1 Aya ndiye ma zina ya bana ba Izilayeli bamene banabwela mu Igupto pamozi na Yakobo, ali onse na banja yake: 2 Lubeni, Simiyoni, Levi, na Yuda, 3 Isaka, Zebuluni, na Benjamini, 4 Dani, Nafutali, Gad, na Asha. 5 Bonse bantu pamozi bamene banali mubadwe wa Yakobo banali 70 kubapenda. Yosefe eve anali ku Igupto kudala. 6 Yosefe, babale bake bonse, na uja mubadwe wonse unamwalila. 7 Bana ba Izilayeli banali bana nkala na bana bambili, nafuti banankala bakali; ziko yonse banali bana zula. 8 Manje kunayamba kulamulila mfumu inangu mu Igupto, yamene si inali kuziba kali konse pali Yosefe. 9 Anauza bantu bake kuti, "Onani, ba bantu ba Izilayeli bapaka maningi nafuti bali na mpavu kutichila ise. 10 Bwelani, tiyeni tiba bele nzelu, ndaba bazapitiliza ku paka, futi ngati kwankala nkondo, baza nkala pamozi na badani batu, nakuyamba kumenyana naise, nakutaba muziko." 11 Mwai ichi baika boba langanila pa ntchito kuti bakazibavuta muku bapasa ntchito zokosa. Ba Izilayeli bana manga mizinda za Falao: Pitomu na Lamesesi. 12 Koma mukulingana na mwamene banali kubavutisila kuli ba Igupto, ndiye mwamene ba Izilayeli banali kuchulukila nakuzula mu ziko yonse. Mwamene umu ba Igupto banayamba kuyopa bantu ba mutundu wa Izilayeli. 13 Ba Igupto bana yamba kulengesa kuti bana ba Izilayeli kuti bayambe kusebenza na mpoavu. 14 Bana panga myoyo zabo kunkala zobaba chifukwa cha kulimba kwa ntchito za malibwe na daka, na mu zintchito zonse zamu minda. Ntchito zamene banali kufunika kutchita zibnali kufuna kusebenza mwa na mpavu. 15 Chokonkapo mfumu waku Igupto anakamba na botandizila azimai ponkala na bana; umozi zina yake inali Shipula, na wina Puwa. 16 Anabauza kuti, "Pamene imwe mutandizila bazimai bachi Hebeli paku nkala na bana, mukaziyanganisisa pamene bankala na mwana. Ngati mwana ni mwamuna, imwe mufunika kumupaya; koma ngati nimukazi, nikumusiya." 17 Koma baja bazimai banali bantu boyopa Mulungu sibanachite mwamene mfumu ya Igupto inabauzila; koma, banaba lekelela bana bamuna na moyo. 18 Mfumu yaku Igupto inaitana baja bazimai botandizila ponkala nabana naku bauza kuti, "Kansi nichani chamene mwachitila ichi, kubalekelela bana bamuna kunkala namoyo?" 19 Bazimai banamuyanka Falao kuti, "Bazimai bachi Hebeli sibali monga bazimai bachi Igupto. Bali na mpavu bama nkala na mwana ise pamene tikalibe nakuyamba kuba tandizila." 20 Mulungu anabachingilizila aba bazimai. Bantu banapaka nafuti banankala na mpavu. 21 Chifukwa chakuti bazimai aba banali boyopa Mulungu, anabapasa na banja yabo. 22 Falao anauza bantu bake bonse kuti, "Muyenela kuponya mwana mwamuna ali onse wamene abadwa mu nyanja, koma mwana mukazi ali onse muyenela kumusiya na moyo."
1 Manje mwamuna wamutundu wachi Levi anakwatila mukazi wachi Levi. 2 Mukazi anakala namimba naku bala mwana mwamuna. Pamene anaona kuti anali mwana mwaumoyo wabwino, anamubisa myezi itatu. 3 Koma pamene analeka kumu bisa kumubisa, anatenga basiketi ya papiras, naku mata na bituman na ulimbo. Manje anamufakomo mwana mukati nakufaka pama tete mumanzi. 4 Mulongo waka anaimilila patali kuti aone vizachitika kuli enve. 5 Mwana mukazi wa Farao anabwela kusamba kumanzi apmene bosebenza bake benze kuyenda mumbali mwa manzi, anaona basiketi pakati pa tete naku tuma banchtio bake baitenge. 6 Pamene anaisegula, anaona mwana. Onani, mwana anali kulila. anankal nachifundo pali enve naku kamba, "Uyu zo'ona nimwana waumozi wama Heberi." 7 Koma mulongo waka mwana anuza mwana wa Farao, "kodi niyende kusakila mukazi wachi Heeri wamene azayamba kusunga mwaa uyu?" 8 Mwana mukzai wa Farao abaumza iye, "Yenda." naku kamusikana kangono kanayenda nakutenga bamai bake ba mwana. 9 Mwana mukazi wa Farao anauza bamai ba mwan, Tenga mwana uyu uninyosheleko, ine nizakulipila." Pamene mukazi anamutenga naku munyosha. 10 Pamene mwana anakulako, bana muleta kuli mwana mukazi wa Farao, anso anankala mwana wake. Amamupasa zina ya Mose naku kamba, "chifukwa ninamu chosa mu manzi." 11 Pamene Mose anakula, anayenda kunja kubantu bake anaona kusebenza maingi kwao. Anaona mu Iguputo anmenya bantu bake. 12 Analangana uku kumbali na uku kumbal, koma pamene anaona kuti kunalibe aliyense, Anapaya mu Iguputo naku bisa tupi yake mu michenga. 13 Anachoka siku yokankapo, na, onani, bamuna babili ba chi Heberi benze kumenyana. Anauza umzi wamne enze olakwa, "Nichani chamene umenyala muzako?" 14 Koma mwamuna anamu'uza, "nindani akupanga mukulu na otiweluza pali ise? Nanga uganiza kunipaya ine monga mwamene unaoaila mu Iguotuo?" Pamene apo Mose anankala na manta anakamba, " vamene nina chichita zo'ona vazibika kuli benangu." 15 Koma pamene Farao anavela pali ichi, anayesa kupaya Mose. Koma anamutaba Farao naku nkala ku ziko yaku Midani. Kuja anakankala pansi pa mbali ya chisime. 16 Manje wansembe waku Midani anali nabana bakazi bali seveni. Bana bwela, kutapa manzi, nakmunfaka muvotapila manza kuti bamwese nyama zosunga. 17 Bobetela bana bwela naku yesa kuba pisha, koma Mose anayenda naku batandiza. Pamene apo anaba mwesela nyama zosunga. 18 Pamene basikanaka banayenda kuli Reueli atate bao, anakamba, "nichani mwabwela kunyunmba musanga lelo?" 19 Bana kamba, " waku Igiuputo atipulumusa ise kuli mbusa. Ati tapilana manzi naku mwesa nyama zosunga." 20 Anabauza bana baka bakazi. "Nanga alikuti? nichani mwamusiya mwamuna? Muitaneni kuti adye chakudya naise." 21 Mose anavomela kunkala na mwamuna, wamne futi anamupasa Zipora mwana wake mukazi kuti akwatile. 22 Anabala mwana mwamuna, na Mose anamupasa zina Geshomu, yachilendo." 23 Pamene kunapita ntau, mfumu yaku Iguputo inafa. Ba Isilayeli banalila chifukwa chanchito yaukapolo. Bana lila kufuna tandizo, naku pempa kwao kunayenda kuli Mulungu chifukwa chaukapolo. 24 Pamene Mulungu ananvela kulila kwao, Mulungu anakumbukila pangano yamene inali pakati pa enve na Abrahamu, Na Isaki, na Yakobo. 25 Mulungu anabaona bana ba Isilayeli, naku ziba kuvutika kwabo.
1 Manje Mose anali akali kubusa vobeta va Yotero mu pongozi wake, wansembe wa Midiyan. Mose anasogolela vobeta ku mbali. yakutali ya chipululu anafika pa Horebu, lupili Mulugnu. 2 Kwamene uko Mungelo wa Yehova anaonekela kuli enve muchi mbili-mbili chamulilo musanga. Mose anayangana, ndipo onani, musanga unali kubuka, koma chisamba sichenze kunyeka. 3 Mose anakamba, "nizapatukila kumambali kuti ni one ichinchintu chodabwisa, chifukwa ni chani chisamba sichinyeka." 4 Pamene Yehova anaona kuti anapatulila pa mbali kuyangana, Mulungu anamuitana kuchokela muchisamba na kukamba, "Mose, Mose." Mose anakamba kuti, "nili pano." 5 Mulungu anakamba kuti, "osabwela pafupi! Vula nsapato zako ku mapzai yako, Chifukwa pamalo apa pamene waimilia ni popatulika kuli ine." 6 Anaikapo, "Ndine Mulungu wa batate bako, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, na Mulungu wa Yakobo." Pamene apo Mose anazivininkila ku menso, chifukwa anayopa Mulungu kuyangana Mulungu. 7 Yehova anakamba, "Naona zo'ona kuvutika kwa bantu banga bali mu Iguputo, namvela kulila kwao chifukwa chabantu bobasebenzesa, chifukwa zakutika kwao. 8 Naseluka pasni kuba masula kuchokela ku mpavu zama Iguputi na kubaleta mumalo ya bwino, malo yakulu, kuziko ya mukaka na uchi ku malo yaku kanani, Ahiti, Aamol, Aperz, Aperizi, Ahivi na Ayebusi. 9 Manje kulila kwa bana banga kwafika kuli ine, ndiponso, naona kutiiliziwa kwawelesawa nama Iguputo. 10 Manje apa, Nizakutuma kuli Farao kuti ubwelese bantu banga, ba Isilayeli, kubachosa mu Iguputo." 11 Koma anakamba kuli Mulungu, "Ndine ndani ine, kuti niyende kuli Farao naku bwelesa bana ba Isilayeli kubachosa mu Iguputo?" 12 Mulungu anayanka, nizamkala naiwe nditu. Ihci ndiye chamene uzabilako kuti ine nakutuma. vikachosa bantu mu Iguputo, uzaniyamika in pa lupili ino." 13 Mose anakamba kuli Mulungu, "Pamene nizayenda kuli ma Isilayeli na kubauza. Mulungu wa makapolo anituma kuli imwe,' ndipo baka kamba kuli ine, zina yake nindani? nichani chamene nizakamba? 14 Mulungu anakamba kuli Mose, "INE NDINE MWAMENE NDILILI." Mulungu anakamba, ufunuka kukamba kuli ba Isilayeli, INE NDINE anituma kuli iwe. 15 Mulungu anakambanso kuli Mose ufunika kukamba ku Isilayeli, 'Yehova, Mulungu wamakolo yanu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo, anituma kuli iiwe. Iyi ndiye zina kumbukiliwa na mibadwo yonse. 16 Yenda ulongane bakuluvbonse bamu Isilayeli pamozi. Kamba nabo kuti, Yehova, Mulungu wa makolo, , Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, aonekela kwaine naku kamba, "nankala ninyang'ana ndipo naona vamene vachitika kuli imwwe mu Iguputo. 17 Nalonjeza kukuchosani mumalo ya botitiliza mu Iguputo kukupelekani kumalo yaku kanakni, Ahiti, Aamori, Aperizi, Ahivi na Ayebusi, muziko yoyendamo mukaka na uchi." 18 Bazakumvelelani imwe. Iwe na bakulu bamu Iguputo, ndipo mufunika ku mu'uza, .Yehova, Mulungu wa Aheberi, akumana naise. Manje tiyende uledno wa masiku yatatu muchipululu, kuti tikapeleke nsembe kuli Yehova Mulungu watu. 19 Koma niziba mfumu yaku Iguptuo sizakuleka ni kuti muyende, koma chabe kukakamiza kwanja yake. 20 Nizatambasula kwanja yanga na kumenya ma Iguputo navo dabwisana vonse pake azakulekani. 21 Nizapasa aba bantu mwai pamenso yama Iguputo, chakuti mukachoka , simuzayenda mulibe chili chonse. 22 Muzimai alionse azafunsa siliva na golide vokomesela vovalika kuchoka kuli bantu bake bamu Iguptuo na bazimai bankala mu manyumba yapafupi. muzavi ika pali bana banu bamuna na bakazi, munjila yiy muza ononga ma Iguputo."
1 Mose anayanka, nanga ngati sibazani kulupilila olo kunimvelela koma benve kukamba, Yehova sana onekela kuli iwe?" 2 Yehova anakamba kuli enve, nichani chili mu manja mwako? Mose anakamba," nkoli." 3 Yehova anakamba kuti, "Iponye pansi." Mose anaiponya pansi, naku sanduka njoka. Mose anatabila kumbuyo. 4 Yehova anakamba kuli Mose Kuti, "Tambusula kwanja uyigwile kumuchila." Chakuti anatambulusa nakuyigwila njoka. Inankala futi nkoli mumanja mwake. 5 "Ivi vili chakuti ba kulupilile kuti Yehova, Mulungu wa makolo yao, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Mulungu wa Yakobo aonekela kuli iwe." 6 Yehova anakamba kuli enve, "Manje apa faka kwanja yako mu chovala chako, "Ndipo Mose anaika kwanja kwake mu chovala futi." Pamene anaichosa, onani, kwanja kwake kunali namakate yoyela monga matalala. 7 Yehova ankamba kuti, "faka kwanja yako mu chovala futi, "Ndipo Mose anaika kwanja yake mu chovala futi." Pamene anaichosa, anaona kuti ya nkala bwino futi, monga tup yonse. 8 Yehova anakamba kuti, "ngati sibana kulupilile iwe-ngati sibanaku fakeko nzelu kuchi zindikilo choyamba champamvu zanga olo ku kulupilila pamene apo bazakulupilila chachibili. 9 Ngati sibazakulupilila ngakale ivi vizindikilo vibili va mpamvu, olo kumvela kuli iwe, pamene apo tenga manzi ya mumana nakutatila pa doti yoyuma. ,anzi yamene uzatenga yaza sanduka magazi pa doti yoyuma. 10 Pamene Mose anakamba kuli Yehova kuti, "Ambuye" nikalibe kukambapo bwino, kapena kudala olo kapena mwamene muna kambilapo nayenve kapolo wanu ndine wachibwibwi na lulimi yanga niyolem." 11 Yehova anakamba kuli enve, nindani anapanga kamwa yamuntu? Nindani anapanga mu tu kuti asakambe olo asakame olo ayangane olo aleke kuyangana? kodi sindine, Yehova? 12 Manje yenda, nizankala na kamwa kako na ku kupunzisa vamene ufunika kukamba." 13 Koma Mose anakamba, "Ambuye, napapata tumani alionse wamene mu ngafune kutuma." 14 Koma Yehova anakalipa na Mose. Anakamba, "Nanga Aroni, mubale wako, mu Levi? Niziba kutianga kambe bwino. Komanso, abwela kukumana naiwe, ndipo akaona iwe, aza kondwela mumutima mwake. 15 Uzakamba nayenve nakufakamo mau yokama mukamwa mwake. Ine nizankala na kamwa kako na kamwa kake, ndipo niza kuonesani mose vochita. 16 Ndiye azaku kambilako kuli bantu. Azankala kamwa kako. Ndipo uzankala kuli enve monga ine, Mulungu. 17 Uzatenga mumanja mwako nkoli iyi. Nayenve uzachita zizindikilo." 18 Pamene apo Mose anabwelela kuli mupongozi wake Yetelo naku kamba naye. "Nilekeni niyende nibwelele kuli babululu banga bali ku Iguputo nione ngati bakali namoyo." Yetelo anakamba kuli kuti, "Yenda mu mutendele." 19 Yehova anakmba kuli MOse mu Mdiyani, "Yenda, bwelela ku Iguputo, chifukwa bonse bantu benze kufuna kutenga moyo wake banafa." 20 Mose anatenga bakzi bake na bana bake na kubaika pa bulu. bwelela kuziko la Iguptuo, ndipo ananyamula nkoli ya Mulungu mumanja mwake. 21 Yehova anakamba kuli MOse kuti, "Pamene uzabwelela ku Iguputo, ona kuti uchite pamenso ya Farao vonse vodabwisa vamene baika mu mpamvu zako. KOma nizza kosesa mutima wake, ndipo sazaleka bantu bayende. 22 Ufunika kukamba kuli Farao, 'Ivi ndiye vamene Yehova akamba: Isilayeli ni mwana wanga mwamuna, mwana wanga oyamba. 23 ndipo nikamba kuli iwe, "Leka mwana wanga mwamuna ayende, chakuti akaniyamike." Koma chifukwa wakana kumuleka kuti ayende, ni zapaya mwana wako, mwana oyamba wako mwamuna." 24 Manje munjila, pamene banaimilila usiku, Yehova anakumana Mose nakuyesa kumupaya. 25 Koma Zipola anatenga mupeni wamwala na kujuba nyama ya mwana wake mwamuna, naku igwilisa kumendo yake. Nakukamba, "Zo'ona iwe ndiwe mukwati wanga wamagazi kuli ine." 26 Pamene apo anamulekelela eka. Anakamba, ndimwe mukwati wanga wama magazi chifukwa chamudulidwe. 27 Yeho a anakmba kuli Aroni, "Yenda muchipululu uka kumane na MOse." Aroni anayenda, anakumana naye palupili ya Mulungu, na kumu pyopyonta. 28 Mose anauza Aro i mau yonse ya Yehova yamene anamutuma kukamba pali zizindikilo za mpamvu zamene anamula mulila enve kuchita. 29 Pamene apo Mose na Aroni banayenda nakuika pamozi bakulu bonse bamu Isilayeli. 30 Aroni anakamba mauyonse yamene Yehova anakmba kuli MOse. Anaoselanso zizindikilo va mpamvu ya Yehova mu muenso ya bantu. Bantu bana kulupilila. 31 Pamene bana mvela kuti Yehova ayangana ba Isilayeli na kuona kutitiliza kwao, pamene benve banagwada pansi naku muyamika.
1 Pamene ivi vintu vibachita, Mose na Aroni bana yenda kuli Farao nakukamba kuti, "Ivi ndiye vamene Yehova, Mulungu wa Isilayeli, akamba: 'Leka bantu banga bayende, kuti bakachite pwando muchipululu." 2 Farao anakamba, "Yehova nindani? Nichani chamene nizabanvelela kuti niba leka bayende? Sinimuziba Yehova: Sinizaleka Isilayeli kuyenda 3 Banakamba, " Mulungu waba Hebeli atikumanya ise. Lekani tiyende pa ulendo wama masiku yatatu muchipululu na kupelka nsembe kuli Yehova mulungu kuti asabwelese pali ise chilango olo mukondo." 4 Koma mufumu ya Igiputo inakamba kulibe, "MOse na Aroni, nichaninmuchos bantu panchito yao? bwelelani pa nchito yanu." 5 Anakamba futi, "Manje mulibantu bambili mumalo yatu, anso ulekengesa kuti baleke nchtio yao." 6 Pasiku yamene ija, Farao anapeleka lamulo kuli mabwana bakulu nabo onelela nchito ku bantu. Anakamba, 7 "Kusiyana nakudala, Osabapase bantu uzu paku panga ma buloko. Baleke bayenda kuzitengela mauzu paboka. 8 Koma, mupitilze kubauza kuti bazipanga nambala yama buloko kulingana na yamene banali kupanga kudala. Osavomela chilichonse chachepa apo, chifukwa bali naulesi. Nichifukwa chake bali kuitana na kukamba, Tileke tiyemde anso tikapeleke nsembe kuli Mulungu watu.' 9 Ikilaponi nchito yao amuna kuti bapitiliza kukamba na osaikilako nzelu ku mau yao yabo." 10 Pamene apo bakulu ba nchito na bamuna boyanganila bantu bana yenda naku bauza bantu. Banakamba, "Ivi ndiye vamene Farao akamba: Sinazakupasani imwe mauzu. 11 Imwe mweka muzafunika kuyenda naku zitengela kwamene munga ipeze, koma nhito yanu siyiza chepesewa." 12 Pamene apo bantu bana salangana pa malo yonse ya Iguputo ku'unjika mauzu. 13 Bakulu ba nchito banapitiliza kubalimbisa naku kambakuti, "Silizani nchito yanu, monga mwamene munali kusilizila pamene mauzu yanali kupasiwa kuli imwe." 14 Bakulu ba nchito ba Farao bana menya boyanganila ba nchito bama Isilayeli, bamene baja banafakiwa kuyanganila ba nchito. Bakulu ba nchito banapitiliza ku bafunsa, "Nichani simuna pange yonse ma buloko yamene mufunikila kupanga, siku yapita na lelo, monga mwamene mwenze kuchitila kudala?" 15 Manje boyanganila nchtio bana bwela kuli Farao na kulila kuli enve. Banakamba kuti, "nichani chamene mutisungila monga ivi ba ncbito banu? 16 Kulibe mauzu yapasiwa kuli ba nchito banu, koma bakali kuti uza ise, 'pangani ma buloko!' Ise, ba nchito banu, bamenyewa manje, koma nivuto ya bantu bako." 17 Koma Farao akamba kuti, "Muli na ulesi! Ukamba kuti! Tivomeleseni kupeleka nsembe kuli Yehova.' 18 Manje apa bwelelani kusebenza. kulibe mauzu yazapasiwa kuli imwe, koma mufunika kuipanga nambala yama buloko yamene ija." 19 Oyanganila nchito baku isilayeli anona kuti banali mubvuto pamene banauziwa, "Simufunika kuchepesa nambala yama buloko pasilu." 20 Banakumana Mose na Aroni, bamene banali kuimilila panja panyumba ya mfumu, pamene banali kuchoka kuli Farao. 21 Banakamba kuli Mose na Aroni, " Lekani Yehova akuone iwe naku kulanga iwe, chifukwa walengesa ise kuoneka olakwa mumenso ya Farao na banchito bake. Iwe waika mukondo mumanja mwao kuti bati paye ise." 22 Mose anabwelela kuli Yehova naku kamba kuti, "Ambuye, nichani mwanitumila ine kuno? 23 Kuchokela pamene nin bwelela kuli Farao kukamba kuli enve muzina yanu, apangisa mabvuto kuli bantu aba, anso simunaleke bantu banu kumasuka."
1 Yehova ankamba kuli Mose kuti, "Maje iwe uzaona vamene niza chita kuli Farao. Uzaona ichi, azabasiya kuti bayende chifukwa chakwanja yanga ya mpamvu, azabapisha benve mu ziko yake. 2 Mulungu anakamba na Mose naku mu'uza enve kuti, "Ine ndine Yehova. 3 Nina onekela kuli Abrahamu, kuli Isaki, na kuli Yakobo ngati Mulungu wa mpamvu zonse, koma na zina yanga, Yehova, sinenze ozibika kuli benve. 4 Ninapanga chipangano na benve, kuti abapase benve ziko mu kanani, muziko mwamene bana nkala monga sibene, mu ziko yamene banali kuzungulukamo. 5 Koma, nanvela kulila kwama isilayelu bamene a'Iguputo bapanga ukapolo, nakukubmukila chipangano changa. 6 Chifukwa chake, uzani ma Isilayeli, 'Ine ndine Yehova. Niza kakuchosani mu kapolo kuli bamu Igupto, naku mumasulani imwe ku mpamvu ya chiweruzo. 7 Niza kamutengani imwe ngati bantu banga, ine nizakankala Mulungu wanu. Muzakazibika kuti ine nfine Yehova Mulungu wanu, wamene ana kuchosani imwe mu ukapolo wa Iguputo. 8 Niza kubwezani imwe ku ziko yamene nina lumbila kuti nizapasa Abrahamu, na kuli Isaki, na kuli Yakobo. Niza kupasni imwe kunkala chintu chanu. Ine ndine Yehova." 9 Pamene Mose anauza ivi kuli ma Isilayeli, sibana munvelele chifukwa chokumusiwa na ukali wa ukapolo. 10 Pamene apo Yehova anakmba kuli Mose, kuti, 11 "Yenda uka Farao, mfumu wa Iguputo, kuti aleke bantu bamu Isilayeli kuchoka pa malo yake." 12 Mose ankamba kuli Yehova, "Ngati ma Isilayeli sibana ninvelele ine, nichani Farao azani nvelela ine, kupeza sinikamba bwino?" 13 Yehova anakamba kuli Mose na Aroni. Anaba pasa lamulo ya Isilayeli na Farao, mfumu ya Iguputo, kuchosa ma Isilayeli mu ziko ya Iguputo. 14 Aba ndiye benze basogoleli bama nyumba yaba tate babo: Bana bamuna ba Rubeni, oyamba kubadwa kuli Isilayeli, benze Hanoki,Pallu, Hezron, na Karmi. Banali makolo ba banja ya Rubeni. 15 Bana bamuna ba Simion banali Jemueli, Jamini, Ohad, Jakin, Zohar, na Shaul-mwana mwamuna wa mukazi wamu kanani. Banali makolo ba banja ya Simion. 16 Aya ndiye ma zina yanali yo lembewaya bana bamuna ba Levi, pamozi na mibadwo yabo. Banali Gershon, Kohath, na Merari. levi anankala mpaka zaka 137. 17 Bana bamuna ba Gershoni banali Libni na Shimei, muma banja yabo. 18 Bana bamuna ba Kohath banali Amram, Izar, Hebroni na Uzziel. Kohath anankala zaka 133. 19 Bana bamuna ba Meriri banali Mahli na Mushi. Aba banankala makolo ya banja yama Levi, pamozi namubadwo yabo. 20 Amram anakwatila Jochebed, mulongosi wa batate bake. Anamubalila Aroni an Mose. Amram anankala zaka 137 nakufa. 21 Bana bamuna Izar banali Kora, Nefegi, na Zichri. 22 Bana bamuna ba Uzziel banali Mishael, Elzafani, na Sithri. 23 Aroni anakwatila Elisheba, mwana mukazi wa Amminadab, mulongozi wa Nahshon. Enve anamubalila Nadab na Abihu, Eleazar na Ithamar. 24 Bana bamuna ba Kora banali Assir, Elkana, na Abiasaf. Bana nkala makolo ya banja ya Korahites. 25 Eleazar, mwana mwamuna wa Aroni, anakwatila umozi mwana mukazi wa Putiel. Nakumubalila Phinehas. Aba banali basogoleli bama nyumba na ma banja yawo. 26 Aba bamuna ba bili banali Aroni na Mose bamene Yehova anauza kuti, "Chosani ma Isilayeli mu ziko ya Iguputo nama gulu ya amuna ba nkondo." 27 Aroni na Mose bankamba na Farao, mfumu wa Iguputo, vomelesa kuchosa ba Isilayeli ku Iguputo. Aba banali ba mozi Mose na Aroni. 28 29 30 Pamene Yehova anakamba na Mose mu ziko ya Iguputo, Enve anakmba kuli enve, "Ine ndine Yehova. Kamba kuli Farao, mfumu wa Iguputo, vonse vamene niza ku'uza." koma Mose anakamba kuli Yehova, "Siniziba kukamba bwino, nichani chamene Farao zani nvelela ine?"
