Atate batu banakamba yendani futi mukatigulile vakudia. 26Ndipo tinakamba, "Sitinga yendeko khoma ngati,mubale wathu wamung'ono alina ife, Tiza endo, chifukwa chakuti sitizakwanisa kuona pamenso pa uja munthu. Koma chabe nufana wathu ankale naife.'27Akapolo wanu atate anga analamba kwa ife kuti'Mu ziba mukazi wanga anabala kuli ine bana ba muna babili. 28Umodzi ananichoka ine ndipo ninakamba kuti, "Zoona anamujuba juba mu ziduswa duswa, 'kuchika apo sinina muonepo futi. 29Apa manje mukatenga uyu kuli ine, na choipa chikumu bwelela, muzabwesa pansi imvi zanga na chikwinyilito ku manda.30Apa, manaje, nikafika ku wanchito wanu atate, tilibe mung'ono wathu, chifukwa moyo wake wamangila pali muyo wa munyamata uyu. 31Chizachitika akaona kuti tilibe munyamata ife azamwalila. Ba kapolo banu bazabwelasa imvi za kapolo wamu atate mu chisoni paka kumanda. 32Chifukwa kapolo wanu ine ninakala chisimikizo ca munyamata kuli batate nokamba kuti, ngati sinza bwela nayeve, kuli imwe, apo nizankala wa milandi kwa atate banga tawi zonse.33Kufika apa manje, napapata lekeni wa nchito wanu ankele mumalo mwa munyamata monga kapolo wa abwana banga,, nakuleka munyamata ayende nabale bako. 34Ningabwelele bwanji kuli atate ngati munyamata sazankala naise? Niyopa kuyenda kuona voipa vinga bwele pali atate banga.

45

1Ndipo Yosefe anakangiwa kuzilesa kuti asalile pa menso pa banchito bake. Anakamba mopunda, " Bonse banisiye," panalibe wanchito aliyense pamene Yosefe anaziulula kuli ba bale bake. 2Analila na chongo, ndipo Aigupto bananvela, na nyumba ya Farao inanvela. 3Yosefe anati kuli ba bale bake, " Ine ndine Yosefe. Ushe batate banga bakali moyo?" Koma ba bale bake sibanamuyake, chifukwa banali namata pamenso pake.4Ndipo Yosefe anati uli ba bale bake, "bwelani pafupi naine, napapata." Banabwela pafupi. Anati ndine Yosefe mubale wanu, wamene muna gulisa ku Igupto. 5Osazibalisa na kuzikalipila mweka kuti munaningulisa ine kuno, chifukwa Mulungu ananituma ine pasongolo panu nikapulumuse umoyo. 6Pa zaka zibili izi kwa nkhala njala mumalo ndipo kulinso zaka 5 pamene sikuzankhala kulima kapena kukolola.7Mulungu ananituma pasongolo panu kuti akakusungeni monga onkhala pa ziko yapansi ndipo kukusungani naumoyo ndi kumasulidwa kukulu. 8Sopano, sindimwe munanituma kuno koma Mulungu, ananifaka kunkhala tate wake wa Farao, bwana wa nyumba yake yonse, ndi olamulila malo yonse ya Igupto.9Yendesani ndipo muyende kuli batate banga nakubauza kuti, ichi ndiye chamene mwana wanu Yosefe akamba, " Mulungu anipanga ine kunkhala bwana mu Igupto monse. Bwelani kwa ine, ndipo musa chedwe. 