1 Jehova anakamba kuli Mose kuti, "Ona, Nakupanga monga mulungu kuli Farao. Aroni mubale wako azankala mneneri wako. 2 Iwe uzakamba vonse vamene nizaku lamulila, Aroni mubale wako ndiye azakamba na Faaro kuti aba lake bana ba Isireli ba chokemo mu malo yake. 3 Koma niza mulimbisa mutima Farao, kuchoka apo niza langiza vounesa mpamvu zanga, zambiri zodabwisa, mu malo ya Egpto. 4 Koma Farao saza munvererani, kuchoka apo nizaika kwanja yanga pa Egpto naku chosa ma gulu yanga ya amuna omenyana, bantu banga, bantu baku Isireli, choka ku a,lo ya Egpto na vilango. 5 Egpto izaziba ati ndine Yehova nikafikiza kwanja yanga pa malo ya Egpto naku chossa ma Isireli pakati pao. 6 Mose na Aroni anachita sochabe; banachita monga mwamene Yehova analamulila. 7 Mose anali na zaka ayite, na Aroni anali na zaka ayite fili pamene bana kamba na Farao. 8 Yehova anakamba kuli Mose na kuli Aroni, 9 Pamene Farao azakamba kulli imwe `chitankoni cho dabwisana,' kuchoka apo uza kamba kuli Aroni, `Tenga nkoli yako uyi ponye pansi pal Farao, kuti isanduke njoka.` 10 Mose na Aroni banayendakuli Farao, naku chita vamene Yehova analamulila. Aroni anaponya pali Farao na nchito bake, naku bwela ku nkala njoka. 11 Pamene apo Farao anayitana ba nzeru na ng'anga zake. banachita monga majik yabo. 12 Mwamuna aliyense anaponya nkoli yake, chokonkapo nkoli inankala njoka. kom nkoli ay Aroni inamela njoka zabo. 13 Mutima wa Farao wenze unakosesewa anso sananvele, monga Yehova anakambila. 14 Yehova anakamba kuli Mose kuti, "Mutima wa Farao ni olimba, kuchoka apo anakana kubaleka bantu bayende. 15 Mukayende kuli Farao kuseni pamene azayenda ku manzi. muka imilile ku mbali kwa manzi muka mukumane, ndipo uka nyamule mumanja mwako nkloi yamene yenze ina sanduka njoka. 16 Mu'uze kuti, ` Yehova, Mulungu wa Ahebri, anitumma kuli iwe kukamba kuti, "Leka bantu banga bayende, chakuti baka niymike muchipulu. Namanje sumunanvele." 17 Yehova akamba kuti: chifukwa chaivi muzaziba kuti ndine Yehova. niza pana manzi yaka mumana ka Nile na nkoli ya kwanja yanga, kuchoka apo ka mumana kazankala magazi. 18 Nsomba zili muka mumana zizafa, naka mumana kazanunka. Ma Egpto sibaza nkwansia kumwa manzi yamu ka mumana. 19 kuchoka apo Yehova anauza Mose, "mu.uze Aroni," Tenga nkoli utambulule kwanja yako pa manzi ya Egpto, na pali kamumana, kamumana, ponkala manzi, na mosungila nsomba, kuti manzi yabo yankala magazi. chitanso kuti munkale magazi pa malo ya Egpto, namu vu gubu va planga na myala. 20 Mose na Aroni banachita vamene anabalamulila munlungu. Aroni ananyamula nkoli naku menya pa manzi yamu ka mumana, pamenso ya Farao naba nchito bake. Mumana onse unasanduka magazi. 21 Nsomba inali muka mumana infa naka mumana kanayamba kununka. Ma Egpto sibana kwanise kumwa manzi yamu musanje na magazi yenzeli pa malo ya Egpto. 22 Koma ba majik baku Egpto banachita monga benve na majik yabo. chokonkapo mutima wa Farao unalimba, nakukana nvelella Mose na Aroni, monga Yehova anakambila viza chitikila. 23 Kuchoka apo Farao anakoneka noyenda munyumba mwaka. sanafakeko na nzelu. 24 Ma Egpto bonse banakumba kumbali kwa kamumuna kuti bapeze manzi yokumwa, koma sibana kwanise kumwa manzi yamu kamunmana. 25 Masiku yali seveni yanapita kuchokela pamene anapandila pa manzi
1 Pamene apo Yehova anakamba kuli Moe kuti, "Yenda kuli Farao naku mu'uza enve, 'Yehova akamba ivi: "Leka bantu banga bayende kuti bakani pempeze in. 2 Uka kana kubaleka kuyenda, niza vutisa ziko yako yonse nama chule. 3 Na kamumana kaza zul nama chule. Viza bwela pamwamba naku zula na kuyenda mu nyumba yako, kuchipinda kwako, napa bedi pako. Viza yenda muma nyumba ya banchito bako. Viza yenda kubantu bako, mumauveni yako, na namo sakani zila mwako. 4 Na machule yaza kumenya iwe, bantu bako, na banchito bako bonse."" 5 Yehova anakamba kuli Mose, "Mu'uze Aroni, "Tambulula kwanja yako na nkoli pali nyanja, tumumana, mwamene manzi nkalila, na ku bwelesa ma chule mu malo ya Igupito." 6 Aroni ana anatambulula kwanja yake pamanzi ya Iguputo, naku ma chule yabwela pamwamba pa naku zula pa malo ya Iguputi. 7 Koma ba majiki bao bana bana chita mwamene banachitila na majiki yabo; bana bwelesa ma chule mumalo ya Iguputo. 8 Pamene Farao anaitana Mose na Aroni naku bauza, "Pmempelani kuli Yehova kuti enve achose ma chule pali ine na bantu banga. Ndiye pamene zibaleka bantu bayende kuti benve ba peleke nsembe kuli enve." 9 Mose anakamba kuli Farao, "Unga nkale namupata oniuza ine pamene ninga kupempelela iwe, banchito bako, na bantu bako, kuti ma chule bachosewe kuli iwe na muma nyumba na kunkala chabe mu mumana." 10 Farao anati, "mailo." Mose anati, "chinkale mwamene wa kambila, kuti uzibe iwe ati kulibe wina monga Yehova, Mulungu watu. 11 Ma chule bazachoka kuli iwe, muma nyumba yako, banchito bako, na bantu bako. bazankala chabe mu mumana." 12 Mose na Aroni banachoka pali Farao. Pamene apo Mose analila kuli Yehova pali vima chule vamene anabwelesa kuli Farao. 13 Yehova anachita monga Mose ana pempa: Ma chule banafela muma nyumba, makoti, na muminda. 14 Bantu banakolonganika pamozi, malo yaja yanali kununka. 15 Koma Pamene Farao anaona kuti amasuka, enve analimbisa mutima ndipo sana mvelele Mose na Aroni, monga mwamene Yehova anaba vamene azachita. 16 Yehova anakamba kuli Mose kuti, "Mu'uze Aroni, 'Tambulula kwanja yako naku menya kalukungu kali pansi , kuti inkale natu doyo pa malo ya Iguputo." 17 Bana chita sochabe. Ndiye pamene Aroni anatambulula kwanja yake na nkoli pansi pa doti. Tudoyo tona bwela pa bantu na vi nyama. Yonse kalukungu inankala natu doyo pa malo yonse ya Iguputo. 18 Ba majik bana yesa majik yabo kuti ba pange tudoyo, koma ina kanga. Chakuti kunali tudoyo mu bantu na nama. 19 Pamene ba majik banakamba kuli Farao, "Ichi nichi kumo cha Mulungu." Koma Farao anakosesa mutima wake, na kukana kuba mvelela. Chinali mwamene Yehova anakamba Farao azachita. 20 Yehova anakamba kuli Mose, "Nyamukani kuseni maningi na kuyenda kuimilila kuntangu ya Farao pamene akalibe kuyenda ku mumana. Mumu uze enve, "Yehova akamba ivi: "Basiye bantu banga bayende kuti bakani pempelele ine. 21 Ngati isuza baleka bantu banga kuyenda, ine inza tuma gulu yaba inzi kuli iwe, banchito vbao, na bantu bako, na muma nyumba yabo. Manyumba yaba Iguputo yazankala nama gulu ya inzi, ndipo na pansi pamene badyaka paza nkala ba inzi bambili. 22 Koma siku ija ine mwamene niza tengela malo ya Gosheni, mosiyanako mumalo mwamene bantu banga bankala, chakuti gulu yaba inzi si'iza nkalako. Ivi vizachtika kuti ndine Yehova ali mumalo yanu. 23 Ine niza faka chosiyanisa pali bantu banga na bantu bako. Cholangiza mpavu zanga chiza oneka mailo. 24 Yehova ana chita so chabe, na gulu ikulu yama inzi ina bwela munyumba ya Farao na munyumba yaba nchito bake. Yonse malo ya Iguputo, malo yana onogeka chifukwa cha gulu yama inzi. 25 Farao anaitana Mose na Aroni na kukamba kuti, "Yenda, Peleka nsembe mumalo yatu." 26 Mose anakamba kuti, "Sichabwino ise kuchita ivo, chifukwa nsembe zamene tima peleka kuli Yehova Mulungu watu nizo nyansa kuli ba Iguputo. Ngati tapeleka nsembe bwino bwino mumenso yabo yo nyansa kuli ba Iguputo, sibaza titema myala? 27 Iyai, nimasiku yatatu yo yenda muchipululu yamene tifunika kupanga, kuti tipeleke nsembe kuli Yehova Mulungu watu, mwamene anatilamulila. 28 Farao anakamba, "ine niza kusiyani muyende ndipo mupeleke nsembe kuli Yehova Mulungu wanu muchipululu. Ngati simuza yenda kutali. nipempeleleni ine." 29 Mose anakmba, "nika choka chabe pano, niza ma inzi yaku kuli Yehova kuti ma gulu yama inzi yaku siye, Farao, Banchito bako na bantu mailo. Koma usa chitenso boza paku salekelela bantu batu kupeleka nsembe kuli Yehova." 30 Mose ana choka pali Farao na kuyenda kupempela kuli Yehova. 31 Yehova anachita vamene Mose anapempela; na kuchosa magulu yaba inzi kuli Farao, banchito bake, pa bantu bake. kulibe nangu kamozi kanasala. 32 Koma pantawi iyi Farao ana limbisa mutima wake. ndipo sana baleke bantu kuyenda.
1 Pamene Yehova anakamba kuli Mose, "Yenda kuli Farao na kumu uza, 'Yehova, Mulungu wa Aheberi, akamba ivi: "Leka bantu banga bayende kuti bakani pempeze." 2 Koma ngati iwe wakana kubaleka bayende, ngati wapitiliza kuba sungilila, 3 pamene kwanja ya Yehova iza leta vili mu munda-hachi, ma bulu,ngamila, ng'ombe na mbelele. 4 Koma Yehova azaka panga kusiyanisa pakati pa vobeta vaku Isilayeli na vobeta vaku Iguputo, kuti kusankale nyama yaba Isilayeli isakafa. 5 Yehova akonza ntawi; akamba kuti, "mailo pamene nizakachita ivi vintu mu malo." 6 Yehova anachita ivi siku yo konkapo: vonse ng'ombe zaku Iguputo zinafa, koma kulibe nyama zaba Isilayeli zinafa, kulibe olo imozi. 7 Farao ana funsa funsa, na, onanoni, kunalibe nangu nyama imozi yaba Isilayeli inafa. Koma mutima wake unali oyuma, mwaicho sanaba leke bantu kuti bayende. 8 Pamene Yehova anakamba kuli Mose nakuli Aroni, "Tengakoni milota mu oveni kuzuzya kwanja. Iwe, Mose, ufunika kuponya milota mu mpepmo ninshi Farao atamba. 9 Viza nkala lukungu yopepuka pa malo ya Iguputo. Viza lengesa vituza na vilonda ku choka ku bantu na ku nyama mu malo yonse ya Iguputo." 10 Pamene apo Mose na Aroni banatenga milota mu oveni naku imilila pa sogolo pa Farao. Pamene apo Mose anaponya milota mumpepo. Milota zina lengesa vituzi na vilonda ku chika mu bantu na vinyama. 11 Bana Yele bana kangiwa kumu lesa Mose chifukwa chavituza, chifukwa vituza banali navituza na bonse bama yele benangu. 12 Yehova analimbisa mutima wa Farao, chakuti Farao sana mvelele Mose na Aroni. Ivi vinali monga anakambila kuli Mose mwamene Farao azachitila. 13 Pamene apo Yehova anakamba kuli Mose kuti, "Uka uke kuseni seni, uka imilile pa sogolo pa Farao na kukamba kuli enve, 'Yehova, Mulungu wa Aheberi, akamba ivi: :Leka bantu banga ba yende kuti bakani pempeze. 14 Chifukwa ino ntawi nizatuma vonse vilango vanga pali imwe, pali banchito banu na bantu banu. Niza chita ini kuti ungazibe kuti kulibe muntu monga ine mu ziko yonse yapansi. 15 Pali manje sembe na tambasula kudala kwanja nakuku ukila nama tenda iwe na bantu bako ngati mwa chose wapo pa malo. 16 Koma nichifukwa cha ichi ninaku vomelekezani kuti mupulumuke: kuti niku langizeni imwe mpamvu zanga, chakuti zina yanga ikambiwe ziko yonse ya pansi. 17 Ukali uzinyamula pa bantu banga naku kana kubaleka bayende. 18 Mvelani! Mailo ntawi mnga yamene iyi nizakaleta chi mpepo cha mpamvu chamene cikalibe kuonekapo mu Iguputo kuchokela pa siku inayamba mpaka lelo. 19 Apa manje, tuma namuna baike pamozi vibeta vanu na vonse muli navo mu mininda ku malo yo tetezewa. Aliyense muntu na nyama zamene zili mu munda ndipo sizina bwele kunyumba mu mund-matala yaza vigwela, ndipo vizafa. 20 Pamene banchitio ba Farao bana kulupilila mu utenga wa Yehova. bana yendesa naku ileta bakapolo babo na vibeto vabo mu manyumba. 21 Koma baja bamene sibana tenge utenga wa Yehova ma fakilako nzelu bana siya ba kapolo babo na vibeto vabo mu minda. 22 Pamene Yehova anakamba kuli Mose, "Nyamula kwanja yako mu mwamba kuti kunkali ngozi monse mumalo ya Iguputo." Pa bantu na vinyama, napa vonse vomela mu minda mu malo ya Iguputo." 23 Mose ananyamula nkoli yake mu mulenga lenga, ndipo Yehova anatuma chimpepo chikulu, matalala na kaleza pansi. Analokesa mwa ngozi pa malo Iguputo. 24 Chakuti kunaki malata yo sankaniza na tuleza, yakali maningi, yamene yakalibe kuchitikapo monse mu malo ya Iguputo kuchokela pamene inankalila ziko. 25 Monse mumalo ya Iguputo, matalala yana gwela vonse vinali mu minda bantu pamozi navi nyama. Vina gwela pa vomela vonse vamu minfa naku tyola mitengo zonse. 26 Koma kumalo ya Gosheni, kwane kunali kunkala ba Isilayeli kunalibe matalala. 27 Pamene apo Farao anatuma bantu kuti baitane Mose na Aroni. Anakamba kulibenve, Ine nachimwa ino ntawi, ehova nii olungama, na ine na bantu banga ndise boipa. 28 Pempelani kuli Yehova chifukwa tuleza tukulu na malata ya pakisa maningi. nizakulekani muyende, ndipo simuzankala pano." 29 Mose anakamba kuli enve, "Pamene apja chabe nikachokamo mu muzinda, niza vungulula mana yanga kuli Yehova. Tuleza tuzasiya, ndipo sikuzankala futi malata. Munjila iyi muza ziba kuti ziko yapansi niya Yehova. 30 Koma kwa imwe naba ncito banu, Ine niziba kuti simu lemekeza Yehova Mulungu." 31 Manje tonje na belele vina onogeka, chifukwa belele inali yokula pachimate mu matu na tonje inali kuchosa maluba. 32 Koma tirigu na rai sivina onongeke. chifukwa vinali voshanga ntawi yaku sogolo. 33 Pamene Mose anasiya Farao na muzinda, anavumbulula manja yake kuli Yehova; tuleza na malata vina leka. na mvula ina leka kugwa. 34 Pamene Farao anaona kuti mvula, malata na tuleza va leka, anachimwa futi naku limbisa mutima wake, pamozi na banchti bake. 35 Mutima wa Farao unankala olimba, chakuti sanaba leke bantu kuyenda, monga mwamene Yehova anakambila mu kwanja ya Mose.
1 Yehova anakamba Kuli Mose Kuti, "Yenda kuli Farao, chifukwa na limbisa mutima wake na mutima zaba nchito bake. Ine nachita ivi kuti nilangize mpavu zanga pakati pawo. 2 Ine nachita ivi kuti muka buaze bana banu na bazukulu vintu vamene nachita, nayi sunga kuipa Egpto, anso na pasa zizindikilo zosiyana kulangiza mpamvu yanga pakti pawo. mwaso muzaziba ati ine ndine Yehova" 3 Kuchoka apo Mose na Aroni banayenda kuli Farao naku mu'uza Yehova, Mulungu wa Aheberi, akamba ivi: muzakana kufika liti kuzichepesa pamaso panga? Leka bantu banga bayende kuti bakaniyamike. 4 Koma ukakana kuba leka bantu banga kuyenda, nvela, mailo nizaleta vidiza pa malo yanu. 5 Viza vininkila pa mwamba pa malo kuti kulibe azayamba kuona pa ziko ya pansi. Bazadya vamene viza salako vina taba mu matalala. Vizadya mitengo yamene ikula mu munda. 6 Viza zula muma nyumba yanu, nayaba nchito banu, na binse bamu Egpto - chamene batate bako olo ba mbuya bako bakalibe kuonapo, kulibe kuchokela pamene bana nkala pa ziko ya pansi kufika siku ya lelo. kuchoka apo Mose anachokapo pali Farao noyenda. 7 Banachito ba Faro banamu'uza, "Uyu mwamuna azaleka kuti vutisa liti? Leka bayende baku Isireli kuti baka nimpempeze Yehova Mulungu wabo. ninshi simuona ati Egpto ya onongeka? " 8 Mose na Aroni banaleta futi kuli Farao, anakamba kuli benve," yendani kuli Yehova Mulungu wanu muka mu pempeze. Koma nibati bantu bazayenda?" 9 Mose anakamba, "Tiza yenda naba ngono batu naba kulu batu, bana batu bamuna na bakazi. Tiyenda na gulu ya vobeta na ng'ombe yatu, chifukwa tizankala nama dyelelo ya Yehhova. 10 Farao anabauza, Yehova ankale naimwe, nikaku lekani muyende natu ngo'no twanu kuyenda. Onani, mulina voipa mu nzelu zanu. 11 Iyayi! yenda, bamuna beka pakat pako, naku mpepeza Yehov, kaili ndiye vamene mufuna."Kuchoka apo Mose na Aroni bana ba pisha pamaso ya Farao. 12 13 Yehova anakamba kuli Mose, "Tambulula kwanja yako pa malo ya Egpto kuli vidiza, kuti vika menye malo ya Egpto na kudya vomela vilimo, vonse matalala yana sala." Mose ana tambulula nkoli yake pa malo ya Egpto, chokonkapo Yehova analeta chimpepo chaku mawa pa malo yaku Egpto muzuba monse na usiku. Pamene kunali kuseni, chimpepo chaku mawa chinaleta vidiza 14 Madiza yana yenda pa malo yonse ya Egpto naku zula konse, pakalibe kuonekako chikalile ku nyinji wa mutundunuyu wa madiza, kulibe yopalana ivi vizaka bwelapo nafuti. 15 Vina vininkila pa mwamba pa malo ya Egpto kuti kunankala na mudima. Vinadya vomela na vonse vi vipaso vaku mitengo yamene matalala yana siya. Pa malo yonse Egpto, palibe chamoyo chomela chinasala, olo mitengo na chomela mu munda. 16 Pamene Farao anayitana mwamusanga Mose na Arnoi naku kamba, "Nachimwa kuli Yehova Mulungu wanu naimwe. 17 Anso pano, nikululukileni ma chimo yanga pa ntawi ino, anso mupempele kuli Yehova Mulungu wanu achose infa pali une." 18 kuchoka apo Mose anachokapo pali Farao naku pempela kuli Yehova. 19 Yehova analeta chi mpepo cha mpamvu kumazulo nonyamula vi iza novi peleka mukamumana yama tete; sipanasale vidiza vili vons pa malile ya Egpto. 20 Koma mulungu ana limbisa mutima wa Farao, anso Farao sanabaleke ba Isireli kuyenda. 21 Kuchoka apo Yehova anakmba kuli Mose kuti, "Tambulula manja yako ku mwamba, kuti ku nkale mudima pa malo ya Egpto, mudima wa bii." 22 Mose anatambulula manja yake ku mwamba,ndipo kunali mudima bii mu malo ya Egpto masiku yatatu. 23 Palibe anali kuona aliyense; palibe anachoka pa nyumba pake masiku yatatu. mwaicho, kunali nkunkala ma Isireli kunali kotuba. 24 Farao anaitana Moe naku kamba kuti. "Yenda uka mu pempeze Yehova. nama banja yanu yanga yende naiwe, koma gulu ya vobeta na ng'ombe mu siye." 25 Koma Mose anakamba kuti, "Tivomelesenu tinkale navo peleka vo shoka kuli Yehova Mulngu watu. 26 Ng'ombe zatu zifunika kuyenda naise; kulibe bologodoili yonse izasala kumbuyo, chifykwa tizafunika kuti tika pempeza Yehova Mulungu watu chifukwa sitiziba vamene vo pempelezako Yehova mpaka tikafika kuja." 27 Koma Yehova anakosesa mutima wa Farao, anso sanaba lekelele kuyenda. 28 Farao anati kuli Mose, "choka pali ine! samalani pali chintu chimozi, kuti musaka ni onepo futi, chifukwa siku muzaka ana nfeshi yanga, muzakafa." 29 Mose anakamba kuti, "Iwe weka wakamba sinizaka onapo nfeshi yaku nafuti."
1 Pamene Yehova anakamba kuli Mose, "kuliko umozi mulili wamene nizabwelesa kuli Farao na Iguputo. Pambuyo pake, azakuvomelesani kuti muchokemo muno. 2 Pamene azakuvomelesani kuyenda, azakuchosani. Bauze bantu kuti mwamunaa na mukazi aliyense afunika kupempa kuli munzake wapafupi vabwino ba siliva na golide." 3 Manje Yehova analengesa A'iguputo kuti bakondelese bana ba Isilayeli. Pamwamba pake, mwamuna Mose anali ukondwelesewa pa menso ya ba nchito ba Farao na bantu ba mu Iguputo. 4 Mose anakamba kuti, "Yehova akamba ivi: 'Pakati pa usiku nizayenda monse mu Iguputo. 5 Bonse bana boyamba muziko ya Iguputo bazafa kuyambila mwana uyamba wa Farao wa Farao, wamene ankala pa mupando ya mfumu, kufikila mwana oyamba wa mukazi wamene ankala pa myala ypoela, na bana bonse ba ba vobeta vabo. 6 Pamene kuzankala kulila mu ziko yonse ya Iguputo, mwamene sikunakalepo olo sikuzankalapo futi. 7 Koma palibe nangu galu azauwapo pa bana ba Isilayeli, ngankale pa muntu kapena chinyama mwaichi. 8 Aba bonse banchito bako, Farao, bazabwela kuli ine na kunigwadila ine. Bazakmba, yenda, iwena bantu bonse bamene ba kukonka pambuyo pa izo niza chokapo; Pamene apo anachoka pali Farao mu ukali kwambili. 9 10 Yehova anakamba kuli Mose kuti, "Farao sazaku nvelela. Nichifukwa niza chita vintu vodabwisa vambili mu ziko ya Iguputo. MOse na Aroni banachita vonse ivi vodabwisa pamenso ya Farao. Koma Mulungu anakosesa mutima wa Farao, anso Farao sana vomekeze bantu ba Isilayeli kutuluka mu malo mwake.
1 Yehova anakamba kuli Mose na Aroni muziko ya Iguputo, anakamba, 2 "kuli iwe, unomwezi uzankala oyamba wa myezi, mwazi oyamba muchaka kuli iwe. 3 Uza gulu yonse ya Isilayelu pa siku ya yeni ya uno mwezi bofunika alionse atenge mbelele olo mbuzi ing'ono mbuzi yabo, banja iliyonse ichite ichi, mbelele ya banja iliyonse. 4 Ngati banja yachepa kuli mbelele, mwamuna na muzake alipafupi atenge nyama ya mbelele olo mbuzi ing'ono yamene iyo bakwana kulingana na bantu. Ifunika yo kwanila bonse kudya, bafunika kutenga nyama yo kwanila kudyesa bonse. 5 Mbelele olo mbuzi ing'ono yanu siyifunika kunkala na choipisa. imuna ya chaka chimozi. mungatenge chimozi pa mbelele olo mbuzi. 6 Mufunika kuisanga kufika pa siku ya fotinifi mwezi ija. Pamene gulu yonse ya Isilayeli bafunika kupaya nyama pa mazulo. 7 Mufunika kutenga magazi enango nakufaka mumambali yabili yachiseko namu mwamba mwachiseko chama nyama yamene mudyelamo nyama. 8 Mufunika kudya nyama usiku ija, pambuyo poshoka pamulilo. Dyani na mukate opange kulibe chofufumusa pambali na masamba yobaba. 9 Osadya ibisi olo yopika mumanzi. mumala wake shoka pamulilo namutu wake, mendo na matumbo. 10 Osa lake iliyonse kusalako kufika kuseni. Mufunika kushoka vonse vizasalako kuseni. 11 Ndiye mwamene mufunika muzidyela: na belti yochuna nsapato zanu kumendo kwanu na vogwilisa nchito kumanja mwanu mufunika midye mwamusanga. Iyi ndiye pasika ya Yehova. 12 Yehova anakamba kuti: nizapitamo mumalo ya Iguputo mukati kusiku na kumenya bana boyamba ba bantu na nyama mumalo Iguputo. Niza bwelesa chilongo pa tonse tumilungu twamu Iguputo. Ine ndine Yehova. 13 Magazi yozankala cho onekela pama nyuma yanu pakubwelo kwanga kuli imwe, niza ona magazi, nizapitilila pamene pakumenya malo ya Iguputo. Ayo malendo siyaza bwela kuli imwe naku kuonongani. 14 Iyi siku iza nkala siku yokumbukilapo yanu chamene mufunika kukumbukila monga madyelelo kwa Yehova: kuba mibadwo banu inkale lamulo yamadyelelo yamene bafunika kusunga ku bantu bonse. 15 Mufunika kudya mukate opanda chofufumisa mumasiku yali seveni. Pasiku yo yamba muzachosa chofufumusa muma nyumba yanu. Aliyense azadya mukate ulina xhofufumisa kuchokela pasiku yo yamba kufikila pasiku ya namba seveni, uyo muntu mumu chose pakati pa Isilayeli. 16 Pasiku yoyamba kuzankala musonkano yopatulika kuli ine, napa siku namba seveni kuzankala winangu musonkala monga uyu. kuliba nchito izayamba kuchitika payaja masiku kuchoselako kupika kuti bonse mudye. Iyi ndiye nchito yeka ifunika kuchitiwa naimwe. 17 Imwe mufunika ku kukumbuka chisangalalo cha mukate osafufumuka chifukwa penze pa siku yamene nanakuchosani muzigabano zanu kockoka muziko ya Aguputo mufunika kukumbukila iyi siku ku bonse bantu bamibaddwo wanu munga malamulo yamuyaya. 18 Mufunikila kudya mukate ulibe chofufumisa kuchokela muma zulo siku yapa fotini mu mwezi yoyamba yamu mwezi. 19 Muma siku yaja yali seveni, kulibe chofufumusa chifunika kupezeka mumanyumba mwanu, Aliyense azdya mukate una chofufumisa afunika kumuchosa mumuzinda ya Isilayeli, olo uyo muntu niobwela ni umozi obadwa mumalo yanu. 20 Imwe simufunika kudya chili chonse chopangiwa na chofufumusa. kulikonse muzankal. mufunika kudya mukate opangiwa kulibe chofufumusa." 21 Pamene Mose anaitana bonse bakulu bamu Isilayeli nakukamba kuli benve, "Yendani musanke mbelele olo bana bambuzi bazakwana kudyesa ma banja yanu na kupaya pa siku ya nkosa. 22 Pamene apo tengani guru hisope na kiidubwisa mumagazi yankala mushomeka. Zolani magazi yali mushomeka pa mwamba chogwililako chiseko na muma felemu yabili kumbali. Kulibe pali imwe ifunika kuchoa panja kufikila kuseni. 23 Chifukwa Yehova aza pitamo kumenya A'Iguputo. Pamene aza ona magazi pamwamba pachogwililaka chiseko namu mafulemu, Aza pitilila paviseko vanu sezavomeleza zo'ononga kubwela mumanyumba mwanu kukamenyani. 24 Mufunika kuona ichi chochitika. ichi ntau zonse chizankala lamulo kuli imwe namibadwo zanu. 25 Pamene muzangena mumala yamene Yehova azakupasani. Monga mwamene ana kulonjezani kukachitila, mufunika kuona machitidwe yama pempelo. 26 pamene bana baza kufunsani, 'Nichani chamene mapempelo yatantauza? 27 pamene apo mufunika kukamba kuti, nichopeleka nsembe yaposika kwa Yehov, chifukwa Yehova ana pitilila manyumba yaba Isilayeli mu iguputo pamene anali kumenya Iguputo. Anamasula ma banja yatu."' Pamene apo bantu banagwada naku mupempelela Yehova. 28 Ma Isilayeli bana chita ndendende monga Yehova analamulila Mose na Aroni. 29 Vinachita pakati pa usiku pamene Yehova ana menya bonse bana boyamba bamu ziko ya Iguputo, kuchokela kuli mwana oyamba wa Farao, wamene anankala pamupando wa chifumu, kufikila ku oyamba wa muntu anali mundende na vonse boyamba va vibeto. 30 Farao ana uka usiku-enve, na bonse banchito bake, na bamu Iguputo, kwene kulila kopunda mu iguputo. chifukwa kunalibe nyumba simuna feko muntu. 31 Farao anaitana Mose na Aroni usiku nakukamba kuti, "Nyamukani, chokani pakati pa bantu banga, imwe na Isilayeli. Yendani mpempele Yehova. monga mwamene munakamba mufuna kuchita. 32 Tengani nkosa zanu na ngombe zanu, monga mwamene munakambila, naku yenda, naku ni dalisa." 33 A'Iguputo benze bo fulumzenza maningi pa bapisa mumuzinda, chifukwa bana kamba kuti, "Tizafa bonse." 34 Chakuti bantu banatenga flaulo yokanya yamene siyenze na chofufumusa. Mabasiketi yabo yanali yomangiwa muvivala pamapewa yawo. 35 Manje bantu Isilayeli bana chita monga Mose anabauzila. Banapempa Iguputo pali nkoni ya siliva na nkoni ya golide, na vovala. 36 Yehova anapanga A'Iguputo kufunisisa bwina Isilayeli. A'Iguputo anabapasa vonse vamene banapempa. Muli iyi njila, ma Isilayeli anaononga A'Iguputo. 37 Ma Isilayeli anayenda kuchokakela ku Rameses kufika ku Sukooti. banali bokwanila 600,000 bamuna banalikuyenda na mendo, kumozi bazimai na bana. 38 Bosankanizika bambili nabo banayenda nabo pamozi na nkosa na ngombe na vibeto vabili. 39 Banapanga mukate unalibe chofufumuisa mi phalo yamene bana chosa mu Iguputo. Ina libe chofufumisa chifukwa benze kukonza chokudya. 40 Ma Isilayeli benze banankala mu Iguputo mayezi 430. 41 Pakusila kwa 430 yezi, pali ija siku, yonse ma guru yomenya nkondo ya Yehova yana choka mumalo ya Iguputo. 42 Yenzeli usiku kunalibe kugona, kuti Yehova anabachosa mumalo ya Iguputo, iyi inali kukumbuka siku ya Yehova kuli bonse ba Isilayeli mumabadwe onse wa bantu. 43 Yehova anauza Mose na Aroni, "Iyi ndiye lamulo ya pasika: kusanklae mulendo alionse azadyako. 44 Koma, bonse bakapolo ba Isilayeli, bana na ndalama, angadye bakamudula mudulidwe. 45 Mulendo na ongenesewa chinto safunika kudya vokudya vilibonse. 46 Vokudya vifunika kudyewa munyama imozi. Simuzafunika kuchosa nyama iliyonse munyumba, anso musapwanye bonzo iliyonse. 47 Yonse guru ya Isilayeli ifunika kukumbukila aya madyelelo. 48 Ngati mulendo ankala naiwe afuna kukumbukila pasika kuli Yehova, bonse babululu bake bamuna bafunika kuduliwa. Manje anga bwele kukumbuka ichi, Azankala monga bantu bana badwela mumalo. Koma, kulibe muntu azadulidwa kudya vokudya vilivonse. 49 Iyi lamulo izasebenza kuli bobawa kuli imwe nabalendo bamene bankala pakagi panu." 50 Chakuti bonse ma Isilayeli banachita monga Yehova ana lamulila kuli Mose na Aroni. 51 Inabwela siku iyo yamene Yehova anachosa Isilayeli pa malo ya Iguputo muma gulu yabo yomenya nkondo.
1 Pamene apo Yehova anakamba kuli Mose kuti, 2 "Patulani mwana mwamuna oyamba - chifukwa chili chonse cho yambilila ku segula mala pa bana ba Isireli nichanga, ankale muntu ono chinyama. 3 Mose anakamba ku bantu, "ikani siku iyi mu nzelu, siku yamene muna choka mu Egipito kuchoka mu nyumba yaukapolo. Kupyolela mukwanja ya mpamvu ya Yehova anaku chosani imwe ku chokela mu malo yano kulibe mukate ulina vo fufumisa uzadyewa. 4 Muza choka mu Egipito pa siku iyi, mu mwezi mwa Abibu. 5 Ngati Yehova akuletani imwe malo ya baku Kenani, Hititi, Amori, Hiviti, na Jebusi, pa malo ana lumbila ku makolo yanu. kupasa imwe, pamalo ya uchi na mkaka-ndipo mufanika ku sunga ichi kufikila mu mwezi osiliza. 6 7 Muma siiku yali seveni mufunika kudya mukate ulibe vo fufunisa; Pa sakata kuzankala chi kondwelelo kupasa ulemu Yehova. Mukate ulibe vo fufumisa ufunika kudyewa ntawi yonse muma siku seveni; pasapezeke mukate uli navo fufumisa pakati panu. Vo fufumisa visa onekela mukati mwaimwe olo mumalile yanu. 8 Pasiku ya muzakamba ku bana banu, ' Nichifukwa cha vamene Yehova ana vichitila pamene nina choka mu Egipito. 9 Ichi chi zankala chi kumbuso kumanja kwanu na chi kumbuso pa mpumi panu. Ichi nichakuti lamulo ya Yehova inkale mu kamwa mwanu, ku pyolela mu kwanja ya mpamvu ya Yehova anakuchosani mu Egitipo. 10 Mwaicho mufunikila kusungu lamulo yiy pa ntawi yoyenela chaka na chaka. 11 Pamene Yehova azakulelani ku malo yaba ku Kenani yamene ana lumbila kuli imwe naku kuli makolo yanu ku chita, anso azaku pasani malo, 12 Mufunika ku patula kuli Yehova chonse cho badwa choyamba ku choka mu mimba ili yonse. Vonse vobadwa voyamba vobeta vimuna, vizankala va Yehova. 13 Chilichonse cho badwa choyamba kuli bulu muzafunika kuchinjanisa na mwana wa mbelele. Ngati simuzamugulafuti, Mufunika kumu tyola mukosi. koma aliyense obadwa oyamba mwana wanu mwamuna mufunka kumu obola 14 Ngati mwana wanu mwamuna akufunsani pa ntawi ina, ' 'chi tantauza chani ichi?' muza mu'uza nikupyilela mu kwanja ya mpamvu kuti anatichosa mu Egipito, munyumba ya uka polo. 15 Pamene Farao mwantota anatikanila kuti tiyende, Yehova anapaya aliyense obadwa oyamba mu Egipio, bonse bo badwa poyamba vaba banthu navi nyama nichifukwa chake nina peleka nsembe kuli Yehova vonse vi muna vina yambilila kusegula mimba koma bonse bana badwa poyamba bana bamuna nina ombola. 16 Ichi chi zankala chi kumbuso kumnaja kwanu, nachi kumbuso pa mpumi panu, chifukwa nimuku pyolela mu kwanja ya mpamvu ya Yehova aniti chosa mu Egipito." 17 Pamene Farao anabaleka bantu kuyenda Mulungu sana ba sogelele mu njila yopita mumalo yaba Philitine, nga nkale malo yanali pafupi. Chifukwa Mulungu anakamba kuti, "Mwina mwake bantu banga chinje nzelu ba kaona nkondo naku bwelela ku Egipito." 18 Chifukwa chaicho Mulungu bantu anaba zungunlusa muchipululu mpaka ku nyanja ya matete. Bana Isireli ba choka mu malo ya Egipito wokonzekela nkondo. 19 Mose anatenga ma bono ya Yosefe ku yenda nayo, chifukwa Yosefe anapanga bana bamuna ba Isireli ku umbila na kukamba, Mulungu zo'ona zakaku pulumusani, muzafunika kutenga ma bonzo yanga. 20 Bana ba Isireli bana yrnda ku chokela ku Sukoti naku panga musasa pa Etamu mu mbali mwa chi pululu. 21 Yehova anayenda kusogolo kwabo muzuba muchi pilala chamakumbi kuba sogolela mu njila. usiku anayenda mu chipilalala cha mulilo kuba pasa ku unika. mu munkalidwe yuy banali kuyenda muzuba na usiku. 22 Yehova sana chosepo pa bantu muzuba chipilala cha makumbi olo chipilala cha mulilo.
1 Pamene Yehova anakamba na Mose, kuti, 2 "Kamba nama Isilayeli kuti ba pindimuke na kale wapafupi na Pi Hahiroth, pakati pa Migdo na nyanja, asanafiken Bao Zifoni. Muza unjikana pa mbali yanja ya Pi Hahiroth. 3 Farao aza kamba zaba Isilayeli, bali kuyenda yenda mu malo mu chipululu cha ba valila be benve! 4 Ni za limbisa mutima wa Farao, kuchoka apo azaba pishamo. nizatenga ulemu kamba ka Farao na silikali bake binse. Ba Iguputo bazaziba kuti ine ndine Yeova. "pamene apo ma Isilayeli bana unjikana monga analamuliliwa. 5 Pamene Mfumu yaku Iguputo ina uziwa isilayeli kuti yataba, nzelu za Farao naba nchito bake zina pindimukila bantu. banakamba, "Tachita chani? Talekelela ma Isilayeli kutisebenzela ife." 6 Pamene apo Farao anakonzeklea ngolo zake naku tenga ba nkondo bake na enve. 7 Anatenga sikisi hadledi osakiwa golo na golo zina zose mu Iguputo, na akulu kwa enve. 8 Yehova analimbisa mutima wa Farao, Mfumu yaku Iguputo, anso mfumu inankokamo ma Isilayeli. manje ma Isilayeli banayenda mogonjesa. 9 Koma ma Iguputo banakonkamo benve. pamuzi na akavalo na golo, edesa akavalo, na bomenya nkondo bake. bana bapa bana ba Isilayeli na nkala ku nyanja kumbali ya Pi Hahiroth. 10 Pamene Farao anabwela pafupi, ba Isilayeli anayangana kumwamba naku badabwisa. Ma Iguputo banali kubwela pambuyo pao, anso bana yopa. ba Isilayeli bana lila kuli Yehova. 11 Banakamba kuli Mose, "nichifukwa kunalibe manda mu Iguputo, kwakuti watichosa kuti tikabwele kufela muchipululu? Nichani watisunga monga ivi, kuti chosa mu Iguputo? Ivi sindiye vamene tinaku'uza mu Iguputo? 12 Tinakamba kuli iwe, 'Tileke teka, chakuti tisebenzele ma Iguputo.' Sembe chinankalapo bwino kuli ise kuba sebenzela kuchila kufela muchipululu." 13 Mose anakamba kubantu, "Musayope. Imililani chilili muone mwamene azaku masulilani Yehova azakupasni imwe lelo. Chifukwa simuzaka ba onapo ma Iguputo bamen muona lelo. 14 Yehova azakumenyeleni nkoni, muzafunika ku imilila chilili." 15 Pamene apo Yehova anakamba kuli Mose, "Nichani iwe, Mose, upitiliza kuitana kuli ine? ba uze ma Isilayeli kuyenda pasogolo. 16 Nyamula nkoli yako, tambulula kwanja yako pa nyanja uyi patule pa bili, chakuti bantu baku Isilayeli ba pita pa nyanja pa malo yoyuma. 17 Chenjelani kuti niza limbisa mutima wama Iguputo kuti bazaba konkamo. Niza tenga ulemelelo chfukwa cha Farao na bonse bomenya nkondo bake, ma ngolo yake, nabo endesa makavalo. 18 Pamene ma Iguputo baza ziba kuti ndine Yehova nika tenga ulemu chifukwa cha Farao, ngolo zake, nabo endesa makavalo." 19 Munegeli wa Mulungu, wamene anayenda paosgolo pa gulu la Isilayeli, anavendela naku yenda kumbuyo kwabo. Pilala ya kumbi ina vendela naku yenda ku imilila kumboyo kwabo. 20 Kumbi ina bwela ku imilila pakati msasa wa Iguputo na msasa wa Isilayeli. Inali kumbi yofipa kuli A'iguputo, koma ina sanikila usiku kwama Isilayeli, chakuti mbali imozi siyina na bwele pafupi nabenangu usiku onse. 21 Mose anatambulula kwanja pa nyanja. Yehova anabweza nyanja nachi mpepo chaku mawa usiku onse naku panha nyanja malo yoyuma. Munjila iyi manzi yana patuliwa. 22 Ma Isilayeli banayenda pakati pa malo yoyuma. Manziyana panga chifapa chabo ku kwa ja ya maja naku mazele. 23 Ma Iguputo yanakonkamo. bana ba konka pambuyo pakati pa nyanja-yonse ma makavalo ya Farao, Ngolo, nabo yendesa makavalo. 24 Koma ntwai yaku kuseni seni, Yehova analangana pansi pama silikali ya Iguputo kupitila mu pilala ya mulilo na kumbi. Analengesa kuvutisiwa pakati pama Iguputo. 25 Ma wilo ya ngolo yabo yenze ayana fasa, nama makavalo yana yendaa movutikila. chakuti ma Iguputo yanakamba, "Tiyeni titabe kuchoka kuli ma Isilayeli, chifukwa Yehova a amenyela kwaise." 26 Yehova ankamba kuli Mose, "Tambulula kwanja yako pa nyanja kuti manzi yabwele pamwamba pama Iguputo, ma ngolo yabo, na makavolo yabo." 27 Chakuti Mose anatambulula kwanja yake pa nyanja, naku bwelela munjila yake pamene kseni kuna onekela. Ma Iguputo banatabila mu nyanja, na Yehova anaba peleka ma Iguputo mukati mwake. 28 Manzi yanabwela naku vininkila ngolo za Farao, oyenda na makavalo, naba silikali bonse bamene benze bana konka ma ngolo mu nyanja. Palibe anapulumuka 29 Ngankale choncho, ba Isilayeli bana yenda pamalo poyuma pakati pa nyanja. ma ja yanali chipupa kuli benve ku kwanja ya manja naku manja naku kwanja ya mazele. 30 Pamene Yehova anapulumusa Isilayeli ija siku ku kwanja yama Iguputo, Ma Isilayeli yana ona matupi yokufa pa mbali pa nyanja. 31 Pamene Isilayeli inaona mpamvu za Yehova zamene anasenzesa kuli ma Iguputo, bantu banamu lemekeza Yehova, naku kululupila muli Yehova na wa nchito wake Mose
1 Pamene apo Mose na bantu bamu Isilayeli bana imbila iyi nyimbo kuli kuli Yehova. Bana yimba, "nizamuibila Yehova popeza wapambana mwa ulemelelo; kavalo na wokwella wake abaponya mu nyanja. 2 Yehova ndiye mpamvu yanga na nyimbo yanga, naku nkala chipulumuso changa. Uyu ndiye Mulungu wanga, anso niza mutamanda, Mulungu waba tate banga, niza mukweza. Yehova niwa nkondo; 3 Yehova ndiye zina yake. 4 Iye aponya ngolo za Farao naba nkondo bake munyanja Anchita osankiwa ba Farao banamila munyanja ya matete. 5 Nyanja inaba vininkila; banayenda pansi mozama monga mwala. 6 Kanja yanu yamanja, Yehova, ni ya ulemelelo mu mpamvu; kwanja yanu yamanja, 7 Yehova, ya phwangu mu dani. mu mpamvu yaikulu inu mwa baukila iwo bamene anakunya mukilani. munatuma mu kwiyoi innbanyekesa bonse monga mauzu. 8 Kupitalamu mpuno ya mpuno mazi yana ibwelesa pamozi: mazi yoyenda yana nkala pamozi. mazi yozama yanamezewa mutima wanyanja. 9 MUdani anakamba kuti, 'nizabakonka, nizaba peza, nizagabanisa vamene niza tenga; kufunisisa kwanga kuza kutulisiwa pali benveniza tenga lupanga yanga; kwanja kwanga kuzaba ononga. 10 koma muza obesewa mpepo yanu, na nyanja inaba meza. anamila monga nsimbi mu manzi ya mpamvu. 11 Nindani ali monga imwe, Ywehova, pakati pa milungu? nindani ali omga imwe, wamukulu muchiyelo, kulemezewa mu matamando, kuchita vodabwisa? 12 Munatambulusa kwanja yanu yamanja, na ntaka inabwela noba mela. 13 Muchipangano chakukupilika kwano mwasogolela bantu amene mwa pulumusa. mu mpavu zanu mwawa sogolela ku malo oyela kwamene munkala. 14 Bantu bazamvela, anso baza njenjemela; Voipa vibagwila bantu bokala mu Filistiya. 15 Pamene ma mfumu yaku Edomu bazayopa; asilikali ba Moabu ba zagwendezekai na bonse bokala mu kanani baza sungunuka. 16 kuyopa na manta kunaba gwela. Chifukwa chamu manja yabo, bazaimilila monga mwala pakana bantu bako bakapitilepo, Yehova- paka bantu unapulumusa bakapite. 17 Uzabaleta naku shanga pa lupili ya choloba chanu, mu malo, Yehova, yamene munapanga ku kalamo, malo oyela, mbuye watu, yamene manja yanu yana manga. 18 Yehova azalamulila muyaya." 19 Akavalo ba Farao pamozi na ngolo na bokwelapo zonse zina yenda munyanja. Yehova anabwesa manzi ya munyanja pa benve. koma ba Isilayeli anayenda pa dothi yoyuma pakati ya nyanja. 20 Miriamu mneneli, mlongo wa Aroni. anatenga cholinza, naba zimai bana tenga vo linza, kuvina pamozi an enve. 21 Mirraimu anabaimbila, "yimbila Yehova, chifukwa wa pambana mwaulemelelo. kavalo na okwelapo abaponya munyanja." 22 Pamene apo Mose anasogolela Isilayeli kuchoka ku nyanja yamatete. kuchoka apo banayenda mu chipulululu cha Sha. Bana yenda masiku yatatu muchipululu koma sibana peze manzi. 23 Banabwela ku mara, koma sibanamwe chifukwa manzi paja yanali yobaba. chifukwa chake banaitana malo yaja mara. 24 Bantu bana dandauka kuli Mose na kukamba, "nichani chamene tizamwa?" 25 Mose analila kuli Yehova, pamene apo Yehova anamu langiza mutengo. Mose anaka ponya mu mazi, pamene apo manzi yana sanduka ya nzuna kumwa, panali pamene apo Yhova anabapasa lamulo yokosa, pamene apo anaba yesela. 26 Anakamba, "Ngati muzamvesesa bwino mau ya Yehova Mulungu, nakuchita voyenela mu menso ya ke, pamene apo ngati uzanvelela malamulo yake na ku mvelela malembo yake yonse - sinaza ikapo matenda yali yonse yamene ninayika pali a Iguputo, ndaba ndine Yehova wamene amaku polesa. 27 Pamene apo bantu banafika ku Elimu, pamene pa malo yali twelovu pochoka manzi na mitengo ya kanjeza yali sevente. Anamanga chihema chao pambali yamanzi.