10Muzankhala mu malo ya Goseni, ndipo muzankhala pafupi naine, imwe na bana banu na bazukulu banu, na nkosa na ng'ombe, na vonse vamene muli navo. 11Nizakupasani imwe kuja, chifukwa kuli zaka 5 zanjala, kuti musabwele kuumpawi, imwe nyumba yanu, na vonse muli navo."12Onani, menso yanu yaona, na menso ya mubale wanga Benjamini, kuti ndi kamwa kanga kamene kakamba kwa imwe. 13Mukabauze batate banga pa ulemele wanga wonse mu Igupto na vonse vamene mwaona. Muyayendesa na kubwelesa batate banga kuno."14Anakumbatila mu'bale wake Benjamini mukosi na kulila, ndi Benjamini analilila mumu kosi wake. 15Anapyompyona ba bale bake bonse na kulila kuchoka apo ba bake bana kamba naye.16Nkhani ya ichi chintu inauzidwa kunyumba kwa Farao: " Ba baleba Yosefe babwela chinakondwelesa Farao na ba nchito bake kwambili. 17Farao anati Yosefe, " Uza ba bale bako chitani ichi: Longani pa nyuma zanu ndipo muyende ku ziko ya Kanani. 18Tengani batate banu na banja ndipo mubwele kwa ine. Nizakupasani vabwino va mu malo la Igupto, ndipo muzadya zonona zamu ziko.'19Manje mwauzidwa, 'Chitani ichi, tengani kochikali ku choka mu ziko la Igupto kwa bana banu na ba kazi banu. Tengani batate banu na kubwela. 20Musaganiza pa vintu vamene muli navo, chifukwa vabwino va ziko ya Igupto nivanu.'"21Bana ba Israeli bana chita zamene izo. Yosefe anabapasa vi kochikali, monga mwamene anakambila Farao. Ndipo anabapasa vakudya va munjila. 22Kuli ali bonse anapasa vovala vinangu koma kuli Benjamini anamupasa siliva ili fili handilendi na vovala vili fivi. 23Kuli ba tate bake anatuma ivi: Ba bulu bali teni wozula ndi vintu vabwino vaku Igupto; ndi mabulu bakazi bali teni, banatenga tilingu, buledi ndi vinangu vofunika va batate bake vamunjila.24Ndipo anabatuma ba bale bake kuti ba yambepo. Anabauza kuti, " Muone kuti musayambane munjila." 25Bana choka mu Igupto nakubwela ku ziko la Kanani, kwa Yakobo tate wabo. 26Banamu uza kuti, " Yosefe akali moyo, ndipo wamene alamulila mu ziko yonse ya Igupto." Mutima wake unadabwa,, chifukwa sana kulupilile vamene bana mu uza.27Bana mu uza mau yonse ya Yosefe yamene ana bauza. Pamene yakobo anaona ma kochikali yamene Yosefe anatuma kumutengelapo, muzimu wa Yakobo tate wawo unauka. 28Israeli anati, " Zakwana. Yosefe mwana wanga akali moyo. Nizayenda mukumuona nikalibe kufa.

46

1Isryeli anapanga ulendo navonse ve enze nazo noyenda ku Beresheba. Kuja anapasa sembe kwa Mulungu wa Tate bake Isaki. 2Mulungu anakamba kuli Israeli muchiloto usiku, anakamba, " Yakobo, Yakobo." Ndipo anati, "Nilipano." 3Anati, "ndine Mulungu, Mulugu wabatate bako. Usayope kuyenda ku Igipito, ndipo kuya nizakupanga ziko yayi kulu. 4Nizayenda naiwe ku igipito, ndipo nizakuleta nafuti ndipo Yosefe azavala menso yako na manja yake."5Yakobo ananyamuka kuchokella ku beresheba. Bana bamuna ba Israeli banamupeleka Yakobo tate wawo, bana bawo, akazi awo, muchikochikala chamene Farao anatuma kumunya mula. 6Banatenga ngo'ombe zawo na zintu zomwe zebana pindula mu malo ya Kenani. Banabwela ku Igipito, Yakobo nabo badwa mumbuyo mwake. 7Analeta ku Igipito bana bake bamuna naba zukhulu, bana bake bakazi, na ba zukhulu bake bakazi, nabo badwa kumbuyo kwake.8Aya nimazina yabana ba muna ba Israeli bana bwela ku Igipito: Yakobo nabobadwa kumbuyo kwake, Rubeni, woyambilila kuli Yakobo; 9Bana bamuna ba Rubeni, Hanoki, Palu, Hezroni, na Karmi; 10Bana bamuna ba Simeoni, Yamwueli Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari, na Sauli, mwana mwamuna wamukazi waku Kanaani; 11bana bamuna ba Levi, Gerisoni, Kohati na Merai.12Bana bamuna ba Yuda banali Eri, Onani, Sela, Perezi na Zera, (koma Eri na Onani anafa muziko la Kenaani). Bana bamuna ba Perezi panali Hezroni na Hamuli. 13bana banuna ba Issakara banali Tola, Puva, lobi,na Simromi; 14Bana bamuna ba Zebuloni banali Seredi, Eloni, na Yaledi. 15Aba banali bana bamuna ba leya be anabalila Yakobo mu padaramu, namwana mukazi Dina. Bana bake bamuna naba kazi banali sate fili.16Bana bamuna ba Gadi banali zifioni, Hagi, Suni ezboni, Eri, Arodi, na Areli. 17Bana bamuna ba Aseri banali Yimna, Yisiva, na Beriya na Sera we anali mulongo wawo. Bana bamuna ba beriya anali Hederi na Makeli. 18Aba ndiye benze ba Zelipa, omwe Labani enze anapasa mwana wake mukazi Leya, aba bana be ana balila Yakobo benzeli Sikisitini.19Bana bamuna bamuka wa Yakobo Rakele banali Yosefe na Benjameni. 20Mu Igipito manese na Efelemu bana badwa kwa Yosefe kwamukazi Asenati, mwana wa Potifa wansembe waku Oni. 21Bana bamuna ba Benjamini banali bela, beka, Ashibile, Gela, Naamani, Ehi, Loshi, Muppimu, Huppini na Adi. 22Aba ndiye benenze bana ba Rakele be anabalila Yakobo fotini pamuzi.23Mwana wa Dani enze Hushimu. 24Bana bamuna ba nafutali banali Jazile, Guni Yeza Shilemu. 25Aba ndiye bana bamuna ba Yakobo kuli biliha, wamene labani atapasa mwana wake mukazi Rakele seveni pamozi.26Onse aba banayenda ku Igipito na Yakobo, banabadwila kumbuyo kwake, kusapendela ko bakazi babana ba Yakobo, banali sikisite sikisi pamozi. 27Nabana bamuna babili ba Yosefe bana badwila kwa eve mu Igipito, bantu bamu banja lake be bana yenda ku Igipito banali seventi pamozi.28Yakobo anatuma Yuda kuli Yosefe kuti amulangise njila yaku Gosheni, ndipo anabwela kumalo ya Gosheni. 29Yosefe anakonza ngolo yake noyenda muku kumanya Israyeli atate bake kumalo ya Gosheni. Ana bawona, no kumbatila mu mukosi, ndipo analila pamukosi, pantawi yayitali. 30Israyeli anauza Yosefe, "anje lekani nife, pakuti nawona pamenso pako, kuti ukachili moyo."31Yosefe anawuza abale ake naba munyumba yaba tate bake, "Nizayenda no uza Farao, kuti, 'Abale anga na ba munyumba yaba tate banga, bamene banali kunkala mumuzinda wa Kenani ba bwela kwayine. 32Bamuna aba nibosunga mbelele, bankala bo sunga nyama. Baleta mbelele zawo, mbuzi, na zonse zamene bali nazo.'33Izafika ntawu pamene Farao azakwitanani no mifunsani kuti, nchito yanu nichani?' 34Koma mukakambe, 'Banchito banu basunga nyama kuchokela ku bunyamata bwatu kufika manje, ise namakol atu. 'Chitani ivi chakuti munkale mu Malo ya Gosheni, osunga mbelele aliwonse niwonyasa kuli baku Igipito."