1 Bantu banayenda kchoka ku Elamu, na gulu yonse ya Isilayeli inafika muchipululu cha chimo, chilipakati pa Elamu na Sinayi, pasiku ya fifitini mumwezi wa chibili pene banachoka muziko ya Iguputo. 2 Gulu ionse ya Isilayeli ina dandaulila Mose na Aroni muchipululu. 3 Bana ba Isilayeli anakamba kuli benve, "Ngati chabe tenze tinafa mumanja ya Yehova malo ya Iguputo pamene tenze kunkala mumbali ya mapop yanyama nakudya buledi maningi. chifukwa wa tileta muchipululu ise bantu bonse kutipaya na njala. 4 Pamene apo Yehova anakamba na Mose kuti, "niza gwesa mukate kuchoka ku mwamba. bantu bazachoka nakutenga gao ya yao yasikuiliyonse kuti nibabonse ngati baza yenda mulamulo olo kapena sibaza yendamo. 5 Kuzabwela pa siku ya nambala sikisi, baza tenga kabili mwamene bantengela masiku yonse, na kuppika vamene waleta. 6 kuchoka apo Mose na Aroni banakamba kuli bantu bonse baku Isilayeli, "kumazulo muzaziba kuti ni Yehova anakuchosani mumalo ya Iguputo. 7 Kuseni muzaona ulemelelo wa Yehova, chifukwa anvela ku dandauka kwanu kuli enve. Ine na Aroni ndife ndani mwati dandaukila ise?" 8 Mose anakamba futi, "muzaziba ichi pamene Yehova akupasani nyama mumazulo na buledi kuseni okuta nabo. chifukwa amvela ma dandaulo yamene mumamu dandaulila. Aroni na ine ndise ba ndani? simudandaukila ise; koma Yehova." 9 MOse anakamba kuli Aroni, "Kamba kuli bantu bonse bana ba Isilayeli, 'bwelani pafupi na Yehova, chifukwa amvela madandaulo yanu." 10 Ina bwela kupita, pamene Aroni anali kukamba na bantu bonse bamu Isilayeli, bana yangana kuchipululu, na, onani, ulemelelo wa Yehova unaonkela muma kumbi. 11 Kuchoka apo Yehova ankamba na Mose, kuti, 12 "Namvela ma dandauko ya bantu ba Isilayeli. Kamba na benve kuti, 'Mumazulo muzadya nyama, naku kuseni muzazulisiwa na buledi. Kuchoka apo muzaziba kuti ndine Yehova Mulungu." 13 Ina bwela kumazulo nyoni zinabwela kuma zulo naku vininkila. Kuseni pamene mame yana zunguluka ponkala. 14 Pamene mamem yanasila, pamwba pa chipululu panali kantu kangono monga chipale pantaka. 15 Pamene bana ba Isilayeli banaona, banakambisana wina na wina, "nichani ich? sibana zibe kuti nichani, Mose pasanin kuit mudye. 16 Iyi ndiye lamulo yamene apasa Yehova: 'Alionse afunika kuyola vamene afunika kufya, omeli imozi ya muntu aliyense ya nambala ya bantu. Ndiye mwamene muzayolela, yolani vambili vakudya va muntu alionse muchihema chanu. " 17 Bana ba Isilayeli banchita vamene ivo. Bena banayo vambili, bena vingono. 18 Pamene bana pima na omeri yo pimila,baja bana yola vambili kulibe vinaslila, mbaja bayolu ving'ono sibanasube kalikonse. Alionse anayola vambili kukwa nisa vofuna vao. 19 Pamene Mose anakamba kuli benve, "Kusaseka aliyense usiyako pakana kuseni." 20 Koma benve, sanamu munvelele Mose. Benve banasiyako paka kuseni, koma inachokamvikusi na kununka. pamene apo Mose anakwiya na benve. 21 Bana kumana pamozi kuseni, Muntu aliyense analonga vambili vakudya vapa ija siku. Pamene ka zuba ina pya, inasungunuka. 22 Inachitika pasiku ya sikisi banayola kabili buledi. ma omeli ya bili ya mutnu slionde. bonse basogoleli bagulu banabwela na ku'uza Mose. 23 Anakamba nao, "Ndiye vamene Yehova akamba mailo na kupumula, sabata yoyela mukuleme Yehova. pangani vamene mufuna kupanga, pikani vamene mufuna kupika, vonse vosala vi ikileni pambali pakana mu mawa. 24 Ndiye anaika pambali paka kuseni, mwamene Mose anabauzila. Sivinaonongeke olo kupezekamo vikusi. 25 Mose anakamba, "idyani chokudya chija lelo, popeza lelo ni siku yopatulika monga sabata kulemez Yehova. elo sumu zavi peza mu munda, 26 Muzayamba kuyola mu masiku sikisi, koma siku ya seveni ni Sabata. Pa Sabata sikuza nkala mana." 27 Anso Inachitika kuchoka apo pa siku ya namba seveni bena bantu banayendaa kuyola mana, koma sibana peza kali konse. 28 Pamene apo Yehova anakamba na Mose, "muzakana kusunga malamulo na malembo yanga futi? 29 Ona, Yehova akupasni sabata. Pasiku ya sikisi akupasni buledi wamasiku yabili. Alionse waimwe afunika kunkala mumalo yake; kusapezke choka mumalo yake pasiku ya seveni." 30 Bantu bana pumula pasiku ya seveni. 31 Bana ba Isilayeli anaitgana vakudya kuti "mana" zinali zoyela monga mbeu ya mpasa, na kamvekedwe monga uchi. 32 Mose anakamba, "Ndiye vamene Yehova alamulila, lekaniomeli ya mana isungiwe na mibadwo ya bantu kuti bana banu bakaone buledi wamene nia kudyesani mu chipululu, pambuyo pokutulusani mu Iguputo." 33 Mose anakamba kuli Aroni, "Tenga poto ikamo omlei yamana, Isunge pamenso pa Yehoa, usungile ku mibadwo yanu. 34 Mwamene Yehova analamula Mose, Aroni anasunga pambali zonenela zachipango mu likasa. 35 Bantu ba Isilayeli andaaya mana zaka fote pakana banabwela kumalile ya ziko ya kanani. 36 Manje omeli niya namba teni ya Efa
1 Bantu bonse ba Isilayeli bana yenda choa ku choka mu chipululu cha chimo, kukonka mwamene Yehova anabauzila. Bana nkala pa Refidim, koma kunalibe manzi yokumwa bantu. 2 chifukwa cha ichi bantu bana kamba kuli Mose ati ndiye alengesa munkalidwe wabo naku kamba kuti, "Tipase manzi timwe." Mose anayanka, "Nichani mukangana naine? Nichani muyesela Yehova?" 3 Bantu banali na njota maningi, naku dandauka kuli Mose. Bana kamba kuti, "uti paye ise na bana batu na vobeta na njota?" 4 Pamene apo Mose analila kuli Yehova, "Nichite bwanji na aba bantu? bali ku konzeke kuni tema myala." 5 Yehova anakamba kuli Mose, "enda pasogolo pa bantu, utenge bakulu ma Isilayeli. Tenga nkoli yamene unachaisa pa manzi, na kupita. 6 Niza imilila pasogolo pako pa mwala a Horeba, anso uzaichaya pa mwala. Manzi yaza choka mu mwala kuti bantu bamwe." Pamene Mose anachita mwamene mu menso ya bakulu ba Isilayeli. 7 Anaitana malo yaja Massa na Meribah chifukwa ma Isilayeli yana dandaula, na chifukwa benze bana yesa Ambuye kukamba kuti, "Yehova ali pakati patu olo iyayi? 8 Pamene apo bantu bomenya nkondo bama Amaleki bana bwela naku bachitila nkondo ku Refidimi. 9 Pamene apo Mose anakamba kuli Yoshwa, "Sankapo amuna muyende. Mumenyane nama Amaleki. Mailo niza imilia pa mwamba pa lupili na nkoli ya Mulungu mu manja mwanga. 10 Pamene apo Yoshwa ana menyana nama Analeki monga mwamene Mose anamu'uzila, pamene Mose, Aroni, Hur banayenda ku mwamba kwa lupili. 11 Pamene Mose ananyamula manja yake ku mwamba, Isilayeli inali ku gonjesa; pamene anaika manja yake ku pumula, Ma Amaleki benze banayamba ku gonjesa. 12 Pamene manja ya Mose yana lema, Aroni na Hur bana tenga myala naku faka pansi pake kuti unkalepo. Pa ntawi imozi, Aroni and Hur banamu gwilila manje yake mu mwamba, muntu umozi kumbali yake, na wina ku mbali kwina. Kuchoka apo manja ya Mose yanali yo imilila mumwamba mpaka zuba kugwa. 13 Pamene apo Yoshwa anaba gonjesa bantu baku Amaleki na panga. 14 Yehova anakamba kuli Mose, "Lemba ivi mu buku naku belenga mu chitundu cho nvela Yoshwa, chifukwa niza chosapo ku kumuka pali ba Amaleki pansi pa mulenga lenga." 15 Pamene apo Mose anamanga guwa naku itana "Yehova nisi." 16 Anakamba kuti, "chifukwa kwanja ina imiwa kuli mpando wa Yehova-kuti Yehova azati menyela nkondo naba Amaleki kuchoka ku mubadwo na mubadwo.
1 Jeturo, wa nsembe waku Mdian, Mupongizi mwamun a wa Mose, ananela vonse vamene Mulungu anachitila Mose na bantu bake baku Isreali. Ananvela kuti Yehova anachosa Isreali mu Igupto. 2 Jeturo, mupongozi wa Mose, anatenga Zippora, mukzai wa Mose, pambuyo pakumutuma ku nyumba, 3 na bana bake bamuna babili; zina yamwana mwamuna umozi inali Geshomu, pakuti Mose anali akamba kuti, "Nankala mulendo mumalo achilendo." 4 Zina yawina inali Eliyeze, paukti Mose anakamba kuti " Mulumgu wamakolo banga anali tandizo yanga." ananipulumusa ku mpanga wa Farao." 5 Jeturo, mupongozi mwamuna wa Mose, anabwela na mwana mwamuna wa Mose na mukazi wa Mose muchipululu kwamene anali wasonkana papili ya Mulungu. 6 Anakamba kuli Mose kuti, " ine, mupongozi mwamuna wako Jeturo, nabwela kuli iwe na mukazi wak na bana bake babili." 7 Mose anayenda kukumana bapongozi bake, anagwada pansi. kuchoka apo anaba fyofyonta.Banafunsa pali umoyo wabo kuchoka apo banangena mumalo yokumanilamo. 8 Mose anauza bapongozi bake vonse vamene Yehova anachita kuli Farao nabantu bam Igupto kamba ka Isreali, navonse vovuta vabo vamene vinabagwela munjila, namwamene Yehova anaba pulumusila. 9 Jeturo anakondwela pavonse vabwino vamene Yehova anachitila Isreali, nakuti anapulumusa mumanja yaba Igupto. 10 Jeturo anakamba kuti, "Lekani Yehiva atandamike, pakuti akupulumusani kuchoka mumanja yaba Igupto na mumanja ya Farao, na kupokolola bantu munja yaba Igupto. 11 Manje naziba kuti Yehova nimukulu chila tumilungu tonse, chifukwa pamene ba Igupto anasunga ba Isreali mozikweza, Mulungu anapulumusa bantu bake." 12 Jeturo, Mupongozi wa Mose, anabwelesa voshoka nsembe ya Mulungu. Aroni na bakulu bonse ba Isreali banabwela kudya chakudya pamenso pa Mulungu na Mupongozi wa Mose. 13 Pasiku yokonkapo Mose anakala pansi kuweluza bantu. Bantu bana imilila mumbali mwake kuchoka kuseni kufika kumazulo. 14 Pamene mupongozi wa Mose anaona vonse vamene anachita kubantu, anakamba kuti, "kodi nichani chamene ukuchita ku bantu? nichani chamene iwe wankalila weka na bantu baimilila kuchokela kuseni kufika kumazulo?' 15 Mose anakmba kuli bapongozi kuti, " Bantu babwele kufunsa Mulungu mochitlia. 16 Ngati bali nakuangana, bamabwela kuli ine. Mina weluza pali muntu umozi na wina, nakuba punzisa monkalila mwa Mulungu na malamulo." 17 Mupongozi wa Mose ankamba kuli enve, vamene uchita sivabwino kwambili. 18 Uza zilemesa iwe nabantu bamene ulinao, chintu ichi nichachikulu iwe. Siuzakwanisa kuchita paiwe weka. 19 Nvela kuli ine. Nizakupasako maganizo, na Mulungu azankala naiwe, chifukwa ndiwe oyimililako bantu kuli Mulungu anso umupeleka vongan ngana vaba kuli iye. 20 Ufunika kubapunzisa va Mulungu na malamulo. Ufunika kubaonesa moyendela na nchito yosebenza. 21 Mopitilza, ufunika kusanka bantu boyenela bamuna kuchoka kubantu onse, amuna opasaa ulemu Mulungu, amuna achilingamo. Ufunika kubaika bo onelela bantu. bankale basogoleli bama sauzande, handiledi, mafifite, nama teni. 22 Bazayamba ku weluza mu nkani zonse zamasiku onse, koma nkani zovuta bazabwelesa kuli ine. kwa nkani zonse zing'ono, banga weluze bamene beka. Munjila iyo chizankala chapafupi kuli ine, anso bazanyamula chintu ichi ndi iwe. 23 Ngati wachita ichi, anso ngati Mulungu akulamulila kuchita so, kuchoka apo uzakwanisa kupilila, na bantu bonse bazakwanisa kupita ku ntumba okutila." 24 Anso Mose ananvela mau yaba pongozi bake bamuna naku chita vonse vamene banakamba. 25 Mose anasanka amuna oyneda mu Isreali na kubaitana basogoleli ba bantu, oyangani masauzande, ma handiledi, mafifite nama teni. 26 Ana weluza bantu moyenela. Nkani zovuta banazipeleka kuli Mose, Koma bene bana weluza nkani zosavuta. 27 Kucoka apo Mose analeka bapongozi bake bamuna kuyenda, na Jeturo ana bwelela kumalo yake.
1 Mu mwezi wachitatu pamene bantu ba isreali banachoka mu malo ya iguputo, pa siku yamene ija, bana bwela ku chipululu cha sinai. 2 Pamene banachoka ku Rephidimi naku bwela ku chipululu cha Sinai, banaika ma hema yao yo gonamo munyansi ya lupili. 3 Mose anakwela pamwamba kuli mulungu. Yehova anamuitana palupili na kumu uza, '' ufunika ku uza nyumba ya yakobo, bantu ba israeli: 4 Muna ona mwamene ninachitila baku iguputo, mwamene ninakunyamulilani pama papiko ya nkwazi nakuku letani kuli ine nemwine. 5 Mwaicho, ngati muzamvelela ku mau yanga naku sunga chipangano changa, muzankala bantu banga bapa dela pa bantu bonse, chifukwa chalo cha pansi chonse ni changa. 6 Muzankala munzi wa ba nsembe na ziko yo yela kuli ine. Aya ndiye mau yamene uzakamba ku bantu ba israeli.'' 7 Mwaicho mose anabwela nakuitana bakulu bakulu pa bantu.Nakuba uza yonse aya mau yamene yehova anamulamulila. 8 Bantu bonse banayanka pamozi nakukamba, '' tizachita vonse vamene yehova akamba.'' Ndipo mose anabwelela ku uza yehova mau yamene bantu banakamba. 9 Yehova anakamba kuli mose, '' nizabwela kuli iwe mukati mwa kumbi kuti bantu bamvele nika kamaba naiwe kuti baku kulupilile kwamuyayaya.'' Ndipo mose anauza yehova mau ya bantu. 10 Yehova anakamba kuli Mose, '' yenda ku bantu.Lelo na mailo baziyelese, na kuwasha vovala vao. 11 Bakonzekele pa siku yachitatu, chifukwa pa siku yachitatu yehova azaseluka pa lupilii ya Sinai. 12 Ufunika ku ika mopelela bantu kuzungululusa lupili yonse .Kamba kuli beve, 'chenjelani kuti musayende pamwamba pa lupili olo kugwila mumbali mwake. Aliyense wamene aza gwila lupili azapaiwa.' 13 Kulibe kwanja ya aliyense yamene izafunika kumugwila muntu uyo. Mumalo mwake, azafunika kutemewa myala olo kumu shuta.Ngankale ni chinyama olo ni muntu, afunika ku paiwa.' Pamene penga izalila ntau itali, babwele mumbali mwa lupili.'' 14 Ndipo Mose anaseluka pa lupili nakuyenda ku bantu. Anauza bantu kuziyelesa na kuwasha vovala vao kukonzekela kamba kaku bwela kawa yehova. 15 Anakamba ku bantu, '' nkalani bokonzekela pa siku yachitatu; osati kuyenda pafupi na bakazi banu. 16 Pa siku ya chitatu, pamene kunali kuseni, kunali bingu na tuleza na kumbi yotikama pa lupili, ndipo pokoso ikulu ya lupenga. Bantu bonse bosonkana bana njenjema. 17 Mose analeta bantu kuchoka mu musonkano ku kumana na mulungu, ndipo bana imilila mumbali mwa lupili. 18 Lupili ya sinai yonse inavaliwa na chusi chifukwa yehova anaselukilapo mu mulilo na chusi. Chusi chinayenda mumwamba monga chusi cha mu nganjo, na lupili inanyan'ganya mwa mpamvu. 19 Pamene pokoso ya lupenga ina kulilako naku kulilako, Mose anakamba, na mulungu anamuyanka mu liu. 20 Yehova anaseluka pa lupili ya Sinai, pamwamba pa lupili, na kuitana Mose pa mwamba. Mwaichi Mose anayenda pa mwamba. 21 Yehova anakamba kuli Mose, '' yenda pansi uchenjeze bantu; banga jumpe malile nakuni yangana. Ndipo bambili muli beve banga onongeke. 22 Na ba nsembe nabeve bamene bafuna kubwela pafupi na ine baziyelese - bazikonzekele chifukwa chaku bwela kwanga - kuti nisaba pase chilango.'' 23 Mose anakamba kuli yehova, '' bantu sibanga bwele pamwamba pa lupili ya sinai, chifukwa unatilamula: ' pangani malile kuzungulusa lupili na kuziyelesa yehova.'' 24 Yehova anakamba kuli eve, ''yenda pansi ubwele na Aron, koma usaleke ba nsembe na bantu bali bonse kujumpa malile kubwela kuli ine. Ngati ba jumpa malile, nizabalanga. 25 Mwaichi Mose anaseluka kuyenda ku bantu nakukamba nabo.
1 Mulungu anakamba mau aya: 2 "Ine ndie Yehova Mulungu wako, wamene anaku chosa mu Iguputo, nyumba yao kapolo. 3 Suzankala na milungu pambali yanga. 4 Suza bumba chili chonse chonpalana na chamu mwamba, olo pa ziko ya pasni, olo mu manzi pansi. 5 Suza gwadila kuli venve olo kuvi oemoeza, chifukwa ine, Yehova Mulungu wako, ndine Mulungunwa nsanje. Nilanga kuipa kwamakolo pakuleta chilango pali bana babo, mpaka bobdwa babo ba chilatu na chinali bonizonda. 6 Koma ni langiza chikondi chosasila kuli ma sauzande ya baja boni konda sunga malamulo yanga. 7 Suza tenga zina ya Yehova Mulungu wako, pa chabe, chifkwa siniza chosapo mulandu pa uli onse akamba zina yanga pa chabe. 8 Kumbuka siku ya Sabata, kuyi patula niyanga. 9 Uza sebenzaa naku chita nchito yako yonse muma siku sikisi. 10 Koma siku ya seveni ni sabata ya Yehova Mulungu wako. Pali iyo siku suza chita nchito ili yonse, iwe, mwana wako mwamuna, olo wa nchito mukazi olo nyama vo sunga vako, olo balendo bo nkala naimwe mu malo yanu. 11 Chifukwa muma siku yali sikisinYehova anapanga ku mwamba na ziko ya pansi, nyanja, na vonse vamene vilimo, naku pumula pa siku ya sabata. Ni chifukwa icho Mulungu ana dalisa siku ya Sabata nakuyi patula. 12 Lemekeza batate bako naba mai bako kuti unkale ntau itali mu malo yamene Yehova Mulungu akupasa. 13 Osa paye aliyense. 14 Osachite chigololo. 15 Osabela aliyense. 16 Osa nkala mboni wa boza pali munzako. 17 Osa kumbwile nyumba ya munzako; Osa kumbwile mukazi wamu zako, wa nchito wake mwamuna, wa nchito mukazi, ng'ombe, bulu, olo chili chonse chamu nzako." 18 Bantu bonse bana ona chogunda na kaleza, ndipo bana nvela kulila kwa lipenga, nakuona chusi ku lupili. Pamene bantu bana ona ichi, bana yopa nakuimilila patali. 19 Bana kamba kuli Mose, "Kamba na ise, ndipo tiza mvela; koma osa leke Mulungu ati kambise, olo tizafa." 20 Mose anakamba ku bantu, "Osa yopa, chifukewa Mulungu abwela kukuyesani kuti ulemu wake unksle muli imwe, kuti musa chimwe." 21 Chakuti bantu bana imilila patalu, na Mose anayend kumu dima kwa mene Mulungu anali. 22 Yehova anakamba kuli MOse, "Ivi ndiye vamene uza bauza baku Isilayeli, imwe mweka mwana kuti naku kambisani chokela ku mwamba. 23 Simuzazi pangila milungu ku chokela ine, milungu za siliva na golide. 24 Mini pangile guwa youmba na doti, ndipo muza pelekelapo nsembe zo shoka, vopeleka vamu nsonkano, mbelele zanu na ng'ombe. Mu malo yali yonse mwamene naku dalisani. 25 Ngati muzani pangila guwa ya myala, osa sebenzesa myala yo juba, ngati wa sebenzesa zintu zaku minshi wayi ononga. 26 Usapite pa guwa yenga mo kwela, kuti kosa vala kwako kunga onekele."
1 Manje ivi indiye vochita vamene uza pasa kuli beve: 2 Ngati wagula mu Heberi wanchito, uyo afunika kusebenza zaka sikisi, ndipo mu chaka cha namba seveni afunika kuyenda omasuka kosa lipila chili chonse. 3 Ngati anabwela eka, afunika kubwelela eka; ngati ni okwatila, na mukazi wake afunika kuyenda naye momasuka. 4 Ngati bwana wake anamupasa mukazi ndipo anamubalila bana bamuna olo bakazi, mukazi na bana bazankala ba bwana wake, ndipo afunika kuyenda omasuka eka. 5 Koma ngati wanchito poyela akamba, '' Nikonda bwana wanga, mukazi wanga, na bana banga; siniza choka omasuka,'' 6 mwaichi bwana wake afunika kumuleta kuli mulungu. Bwana wake afunika kumuleta pa komo, bwana wake afunika kumubo ola kukwatu na chobo olela. ndipo wanchito azamu sebenzela mu umoyo wake onse. 7 Ngati muntu agulisa mwana wake mukazi monga wanchito mukazi, safunika kuyenda monga wanchito mwamuna amachitila. 8 Ngati sakondwelesa bwana wake, wamene anali kufuna kumupanga mukazi wake waku mbali, amugulise futi. Koma si ovomelezewa kumu gulisa ku bantu bakwinangu. si ovomelezeka, chifukwa apwanya lamulo yomusunga mwaboza. 9 Ngati bwana wake afuna kuti ankale mukazi wa mwana wake, afunika ku musunga monga chabe ni mwana wake mukazi. 10 Ngati akwatila mukazi winangu mwine wake, safunika ku mutana vakudya, vovala, olo ufulu wachikwati chake. 11 Koma ngati samupasa ivi vintu vitatu, amuleke ayende omasuka osalipilako ndalama iliyonse. 12 Ngati aliyense amenya muntu nakumupaya, uyo muntu afunika kupaiwa naeve. 13 Koma ngati muntu uyo sanachitile dala, inali chabe ngozi, nizapanga malo kwamene angatabile. 14 Koma ngati , muntu achitila dala mokalipa nakupaya muntu wamene amankala naye pafupi, mufunika kumutenga, olo pa guwa ya mulungu, kuti afe. 15 Aliyense wamene amenya batate bake olo bamai bake afunika ku paiwa. 16 Aliyense wamene aba muntu - olo wamene amuba amugulisa, olo uja muntu apezeka mu manja yake - uja wamene anamuba afunika ku paiwa. 17 Aliyense wamene atembelela atate bake olo amai bake afunika ku paiwa. 18 Ngati bantu bamenyana ndipo umozi amenya muzake na mwala olo kofi, na uja muntu sanafe, koma azichita ndipo afunika ku pumulako pan'gono; 19 ngati apola akwanisa nakuyenda na nkoli, muntu ana mumenya afunika kulipila chifukwa cho mutaila ntau; nakumulipila pa ntau yopolelatu. Koma muntu uyu alibe mulandu opaya muntu. 20 Ngati muntu amenya wanchito wake mwamuna olo wanchito wake mukazi na nkoli, ndipo ngati wanchito afa. Mwaicho muntu uyo afunika kupasiwa chilango. 21 Koma, ngati wanchito akali moyo siku imozi olo yabili, bwana wake safunika kumupasa chilango, kusankala na wanchito omusebenzela ndiye chiza nkala chilango chake. 22 Ngati bantu bamenyana naku chita mukazi ali na mimba yabwela yachoka, koma alibe vilonda vilivonse, muntu wamene apanga mulandu afunika kulipila monga mwamene mwamuna wamukazi afunila, ndipo afunika kulipila monga mwamene oweluza bakambila. 23 Koma ngati kuli chilonda chikulu, wamene amupanga chilonda naeve afunika kumupanga chilonda. 24 Linso pa linso, lino pa lino, kwanja pa kwanja, kwendo pa kwendo, 25 mbonje pa mbonje, chilonda pa chilonda. 26 Ngati muntu atema mulinso ya wanchito wake mwamuna olo wanchito wake mukazi nakui ononga, afunika kumuleka aende omasuka kuti yankele malipilo ya linso. 27 Ngati achosa lino ya wanchoito wake mwamuna olo wanchito wake mukazi, afunika kumuleka wanchito aende momasuka kuti yankele malipilo ya lino. 28 Ngati ngombe yachita vilonda muntu mwamuna olo muntu mukazi mpaka afa. Ngombe iyo ifunika kutemewa, na nyama yake si ifunika kudya; koma mwine wa ngombe safunika kupasiwa mulandu. 29 Koma ngati ngombe inali namukalidwe opanga bantu vilonda kodala, namwine wake anauziwapo kudala koma sana ivalile mukati, na ngombe yapaya muntu mwamuna olo muntu mukazi, iyo ngombe ifunika kutemewa, na mwine wake afunika kupaiwa. 30 Ngati malipilo yafuka pa umoyo wake, afunika ku lipila monga mwamene afunikila kulipilila . 31 Ngati ngombe yapanga vilonda mwana mwamuna wa muntu olo mwana mukazi wamuntu, mwnine wa ngombe afunika kuchita mwamene lamulo iyi ifunila kuti achitile. 32 Nagti ngombe yapanga vilonda wanchito mwamuna olo wanchito mukazi, mwine wangombe afunika kulipila siliva ili sate, ndipo ngombe ifunika kutemewa. 33 Ngati muntu asegula pamugodi, kapena muntu akumba chimugodi koma sanavalepo, ngómbe kapena bulu ikagwelamo mwamene, 34 mwine wa uja mugodi afunika alipile chifukwa cha ngozi iyi. Ayenela kumupasa ndalama mwine wauja nyama yamene yafa, na ija nyama yamene yafa izankala yake. 35 Ngati ngombe ya muntu yapanga vilonda ngombe yamuzake mpaka yafa, mwaicho bafunika kugulisa ngombe yamoyo nakugabana ndalama, ndipo bafunika kugabana ngombe yafufa. 36 Koma ngati nkani inali yozibika kuti ngombe inali namukalidwe opanga vilonda ku dala, ndipo mwine wake sani ikomele mukati, afunika kulipila ngombe pa ngombe, na ngombe yokufa izankala yake.