47

1Ndipo Yosefe anangena ndipo anauza Farao, Atate banga na bale bannga, na nyama zabo na zosunga zabo ndi zonse zamene balinazo, bafika kuchokela kumalo ya Kanani. Ona, bali kumalo ya Gosheni." 2Anatenga abale bake bamuna bali feivi ndipo anabazibisa kuli Farao.3Farao anakamba kwa abale bake, " Mugwila nchito bwanji?" Bana kamba kwa Farao, " Banchito banu ama onera mbelele, za makolo bantu." 4Ndipo banakamba kuli Farao futi, " Ise tabwela monga alendo muno mumalo. Kulibe zodwesela nyama zabachito bananu, chifukwa kuli njala yopitilila mumalo ya Kenani. Sopano manje, napapata lolani banchito banu kukhale mumalo ya Gosheni."5Ndipo Farao anakamba kuli Yosefe, kukamba kutii, " Atate bako na babale bako babwela kuli iwe. 6Malo ya Igipito yali pamaso yanu. Khazikisa ba tate bako ndi babale bako malo kudela ya bwino, malo ya Gosheni ngati uziba bamuna boyenera pakati pao, ubafake otsogolela zobeta."7Ndipo Yosefe analota Yakobo atate bake na baonesa kuli Farao. Yakobo anadalisa Farao. 8Farao anauza Yakobo kuti, " Kodi wamkhala kwanthawi itali bwanji ?" 9Yakobo anuza Farao, " zaka zakuyenda kwanga ni 130 zaka zamoyo wanga ni zing'ono ndipo zobaba. Sizambili ngati zamakolo banga banafa." 10Ndipo Yakobo anadalisa Farao na kuchoka pameso yake.11Ndipo Yosefe anakhazikisa atate bake ndi abale bake. Anabapasa malo mudziko ya Igipito, malo opambana, mumdzinda wa Rameses, monga mwamene Farao anakambila. 12Yosefe anapasa zakudya atatee bake, abale bake na onse bamunyumba mwabatate bake, kulingana ndi namba ya onse osungidwa.13Manje kunalibe zakudya mu ziko monse: cifukwa njala yenze yopilila. Ziko ya Igipito, na Kanani anaonongeka cifukwa ca mvula osankhalako. 14Yosefe anaunjika ndalama zonse zinali mu Igipito namu Kanani, mogulisa zakidya kubantu. Ndipo Yosefe anapeleka ndalama ku malo ya amfumu Falao.15Pamene ndalama zonse za mu Igipito na Kanani zinasebenzewa, bantu bonse ba m Igipito banayenda kuli Yosefe kukamba kkuti, "tipase vokudya! Tizafela cni pamenso yako pakuti ndalama zathu zasila." 16Yosefe anakamba kuti, "Ngati ngati ndalama zanu zasila, letani nyama zanu ndipo nizakupasani cakuddya mocinjana na nyama zanu. 17Ndipo anabwelesa zosunga zao kuli Yosefe. Yosefe anabapasa cakudy mocinjana na mabulu, nyama siyana-siyana, zosunga zao na madonki. Anabadyesa mukate mocinjana na zosunga zao caka cija.18Pamene chaka china sila, bana bwela kwa ioe chaka chokokhapo ndipo bakamba kwa iye, " Siti zakubisani bwana kuti ndalama zonse zantu ndipo ngombe zonse ndi za bwana wanga kulibe zasalako mumaso bwana, kuchoselako matupi yatu napamene tikhala. 19Nichifukwa chani tizafela pameso panu, ise pamozi na dziko yatu? Tiguleni, ndipo ise na dziko tizikhala banchito ba Farao. Tipaseni chakudya kuti tinkale namoyo kuti tisafe, na malo asankhala alibe kantu."20Ndipo Yosefe anagulila malo yonse ya Igipito Farao. Pakuti muntu aliyese wamu Igipito anagulisa munda wake, chifukwa kunali njala yopitilila. Munjila iyi, malo anakhala ya Farao. 21Kuli bantu, banakhala akapolo bake kuchokela kumalile ena ya Igipito kufika kumalile kosiliza. 22Nimalo aba sombe chabe yamene Yosefe sanagule, chifukwa basembe anabapasa zobatandizila. Banadya zobangabila kuchokela kwa Farao zamene anabapasa. Mwaiche sanagulise malo yao.23Ndipo Yosefe anakamba kubantu kuti, " Onani, nagulila Farao imwe na malo yanu lelo. manje izi ni mbeu zanu, zamene muzashanga mu malo. 24Pa kukolola, mufinika kupasa Farao zachisanu ndipo mbali fo zizankhala zanu, chifukwa mbeu za mumunda ndi za chakudya niza munyumba mwanu nabana banu."25Bana kamba kuti, " Wapulumusa umoyo wantu. Tipeze chisomo mumenso yanu. Tizakhala ba chito ba Farao." 26Ndipo Yosefe ana iyika lamulo yokokhewa mudziko la igipito kufikila lelo, kuti chachisanu chimozi ndi cha Farao. Malo chabe yabasembe niyamene Siyanakhale ya Farao.27Ndipo Israeli anakhala mu Igipito, mu malo ya Gosheni. Batu bake bankhala ndi zintau kumene kuja. Bana paka kwabili. 28Yakobo anakala mu Igipito zaka seventini, ndipo zaka za umoyo wa Yakobo zinali handredi foti seveni.29Pamene nthawi yakufa kwa Israeli inafika pafupi, anaitana mwana wake Yosefe ndipo anati kuli yeve, " Manje napeza chisomo mwako, ika manja yako pansi pachibelo, ndipo unilagize kukulupilika ndi chilungamo. Napapata osanishika mu Igipito. 30Nikagona ndi makolo achimuna banga, uninyamule kunichosa mu igipito naku nishika mu manda yamakolo banga bakudala." Yosefe anati, " Nizachita mwamene mwakambila." 31Israeli anakamba, " Lapa kuli ine," Yosefe analapa kuli yeve. Ndipo Israeli ananguwesa mutu wake pongona pake.

48

1Ina chitika pa mbofu paizi zintu, umozi anakamba kuli Yosefe, " Ona, atate bako ba dwala." Ndipo anatenga bana bake babili amuna , Manase na Efuraimu. 2Pamene Yakobo ana uziwa, " Ona , mwana wako Yosefe afika kukuona," Israeli ana sakila mphamvu naku nkhala pa bedi.3Yakobo anti yosefe, " Mulungu wa mphamvu anaonekela kuli ine pamalo ya Luz mu Kanaani. Anani dalisa. 4Ana kamba kuli ine, ' Onani, nizaku panga muntu ochuluka, naku kuchulukisa. Niza panga iwe muli maiko Yambili. Niza pasa malo aya kuli bo badwa mu mbuyo mwako na zintu zo yendelela.5Manje bana bako babili, anabadwa kuli iwe mu Egipito nikalibe ku bwela kuli iwe mu Egipito, ni banga. Efuraimu na Manase ni banga, monga mwamene Rubeni na Simeoni ni banga. 6Bana bamene uza nkhale nabo kucho aba baza nkhala bako; baza nkhala bo pendewa ma zina pamozi nabo badiwa nabo potengo zo lobelela. 7Koma pa ine, nika bwela ku choka ku paddani, kulila kwanga Rakele anafa mu malo ya kanaani mu njila, pamene panali mutunda kufika ku Epafra. Ninamu shika kuja pa njila yantu yaku Epafra" (Iyo ni Betelehemu).8Pamene Israeli anaina mwana wa Yosefe, anati, " niba ndani aba ?" 9Yosefe anati kuli atate ake; " nibana banga, bamene Mulungu anani pasa kuno." Israel anati, " balete kuli ine, kuti ningaba dalise." 