1 Ngati muntu aba ng'ombe olo mbelele nakuipaya olo kuigulisa, azafunika kulipila ng'ombe zilifaivinpali ng'ombe imozi, na mbelele zili fo pali mbelele imozi. 2 Ngati kawalala bamu peza akuba, bakamunganeya abwela afa, ninshi kulibe mulandu wamene apanga. 3 Koma akamu paya ngati kazuba kachoka, ninshi apanga mulandu amu paya. Kawalala azafunika kubwezelapo.mngati alibe vili vonse ninshi nikumju gulisa chifukwa chau kawalala wake. 4 Chinyama chikapezeka chikali moyo mu manja yake. inga nkale ng'ombe, kapena bulu olo mbelelele, azafunika kulipila kabili. 5 ngati mwanamuna adyesa vobeta vake mu munda yake noku lekelela chinyama chake, chayenda kudya mu munda ya mwamuna winangu, azafunika kubwezelapo kuchosa mu munda wake vamushe maningi. 6 Mulilo ukayaka naku fika uma saka yolongwe ya mbeu, olo yo yimilila, olo munda wadyeka, wamene ayamba mulili azafunika kulipila mulandu 7 Ngati mwamuna asungaiza ndalama olo katundu kuli muntu wamene ankala naye pafupi kuti amusungileko, ngati bamu bela mu nyumba uja mwamuna, kawalala baka mupeza, kawalala uja azafunika kulipa kabili. 8 ngati kawalala sanapezeke, mwine wa nyumba azafunika kubwela pamenso ya uweluza kuona ngati agwilapo na kwanja yake. 9 ngati niku shusha pali katundu, kapena inkale ng'ombe, bulu, mbelelele, chovala, olo chili chonse chizasoba muntu azakamba, "Ichi ni chang," ngati babili balilila chinto chimozi bazafunika kubwela kuli boweluza. Mwamuna azapezeka na mulandu azafunika kulipila kabili kuli wamene ankala naye pafupi. 10 Ngati mwamuna asongisa bulu, ngómbe, mbelele, olo chinyama chili chinse kuli wamene ankala naye pafupi, ngati chafa olo chazi chita olo chanyamuliwa kulibe muntu alionse kuonako, 11 bonse babili bazafunika kupanga chipangano kuli Yehova, kapena umozi agwila olo sanagwilepo muli katundu yawamene ankala pafupi naye. Mwine wake afunika ku vomela ivi, namuzake sazafunika kubwezelapo. 12 ngati banamu bela, azafunika amubwezele mwine. 13 ngati chinyama chabwela nicho ng'ambiwa muzidusa, lekani mwamuna uyo achilete chinyama kutibchinkale cho'oneselako. Sazafunika kulipila chamene chenze chinana ng'ambiwa. 14 Ngati mwamuna abwelelka chinyama kuli wamene ankala naye pafupi nobwela kuzichita olo kufa kulibe mwine ku mkale nacho, uja mwamna azafunika kubwezelapo. 15 koma ngati mwine analinacho, muzake sazafunika kulipila vili vonse; ngati chinyama chagenesewa nchito chizalilipilwa mtengo ungenesewelako nchito. 16 Ngati mwamuna anyengelela namwali, nakugona nainve, azafunika alipile lobola yokwanila enve kuti amupange mukazi wake. 17 Batate bake baka mukanila kumu pasa kwanja yake, azafunika kulipila lobola yokwanila mutengo wa namwali. 18 Musaleke mfwiti inkale moyo. 19 Wamene azagona na chinyama azafunika kumupaya. 20 Wamene azapeleka nsembe kuli mulungu winangu kuchoselako Yehova azafunika kumu onengelatu. 21 Musaluvyane mulendo olo kumuvutisa, chifukwa naimwe munali balendo mu malo ya Egpto. 22 Musavutise mukazi wamasiye olo tate alibe mwana. 23 Mukaba vutisa, baza lilila kuli ine niza nvela kuitana kwabo. 24 Kukalipa kwanga kza oneka, niza kupayani na panga; bakaz banu bazankala bamasiye, anso bana banu bazankala balibe batate. 25 Muka congolesa ndalama pakati pa bantu banga bovutika, usamufakileko pindu. 26 Ukapempa chovala mulonjezo kuli wamene unkala naye pafupi, uza funika kumu bwezela pamene kazuba kakalibe kungena, 27 chifukwa ndiye chovinikila chamene alinacho; nicho vala chake chapa mubili wake. nichani chinangu chamene anga gonemo? akaitana kuli ine, nizamu nvela, ine ndine wachisomo. 28 Musanyonze ine,Mulungu, olo kutembelela basogoleli banu. 29 Musa gwililile vopereka vanu kuchokela kuvo kolola vanu olo chopangila vinyu. Muzafunika kunipasa bana banu bamuna boyamba. 30 Muzafunika kuchita vimozi na ng'ombe yanu na mbelele yanu. Masiku yali seveni vizasala na mai wao, koma sikuya nambala eyiti muzani pasa ine. 31 Muzankala bantu bopatulika baine kuchoka apo simuzdya nyama yopaiwa mu munda. Muzapasa ma galu.
1 Usapase utenga oipa pali munthu aliyense. Osatandizana na munthu oipa nakunkala mboni yosakulupilika. 2 Usakonke chigulu kuchita voipa, kapena kusunga umboni wosushana na vazoona. 3 Usalangize kusanka ku muntu osauka ku mulandu wake. 4 Ukakumana na ng'ombe olo bulu ya mudani wako yasoba, ufunika kuibweza ku mwinewake. 5 Ukaona bulu wa muntu wamene akuzonda yangwela pansi pamozi na katundu, usamusiye uyo muntu. ufunika kumutandiza pamozi na bulu wake. 6 Osalimbisa mulandu wa munzako wosauka. 7 Osakonka benangu mu kupanga zoipa zonamizila, ndiponso osapaya muntu wakayele kapena olungama, chifukwa sinizatandiza muntu oipa. 8 Osatenga chovalisila mulandu, chifukwa chovalisila mulandu chimavala menso ya oona, nakuwononga mau ya bathu ba bachilungamo. 9 Usavutise mulendo, chifukwa uziba umoyo wa mulendo, chifukwa munali balendo mu Ziko ya Ejipito. 10 Mu zaka zili sikisi muzashanga mbeu mumalo yanu na kukolola vochokamo. 11 Koma mu chaka cha seveni muzauleka kuti ugonele, kuti osauka mwa imwe nawo badye. Vamene bazasiya, nyama zamusanga zizadya. Muzachita chimozimozi ndi munda wanu wa mpesa ndi munda wa azitona. 12 Mu masiku yali sikisi muzachita nchito yanu, koma pa siku ya seveni muzipumula. Muchite ichi kuti ng'ombe zanu na babulu banu bazipumula, kuti mwana wake mwamuna wa kapolo wako makazi na mulendo aliyense apumule na kuyamba futi. 13 Nvesesani kuli vili vonse vamene nakuuzani. Musakambe pa mazina ya milungu inangu, kapena mazina yawo kunveka mukamwa mwanu. 14 Muyenda na kunkala na madyelelo katatu mu chaka. 15 Muzisunga chikondwelelo cha buledi ilibe vofufumulisa. Mwamene nakuuzilani, muzadya bread ilibe vofufumulisa masiku yali seveni. Pa ntawi ija, muzaonekela kwa ine mu mwezi wa Abibu, mucholinga chinafakiwa. Unali uno mwezi wamene munachoka ku Ejipito. Koma musaonekele pamenso mulibe kantu. 16 Muzisunga chikondwelelo cha kukolola, na vipaso voyamba va nchito yanu yamene munashanga mbeu mu minda yanu. ndiponso muzisunga chikondwelelo cha kubwelesa pamozi pa kusila kwa chaka, mukaika pamozi vokolola vanu va mumunda. 17 Bonse ba muna bazionekela kuli Ambuye Yehova katatu mu chaka. 18 Usapeleke magazi ya nsembe yonipangila pamozi na buledi ili nachotupisa. Zamafuta kuchokela ku nsembe ya chikodwelelo changa zisankale usiku wonse kufikila kuseni. 19 Ufunika kubwelesa vosankidwa vipaso voyamba kuchoka ku malo yanu kubwelesa kunyumba kwanga, nyumba ya Yehava Mulungu wako. Musapike mbuzi in'gono ikhali na mukaka wa bamai bake. 20 Nizatuma mungelo pasogolo pako kuti akuchingilize munjila, nakukubwelesa ku malo yamene nakukonzela. 21 Umunvesese iye ndi kumunvelela. Osamukalipisa, chifukwa sazakukulukila voipa vako. Zina yanga ili pali eve. 22 Ngati uzanvelela mau yake na kuchita vonse vamene nakuuza, ndipo nizankala mudani wa badani bako ndiponso nizasausa wokusausa. 23 Mungelo wanga azayenda pasogolo pako nakukubwelesa kwa Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, ndi Akanani, ndi Ahivi, ndi Ayebusi; ndipo nizabaononga. 24 Usabelamine milungu yawo, kuyapembeza, kapena kuchita vamene bachita. Mumalo mwake, ufunika kuvitaya vonse naku pwanya vi pilala vawe vamyala mu mapisi. 25 Ufunika kupembeza Yehova Mulungu, ndipo azadalisa buledi yako na manzi. Nizachosa matenda pakati panu. 26 Sikuzankala mukazi osabala kapena kutaya mimba in malo mwanu. 27 Nizakupasa umoyo wautali. Nizatuma manta yanga pali iwo kwamene ku malo uyenda. Nizapaya bantu bonse bamene ukumana nawo. Nizalengesa badani bako kukuonesa mbuyo zabo mwamanta. 28 Nizatuma mavu pasogolo pako yamene yazabachosa ba Ahivi, Akanani, ndi Ahiti pamenso pako. 29 Sinizabachosa pamenso pako mu chaka chimozi, kuti malo yaka kanidwe, chifukwa nyama zamusanga zingankale zambili kwa imwe. 30 Koma, nizabachosamo pan'gono pan'gono kuchoka pamenso panu kufikila pamene muzankala bambili na kunkala malo yanu. 31 Nizakonza malile yanu kuchokela ku nyanja yofiira naku nyanja ya Afilisti, ndi kuyambila ku chipululu kufikila ku munana wa Euphrates. Nizakupasa iwe upambane mu malo wonkalamo. muzabachosamo pa sogolo panu imwe beka. 32 Musapange chipangano nabeve olo na milungu yawo. 33 Sibafunika kunkala mu malo yanu, chifukwa bangalengese kuti mwanichimwila ine. Mukapembeza milungu yawo, ichi chizankala chokuteyani.
1 Pamene Yehova anakamba kuli Mose kuti, "Nyamukani bwelani kuli ine - iwe, Aroni, Nadabu, Abuhi, na sevente asogoleli wa Isreali, anso munipembeze patali. 2 Mose yeka angabwele pafupi naine. Imwe benangu usabwela pafupi, na bantu basakwele pamozi naye." 3 Mose anayenda nakuwuza bantu mau na malamulo yonse ya Yehova bantu wonsee anayanka na mau yamozi kuti, "Tizachita mau yonse yamene Yehova anakamba." 4 Pamene apo Mose analemba yonse mau ya Yehova kuseni seni, Mose anamanga guwa munyansi mwalupili na kukonza bwino mapilala yamyala yali twelufu, pakuti iyimilile mitundu twelofu ya Isilayeli. 5 Anatuma anyamata baku Isilayeli kupeleka nsembe yoshoka na kupeleka vopeleka va umozi va ng'ombe zolimila za Yehova. 6 Mose anatenga magazi pakati na kuyika muma besini; iye inangu inasalapo anawaza pa guwa 7 Anatenga buku yachi pangano naku ibelenga mukwana ku bantu. Banakamba kuti, " Tizachita vonse vamene Yehova akamba, Tizankala onvelela." 8 Pamene apo Mose anatenga magazi naku yatila momwaza pa bantu. Anakamba kuti. "Aya ndiye magazi yachi pangano chamene Yehova anapanga na imwe. pokupasni ichi chipangano na mau yonse aya. 9 Pamene Mose, Aroni, Nadab, Abihu, na basogoleli sevente baku Isilayeli banakwela pamwamba pa lupili. 10 Banaona Mulungu wa Isilayeli. Pansi pamapazi yake panali poyanzika musewu yopangiw namwala ya safile, yo'oneka kuwala monga mutambo wamene. 11 Mulungu sanapayepo olommumozi mwa asogoleli wa Isilayeli. Anaona Mulungu, koma anadya nakumwa, 12 Yehova anakamba kuli Mose kuti, "Bwela ukwele kumwamba kwa ine ku lupili anso unkale pamene pano. Ine nizakupasa myala yosema na malamulo na chilamulo yamene nalemba, pakuti ukabapunzise." 13 Pamene apo Mose anatulukila kunja pamozi nawotandiza wake Yoshua anso anakwela kulupili ya mulungu 14 Mose enze anakamba kuli basogoleli kuti, Nkalani pano mutiyembekeze mpaka tibwele kuli imwe. Aroni na Hara ali pakati pa imwe, ngati aliyense wa imwe ana dandaulo, mulekeni ayende kuli benve." 15 Kuchoka apo anakwela kumwamba ku lupili na makumbi unayivinkila 16 Ulemelelo wa Yehova unankazikika pa lupili wa Sinayi. na makumbi yanayi vininkila masiku yali sikisi. Pasiku ya namba seveni anaitana Mose kuchokela mukati mwakumbi. 17 Kuoneka kwa ulemelelo wa Yehova kunali monga mulilo ukali kwambili pamwamba pa lupili mumenso mwama Isilayeli. 18 Mose anangena mukati mwakumbi naku yenda pamwamba pa lupili. Anakala pamwamba pa lupili masikun fote muzuba na usiku.
1 Yehova anakamba kuli Mose kuti, 2 "Bauze ba Isilayeli batenge chopeleka changa kuchokela kuli muntu aliyense alimbikisiwa namutima yofuna. Ukazini landilako ivi vopeleka. 3 Ivi ndiye vopeleka vamene ufunika kulandila ku choka kuli benve: golide, siliva, na mukwa; 4 bulu, pepo, na nyula yafila, nyula yopepuka, usako uso mbuzi; 5 Vikumba va nkosa vopanga na ledi na vopeleka mpapa za ku mendo; mitengo ya akasiya. 6 Mafuta ya nyali ya mumelo yoyela; vosukila va mafuta yozozela na vonunkila bwino; 7 Miolo ya myala na inangu yomutengo yapatali kuti backite pa efodi na pa chifuba. 8 Balekeni banimagile malo yopatulika kuti ukankle pa kati pao. 9 Ufunika kumanga monga miza kuonesa mu maganizo ya kachisi na vonse vomanila. 10 Bazafunika kupanga likasa ya mitengo wa akasiya. Mu utali yo kwanila zibili na hafu yama kubiti; mukufupika kusake muzankala imozi na hafu; nakutalimpa kwake muzankal kubiti imozi na hafu. 11 Ufunka kuyivininkila mukati na kunja na golide yo tuba, ndipo ufunika upange chovininkilako cha golide chozungulukila pa mwamba pake. 12 Ufunika ku kuponya mpete zili folo za golide wake, nakuika pa mendo ili folo likasa na zibili mpete ku mbali yake imozi, na zibili mpete kumbali inangu. 13 Ufunika kupanga mitengo yo nyamulila ya akasiya na kuyavalika golide. 14 Ufunika kuika mitengo yonya mulila mu mpete mumbal mwa likasa, kuti ikanyamuliwe likasa. 15 Mitengo yonya mulila zizafunika isalile mu mpete ya likasa; sizifunika ku ichosako. 16 Ufunika kuika mukati mwalikasa muli mboni za chipangano chamene nizakupasa. 17 Ufunika kupanga chovalila chochingilila ya golide yotuba. Mu utali wake inkale ibili na hafu makyubiti , namu ufupi wake kyubiti imozi na hafu. 18 Ufunuka upange yabili ma berubi ya golide yomenya yamumbali yabili yazovalila cho chongiliza. 19 Panga imozi kerubi osilizila chovalila cholingana na inangu kerubi kosilizila kumbali inangu. Ifunika ipangiwe monga chintu chimozi na chovalila chochingiliza. 20 Akerubi afunika ku tambasula mapapiko yawo pamwamba naku vimba chovala chochingilza akerubi afunika kuyanganana nakugana pakati pa chovala cho chingilza. 21 Ufunikila kuika chovalila chochingila pamwamba pa likasa, ndipo ufunika kuika mukati mwa likasa mboni zachi pangano chamene nikupasa. 22 Nipali likasa pamene nizakumana naiwe. Niza ka kamba naiwe kuchokela ku malo yanga ya kumwamba pa chovalila pa chochingiliza. chizankala ku chokela pakati pa makerubi abili yali pamwamba pa likasa ya mboni yamene nizakambapo malamulo yonse nizapasa yaba Isilayeli. 23 Ufunika ku panga tebulo ya mitengo ya akesha. Mu utali mwake munkale ma kyubiti yabili, mu ufupi wake mufunika mukono umozi, na mu uatali wake mufunik munkale na hafu. 24 Ufunika kui valika na golide yotuba nakuika malile ya golide yozunguluka pamwamba. 25 Ufunika kupanga felemu yozunguluka monga kwanja imozi mu ufupi mwake, na chozungulila malile ya golide yozungilila pamwamba. 26 Ufunika kupanga mpete zili folo za golide na kuzigumanisa mpete mumakona yali folo, kwamene kuli mendo yali folo. 27 Mpete zifunika kugwilisisa ku mafulemu kuti kupezeke malo ya mitengo yo nyamulila, kuti tabulu inyamulike. 28 Ufunika kupanga mitengo yonyamulia zochokela ku mitengo ya akesha kuvalika na golide kuti tebulu inyamuliwe pamozi nazo. 29 Ufunika kupanga ma dishi, ma sipuni, vopakulila, na mambale yosebenzesa chosposilo chkumwa uyapange ya golide yotuba. 30 Ufunika kabili kabili kuika mukate wapamenso panga pa mwamba pa tebulo ili pasogolo panga. 31 Ufunika ku panga poika nyali ya golide yotuba yomenyewa. Choikapo nyali chipangiwe na chonkalila chake na chogwilila. Ma kapu, chapnsi pake monga cha matepo maluba yake yopangiwa na chintu chimozi. 32 Misambo zili sikisi zifunika ku chokela mumbali mwake-misambo zitatu zichokela ku mbali inangu, na misambo yomikililapo nyali ichokele kumbali kwinangu. 33 Misambo yoyambilila ifunikila kunkala na makapu yatatu yonomangiwa monga katungulume, na chapansi monga chama tepo na luba, na makapu yatatu yopangiwa monga katungulume ali ku misambo yinangu, a chapansi monga matepo na luba chifunika kunkala chimozi mozi pa vonse vili sikisi mpando zochokela poika nyali. 34 Poika nyali pamene, paka nsimbi ka pakati, pafunika pa nkale ma kapu yali folo yopangiwa monga kutungulume wa maluba oshuma, ponkala matepo na maluba. 35 Pafunika kunkala chapansi monga cha matepo pansi ya gawo yoyambilila-yopanga monga chimozi, na chapansi monga chamatepo yogawa ya chibili ya misambo-nayenve yo pangiwa monga chimozi munjila yamene iyi kufunika kunkale chapansi monga cha matepo pansi pa chigawo cha chitatu ch misambo, yopangiwa monga chintu chimozi. kufunika kunkale chimozinmozi pa misambo yonse ili sikisi yochokela mukati mwa poika nyali. 36 Ponkalapo chapamsi monga cha matepo na misambo ifunika yonse inkale chintu chomiz, chimozi chomenyewa gawo ya nchito ya golide yotuba. 37 Mufunika ku panga choikapo nyali na nyali zake zokwanila seveni, na kuikapo nyalizake kuwala kuzizhokela kwa mene. 38 Vogwilila na mateleyi yake yafunika ku panga na golide yotuba. 39 Usebenzese talente imozi ya golide yotuba kupanga ponkala nyali na vonse vosebenzesa vake. 40 Usimizile kuti vamangiwa monga mufanizo yamene ulangiziwa pamwamba pa lupili.
1 Mufunika kupanga chalichi ndi nsalu zili teni zopangidwa bwino ndi zobuluwa, zo fililla, na zo fiila za tonje zili na vo oneka monga Akerubi. Iyi izankala chito ya bamene baziba nchito. 2 Mu utali wa nsalu iliyonse inkhale na mamita yali twenti eiti, muufupi inkhale mamita folo. Nsalu zonse zinkale zolingana. 3 Nsalu zili faivi zifunika kugwilana pamozi. 4 Mupange vokolobekamo nsalu ya bulu mumbali mo silizila nsalu imozi. Mwamene umo, mufunika kuchita monga mwanene mwachitila mu nsalu ya chibili. mufunika kupanga vokolobekamo vili fifite mu nsalu yo yamba, 5 ndiponso mupange vokolobekamo vili fifite, mu nsalu yosiliza. Chitani ichi kuti vokolobekamo viyanganane. 6 Mufunika kupanga ngowe ya golide na kuilundikiza ku nsalu pamozi kuti chalichi inkale yogwilizana. 7 Mufunika kupanga nsalu za sisi ya mbuzi ya tenti pamwamba pa chalichi. Mufunika kupanga nsalu zili leveni. 8 Utali wa nsalu iliyonse ifunika kunkala feti, na muufupi mwa nsalu iliyonse ifunika kunkala ma cubiti yali folo. Nsalu nzonse zili Leveni zifunika kulingana. 9 mufunika ku gumiza nsalu zili faivi kuli zinzake. mufunika kupampikiza nsalu zili sikisi kusogolo kwa tenti. 10 Mufunika kupanga vili fifite vokolobekamo kwamene kusilila nsalu yo yamba. 11 Mufunika kupanga fifite zamukuwa nakuzifaka mokolobekamo. Ndipo mulundikize tenti pamozi kuti inkale imozi. 12 Zosalilako za nsalu, ndi nsalu yosalilako ku tenti, ifunika kuikolobeka kumbuyo kwa kachisi. 13 Kufunika kunkala mukono umozi wa nsalu kumbali kwina, ndi mukono winangu kumbali inangu. yamene izasalilako yamuutali mwa nsalu ya mutenti muikolobeke pamwamba kumbali kwa chalichi kumbali imozi na kumbali kwinangu, mu kuichingiliza. 14 Mufunika kupanga kachisi ndi chopimba zikopa za nkosa redi, na chopimba cha akatumbu pamwamba pake. 15 Mufunika kupanga yoimilila matambwa yochokela ku mutengo wa Akesha pa kachisi. 16 Utali wake wa tambwa imozi ifunika kunkala teni kubiti, ndipo muufpi mwake inkale imozi na hafu kubiti. 17 Kufunika misunkwa ibili pa mu fulemu yo lundikizila ma fulemu kuli inzake. Mufunika kupanga kupanga ma fulemu ya kachisi muli iyi njila. 18 Mukapanga ma fulemu ya kachisi, mufunika kupanga twenti mafulemu ya kumbali yaku mumwela. 19 Mufunika kupanga fote maziko ya siliva pansi pa fulemu yali twenti. Kufunika kunkala maziko babili pansi pa fulemu yoyamba mu misukwa yake yabili, ndi maziko yabili pansi pa yenangu mafulemu ya vibili vi misukwa. 20 Kumbali yachibili ya kachisi, kumbali yaku mupoto, mufunika kupanga ma fulemu yali twenti , 21 ndi maziko yali fote ya siliva. Kufunika kunkala maziko yabili pansi pa mafulemu, maziko yabili pansi pa inangu fulemu, na kuyendelela. 22 Za Ku mbuyo kwa kachisi ku mbali kwa kumazulo, mufunika kupanga sikisi fulemuzi. 23 Mufunika kupanga ya bili ma fulemuzi ku mbuyo kukona kwa chalichi. 24 Aya mafulemu yafinika kunkala yosiyana kunyansi, koma yolundikana pamwamba pa vimbango volingana. Ifunika kunkala sochabe kumbuyo kwa makona. 25 Kufunika kunkala eiti mafulemu, pamozi na chapansi cawo siliva. Pafunika kunkala sikisitini mumaziko monse, maziko yabili pansi pa inangu fulemu and kuyendelela. 26 Mufunika kupanga mitanda ya mutengo wa Akesha-faivi yama fulemu kumbali kwina kwa kachisi, 27 faivi mitanda ya ma fulemu kumbali kwina kwa kachisi yaku mazulo. 28 Mpindi pakati pa mafulemu, ndiye kuti, hafu pamwamba, ifike kuchoka kosilizila ndi kosilizila. 29 Mufunika kuvinikila ma fulemu ndi golide. Mufunika kupanga mphete zabo za golide, kuti izo zitumikile mwa mitanda, ndipo mufunika kuvininkila ndi golide. 30 Mufunika kuyamba kachisi na pulani yamene munaonesedwa pa lupili. 31 Mufunika kupanga nsalu yabulu, yo pepo, ndi ya bafuta ya tonje, ndi nyula yabwino, yolingana monga Akerubi, nchito ya woiziba nchito mwamuma. 32 Mufunika kuikolobeka pa ma pila yali folo ya mutengo wa akesha yovininkiliwa na golide. Aya ma pila yafunika kunkala na vongwililako va golide yoikidwa pali folo pa maziko ya siliva. 33 Mufunika kukolobeka nyula pansi pa kilasipu, mufunika kubwelesa mu likasa ya Umboni. 34 Mufunika kuika chotetezelapo pa likasa ya umboni, yamene yali mumalo yopatulika. Mufunika kufaka tebulo panja pa nyula. 35 Mufunika kufaka choikapo nyali chilanganane ndi tebulo kumbali ya kumwela ya chalichi. Tebulo ifunka kumbali yaku mupoto. 36 Mufunika kupanga chokolobekamo pa komo ya tenti. Mufunika kuipanga kuchokela ku bulu, pepo, ndi zopangila za sikaleti ndi nyula yotelela kwambili, nchito ya oika maula pa zovala. 37 Pa chokolobekamo, mufunika kupanga faivi mapilala ya akesha na kuyavininkila ndi golide. Chogwilila chake chifunika kunkala cha golide, ufunikila kuika maziko yokwanila faivi ya bulonzi.