10Tsopano menso ya Israeli yanali ku lepela chifukwa chau nkhalamba waka, ndipo sanali ku ona. Ndipo Yosefe anaba lefa pafupi nabo, anabafyofyonta nakuba kumbata.11Israeli anati kuli Yosefe, " Sininali oyemebekezale kuona pamenso panu futi, koma Mulungu ani vomekeza kuona bana bako." 12Yosefe anaba chosa mukati ya mendo ya Israeli, analangana pansi mozichepesa. 13Yose anaba tenga bonse babili, Efuraimu ku zanja la manja kufupi na kwanja ya mazele ya Israeli, na Manase ku kwanja ya mazele kufupi na kwanja ya manja ya Israeli, nakuba leta pafupi na eve.14Israeli anatambika zanja lake la manja naku ika pali Efuraimu pa muntu, wamene anali mufana, na kwanja ya mazele pa mutu wa Manase. Anapapambanisa manja yake, chifukwa Manase anali oyamba ku badwa. 15Israeli anadalisa Yosefe, naku kamba ati, " Mulungu wamene atate banga Abrahamu na Isaki, Mulungu wamene anisunga kufika pano, 16mungeli wamene anani cingiliza ku vofipi vonse, lekani aba anayamata aba. Lekani zina yanga itanidwe pali beve, na zina yaba tate banga Abrahamu na Isaki. Lekani bakule bochuluka pa ziko la pansi."17Pamene Yosefe anaona kuti atate bake bana ika zanja la manja pa mutu wa Efereimu sichinamu kondwelese. Ana tenga kwanja yaba tate bake nakuyi vendeza ku choka pa mutu wa Efureimu kuyi ika pa mutu wa Manase. 18Yosefe anakamba kuli atate bake, " Simwamene, atate banga; uyu ndiye wachiyambi. Ikani zanja la manja pa mutu pake."19Atate bake bana kana no yanka, " Niziba, mwana wanga, niziba. Naye aza nkhala bantu, azankala opambana. Koma uyu mufana azankhala opambanapo kuchila eve, nabo badwa bake bazankala maiko yambili." 20Israeli anabadalisa ija siku na mau aya. " Bantu ba Israeli baza kamba ma daliso pama zina yanu kuti, 'Ukani MUlungu akupanga monga Efureimu na Manase.'" Muli iyi njila, Israeli ana ika Efureimu pasongolo pa Manase.21Israeli anati kuli Yosefe, " Ona, nili pa fupi na kufa, koma Mulungu azankala naiwe, azaku bweza kumalo yaba tate bako. 22Kuli iwe, monga muntu ali pamwamba paba bale bake, nakupaso chiguli chamene nina tenga kuli ma Amorites na lupanga na uta yanga."

49

1Pamene apo Yakobo anaitana bana bake bamuna, naku kamba kuti, "Mukumane pamozi, niku uzeni vizakutchitkilani kusogolo kwanu. 2Zi'ikeni pamozi na kumvelela, imwe bana bamuna ba Yakobo. Nvelelani Isilayeli, tate wanu.3Rubeni, ndiwe mwana wanga oyamba, mpamvu yanga, na kuyamba kwa mpamvu yanga, ulemu opambana na mpamvu yopambana. 4Osauzika monga manzi oyenda na mpamvu suzapambana, chifukwa unakwela pa bedi ya batate bako. Pamene unaipisa; unakwela pa bedi panga.5Simeoni na Levi nipachi bululu. Vida va chongo ndiye mapanga yabo. 6O moyo wanga, usangenemo muchiweruzo chabo; osangenemo mu musonkanonyao, pakuti mutima wanga uli na ulemu ngako pali icho. Pakuti mu ukali wao anapaya bantu, mukukondwela banalemalika ng'ombe.7Kutembelelamkukalipankwao pakuti wenze oyofya-na ukali wao, pakuti kwenze koipa. Nizabagaba muli Yajobo na kubamwaza mu Isilayeli.8Yuda, azibululu bako bazakutamnda. Kwanja kwako kuzakankala pamukosi pa badani bako. Bana ba batate bako bamuna bakugwadila pemenso pako iwe.9Yuda ni mwana wa nkalamu. Mwana wanga mwamuna, wayenda pamwamba kuchoka ku gonjesewa bako. Anabelama pasni, anabendelela monga nkalamu, monga nkalamu ikai, Nindani angayese kumuyimya?10Nkoli yau mfumu siyizakachoka pali Yuda, kapena cholamulila pakati pa mendo yake, mpaka shilo akabwele. Maziko yazamunvelela.11Kumangila bulu wake ku mpesa, na mwan wa bulu wake pa mpesa osankiwa, A'washa vovala vake mu moba, na mukanjo wake mu magazi ya mpesa. 12Mu menso mwake bazakankala wofipa mong ni niyu, na meno yake kuyela monga ni mukaka.13Zebuloni azankala kumbali kwa nyanja. Azankala pofkila pa ma bwato, na malile yake yazafika ku Sidoni.14Isaka ni bulu wolimba kugona pakati pa mogona mbelele. 15Aona alo bwino opumulilamo na malo okondwelesa. Azagwesa pewa yake kukatundu na kunkala kapolo wa nchtio.16Dani azakaweluza bantu bake monga wa mitundu ya Isilayeli. 17Dani azakanla njoka mbali mwa mseu, nkoka yoipa munjila yamene iluma ku mendo kwa bulu, kuti okwelapo amagwela kumbuyo. 18Nizaymbekeza chipilumuso chanu, Yehova.19Gadi-vigabenga vizamumenya, koma azabamenya ku mendo kwao. 20Vokudya va Asha vizakankala vabwino, ndipo azapeleka vonona ku ufumu. 21Nafitali ni ka nyama komasuka, apa mau abwino.22Yosefe ni msambo obala, Mutengo obala mbali mwa manzi, yamene misambo yake misambo yake ikwela pamwmba pa chiumba. 23Badani bake bazamumenya na kumulasa na kumuvuta.24Koma cholasila chake chizankala cha mpamvu, na manja yake yazalimbikisiwa chifukwa cha zina mbusa, mwala wa Isilayeli.25Mulungu wa batate bako azakutandiza na Mulungu wa mpamvu azakudalisa na madaliso ya kumwamba, madaliso yoyendelela pasni pa manzi, na madaliso ya maziba na mumala,26Madaliso ya batate bako nibopambana kuchila madaliso ya kudala olo vintu yokumbukila va kumalupil yang'ono ya kudala. Lekani yankale pamutu pa Yosefe, nangu pa kolona ya pa mutu pa mwana mwamuna wa mfumu ya abululu bake.27Benjamini ndiye galu yamsanga yanjala, mumawa azadya na muzulo."28Aya ndiye mitundu twelofun ya Isyalei. Ichi ndiye chamene anakamba batate bao pamene anabadalisa. Alyense anamudalisa na madaliso yake. 29Pamene anabalangiza benve na kukamba kuli benve, "Nili pafupi kuyenda kuli bantu banga. Mukanishike na makolo bana mankwema chili mu munda ya Efroni mu Hititi, 30Munkwema ili mu munda wa makipela, ili pafupi na mare mu malo ya Kanani, malo yamene Abrahamu anagula kwa Efroni Hititi kuti ankale manda.31Kuja banashika Isaki na Rabeka mukazi wake; ndipo kuja ninshika Leya. 32Munda na nkwema yamene vilimo vinguliwa ku bantu baku Heti." 33Pamene Yakobo pamene anasiliza malandizo aya ku bana bake, anadonsela mendo yake pa bedi, ma kupema kosilizila, nakuyenda kuli bantu bake.