1 Muza panga guwa wamutgengo wakasiya, faive mikono utali na faivi mikono muku tambala. Guwa inkale mo linganzia na mikono itatu ku mwamba. 2 Uzafunika kupanga vo ikilako koma kona yake yali folo yopalana na nsengo za ng'ombe. Nsengo ziza pangiwa chimozi na guwa, ndipo muzai vala na bronze. 3 Mupange vo sebenzesa pa guwa: mpolo ya milota, nama fosholo, mabeseni, foloho ya nyama, nama pani yapa mulilo. upange vo sebenzesa na bronze. 4 Mupange sefa ya guwa, naku ika pamozi kwa bronze. Upange mpete ya bronze sefa yama kona folo. 5 Uzaika sefa pansi pambali pa guwa, pakati poyenda panis. 6 Uza panga mitengo ya wakasiya, nakuyi vininkila na bronze. 7 Mitengo izo zika ikiwe mu mpete, namutengo ku mbali ibili ya guwa, kuyi nyamula. 8 Ufunika kupanga guwa yo gona pakati, yama pulanga. Uyi panga monga mwamene ninaku langizila pa lupili.. 9 Upange malo ya panja yo pempelelamo. kufunika ku nkala co lelemba ku mwela, cholelemba chosalala nyula mikono wani handiledi. 10 Vo lelemba vinkale nama pilala twente, na vapansi va bronze twente. kufunika futi ku nkale mbeza vo gwila ma pilala, pamozi na nsimbi ya siliva. 11 Munjila imozi, mbali yamkumpoto, ku nkale volelemba mikono wani handiledi mu utali wake na twente ma pilala ya bronze pansi, mbeza yo gwilila ma pilala ya siliva ntambo. 12 Pa njila ya malo ya mbali yaku mazulo ku nksle ma ketoni fifite mikono utali. ku nkale ma pilala teni na chapansi teni. 13 Mbali yaku mawa naye inkale fifite mikono mu utali malo ya panja. 14 Volelemba vaku mbali imozi yo ngenela inkale mikono fifitini utali: ku nkale ma pilala yatatu nava pansi vitatu. 15 Kumbali ina kukale volelemba mikono fifititni kutalimpa kwake. 16 Pa chipata chapabwalo pankale chi nyula kutalimpa kwake mikono twente. chi nyula chi nkale cha bulu, pepo na cha redi na tosova bwino. na chito ya votunga tunga vili imbloloidale. vinkale nama positi yanai an vapansi vinali. 17 Ma positi yonse ya capabwalo vinkale na nsa ndamina ya siliva, vogwila va siliva, na chapansi cha bronze. 18 Kutalimpa kwa chapabwalo chi nkale mikono ya wanu hundiredi, kufupika mikono fifite, nakulalika mikono faivi na vounga-tunga vabwino volelemba, pansi pali bronze. 19 Vosebenzesa vonse mu kachisi, vonse vogwilila hema ya kachisi na chapa bwalo vifunikila kupangiwa kuchokela ku bronze. 20 Ufunika ulamulile bantu ba Isireli kuti balete mafuta ya oliva, yoyela na yofiniwa, ya nyali kuti vipitilile kuocha. 21 Mu hema yokumanilamo, kunja kwa kwa chinyula chamene chili kusogolo kwa kachisi kwamene kuli likasa ya afunika kuona kuti nyali ipitilize kuyaka pa menso pa Yehova, kuyambila kumazulo kufika mumawa. ichi chifunika chizinkala sochabe kuli mibadwo yonse ya bana ba isilayeli.
1 Itana aron mubale wako na bana bake bamuna -Nadab, Abihu, Eleazar, na Ithamar - pa bana ba isreali kuti banisebenzele monga ba nsembe. 2 Ufunikila ku panga Aron, mubale wako, mikanjo yo yela kuli ine. Iyi mikanjo izankala ya ulemu wake na ulemelelo wake. 3 Ufunika ku kamba na bantu bonse ba nzelu mu mitima, baja bamene nina zuzyamo muzimu wa nzelu, kuti bapange mikanjo ya Aroni kumu yelesa kuti anisebenzele monga wa nsembe wanga. 4 Mikanjo yamene ba funika kupanga niya pa chifuba, efodi, ntambo, inkale yotungiwa, duwila,na lamba.Bafunika kupanga iyi mikanjo yo bayelesa kuli ine. Yaza nkala ya mubale wako Aron na bana bake bamuna kuti bani sebenzele monga ba nsembe. 5 Bo beza bafunika kusebenzesa nyula za bwino za golide, yo buluwa, yofilila, na yofila. 6 Bafunika kupanga efodi ya golide, yo buluwa, yofilila, na yofila na tonje, ndipo yo tungiwa bwino. Ifunika ku nkala nchito ya bantu bobeza boziba maningi. 7 Ifunika ku nkala na tudunswa to gwililila kubilio ku makona. 8 Chotungiwa cha bwino cha mumusana mwake chifunika ku nkala monga efodi, yopangiwa na nyula yo tungiwa bwino ya golide, yo buluwa, yofilila, na yofila. 9 Mufunika kutenga myala zibili nakubezapo mazina ya bana ba israeli. 10 Yali sikisi mazina yao yafunika pa mwala umozi, Yali sikisi mazina yafunika pa mwala winangu, monga mwamene bana bamuna bana badwila. 11 munchito ya muntu obeza mumwala, monga chikwangwani cha obeza, mufunika kubeza myala ibili nama zina ya bana bamuna ba isreali. Mufunika kufaka myala pa golide. 12 Mufunika kufaka myala zibili pama pewa mutu dunswa twa efodi, kunkala myala yokumbusa yehova bana bamuna ba israeli. Aron azanyamula mazina yao pamenso pa yehova pama pewa yake yabili monga chikumbuso kuli eve. 13 Mufunika kupanga vopimila va golide 14 nama cheni yabili ya golide yo yela monga ntambo, ndipo muya gwilisane na vopimila . 15 Mufunika kupanga tudunswa twapa chifuba ,kunkala chonsankilako, nchito yaoziba maningi, yopangiwa monga efodi. Ipangeni ya golide, yo buluwa, yo filila, na yofiila ya tonje, ndipo ya nyula yabwino. 16 Ifunika kunkala yo lingana. Mufunika kupanga tudunswa twapa chifuba topetekewa pabili. Inkale itali kumbali kumozi na kuvunguluka. 17 Mufunika kui ika mumalo yali fo ya myala zabwino. Mulaini oyambilila ufunika kunkala na mwala odula, topazi na nkhokwe. 18 Mulaini wa chibili ufunika kunkala na emarald, safule, na diamondi. 19 Mulaini wachitatu ufunika kunkala na jakini, na gate, ndipo,ameri. 20 Mulaini wanamba fo ufunika kunkala na beryl, na onyx, ndipo na jasper. Yafunika kuikiwa pacha golide. 21 Myala zifunika kunkala moyendelana nama zina yabana bamuna ba israeli. Zifunika ku nkala monga zobeza mpete, zina iliyonse kuimililako umozi pali mitundu ili 12 ya bana ba israeli. 22 Mufunika kupanga choika pachifuba macheni yali monga natmbo, zotungiwa monga chinto ya golide ya bwino. 23 Mufunika kupanga mphete zibili za golide ku choika pachifuba nakuika ku malile ya chaika pa chifuba. 24 Ndipo mufunika kuika macheni yabili ya golide ku malile ya choika pachifuba. 25 Mufunika kuika malile yenangu yabili yotungiwa ku vopimilako vibili. Ndipo mufunika ku tu ika pama pewa ya efodi ku sogolo. 26 Mufunika kupanga mpete zibili za golide, ndipo mufunika kuika pama kona yabili yapa chapachifuba, kumbali pafupi na malile. 27 Mufunika kupangilapo mpete zibili za golide, ndipo mufunika kuizi ika pansi pama pewa pasogolo pa efodi, pafupi na chotunga chapamwamba pa musana wa efodi. 28 Bafunika kumanga choika pachifuba kusebenzesa mpete zake ku efodi ndi chobbuluwa, kuti chinkale chogwililila pamwamba pa efodi chotunga chamu musana. Ichi ni chifukwa chakuti chaika pachifuba chinkale chogwililila ku efodi. 29 Pamene Aron angena mu malo yo yela, afunika kunyamula mazina ya bana banuna ba israeli pamwamba pa mutima wake pa choika pachifuba chosankilapo , monga chikumbuso choyendelela kuli yehova. 30 Mufunika kufaka urim na thummim pachoika pachifuba chonsankilapo, kuti vinkale pamutima wa Aron pamene ayenda kuli yehova. mwaichi Aron azayamba kunyamula ntau zonse vinto vosankilako va bantu ba israeli pamutima pake kuli yehova. 31 Muzapanga ntambo ya efodi yobuluwa yonse yotunga. 32 Inkale na posengulila pakati kumutu, posengulila pafunika kunkala po tungiwa kumbali kuzungulusa kuti pasa n'gambike. Iyi inkale nchito yaotunga. 33 Kunyansi, mupange vidindo vo buluwa, vo filila, na vo fiila kuzungulusa. 34 Mabelo ya golide yafunika kunkala pakati kuzunguluka. Kufunika kunkala belo ya golide na chidindo, belo ya golide na chidindo - sochabe - kuzungulusa ntambo. 35 Ntambo ifunika kunkala na Aron pamene asebenza, kuti pokoso yake ikazimveka ngati angena mumalo yo yela muli yehova na pamene achoka. Ichi nichakuti asafe. 36 Mufnika kupanga mbale ya golide yoyela naku ibeza, monga kubeza kwachi kwangwani, '' choyela kuli yehova.'' 37 Mufunika kumatika iyi mbale na muchombo obuluwa kusogolo kwa duwila. 38 Chifunika kunkala pa mpumi pa Aron; afunika ntau zonse kunyamula mulandu wamene uli mu nsembe ya mpaso zoyela zamene ba israeli ba yelese kuli yehova. Duwila ifunika ku nkala pa mpumi pake ntau zonse kuti yehova avomele mpaso zao. 39 Mufunika kupanga mukanjo na nyula yopepuka, ndipo mufunika kupanga chikwangwani cha nyula yopepuka. Mufunika futi kupanga beoti, nchot ya otunga. 40 Kubana bamuna ba Aron mufunika kupanga mikanjo, ma beoti, na tusote ku ulemu na ulemelelo wao. 41 Ufunika kuvalika Aron mubale wako, na bana bake bamuna alinabo. Ufunika kubazoza, kubapasa udindo, nakuba yelesa kuli ine, kuti banisebenzela monga bansembe. 42 Ufunika kubapangila tumanyula twa mukati kubisa vintako vao, twamene tuzavininkila vintu voipa. 43 Aron na bana bake bamuna bafunika kuvala iyi mikanjo pamene bangena muhema yokumanilamo olo pamene bafika pafupi na guwa kusebenza mu malo yo yela. Bafunika kuchita ichi kuti basankale na mulandu chifukwa bangafe. Iyi ni lamulo yankalilila kuli Aron na bana bo badwa musongolo.
1 Manje ichi ndiye chamne ufunika kuchita kuti ubapatule pakuti bakasebenze ngati ba nsembe. Tengani ka mwana ka ng'ombe ka muna ka mozi na tubana tubili twa nkosa tulibe choipa chilichonse. 2 Buledi ilibe chotupisa, na makeke yalibe chotupisa yosakaniza na mafuta. Futi tengani vitumbuwa vilibe yisiti vokwakwasha mafuta. upange vitumbuwa kubewnzesa fulawo yabwino ya witi. 3 Ufunika kufaka mu basiketi imozi, uviletele mu basiketi, kuchoka apo uviletele pamozi na ng'ombe imuna na tumbelele tubili. 4 Ufunika peleka Aroni na bana bake bamuna na pongenela mu tenti yokumanilamo. Ufunika kusambika Aroni naba bake bamuna mu manzi. 5 Ufunika kutenga vovala naku valika Aroni kuyikapo na chikoti, mukanjo ya efodi, efodi, na chapa chifuba, kumangisa belti yamu musana yotungiwa bwino imuzunguluke tupi yonse. 6 Ufunika kuyika chovala chamumutu pa mutu pake nakuyiwa chisote choyela pamwamba pa tabani. 7 Pambuyo pake tenga mafuta yozezela nakutila pamutu pake, anso munjila iye. 8 Ufunika kubwelesa bana bake bamuna naku bavalika makoti. 9 Ufunika kuvalika Aroni na bana bake bamuna ma sashi natu ntambo mutu mwao. Nchito ya ba nsembe izankala yawo kwamunyaya mwa lamulo.Munjila iyi muzafunika kumu yika mopatulika Aroni na anyamata bake pakuti bazini tumikila. 10 Monse mufunika kubwelesa ng'ombe imuna ku chihema chokumanilamo namo, kuchoka apo Aroni na bana bake bamuna bafunika kuyikapo manja pa mutu pake. 11 Mufunika kupaya ng'ombe imuna pamensi ya Yehova pongenela mu chihema cha musonkano. 12 Ufunika kutenga magazi ya ng'ombe imuna naku ifaka pa nsengo yapa guwa nachikumo chake, chokonkapo uzafunika kutila magazi yasalapo munsi mwa guwa. 13 Ufunika kutenga mafuta yonse yovininkila liva na kidini yabili na mafuta pamozi namafuta yamene yaliko; muvishoke vonse pa guwa. 14 Koma nyama ya ng'ombe imuna, na chikumba chkayena, na matuvi, mufunika kuvishokela panja pa munzi wanu. chizankala chopeleka chpepeselako machimo. 15 Mufunika kutenga futi kankosa kamozi, anso Aroni na bana bake bamuna bazafunika kufaka manja yawo pamutu pake. 16 Ufunkinka ku kapaya ka mbelele, chokonkapo mutenge magazi yake naku waza mumbali konse kwa guwa. 17 Ufunika kujuba ka mbelele muzigawo naku kasuka vamukati na mendo yake, chokonkapo ufake vamukati, pamozi na vigao na mutu wake, 18 pa guwa. chokonkapo mu shoke konse ka mbelele. Izankala pelekelo yo shoka kuli Yehova, kafungo konunkila kabwino, pelekelo yo pangila kuli Yehova namulilo 19 Kuchoka apa uufunika kutenga nkhosa inangu, na Aroni na bana bake bamuna bafunika kufaka manja yabo pamutu pake. 20 Chokonkapo mufunika kupaya nkhosa na naku tenga magazi. Mufake kuwatu yaku kwanja ya manja, naku matu kwa bana bake bamuna yaku kwanja ya manja, naku chikumo chaku kwanja ya manja, naku chikumo chikulu chaku manja yakumendo. Chokonkapo muzafunika kumwaza magazi kumbali konse kwa guwa. 21 Uzafunika kutengapo magazi yamene yalipa guwa na kutenga mafuta yozozela yenangu, naku viwaza vonse kuli Aroni napa vovala vake,na pali bana bake bamuna na pali vovala vabo. Kuchoka apo Aroni azafunika kumu patula kuli ine, na vovala vake, bana bake bamuna na vovala vabo. 22 Uzafunika kutenga mafuta ya nkhosa, mafuta yakumuchila, mafuta yamene yavininkila vamukati, vovininkila liva, ma kidini abili na namafuta yali oali yenve, nakwanja yaku manja kwa chibelo-iye nkhosa niya bopeleka nsembe yokoselesa kuli ine. 23 Tengani buledi imozi, kamukate kamozi kopangiwa namafuta, na chitumbuwa chimozi kuchosa mubasiketi ya buledi ilibe chotupisila yamene ipezeka pamenso ya Yehova. 24 Uyenela kuyika izi mumanja mwa Aroni na Mumanja mwa bana bake bamuna muonese kuli ine monga chopeleka cha chioneselo pamneso pa Yehova. 25 Uyenela kutenga vokudya kuvchosa mumnaja mwawo nakuvishoka pa guwa pamozi na chopelekela kwa ine chopangiwa namulilo 26 Uyenela kutenga chapachifuba cha Nkhosa ya Aroni yoyikiza nakuisukusa monga chopeleka choukusa cha Yehoova kuti inkale guwa yako. 27 Muniyikile payeka nyama yapachifuba yochokela ku chokela chosukusa, na chibelo iyo ndiyer yamene nizalundilapo yansembe-ndiye vonse chifuba chamene chinasukiwa na chibelo chamene chinasonkelewapo niva Aroni nabana bake bamuna. 28 Iyi mbali izankalalila yake Aroni na bana bake bamuna. Izankala musonkano kupasa kwa Yehova kucjosa pa chopeleka chamutendele. 29 Nyula zoyela za Aroni nazo zifunika kusungila mbadwo zamene zizakonka pali yenve. Pobazoza na poba lamulila azafunika kuvala vamene ivi. 30 Wansembe wamene azatenga malo yake uchokela pabana bake, wamene amabwela chihema chokumanilamo kumutumikila ine mumalo yoyera ayenela kuvala ivo vovala kwamasiku seveni. 31 Mufunika kutenga ka nkosa konkazikilako ansembe ka kwa ine nakuika nyama yake mumanzi yobila pa malo yoyela. 32 Aroni na bana bake bamuna bafunika kudya nyama ya nkhosa na buledi yamene ipezeka mubasiketi palobela mutenti yamusonkano. 33 Afunika kudya nyama na buledi zamene zina pasiwa kuwa patulilako nakuwa nkazika pa utumikai, kuti ayikidwe papdela kwa ine. kulibe winangu aliyense wamene ayenela kudya chija chakudya, chifukwa afunika kuchiyesa nicho yeleswa kwa ine, nichosungila ine. 34 Ngati nyame iliyonse ya chopeleka chonkazikila pautumiko, kapena buledi iliyonse, chizakonkapo mufunika kuyishoka siyifunika kudyewa chifuwka yayikidwa padela kwa ine. 35 Mwanjila yiy, pakukonka malamulo yonse yamene nakulamulilani kuti kuchitila Aroni na bana bake bamuna. ya masiku seveni mufunika kuwa konzelekela iwo. 36 Siku iliyonse mufunikila kupeleleka ng'ombe imuna kuti inkale chopeleke;a chochosela machimo kukuombo ledwa. Mufunuka kuyelesa guwa pakupelekapo nsembe, anso mufunika kuzoza pakuti muipatule kwa ine. 37 Kwa masiku seveni muyenlea kopeleka ansembe yachipepeso kamba ka guwa naku ipatula kwa Yehova na guwa iza patulika mwazo'ona chakumya guwa chizapatuliwa kwa Yawe. 38 Mufunika kawili kabili kupelekapo pa guwa ssiku iliyonse tunkosa tubili twa chaka chimozi. 39 Kankosa kamozi muyenela kupeleka kuseni, nakenangu kupeleka pamene kazuba kakugwa. 40 Pamazi naka nkosa koyamba, pelekelani afa pa muyeso wa kumi ya fulawo wogayika mainigi kusakaniza na mayeso wachi folo wa kabotolo kamafuta ya oliva, anso chigawo cha folo cha kabotolo ka vinyu, monga chopeleka cha chakumwa 41 Mufunika kuleka kankosa kachibili psmene zuba ingena. Mufunika kupeleka chopeleka cha vamu munda molingana na vakuseni, anso chopeleka chacha kumwa chopalana. ivi vizachosa kafungo kabwin kwaine chopangiwa na mulilo. 42 Ivi vinyenela kunkala vopeleka voskoka va chibili chibili kupitila mumibadwo yanu yonse, oakomo ya chihema yamusonkano pameneso ya Yehova pamene niakumana na imwe kukamba naimwe pamene apo. 43 Apo ndiye pamene nizakumana na a Isilayeli; muchihema izapatulika kwaine kupitila mu ulemelelo wanga. 44 Nizapatula payeka chihema yamusonkano na guwa pakuti ivi vinkale vanga chabe. Nizayikafuti payeka Aoni na bana bake bamuna kuti bazinisebenzdela monga ansembe. 45 Ine nizankala pakati pa a Isilayeli nakunkala mulungu wao. 46 Bazaziba kuti ndine Yehova Mulungu wao, wamene anaba chosa mu ziko ya Iguputo pakuti nizinkala pakati pawo. iwe ndinoYehova mulungu wao.
1 ufunika kupanga guwa yoshokelapo vonunkila bweno. ufunika kupanga na mapulanga ya Mthethe. 2 Utali wake ufunika mikono imozi, na kufupika kwake mikono imozi. Yafunika kunkala malo yo lingana, na mu utali mikono zibili. Nsengo yake ipangiwe muchigabo chimozi. 3 ufunika kuvalapo pa guwa ya vonunkila bwino na golide yakili - pamwamba, kumbali, na nsengo yake. Ufunika kupanga malo ya malile ya golide. 4 Ufunika kupanga mpete za golide zo gwilisa kunsi kwamalile kumbali zo siyana. Na mpete zifunika kunkala na vogwililako mtego otengelako guwa. 5 ufunika kupanga mtego wa mthethe wa mapulanga, ndipo ufunika kuvi vweninkila na golide. 6 ufunika kufakapo zonunkila bweno pa guwe pali ketani ili pafupi na arki ya umboni. izankala pafupi na lidi ya ntentezo ili pamwamba ya arki ya umboni, ndiye kwamene ine nizakumana na imwe. 7 Aroni afunika ku shoka vili nakafungo kabwino lyonse kusensen. afunika kushoka aka faka nyali, 8 na Aroni ayashe nyali futi muma zulo kuti zonunkila bweno zikazipya lyonse kuli Yehova, kuli mibado yonse. 9 Koma usapeleke vina vonunkila pa guwe ya vonunkila bweno, kapena kupeleka voshoka olo mbeu yo peleka. usa tile vokumwa pa chopeleka. 10 Aroni ufunika kupanga ntetezo pa nsengo muchaka chimozi. Namulopa opelekela machimo azapanga ntetezo yake chaka chimozi pa mibado yonse. Nichopatuliwa kuli Yahwe." 11 Yehova ankamba na Mose, kukamba, 12 "Mukankala na Chipedeledwe cha Izrealile, ali ense muntu afunika kupasa malipilo ya moyo wake kuli Yehova. ufunika kuchita ichi uka siliza kubapenda, kuti kusankale chionogeko pali imwe ngati waba penda. 13 Onse wamene apendewa mu chipendelo azalipila shakeo ya hafu ya siliva, kukonka na kalemeledwe ka Shakeo ya mu malo yo yela (Shakeo ni chimozimozi na twenti gelas). Shakeo ya hafu izankala chopeleka kuli Yehova. 14 Onse wamene apendewa, kuyamba zaka twenti na pamwamba, afunika kupasa chopeleka kuli ine. 15 Pamene bantu ba pasa chopeleka kuli ine kuti pange ntetezo ku umoyo wao, bolemela bafunka kupasa nakuchilapo hafu ya shekeo, na bosauka basa pase pangono. 16 bafunika kulandila ntetezo ya ndilama kuchoka ku ba Izreali ndipo ufunika ku pasa kunchito ya tenti yo kumanilamo. Chifunika kunkala chikubuso kuli ba Izrealiti kuli ine, nakupanga ntetezo ya umoyo wanu." 17 Yehova anakamba na Mose, kukamba, 18 "mufunika kupanga baseni ikulu ya bronzi na choimilikapo cha bronzi, baseni yo sambilamo. unfunika kufaka pakati ka tenti yokumanilamo na guwa, nakufakamo manzi. 19 Aroni nabana bake bafunika kusamba manja na mendo na manzi muja. 20 koma bakayenda mutanti yo kumanilamo kapena kuyenda pafupi na guwa kuti banisebenzele mukushoka zopeleka, bafunika kusamba namanzi kuti basafe. 21 Bafunika kusamaba manja yao na mendo kuti bazafe. iyi ifunika inkale lamulo yonkalilila ya Aroni na mibado kufika kubantu bao mumibado." 22 Yehova anakamba kuli Mose, kumu uza kuti, 23 Tenga aya maspici yabwino: five handiled shakeos ya flowing myrrh, 250 shakeos yokoma - kununkila sinamoni, 250 shakeo yokoma - kununkila 24 cane, five handiled shakeos ya cassi, yopimiwa na kulema kwa shakeo ya mumalo yo yela, na imozi hini ya mafuta ya olive. 25 ufunika kupanga mafuta yamuzozo yoyela na ive vofakamo, nchito ya vonunkilisa. Yazankala mafuta yamuzozo oyela, yonilandililako ine. 26 Ufunika kuzozo tenti yo kumanilamo na aya mafuta, ndipo na arki ya umboni, 27 tabulo na zonse zo sebenzesa, choimilikapo nyali na chisulo, na guwa ya zonunkila bweno, 28 na guwa ya vopeleka vo shoka na visulo, dishi na choimilikapo. 29 Ufunuka kuvipatula ive kuli ine kuti vinkale vo yela kuli ine. Chilichonse chiza vigwilako chizankala cho yela. 30 Ufunika ku zoza Aaroni na bana bake bamuna na kuba patula kwa ine kuti banisebenzele ine monga babambo. 31 Ufunika unkambe na Israelile,' ichi chifunika kunkala mafuta ya muzozo yopatulika kuli Yehova kumibado yonse ya bantu. 32 Siifunika kuzola kutupiya bantu, kapena kupanga mafuta yena nakapangidwe kamene aka, chifukwa niyo patulika kuli Yehova. Ufunika kuchionela mungila iyi. 33 Alionse wamene aza panga vonunkila monga ivi, kapena kufaka palimuntu wina, uyo muntu afunika kumu jubako ku bantu." 34 Yehova anakamba kuli Mose Kuti, "Tenga vovence bwino - stacti, onychi, na galbanumi - zo mvesabwino sweti pamozi na vonunkila bwino, chonse choliganisiwa. 35 ipangani muchintu cho oneka na kuninkila vabweno, kugwilizana na vonunkilisa, yefakiwako sauti, kuyenela na kupatuliwa. 36 uzagaya mulituntu tungono to sankana. fakani vinangu pantagu yae arki ya umboni. Yamene ili mutanti yokumanilamo,mwamene nizakumana na imwe. Uza zachiona choyela manigi. 37 pali izi zanunkila bweno uzapanga, siufunika kupanga chilichonse mukapangidwe kamozi kanu. Chifunika kunkala choyela kuli iwe. 38 Alionse wamene aza panga chilichonse kusebenzesa monga zonunkila afunika kumu jubako kubantu bake."