50

1Ndipo Yosefe ana lemesedwa kwa kuti anagwa pa nkhope yake ba tate. Ndipo anamulilila eve, ndipo ana mu fyofyonta. 2Yosefe ana lamilila a dotolo ba chito bake ku konza tupi ua tate bake. Sopano a dotlo ana konza Isreali. 3Bana tenga masiku fote, pakuti inanli ntawi yakwanila kwakuti amukonze. Ba ku Egipito analila masiku okwanila seventi.4Pamene masiku olila ana sile, Yosefe anakamba ku nyumba ya Falao, anakamba, "ngati manje napeza mwai mu meso yako, napapata nikambileni kuli Falao kukamba kuti. 5Ba tate banani Lepisa kukamba, "Ona nili pa fupi kufa. Ne shikeni mu manda mwamene niza zikumbila ine neka muziko ya Kenaani. Ukudiye muzanishika ine." Manje lekani ine niyende nika shike ba tate banga. Ndiponso nizabwelela. 6Falao anayanka, "Enda ka shike ba tate bako ba, banani lapisa.7Yosefe ana yenda ku ka shika atate bake. Ba nchoti bonse ba Falao bana yenda na eve bakulu bakulu bonse muyumba yake. Bonse bamu ziko la Egipito, 8na nyumba yonse ya yosefe ndi abale bake bonse, ndipo ba munyumba yabatate bake. Koma bana babo, Vobeta kabo, ndi ngobe zao zina sala mu malo ya Gosheni. 9Golo ndi aka valo zina yenda beve cinali cigulu cacikulu cabanthu.10Pamene bana bwela ku malo yopepeptela ya Atadi kumbali ina ya Yolodani, ana lilila kwakululu movesa chifundo. Uku Yosefe ana panga ma siku asanu ndi ziwili kulila ba tate bake. 11Ndipo onkhala mu ziko amu Kenaani, anaona kulila pasi ya Atadi, bana kamba, "Ici ni cisoni cacikulu kwa banthu ba ku Egipito." Chifukwa cake malo a itaniwa Abeli Mizraimu kupitilila Yodani.12Sopano bana bake ba Yakobo ana chita zamine ana ba lamulila beve. 13Bana bake bamuna anamunyamula eve ku malo ya Kenaani ndi kumshika muci kwema mumunda wa machipela pafupi na Mamri . Abrahamu ana gula mukwema ndi munda malo yo shikilako. Anagula kwa Efuraimu ma Hititaiti. 14Pambuyo yo shika ba tate bake. Yosefe ana bwelelela ku Egipito. Eve, pamozi na abale bake ndipo bonse ana mupelekeza eve mu shika ba tate bake.15Ndipo abale ba Yosefe pamene bana one kuti ba tate babo bafa, bana kamba manja ngati Yosefe akati nkalila naukali ise ndipo nakufuna kytibweza ise zoipa zose tina chita kwa eve? 16Sopano bana lamulila ku pezekapo kwa Yosefe. kukamba kuti, "Ba tate banapasa malamulo bakelebe kufa kukamba, 17Uzeni yosefe izi," napapa ba kukukila abale bako machimmoyabo ndi zolakwa zawo pamene bana chita zoipa kuli iwe." Manje napapata ba kukukile ba tumiki ba Mulungu ba batate bako." Yosefe analila pamene bana kamba na beve.18Ba bale bake futi ana yenda ndi kugona choyangana pasi pamaso pake. Bana kamba, "One, ndise ba nchito bako." 19Koma Yosefe ana bayanka beve, "Musayope. kodi nilimumalo ya Mulungu? 20Kwa iwe, munanifunila zoipa ine. Koma ana ni funila zabwino. Ku pulumusa miyo zaanthu ambili. Monga muona lelo. 21Manje musayope nizakupasane vintu iwe na bana bangona anabalikisa beve munila yambwinno akukamba zabwino ku mitima yabo.22Yosefe ana nkhala mu Egiito, pamozi na banja yaba tate bake. Ana nkhala zaka 110. 23Yosefe ana ona bana ba Ephraimu na bana bana badwa mumubada wachitatu, ndiposo ana ona bana ba Makira aba ba Muna ba Manase, ba mane ba Fakiwa pama nkhonkhola ya Yosefe.24Yosefe ana kamba kwa abale bake, "Nalipa fupi kufa, koma Mulungu zoona azabwela kwa imwe na kuku sogolelani kuku chosa mu malo yamene ana lapa ku pasa Abramu kwa Isaki ndi Yakobo. 25Ndipo Yosefe ana panga bana ba muna ba Israeli kulapila pangano, "Mulungu chazoona aza bwela kwa inu. Patiwe ija mufunika muka yamule ma boza yanga kuyta chosa muno." 26Sopano Yosefe anafa, na zaka 110 bana koza tupi yake ndi po ana ika mu bokosi ku Egipito.