1 Pamene apo Yehova anakamba kuli Mose kuti, 2 "Ona, Namuitana na zina Bezalele mwana mwamuna wa Uri mwana mwauna wa Hur, wa mutundu wa Yuda. 3 Nazulisa Bezalele na Muzimu wanga, kunvesesa, kumupasa nzelu, na kuziba, nchito zili zonse, 4 kapanga zakulingirila an kusebenza na golide, siliva na mukuwa; 5 anso kujuba naku ik myala na mitengo naku chita nchito zilizonse. 6 Mofakilapo kuli enve, na sanka Oholiab mwana mwamuna wa Ahisamak, wa mutundu wa Dani. Nafaka moziba mu mitima ya bonse bali na nzelu kuti bapange vonse vamene naku'uza iwe. kufunika 7 chihema chokumanilamo, likasa ya umboni, chovininkila pa likasa, na zapangi zonse za chihema- 8 Na tebulo na zopangila zake, na choikapo nyali na vonse vopangilako, na guwa ya nsembe, 9 na guwa ya nsembe na vonse vopangilako, na dishi ikulu na choikapo. 10 Nakufakilapo vovala votumikilamo, vovala voyela va Aroni wansembe, naivo vabana bake bamuna, vosungiwa kuli ine kuti bakani sebenzele monga ba nsembe. 11 Kufakila mafuta yozoza na vonzuna va mumalo yoyela. Bosebenza bafunika kupanga vonse ivi vintu monga mwamene na lamulila kuli iwe." 12 Pamene apo Yehova anakamba kuli Mose kuti, 13 "Uza ma Isilayeli: 'Mufunika kusunga masiku ya Sabata ya Yehova, chifukwa ivi vizankala vizibiso pakati pa ine na bonse bazabwela kuti muzibe kuti ati ni Yehova, anakupatulani kwake eka. 14 Mufunika kusunga Sataba, chifukwa ifunika kusungiwa kuli imwe chifukwa ni yoyela, kusungila enve. Aliyense azaipisa azafunika kumupaya. Aliyense wamene asebenza pa Sabata, uja muntu azafunka kumujuba pa bantu bake. 15 Nchito izachitika mu masiku yali sikisi, koma siku ta nambala seveni ifunika kunkala Sabata yopumula, yoyela kuli Yehova. Aliyense azagwila nchito pa Sabata afunika kupaiwa 16 Chifukwa chake bana ba Isilayeli bafunika kusunga Sabata. Bafunika kusunga Sabata mumubadwo ya bantu bonse moga chipangano chamuyaya. 17 Sabata izankala chilangizo pakati pa Yehova na bana ba Isilayeli, Chifukwa mu masiku sikiksi Yehova analenga kumwamba na pansi, napa siku ya seveni anapumula" 18 Pamene Mulungu anasiliza kukamba na MOse palupili ya Sinayi, anamupasa magome yabili ya chipangano, yopangiwa na myala yolembewa na kwanja kwake.
1 pamene bantu bana ona huti Mose achedwa kubwela pansi kuseluka palupili, bana sonkana pali Aroni naku kamba kuli enve, "bwela utipangile mafano kopempeza kamene kaza yenda pasogolo patu. 2 Manje pali uyu Mose, mwamuna anati chosa mu malo ya Egipito, sitiziba vamene vachitika kuli enve."Manje Aroni anakamba kuli benve, " chosani mpete zamene zili pa matu ya bakazi banu, na matu ya bana banu bamuna naba bakazi, na kuzileta kuli ine." 3 Bonse bantu bana vula mpete za golide zinali pa matu yabo nakuleta kuli Aroni. 4 Analandila golide kuchokela mu manja yabo na kuyi pangamo na chopangila na kupanga mafano kopempeza muma onekede ya mwana wangombe. pamene apo bana kamba kuti, "izi ndiye mulungu zanu, Isreli, zina kuchosani mu malo ya Egipito. 5 Pamene Aroni anaona ichi, anamanga guwa pa sogolo pa mwana wangombe naku sindikiza vokamba vate; anakamba, " Mailo kuzankala madyelelo mu ulemu Yehova." 6 Bantu bana uka kusen siku yokonkapo naku leta nsembe zo shoka na nsembe zo pembeza. Pamene apo banakala pansi kuti badye no kumwa, naku imilila muma sangalo chamu chalo. 7 Kuchoka apo Yehova anakamba kuli Mose kuti, "Yenda mwamusanga, chifukwa bantu bako bamene una chosa mu malo ya Egipito bazi ipisa beka. 8 Baisiya njila mwamsanga yamene ninaba lamulila. Bapanga kamulungu kopempeza mu maonekedwe ya mwana wangombe nakuka pempeza. Bakamba kuti, "Izi, nimilungu zani, Isireli, zinaku chosani mu malo ya Egipito. 9 Pamene apo Yehova anakamba kuli Mose, " naba ona aba bantu. ona, nibantu ba ntota. 10 Apa manje, osayesa kunilesa. Ukali wanga uzaba shoka benve. Mwaicho nizaba onong benve. kuchoka apo niza panga ziko ya mpamvu kuchokela muli iwe." 11 Koma Mose anayesa kubwelesa pansi ukali wa Yehova Mulungu wake. Anakamba kuti, "Yehova, nichani ukali wanu che upyela pa bantu banu, bamene muna chosa mu malo ya Egipito na mpamvu zambili na mpavu zonse za kwanjia yanu? 12 Nchifukwa chani ba Egipito bazakabila, " Anaba sogolela kuba chosa muma ganizo nama ganizo yoipa kuti abapaye mu malupili nakuba ononga kuchoka pa menso yapa ziko ya pansi?" Bwezamo mutima naku chosapo chilango pa bantu bako. 13 Kumbukila Abrahamu na Isaac na Isireli, banchito bako, kuli bamene una lambila kuli iwe weka naku kamba kuli benve, "Niza panga ba mibadwo wako kuti bapake monga nenyezi mu mwamba, anso niza pasa kuli ba mibadwo bako malo yonse aya ninakamba, bazayi landila mwa muyayaya." 14 Kuchoka apo Yehova anachinja nzelu pa chilango chamene anakamba azachita pa bantu bake. 15 Kuchoka apo Mose ana zunguluka naku seluka lupili ninshi aimya magome yabili ya chipangano mu manja mwake. Magome yanali yolembeka ku mbali zonse zibili ku sogolo naku mbuyo. 16 Magome yanali nchito ya Mulungu eka, na vilembo vinali vilembo va Mulungu eka, vodindika pa magome. 17 Pamene Yoshua anamvela chongo cha bantu pamene bana punda, anakamba kuli Mose kuti, "kuli chongo cha nkondo mumsokano. 18 koma Mose anakamba, " sichongo chakupambana, anso sichongo chabo Gonjesa bantu, ni chongo chabamene baimba chne nmvela. 19 Pamene Mose anali kufika pa musonkano anaona mwana wangombe na bantu baivn. Anabwela akalipa maningi. Anataya magome kuchoka mu manja yake na kuya pwanya pansi pa lupili. 20 Anatenga mwana wangombe wamene bantu bana panga, ku ushoka, kuyitwa mosala, naku itila mu manzi. nakunpanga bantu bamu Isireli kuimwa. 21 24 Kuchoka apo Mose anakamba kuli Aroni kuti, "Bana kuchita chani aba bantu, kuti ulete ma chimo yakuli pali benve?" 22 Aroni anakamba kuti, "Musakalipe maninig bwana. Mubaziba aba bantu, mwanene ba kondela kuchita voipa. Banakamba kuli ine kuti, 'Tipangile Mulungu aza yenda pa sogolo patu. Manje pali uyu Mose, Muntu wamene anatichosa mu malo ya Egipito, sitiziba vamene vamu chitikila. 23 Mwaicho ninakamba kuli benve kuti, "Aliense alina golide, lekani ayivule; Banani pasa golide na kuitila mu mulilo, na kuchoka mwana wangombe." 25 Mose anaona kuti bantu bachita vamene benzo funa kuchita (Chifukwa Aroni anaba lekelela kupita malile, chinalengesa ba gudani babo kubaseka). 26 Mwaicho Mose anaimilila pongenela mumusonkano naku kamba, "Alionse ali kmbali ya Yehova, bwela kuli ine." Bonse ma Levitisi banamu zunguluka. 27 Akamaba kuli enve, "Yehova, Mulungu wa Isirelio akamba ivi: Lekani mwamuna alionse amange luoanga pa mbali pake na kuyenda kusogolo naku mbuyo kuchoka po ngenera kufika ngenera mu malo yonse ya musonkano, nakupaya mubale wake, munzake na onkala pafupi pake." 28 Ba Levite banachtia vamene Mose anabauza. Ija siku bantu fili sauzande banafa. 29 Mose anakamba kuli ma Levitisi, Mwaikiwa mu nchito ya Yehova lelo. chifukwa aliense pali imwe aimila mwana mwamuna wake na mubale wake, kuti Yehova anga kupaseni daliso. 30 Siku yokonkapo Mose anakamba kuli bantu, "Mwachita chimo ikulu maninigi. Manje niza kwela kuli Yehova, kapena nizachita chotetezela pama chimo yanu." 31 Mose anabwelela kuli Yehova anaku kamba, "Iyee, aba bantu bachimwa chimo ikulu na kupanga kamulungu ka golide. Koma manje, napapata bakululukileni machimk yabo; 32 koma ngati simuna chite ivo, mu nichosemo mu buku yamne muna lemba." 33 Yehova anakamba kuli Mose, "Ulionse achimwa kuli ine, Uyo muntu niza muchosa mu buku yanga. 34 Apa manje yenda, sogolela bantu bamene nakamba kuli iwe. Ona, mungeli wanga azayenda pa sogolo panu. Koma pa siku nizaba langa benve, nizaba langa pama chimo yabo." 35 Yehova anatuma chisongo pali bantu chifukwa benze bana panga mwana wangombe, wamene Aroni anapanga.
1 Pamene Yehova anakamba kuli Mose, "Yenda kuchoka pano, iwe na bantu bamene unachosa mu Iguputo. Yenda ku malo yamene nina panga ku lapila kuli Abrahamu, kuli Isaki, na kuli Yakobo, pamene nina kamba, niza pasa ku bana bobadwa kumbuyo kwanu, ' 2 Nizatuma mungeli kusogolo kwanu, nizaku choselani amu Kanani, Amorati, Hititati, Perezati, Hivazati, na Jubuzati. 3 Yendani kumalo, yoyenda mukaka na uchi, koma siniza yenda na imwe. chifukwa inu ndimwe bantu olimba mikosi. ninga kuonogeni imwe munjila." 4 Pamene bantu bana nvela mau chinaba vutisa, banalila, kulibe anavala vomu mukosi. 5 Yehova anakamba kuli Mose, "kamba kuli Isilayeli, 'ndimwe bantu bolimba mikosi. ngati naenda pakati panu inga nkale ntawi imozi, ninga kuonengeni, manje apa chosani vamu mukosi kuti ninga zibe vochita naimwe." 6 Sopano Isilayeli sinavale vokobekela ku chokela ku lupili ya Herobu kuyenda musogolo. 7 Mose anatenga tenti na kuimika panja kutalukila po nkala. Anaitana tenti po kumanila. Aliyense ana funsa Yehova kalikonse nali kuyenda ku tenti ko kumanila, panja ba campu. 8 Pamene Mose anali kuchoka kuptia ku tenti, bonse bantu benze ku yenda kuma tenti pongenela pao naku yangana Mose kufikila aka ngena mukati. 9 Pamene paliponse Mose aka ngena mutenti, kumbi yenze ku bwela pansi naku mulamulilanpo ngennela pa tenti, ndipo Yehova anali ku kamba na Mose. 10 Pamene bantu bonse bana ona kumbi yaimilila pongenela pa tenti, anali ku yamika naku lambila, mwamuna aliyense pongeneka mutenti yake. 11 Yehova anali ku kamba kuli Mose nkope na nkope, monga mutnu akamba na muzake. Pamene Mose anali kubwelela ku campu, koma wanchito wake Yoshwa mwana wa Nan, munyamata, anali ku salila mutenti. 12 Mose anakamba kuli Yehova, "Onani, mwankala mu kamba kwaine, 'Tenga aba bantu pa ulendo, 'koma zimuna nizibise bamene muzani tuma nabo. mwa kamba, "nikuziba na zinalako. naku peza mwai mu manso yanga. 13 Manje ngati na peza mwai mumaso yanu, nioneseni njila zanu kwakuti nkakuzibeni imwe na kupitiliza ku peza mwai mumaso yanu. kubukilani kuti ziko ili ni bantu banu." 14 Yehova anayanka, "kupezekapo kwanga ku zaenda ma iwe, ni zakupasa mupumulo." 15 Mose anakamba kuli enve, "Ngati kupezekapo kwanu siku yenda naise, musati chose pano. 16 Ndaba, chizazibika bwanji kuti napeza mwai mu menso yanu, ine na bantu banu? Sichiza nkala ngati muyenda naise kuti ine na bantu banu kunkala bosiyana na bantu bena bali paziko ya pasni?" 17 Yehova ana kamba kuli Mose, "nizachitanso ichi chamene wani pempa, chifukwa wapeza mwai mu manso yanga, niku ziba na zina." 18 Mose anakamba kuti, "Napapata ni oneseni ulemelelo wanu." 19 Yehova anakamba, "niza lengesa ubwino wanga kupita pa sosgolo pako, naku kamba zina yanga 'Yehova' pamenso pako. Niza chitila chisomo wamene niza chitila chisomo, naku onessa chifundo kuli iye wamene niza onesa chifundo." 20 Koma Yehova anakamba, "suzaona nkope yanga, chifukwa kulibe angone nkpoe yanga naku nkala namoyo." 21 Yehova anakamba, "ona, apa nipa malo panga; uzaimilila pa mwala uyu. 22 Pamene ulemelelo upita, niza kuika kumbuyo kuli mwala naku chingilza iwe na kwanja yanga kufikila nikapita. 23 Pamene niza chosapo kwaja yanga, ndipo uzaona kumbuyo kwanga, koma nkope suzai ona."
1 Yehova anakamba kuli Mose kuti, "Juba matabweli yabili yamyala monga monga yamutundu yoyamba uja. Nizalemba pa matabweli mau yamene yanali pa matabweli yapoyamba yaja. matabweli yamene unapanga. 2 Ukakonzeke mailo kuseni uka bwele pamwamba pa lupili ya Sinayi, kuchoka apo uzakazi onesa kuli pamwamba pa lupili. 3 Osabwela na aliyense. Osaleka aliyense kuonekela pafupi na lupili. kulibe vobeta olo ng'ombe vizafunika kudya munyansi mwa lupili. 4 Pamene apo Mose anajuba matabweli yabili monga zapoyamba, kuchoka apo anauka kuseni seni anku yenda pa lupili ya Sinayi, monga Yehova anamu'uzila. Mose ananyamula ma matabweli yamyala mumanja mwake. 5 Yehova anaseluka mukumbi naku imilila naye Mose oamene anali, kuchoka apo anatomola zina ya "Yehova". 6 Yehova anapitila pafupi naku nena kuli enve, Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo na chikondi, amachedwa kukalipa, naku sefukila mosalekeza mu chikondi nakukululupilika, 7 Kusungila chikondi chosata muma sauzande, kukulukila machimo, volakwa nama chimo, nama chimo. koma sazabaleka chabe bolakwa loko vivute bwanji. Azaleta chilango cha atate babo pa bana ba mbadwo chitatu, mpaka kumubadwo wachitatu na cha namba folo." 8 Mose anagwada pasni mwamusanga nakupembeza. 9 Pamene apo anakamba kuti, "ngati napeza ubwino mumenso yanu, Mbuye wanga, napapata pitani pakati paise, chifukwa bantu nibokosa mikosi. Kulukilani kusalungama na chimo yatu, anso mutenge monga wolowa wanu." 10 Yehova anakamba kuti, "Ona, nifuna kupanga chipangano, pali wonse bantu bako, Nizachita vodabwisana vamene vakalibe kuchitikakapo muchalo chonse olo muziko iliyonse ya pansi. Bantu bonse pakati panu bazaona vochita vanga, chifukwa nichintu choyofya chamene nichta naiwe. 11 Umvelele chamene niku lamulila lelo. Nizapilikisha pali iwe ma Amorites, Kananites, Hittites, Perizzites, Hivayites, nama Jebusites. 12 Munkale uchenjela kuti musapange chipango na bantu bamu malo kwamene muyenda, ndaba chingankale chokuteya nacho pakati panu. 13 Mumalo mwake, mufunika kupwanya maguwa yawo, vipilala vao vamyala pwanyani, na vosema va Ashila. 14 Pakuti simufunika kupempela mulungu inangu, chifukwa Yehova, zina yake ni Nsanje, ni Mulungu wansanje. 15 Pamene apo muchenjele pakusapanga chipangani na bantu bamene ba nkala mumalo, pakuti bazachita uhule ku mulungu yabo. anso nsembe bamapasa milungu yawo. Pamene apo umozi azakuitanani anso muzadyako nsembe zabo, 16 Chamene chokonkapo uzatenga na bana nake bakazi kupasa bana bako bamuna. kuchoka apo bana bake bakazi bachita uhule ku mulungu yabo. 17 Musazipangile imwe milungu za malata yosungumuka, 18 Mufunika kusunga mwambo wa buledi ilibe chotupisila. monga mwamene ninakulamulilani, Muzafunika kudya buledi ilibe chotupisila masiku yali seveni pa ntawi yosachinjiwa mu mwezi wa Abibi, pakuti munali mu mwezi wa Abibi pamene munachokamo mu Igupto. 19 Bobadwa boyamba nibanga wonse, navonse vimuna vobeta vanu voyamba, chinkale ng'ombe olo mbelele. 20 Muzafunika kuombola mwana woyamba wa donke na kamwana kambelele. koma ngati simunyiwombole mufunika kuityola mukosi. Mufunika kuombola bonse bana banu bamuna boyamba. Osaonekela kuli ine chimanja manja 21 Musebenze masiku yali sikisi, koma siku ya namba seveni mufunika kupumula. Nangu nipa ntawi yolima kapena pokolola mumunda mufunika kupumula. 22 Muzachita mwambo wama sabata na vochosa voyamba va witi, naku yangana mwambo oleta va mumunda pakusila kwa chaka. 23 Katatu pa chaka onse ya bamuna ba bazafunika kuonekela pamenso pa Ambuye Yehova, Mulungu wa Isilayeli. 24 Chifukwa nizapisha maziko pamenso panu naku kulisa malile yanu. Kulibe azafuna kunkala namalo yanu kuti yankale yabo pamene uzakwela pamwamba kuonekela pamenso ya Yehova patatu pa chaka. 25 Osapeleke pelekelo yamagazi ya nsembe yanga pamozi na votupisila. kapena nyama iliyonse yochoka kunsembe yachisangalalo cha pasika osaisiya kufika kuseni. 26 Mufunika kuleta kunyumba yanga vabwino maningi pavi paso voyambilila kupya kuchokela mu munda yanu. Musa pike ka kamwana ka mbuzi mu mukaka ya mai wake. 27 Yehova anakamba kuli Mose kuti, "Yalembe aya mau, pakuti kulingana na aya mau napanga chipangano na iwe na Isilayeli. 28 Mose anakala pamene apo na Yehova masiku fote muzuba na usiku. Sanali kudya chakudya chilichonse ono kumwa manzi. Analemba pa matabweli mau yachipangano, malamulo yali yeni. 29 Pamene Mose anaseluka kuchokela ku lupili ya Sinayi na matabweli yabili ya chipangano na malamulo mumanja mwake, sana zibe kuti nkanda ya pamenso pake inayamba kuyaka pamene enzokamba na mulungu. 30 Pamene Aroni nama Isilayeli yana ona Mose, Nkanda ya pamenso pake inali kubeka. anso banali kuyopa kubwela pafupi na enve. 31 Koma Mose anabaitana, anso Aroni na basogoleli bonse ba magulu yaja banakwela nakubwela kuli enve. Pamene apo Mose anakamba nabenve. 32 Kuchoka apo, Bantu bonse bamu Isilayeli banabwela kuli Mose, naku bauza malamulo yamene Yehova anamupasa pa lupili ya Sinayi. 33 Pamene Mose anasiliza kukamba na benve, avininkile chitambala kumenso. 34 Pamene Mose anayenda pamenso ya Yehova kukamba na enve, anali kuchosa chitambala, mpaka kuchoka. Pamene anachoka, Aza uza bana ba Isilayeli malamulo yamene banamu uza. 35 Pamene ma Isilayeli banamu ona Mose na nfeshi yobeka, azavinikila pamenso pake futi mpaka abwelela kukamba na Yehova.
1 Mose anaika pamozi gulu ya bana ba Isilayeli naku bauza kuti, "Ivi ndiye vintu vamene Yehova analamulila kuchita. 2 Pa masiku sikisi nchito ingagwililewe, koma kuli imwe, siku ya seveni ifunika kunkala yoyela, siku ya Sabata niyopumulatu, yoyela kuli Yehova. Aliyense wamene agwila nchito iliyonse pa siku iyo afunikila kupaiwa. 3 Simufunikila kuyasha mulilo munyumba iliyonse pamsiku ya Sabata." 4 Mose anakamba na gulu ya Isi, kukamba kuti, "Ichi ndiye chintu chamene Yehova alamulila. 5 Mupeleke pelekelo kuli Yehova, bonse ba imwe muli na mutima ofunisa. Muletee chopeleka kuli Yehova.-golide, siliva, mukwa, 6 bulu, pepo, na tonje na nyula yopepuka; masako ya mbuzi; 7 chikumba cha mbelele chamaonekedwe ya daya ya redi; 8 mafuta ya mnyala ya malo yopatulika, vonunkilisa mafuta yozozela na chifungo yabwino, 9 myala ya onika na myala zinangu zabwino kuti vi'ikiwe pa efodi napa nyula ya pachifuba. 10 Mwamuna aliyense wa uiso pakati pa imwe abwele na kupanga vilivonse vamene Yehova alamulila- 11 kachisi na chihema zake, chovininkila, chofyantila cake, mafelelmu, togwililila, sandamile, na maizko; 12 futi likasa na sandamika zake,chovininkila cha chitetezo, na nyula yachobisila. 13 Banaleta tebo na nsandamila zake, na mukate wa pamenso pa mulungu; 14 na choikap nyale, yo sanikila na vosebenzela vake, nyale zake, na mafuta ya munyale; 15 Vonunkila yapaguwa na nsandamila zake, mafuta yozezelewa na fungo yabwino: chinyula chovalila pa chiseko; 16 guwa yoshokelapo vopeleka na kabati ya mukuwa na nsandamila zake na vosebenzela; na dishi ikulu maziko yake. 17 Banaleta volelenga va pamalo ya panja na nsandamila zake na maziko, na kelani ya panja pongenela; 18 na chopinila cha chihema cha kachisi na panja pamozi na ntambo zake. 19 Banaleta mukanjo yopepuka yotungiwa bwino yosebenzesa mu malo yoyela, mikanjo yoyela ya Aroni wansembe na bana bake bamuna kuti batumikike ngati bansembe. 20 Pamene apo gulu yonsr ya bana ba Isilaeli banachokapo pamenso pa Mose. 21 Aliyense wamene mutima wake unagwidwa wamene muzimu wake unapanga kufunisisa anabwela na nakuleta chopeleka kuli Yehova kuti bapangile kachisi, vonse vintu vautumiki mukati, na mikanjo zoyela. 22 Banabwela, bonse bamuna na bakazi, bonse benze na mutima ofunisisa. Banaleta tubangili, mpete za kumatu, za kukakumo, na vokonngoles na mutundu yonsr ya jeweli ya golide. Bonse banaleta chopeleka cha golide kuli Yehova monga chopeleka cha chonesela. 23 Aliyense enzeli na bulu, pepo, kapena tonje yofila, nyula yopepuka, chikumba cha mbuzi chikumba cha mbelele cha maonekedwe ya redi, kapena chikumba chopepuka vinaletawa kuli benve. 24 Aliyense opanga chopeleka cha siliva kapena mukwa banaleta monga chopeleka kuli Yehova, ndipo aliyense wamene anali na mutengo wa akesha ku'ugwilisila nchito iliyonse banauleta. 25 Aliyense mukazi wa luso yotunga tonje na manja yake, analeta vamene banatunga bulu, pepo kapena tonje yofila, kapena nyula yopepuka. 26 Bakazi bonse bamene mutima wabo unfunisisa na benzeli na luso yopana masako yambuzi. 27 Basogoleli banaleta myala ya oniki na myala yobeka kuti yaikiwe pa efodi na chachifuba; 28 Banaleta vonunkisa na mafuta ya munyale, va mafuta yozozelako naya fungo yabwino. 29 Ba Isilayeli banaleta chopeleka mosakakamiziwa kuli yehova mwamuna na mukazi aliyense wamene mutima wake unafuna analeta vintu va nchito yonse yamene Yehova analamulila kupitila muli Mose kuti chipangiwe. 30 Mose anakamba kuli ba Isilayeli, "onani, Yehova aitana pa zina pa Bazale, mwana mwamuna wa Uri mwana mwamuna wa Huri, kuchokela ku mutundu wa Yuda. 31 Anazulisa Bazala na muzimu wake, kumupasa nzelu, kumvesesa, naku ziba, kuli mutundu yonse yopanga za manje, 32 kupanga zaluso na kusebenza mu golide, siliva, na mukwa; 33 futi ku juba na kuika myala na kusema mitengo-kuchita mutundu yonse ya luso na kupanga va manja. 34 Wachika mu mutima mwake kuchipunzisa, bonse benze na Oholiabu mwana mwamuna wa Ahisamaki, kuchokela mu mutundu wa Dani. 35 Wabazuzya na luso kuchita mutundu yonse ya nchito, ku sebenza monga opanga, bokumba, botunga mu bulu, pepo na vofila na nyula yopepuka, ndipo monga mukanjo. Nibaluso mu nchito zosiyana siyana, na bopanga.
1 Chakuti Bazalo na Oholiabi naba kaswili bamene Yehova anapasa paso mpamvu zoziba kuchta nchio yomanga malo yoyela nachito zamene Yehova anaba lamulila." 2 MOse anaitana Bazalo, Oholiab, na bonse bakaswili bamene Yehova anafasa paso, na uli onse wamene mutima wake unanyamulisa kuchita nchito. 3 Banalandila kuchokela kuli Mose chopeleka chamene ba Isilayeli bana leta kumangila malo yoyela. Bantu benze bakali kuleta vopeleka kuli MOse pamutima wawo siku zonse. 4 Chakuti bakaswili bonse banalikusebenza pa malo yoyela bana sebenza kuli vamene banali kuchita. 5 Bobaza banuza Mose. "Bantu baletavambili kuli vamene vifunika kuchita nchito yamene Mulungu anatilamulia kuchita." 6 Chakuti Mose analesa bantu bamugulu kuleta vopeleka vomangila malo yoyela. Pamene apo bantu bana leka kuleta paso. 7 Banali navintu vambili vo chitila nchito. 8 Bonse bobaza pakati pawo banamanga malo yopempelelamo na nyula yolingana zili teni kuchokela kunyula ya tonje naya bulu, pepo, na nsalu ya maonekelo ya kelubi. Iyi inali nchito ya Bazlo, na bonse akaswili obaza. 9 Utali wa nyula iliyonse inali twenti-eyiti mikono, bufupi unali fo mikono. Nyula zonse zenze zo lingana. 10 Bazalo anakumanisa nyula zili faivi pamozi, na nyula zinangu zili faivi anakumanisa. 11 Anapanga ntambo ya bulu mumbal msilisa nyula imozi, anachita vamene mwa nyula inakonkapo. 12 Anapanga ntambo zili fifite pa nyula yoyambila na ntambo zili fifite mumbali mwanyula inakonkapo. Ntambo zinali zosiyana mumbali ina na mumbali ina. 13 Anapanga vogwilila va golide vili fifite nakuzi kumanisa pamozi nazina zachi kuti malo yopempelelamo yankale yogwili zana. 14 Bazalo anapanga nyula yachikumba chambuzi cha tenti yapa malo yopempelelamo; anapanga nyula izi zili leveni. 15 Utali wa nyula izi wnze sate mikono, na mufupi wa nyula yonse unali fo mikono. 16 Pa nyula zizli leveni zonse zanali zolingana. Anakumanisa nyula zili faivi pamozi na nula zili sikisi pamozi. 17 Anapanga ntambo zili fifite mumbali mwa nyula yoyambila, nantambo zili fifite mumbali mwanuyla nozikumanisa kuli zinakonkapo. 18 Bazalo anapanga vogwiliza va bronzi vili fifite kugwila tenti pamozi kuti inkale imozi. 19 Anapangila malo yo pempelelamo chivininkilo chinangu chachikumba chotelela chianli pamusamba. 20 Bazalo anapanga mafulemu yoyimilia ya mutengo ya akesia yapa malo ya kachisi. 21 Utali wama fulemu unali mikono, na mufupi wafulemu ulionse unali mukono umozi napakati. 22 Fulemu ulionse inali nama pegisi yama pulanga yabili. Anachita vamene ivi kuma fulemu yonse yapa malo yopempelelamo. 23 Anapanga mafulemu yamalo yopempelelamo munjila iyi: twenti fulemuzi kumbali yakumwela. 24 Bazalo anapanga vapansi pamafulemu ya siliva zili fote zofaka pansi pafulemu kugwilisa mafulemu pamozi. 25 Kumbali kwina kwa malo yopempelelamo, ku moto, anapanga mafulemu twenti. Nava pansi va siliva vili fote. 26 Kunali vampansi vibili apsni pa fulemu yoyamba, vampansi vibili pali ina kukonkapo, no konkanya. 27 Kumbuyo kwa malo yopempelelamo kumazulo, Bazalo anapanga ma fulemu sikisi. 28 Anapanga ma fulemu yabili pa kona kumbuyo kwa malo yopempelelamo. 29 Aya mafulemu siyenze yokatana pansi, kona yenze yokumana pamwamba na mpete. Anapanga yabili manjila iyi mumakona yabili. 30 Yenzeli mafulemu eyiti, pamozi naza pansi za siliva. Zinali sikisitini zapansi pamozi, zapansi zibili pa fulemu yoyambila, zibili zapansi pa fulemu ina konkapo, nakupitilza. 31 Bazalo anapanga mutanda na mutengo wa akasiya-faivi mafulemu kumbali imozi yamalo yopempelelamo, 32 mitanda ili faivi yama fulemu kumbali jwina kwa malo yopempelelamo, na mitanda ili faivi kuma fulemu yakumbuyo kwa malo yopempelelamo ku mazulo. 33 Anapanga mitanda pakati pama fulemu, ndiye pakati, kufika kosilila. 34 Anapanga mafulemu na golide, anapanga mpete ya golide, kuti yakale chogwila chamitanda, anavalisa mitanda na goldie. 35 Bazalo anapanga nyula za bulu, pepo na redi, nyula za tonje, yo'oneka monga kelubi, nchito ya kaswili. 36 Anapanga nyula za nsandamila zili fo kuchokela kumutengo wa akasile, nakuzi valikapo golide. Anapanga nazo kobekela za golide muma nsandamila nakuzi ponyela pali zapansi za siliva zili fo. 37 Anapanga chokobekela pongenela mu tenti. china pangiwa na bulu, pepo, redi na nyula ya tonje, nchito yabo tunga. 38 Anapanga mokobekela mo pa nsandimila zili faivi na nkobekelo. Anazivalika pamwamba na nkoli na golide. zza pansi zili faivi zinali zo pangiwa na bronzi.
1 Bazalo anapanga likasa kuchokela ku mutengo wa akashiya. kutalimpa kwake kunali kokwanila mikono tu na hafu; mukufupikila kwake wanu na hafu mikono, na kutalimpa mikono wanu na hafu; 2 Anavininkilamo mukati na kunja na golide yoyela nakuika mumbali mwake golide na pa mwamba pake. 3 Anaikapo mpete zinai za golide pasni pa mendo yak yinai, kumbali kumozi, mpete zibili, na kumbali ina mpete zibili. 4 Anapanga sandamina ya mutengo ya akashiya na golide. 5 Anamikiza sandamina mukati mwa mpete ku mbali kwa sandamina, kuti itandizile kunyamula likasa. 6 Anapanga chotetezelako chovininkila cha golide yoyela. Kutalimpa kwake tu na hafu mikono na mukufupika kwake kunali wanu na hafu mikono yake. 7 Bazalo anapanga makelubi yabili kuchokelamku golide yomenyewa, kosiliza kubili kwa vininkila yotetezela. 8 Kelubi umozi onali kosiliza kwa vininkilo yotetezela. na kelubi wina anali kosiliza kwina. zinali zopanga ka mogwilizana na vinikilo yoteteza. 9 Na makelubi yana tambulula mapapiko yao kumwamba nakuchinga vinikilo yotete pakati pa vininkilo yotetezela. 10 Bazalo anapanga tebulo yochokela ku mutengo wa akashiya. kutalika kwake mikono ibili kufupika kwake mikono ili umodzi, nakutalika inali mikono umozi na hafu. 11 Anavininkila na golide yosuikwa bwino kuika mbali mwake na golide yosukiwa bwino. pamwmba pake. 12 Anapanga chamumbali kukula kwake monga kwanja, na kuikako golide. 13 Anaikako mpete zinai za golide nauikapo mpete kumbali zonse zinai, kwamene muyendo inai inali. 14 Mpete inali yolumikiza ku chamumbali, kupeleka malo yonyamulila tebulu. 15 Anapanga sandamina kuchokela ku mutengo wa akashiya naku ivinnkila na golide, kuti akwanilise kunyamula tebula. 16 Anapanaga vintu vamene vinali kufunikila pa tebulo, mbale, masipuni, mabeseni na nigomo kusebenzsea popoeleka vopeleka. Anapanga vonse kuchokela ku golide yosukiwa bwino nomenyewa. 17 Anapanga choikapo nyali kuchokela ku golide yosukiwa bwino yomenya. Anapanga choyikela nyali nachapansi chake na chapa mwamba chake. 18 Mbali mwake munlai mbanda zili sikisi - mbali iliyonse yoikapo nyali kunali zitatu. mapnda yoyamba inali na makapu yatatu-monga maluba wopuka ya almondi, na chapansi chake na maluba, makapu yatatu monga maluba wopuka kumbali. 19 na chapansi chake na malubaq. chinali cholingana na vonse mpanda zili sikisi zo chokela ku choyikapo nyali. 20 Pa choikapo nyali, chapakati, chake panali makapu yanai yopangiwa monga kupuka kwa almondi, na chapansi cha matepo na maluba. 21 Kunali chapansi, chamatepo pansi pa mpanda zibili zopangiwa monga chimozi, mwaizo chimozi mozi kunali chapansi chama tepo pansi pa chachitatu chazibili champanda, chopangiwa ngati chimozi, chinali chimozi mozi kuli vonse sikisi mpanda vochokela ku choikapo nyali. 22 Matepo ya pasni na mpanda zonse zinali chimozi. Mbali imozi inali yomonyee wa nchto ya golide yosuka bwino. 23 Bazalo anapanga choyikapo nyalina nyali zili seveni, mbaniro na choyelapo pulusa cha golide youska bwino. 24 Anapanga choyikapo nyali na zosebnzesa na gao imozi ya golide yoyela. 25 Bazalo anapanga guwa yazonukila. Anapanga kusebenzesa mutengo wa akashiya. Kutalimpa kunali mukono umozi, na kufupika kwake mukono umozi. mbali zonse zinali zolingana na kutalumpa kwake kunali mukono ibili. Nsengo zake zinali zopangika ngati guwa imozi. 26 Anavininkila guwa ya zonunikila na golide yosukiwa bwino pamwamba, mumbali na nsengo zake. Anapanganso na mbali mwake na golide. 27 Anapanga mpete zibili za golide kuti igwile kosiliza kumbali zonse zubili zosiyanako. mpete zinali zogwililalna na pansi pa nsandamila yonyamulila likasa. 28 Anapanga nsandamila ku mutengo wa akashiya. na kuyivinikila na golde. 29 Anapanga mafuta yoyela yozozewekila kuti inukulishe bwino, nchito yaonukilisa.
1 Bazele anapanga guwa yoshekelapo nsembe ya mitengo. inali yolingana mu utali - na katatu kutalimpa kuyenda mu mwamba. 2 Ana kulisako mumbali munali kuoneka monga nsengo za n'gombe. Nsengo zinali zogwilana na guwa, ndipo anavininkilapo na mkuwa. 3 Anapanga vonse vofunikoila va guwa - mpoto za milota, ma fosholo, madishi, vo pindamulilako nyama, na poika mulilo. Ndipo anapanga vonse vo funikila na mkuwa. 4 Anapanga komo ya guwa, mkuwa yo gwililila mitengo na poyakila mulilo. 5 Banapanga komo pansi pa limu inali kuzunguluka guwa. Bana ipanga mukati mwa guwa, panyansiko pan'gono kuti igwililile mitengo. 6 Bezele anapanga mizati yamitengo naku zivininkila na mkuwa. 7 Anaika mizati yamitengo mumbali mumbali mwa guwa, mo nyamulila. Anapanga guwa yamubo mukati kusebenzesa mapulnga. 8 Bezele anapanga choikilamo chikulu cham mkuwa. Anapanga choikilamo kusebenzesa magilasi ya bakazi bamene banali kusebenza pa komo ya hema yokumanilamo. 9 Anapanga chochingilizila hema kuzunguluka malo yokumanilamo.Nyula zakumbali kwa chochingilizila zinali zabwino, mukono handiledi kutalimpa. 10 Nyula zinali na poika pali twente, na mkuwa zili twente. Kunali to kobekelako moika, na ntambo za siliva. 11 Chimozimozi naku malo ya ku mpoto, kunali vokobeka mikono handiledi kutalimpa na poika twente, na poika pa mkuwa pali twente, tokobekapo poikila, na nkoli za siliva. 12 Vokobeka vaku mbali yaku mazulo zinali mikono fifite kutalimpa, na poika teni na vofakapo. Tokobekapo na ntambo zapoika zinali za siliva. 13 Chochingilizila chinali mikono fifite kutalimpa kumalo yakumwela. 14 Vokobeka kumbali imozi ya pongenela vinali mikono fifite kutalimpa. Vinali na poika patatu na vofakapo vitatu. 15 Kumalo kwina kongenela muchochingilizila kunali vokobeka va mikono fifite kutalimpa, Vinali na poika patatu na vofakapo vitatu. 16 Vonse vokobeka vinali kuzunguluka chochingilizila vinali vabwino. 17 Vofakilapo vinapangiwa na mkuwa. Vokobekapo na nkoli vinapangiwa na siliva, na vovininkila poika vinapangiwa na siliva.Vonse vochingilizila vinali vo vininkilika na siliva. 18 Nyula ya pongela muchochingilizila inali mikono twente kutalimpa.Nyula inali kuoneka yo buluwa, yofiilila, na yofila, yotungiwa bwino, ndipo inali mikono twente kutalimpa. Inali mikono twente mukutalimpa na mikono faivi mukutalimpa kuyenda mumwamba, monga nyula za chochingilizila. 19 Inali na voikapo vili folo na vokobekako va siliva. Chovininkila pa mwamba pake na nkoli zake zinapangiwa na siliva. 20 To kokomelelako hema ya chalichi na chochingilizilako tunapangiwa na mkuwa. 21 Ivi ndiye vintu vamene vinasebenza kupanga chalichi, chalichi ya chipangano cha malamulo, monga mwamene mose bana mu uza pachitenga. Inali nchito yaba levi mwamene anaba uzila itahama mwana mwamuna wa Aroni wa nsembe. 22 Bezele mwana mwamuna wa Uri mwana mwamuna wa Hur, waku mutundu wa yuda, anapanga vonse vamene mulungu ana uza mose. 23 Oholiabi mwana mwamuna wa Ahisamaki, waku mutundu wa Dan, anasebenzela pamozi na Bezele mukupanga vobeza, monga woziba maningi, ndipo monga wotunga vo buluwa, vofiilila, na vofila, na nyula zabwino. 24 Yonse golide inasebenza kuchita nchito, mumalo yonse yogwilana na malo yoyela - golide kuchokela ku nsembe -inali twente naini na 730 tudunswa, to pimiwa mofunikila na malo yo yela. 25 Siliva inpasiwa kuchoka ku bantu inali kulema handiledi imozi na 1,775 tudunswa, monga mu malo yoyela, 26 olo meda imozi muntu aliyense, yojuba pakati, yopimiwa na kadunswa kamu malo yoyela. Iyi nambala inavomelezewa kulingana na bantu bonse bamene bana pendewa, banali na zaka twente -603,550 bamuna beka. 27 Handiledi imozi yama siliva yana ikiwa pa malo yoyela na pansi pa mayula -Handiledi imozi, imozi pali ponse. 28 Yamene yanasalako pa 1,775 tudunsawa twa siliva, Bezele anapangila tokobekelako, anavininkila pamwamba pa toikilapo, nakupangilako nkoli. 29 Nsembe ya mkuwa yolema 2, 400 tudunswa. 30 Anapanga pongenela mu hema yokumanilamo kusebenzesa ivi, guwa ya mkuwa, kabati ya mkuwa, vonse vosebenzesa vapa guwa, 31 munyansi mwa chochingilizilako, munyansi mwa pongenela mu chochingilizilako, tonse to popomelelako twa chalichi, na tonse to popomelelako twa hema twa chochingilizilako.
1 Naya blue, pepo, tonje ya reedi, bana panga nsalu zooneka bwino zo sebenzelako mumalo yo yela. Bana panga nsal ya Aroni yamu malo yoyela, monga Yehova analamulila Mose. 2 Bazalo anapanga efodi ya goilde, ya b ulu, pepo, tonje ya redi, na nyula yopepuka zibili-zibili. 3 Bana koma malata ya golide naku ya juba muma waya, kuya sebenze sa muli tonje ya bulu,pepo, na redi, namu manyula yopepuka, chito ya ba kaswili. 4 Bana pangan vigawo vamumapewava efodi, vogwilana ku vili vamumakana yapa mwamba. 5 Chamumusana chopangiwa bwino chenzeli monga efodi; chenze chopangiwa na chigawo chiozi na efodi, yopangiwa na nyula zopepuka zibili zibili yamene yenze golide, bulu, pepo, na redi, mongamwamne e Yehova analamulila Mose. 6 Bana konza myala za onyi, bana ika tofaka twa golide, yokonzewa na volemba kwati chozibililako nama zina yabana bamuna ba Isilayeli. 7 Bazalo anafaka magawo yama pewa ya efodi, kunkala myala yokumbukilapo kuli bana bamuna ba Isilayeli, Monga Yehova analamulila kuli Mose. 8 Anapanga gawo yapa chifuba, nchitoyaba kaswili vopanga monba efodi. Anavi panga na golide na bulu, na pepo, na tonje ya redi, na nyula yopepuka. Inali yolingana konse konse. 9 Bana peteka nyula zapa chifuba pabili. 23 sentimita mu'utali na 23 sentimita mu'ufupi. 10 Bana ikamo mizela folo ya myala zamutengo. mizela yoyamba yenze na ya odemu, ya pitida, naya bareketi. 11 Wachibili muzela wenze nayanfoki, ya safiro,na yahalomu. 12 Wachitatu muzela wenze na lelmu na sibu, naya akalama. 13 Muzela wachifolo wenze na Tarsisi, ya sahamu ya yasefe. Vinaikiwa moikiwa golide. 14 Kunali myala zili twelovu, iliyonse nazina imozi yabana bamu a ba iliyonse yenze yodindiwa na zina yamutundu umozi mumitundu zili twelovu. 15 Pa nsalu yapachifuba bana panga munyolo monga ntambo, yomangiwa nagnide yabwino. 16 Bana panga ma kanzedwe yabili ya golide na mpete zibili, naku zigwilizana mpete zibili kuma kona ya nsalu zapachifuba. 17 Bana faka minyolo zomanga zibili za golide muma mpete yabili ku kona ya nsalu yapa chifuba. 18 Bana gwilanisana zinangu zibili kosilizila kwa vomabga va munyolo kuma konzedwe yabili. bana vigwilisana ku gawo yaku ma pewa ya efodi ngati pasogolo pake. 19 Bana panga mpete zibili za golide naku zifaka pali ma kona yabili yenamgu yansali zapa chifuba mu mbali mwamukati mwama lile. 20 Bana panga futi mpete zibili za golide naku zigwilanisana kunyasi kwama gawo yabili yapama pewa yaku sogolo kwa efodi, pafupi na msoko pamwmba pa mumusana chopangiwa bwino a efodi. 21 Bana manga nsalu yapa chifuba na mpete zake kuma mpete ya efodi na ntambo ya bulu, kuti inkale yogwilana pa mwamba pa chamu musana chabwino cha efodi. Ivi venzeli chifukwa nyula yapa chifuba isa lekeko kuli efodi, ivi vinachitika monga Yehova analamulila Mose. 22 Bazalo anapanga mukanjo ya efodi nanyula ya bulu konse, nchito yabo tunga. 23 Yenzeli na poseguka pongenesela muli pakati poseguka panali potungika mumbali mose kuto isangamwike. 24 Pansi pamu soko, bana panga ma kanza ya bulu, pepo na redi na nsalu zopepuka. 25 Bana panga mabelo ya golide yoyela, naku faka ma belo pakati pama kanza kuzungulila kunyansi kwa mkano, pakati pamakanza. Belo namakanza- 26 belo na makanza munyasi mwa mukanjo kuti Aroni atumikilemo. Ichi chinali monga Yehova analamulila Mose. 27 Bana panga vovala pa mwamba nanyula yopepuka va Aroni nava bana bake bamuna. 28 Bana panga chisote chakumutu kusebenzesa nyula yopepuka, vowamisa kumutu va nyula yopepuka nsalu zovala mukati ya nyula yopepuka, 29 nachovala mumusana cha nsalu yopepuka naya bulu, na pepo naya chingwe cha redi, nchito yabo tunga. ichi chinali monga Yehova analmulila Mose. 30 Bana panga mbale yakolona yoyela nagolide yabwino, bana dindapo monga kulemba kwapa chidindo, "Oyela kuli Yehova." 31 Bana giwilanisana kulichovalakumutu na ntambo ya blue kumwamba kwa chovala kumutu. Ichi chenzeli monga Yehoa analamulila Mose. 32 Manje nchito yamu kachisi, yamu hema yokumanila, insila. Bantu ba Isilayeli bana chita vonse. Bana konka malangizo yamene Yehova anapasa Mose. 33 Banaleta kachisi kuli Mose-hema na vosebenzesa vonse mutanda, mafelemu, voimilila va kachisi na vapansi. Ku vininkila; 34 kwavikumba vankosa vadai ya redi, kuvininkila kwa kwachikumba chopepuka, nama ketani kuti kubisike 35 likasa ya umboni, nami tanda nachi valilo chachitetezo. 36 Bana leta tebulo, viya vonse, namu mukate wopezekapo; 37 poimilila nyali ya golidde yoyela na nyali yake mumi zela, votandizila na mafuta yamu nyali; 38 yachi golide guwa, mafuta yozoela na vonunkilisa cholelemba chapa komo pongenela mukadisi. 39 Guwa ya chisulo na bwalo ya chisulo natanda yake na viya na chidebe chitulu na chapansi chake. 40 Bana leta cholelemba chapa bwalo nama pasita yake na vapansi, nama ketani yapakomo pongenela mukoti ntambo zake nama pegesi ya hema navonse vo sebenzesa pogwila nchito yamu kachisi, hema yokumanilamo. 41 Bana leta mukanjo wopangiwa bwino yosebenzelako mu malo yoyela mukanjo yoyela ya Aroni wa nsembe na bana bake bamuna kuti bagwile nchito ngati ya wansembe. 42 Pamene apo bantu bamu Isilayeli bana chita zonse nchiito monga Yehova analamulila Mose. 43 Mose anafufuza nchito yonse, manje, onani, bana vichita. monga mwamene Yehova analamulila muli ichi bana chichita. Pamene apo Mose anaba dalisa
1 Pamene Yehova anakamba na Mose, kuti, 2 "Pasiku yoyamba ya mwezi yoyamba chaka chanyowani ukakonze kachisi, mu chihema chokumanlamo. 3 Ufunika kufakamo Likasayaumboni, ufunika kuchingiliza likasa na nsalu. 4 ufunika kubwelesa tebulo na kuikapo vintu vonse vofunikila bwino vamene vipezekapo. Chokonkapo ufunika kubwelesa choikapo nyale naku yasha nyale. 5 Ufunika kuika guwa yansembe ya golide pa likasa ya umboni, anso ufunika kuikapo nsalu pa lobela mu kachisi. 6 Ufunika kuika guwa yansembe vo shoka ku sogolo ko ngenela kwa kachisi, chihema chokumanilamo. 7 ufunika kuika chidishi chikulu pakati ka chihema yo sonkanilamo na guwa anso ufunia kuikamo manzi. 8 Ufunika kupanga mupanda bo yozungulila, anso ufunika ku pachikapo nsalu pa komo yamu panda. 9 Ufunika kutenga mafuta ozezela naku zoza kachisi na vonse vamene vipezeka mukati. Ufunika kuchipatula na vonse vipangizo kuli ine; pamene apo chizayela. 10 Ufunika kuzozoa guwa yansembe zopeleka na cipangizo vonse. Ufunika kupatula guwa kwa ine anso izankala yoyela kuli ine. 11 Ufunika kuzuzya dishi ya bronzi na pansi na kuipatulila ine. 12 Ufunika ku leta Aroni na bana bake bamuna kongenela ya chihema chokumanilamo anso ufunika ku basambika na manzi. 13 Ufunika kuvalika Aroni vovala vopatulika kuli ine, muzoze naku mupatula kuti atumikile monga wansembe wanga. 14 Mufunika kuleta bana bake bamuna na kubavalika vovala. 15 Ufunika kubazoza mwamene wazozela ba tate bao kuti bani tumikile monga bansembe. kuzozewa kwao kuzabapangila ubusa wachikalile kufikila mibadwo ya bantu bonse." 16 Ndiye vamene Mose anachta; anakonkamvonse vamene Yehova anamu'uza. anachita vintu vonse ivi. 17 Chakuti kachisi kana konzewa pasiku yoyamba yamwezi muchaka chibili. 18 Mose anapanga kachisi. anaika vonse malo mwake, nakazika makamwake, naimika mapulanga, namatanda, nausa mizati nz nsandamilaa zake. 19 Anayalika hema pamwa pa kachisi, naika chovininkila pamwamba pake, mwamene Yehova anamu'uzila. 20 Anatenga vokambilila va chipangano naku ika mu Likasa. Anaika mitengo pa likasa na chotetezela pamwamba. 21 Anabwela likasa mu kachisi, anaikapo nsalu yo chingiliza likasa ya umboni, mwamene Yehova anamu'uzila. 22 Anaika tebulo muhema yokumanilamo, kumbali ya kumpoto kwa kachisi, panja pa nsalu. 23 Anaika mukate pa tebulo pamenso ya Yehova, mwamdene Yehova anamulamulila. 24 Anafka choikapo nyali mu hema yokumainlamo, pasogolo yatebulo, ku mwela ya kachisi. 25 Anayasha malampu pamenso ya Yehova, mwamene mulungu enze anamulamulila. 26 Anaika guwa ya nsembe yopyeleza ya golide muhrma yosankanilanamo kusogolo kwa nsalu. 27 Anashokelapo nsembe zonunkila bwio, mwamene Mulungu analamulila. 28 Anapachika nsalu pakomomya kachisi. 29 Anaika guwa ya nsembe yo shoka pa komo ya kachisi, mu hema yokumanilanamo. Anaikapo nsembe yo shoka na nsembe yaunga, mwamene Mulungu anamu'uzila. 30 Anafaka dishi pakati ka hema yokumanilanamo na guwa, anaikamo manzi yosambila. 31 Mose, Aroni, na bana bake bamuna banasamba mumanja naku mendo yao muka dishi. 32 Ntawi iliyonse akayenda mu hema yokumanilanamo anso baka yenda ku guwa. Anali kuzisambika, mwamene Yehova anabauzila Mose. 33 Mose anamanga mupanda ozunguluka kachisi an guwa. Anaika nsalu pakomo ya mupanda, munjila iyi, Mose anasiliza nchito. 34 Pamene kumbi inavininkila chihema chokumanilanamo, anso ulemelelo wa Yehova unazaza kachisi. 35 Mose sanakwanise kungena muchihema chokumanilanamo chifukwa kumbi ina unankalapo, na chifukwa ulemelelo wa Yehova unazula kachisi. 36 Pamene paliponse kumbi ukachoka pa kachisi, bantu bamu Isilayeli banali kuyenda paulendo yao. 37 Koma ngati kumbi siyi nachokepo pa kachisi, nishi bantu kunalibe kuyenda. Banali kunkala paka siku inaza nyamuliwa. 38 Chifukwa kumbi ya Yehova inali pa kachisi ya muzuba, na mulilo wake unalipo usiku, pamenso ya bantu bonse bamu Isilayeli pa ulendo wabo onse.